Mmene Chivomezi Chimachitikira
Mmene Chivomezi Chimachitikira
“ANTHUFE TINAZOLOŴERA KUTI NTHAKA SIIGWEDEZEKA MOTERO NTHAKAYO IKAYAMBA KUGWEDEZEKA MAGANIZO ATHU AMASOKONEZEKERATU.”—LINATERO BUKU LA “THE VIOLENT EARTH.”
“ZIVOMEZI zili m’gulu la zinthu zowononga ndiponso zamphamvu kwambiri m’chilengedwe chonse,” linatero buku la World Book Encyclopedia. Mawu ameneŵa si okokomeza ayi, chifukwa chakuti mphamvu ya chivomezi chachikulu ingakhale yaikulu kwambiri kuŵirikiza ka 10,000 kuposa mphamvu ya bomba loyamba la nyukiliya. Komanso chowopsa kwambiri n’chakuti zivomezi zingachitike kwina kulikonse, panyengo iliyonse, ndiponso panthaŵi iliyonse m’kati mwa tsiku. Ndipo ngakhale kuti asayansi angadziŵe pang’ono chabe kumene kungachitike chivomezi, sangathe kunena mwatchutchutchu kuti chidzachitika liti.
Zivomezi zimachitika matanthwe aakulu akamasunthasuntha pansi panthaka. Zimenezi zimachitika nthaŵi zonse. Kungoti nthaŵi zambiri matanthweŵa akamasuntha sagwedeza dziko kwambiri moti mpaka nkumveka pamwamba panthaka, koma kugwedezekaku kungayezedwe pogwiritsa ntchito makina oyezera zivomezi. * Nthaŵi zina matanthwe ambiri amasweka ndipo akamasuntha nthaka imagwedezeka kwadzaoneni.
Koma kodi n’chifukwa chiyani dziko limagwedezeka nthaŵi zonse? Bungwe lolongosola za zivomezi lotchedwa National Earthquake Information Center (NEIC) linati “Funso limeneli lingayankhidwe ndi mfundo yolongosola kuti pansi padzikoli pali matanthwe aakuluakulu ogundizanagundizana amene amayendayenda, ndipo mfundo imeneyi yasintha maganizo a anthu ophunzira za mmene dziko lilili. Tsopano tikudziŵa kuti padzikoli pali matanthwe ogundizana asanu ndi aŵiri, ndipo n’ngogaŵikananso m’tizigawo tinanso ting’onoting’ono.” Bungweli linawonjezeranso kuti, “Zigawo zonsezi zimasuntha nthaŵi zonse mogwirizana ndi mmene zinagundizirana, pampata wotalikirana mamilimita 10 mpakana 130 pachaka.” Bungweli linanena kuti zivomezi zambiri, zimachitika m’zigawo zimene mwadutsa malire a matanthwe ameneŵa. M’zigawo zimenezi ndimo mmene zivomezi zazikulu 90 pa 100 zilizonse zingachitikire.
Kukula ndi Kuwononga Kwake
Kuopsa kwa chivomezi amakuyeza poona kukula ndi kuwononga kwake. Cha m’ma 1930 Charles Richter anakonza chida choyezera kukula kwa zivomezi. Nyumba zoyeza zivomezi zitayamba kuchuluka, anthu anapanga zida zina potengera nzeru za Richter. Mwachitsanzo palinso chida china chimene chimayeza pamene pachitika chivomezi kuti aone mphamvu ya chivomezicho.
N’zoona kuti zida zoyezera zimenezi sikuti nthaŵi zonse zimasonyeza mmene chivomezi chawonongera zinthu. Mwachitsanzo m’mwezi wa June mu 1994 ku Bolivia kunachitika chivomezi chimene atachiyeza chinafika pa 8.2 pa chida choyezera zivomezi, koma akuti chinangopha anthu asanu basi. Komano, mu 1976 mumzinda wa Tangshan, ku China munachitika chivomezi chaching’onopo chongokwana 8.0 basi koma chinapha anthu masauzande ankhaninkhani!
Mosiyana ndi kukula kwake, kuwononga kwa chivomezi kumasonyeza mmene chivomezi chimakhudzira anthu, nyumba, ndiponso chilengedwe. Njira imeneyi imasonyeza bwino mmene anthufe timaonera kukula kwa chivomezi. Chifukwatu nthaŵi zambiri kugwedezeka kwadziko pakokha sikuvulaza anthu. Koma anthu ambiri amavulazidwa ndiponso kuphedwa makoma akamagwa, zosungira gasi zikamaphulika kapena mawaya amagetsi akamaduka, ndiponso zinthu zosiyanasiyana zikamagwa.
Cholinga chimodzi cha akatswiri oyeza mphamvu ndi kukula kwa zivomezi ndicho kuchenjeza anthu mwamsanga chivomezi chisanachitike. Panopa ali mkati mokonza njira yapamwamba yoyezera zivomezi. Malingana ndi lipoti la wailesi yakanema ya CNN, akuti njira imeneyi pamodzinso ndi changu chake pokudziŵitsani zinthu komanso makompyuta amphamvu kwambiri, zithandiza kuti odziŵa za zivomezi “azitha kuona nthaŵi yomweyo madera amene chivomezi chagwedeza kwambiri.” Motero zimenezi zidzachititsanso kuti akuluakulu asamadzavutike popereka chithandizo ku madera amene awonongedwa.
N’zachionekere kuti kukonzekera chivomezi kungachepetse anthu ovulala, kungachepetse katundu wowonongeka ndipo chofunikanso kwambiri n’chakuti kungapulumutse anthu ambiri. Komabe zivomezi zikuchitikabe. Choncho funso n’lakuti: Kodi anthu athandizidwa bwanji kuti athane ndi mavuto obwera ndi zivomezi zimenezi?
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 4 Makina oyezera zivomezi amayeza n’kusonyeza mmene nthaka ikugwedezekera kukamachitika chivomezi. Makina oyamba otere anapangidwa m’chaka cha 1890. Masiku ano, padziko lonse pali malo opitirira 4,000 oyezera zivomezi amene amagwiritsa ntchito makina otere.
[Bokosi patsamba 19]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Kodi Zivomezi Zimachitika Kangati?
Mmene Amazitchulira Kukula Kwake Pachaka Mwina Zimakhalapo
Zazikulu Kwambiri 8 kapena kuposapo 1
Zazikulu 7 mpaka 7.9 18
Zazikulupo 6 mpaka 6.9 120
Zazikulu Mosaopsa 5 mpaka 5.9 800
Zazing’ono 4 mpaka 4.9 6,200*
Zazing’onopo 3 mpaka 3.9 49,000*
Zazing’ono Kwambiri Zosakwana 3.0 Zazikulu kuyambira pa
2 mpaka 3: pafupifupi
1,000 tsiku lililonse
Zazikulu kuyambira pa 1
1 mpaka 2: pafupifupi
8,000 tsikulililonse
* Mongoyerekeza.
[Mawu a Chithunzi]
Source: National Earthquake Information Center By permission of USGS/National Earthquake Information Center, USA
[Mawu a Chithunzi patsamba 18]
Seismogram pamasamba 18 ndi 19: Mwachiloleza cha Berkeley Seismological Laboratory