Mmene Zivomezi ndi Maulosi a Baibulo Zimakukhudzirani
Mmene Zivomezi ndi Maulosi a Baibulo Zimakukhudzirani
ASANAMWALIRE, Yesu analosera zinthu zimene zidzaikire umboni wakuti dzikoli lafika pa “mathedwe a nthaŵi ya pansi pano.” Iye anati, nthaŵi imeneyo, idzadziŵika ndi zinthu monga miliri, njala, ndiponso nkhondo zikuluzikulu. Iye ananenanso kuti kudzakhala “zivomezi zazikulu” zimene zidzachitike “m’malo akutiakuti.” (Mateyu 24:3, 7; Luka 21:10, 11) Kodi Yesu ankanena za masiku athu ano?
Ambiri amati ayi. Iwo amanena kuti zivomezi si kuti zayamba kuchuluka masiku ano. Kwenikweni, bungwe la U.S. National Earthquake Information Center linanena kuti zivomezi zambiri m’zaka za m’ma 1900 “zimangolekezera” pa 7.0 kukula kwake. *
Komabe zindikirani kuti sizolira kuti pakhale zivomezi zambiri kapena zamphamvu kuti tinene kuti ulosi wa Yesu uja wakwaniritsidwa. Yesu anangonena kuti kudzakhala zivomezi zazikulu m’malo akutiakuti. Komanso ananena kuti zimenezi zidzasonyeza “zowawa zoyamba.” (Mateyu 24:8) Simungayeze “zowawa” zimene anthu akumana nazo poŵerengetsera zivomezi kapena kuziyeza pa chida cha Richter, koma mumaona mmene anthuwo avutikira nazo.
N’zoona kuti zivomezi zabweretsa zowawa zambiri masiku ano. Ndipotu m’zaka za m’ma 1900, anthu mamiliyoni afa kapena nyumba zawo zawonongedwa ndi masoka ameneŵa. Akatswiri amanena kuti anthu akanatha kupeŵa imfa zambiri zoterezi. Bungwe lofalitsa nkhani la BBC linafalitsa nkhani yakuti, “Pofuna kuthana ndi vuto la kuchuluka kwa anthu m’tauni, m’mayiko osauka anthu nthaŵi zambiri samaganizira za malamulo aboma okhudza zakamangidwe kanyumba motero amangomanga nyumba zosadya ndalama komanso zosadya nthaŵi.” Pokambapo za masoka aŵiri amene anachitika posachedwa, Ben Wisner, amene ali katswiri wa masoka ochitika m’tauni, ananena kuti: “Si zivomezi zimene zinapha anthu ameneŵa. Anthuŵa anafa chifukwa cha kulakwitsa kwa anthu, kusoŵa chidwi, ziphuphu, ndiponso umbombo.”
Inde, nthaŵi zina zinthu zimene zimachititsa kuti anthu azifa kukachitika chivomezi ndizo khalidwe la anthu losaganizira ena ndiponso kunyalanyaza zinthu. N’zochititsa chidwi kuti makhalidwe ameneŵa amatchulidwanso mwapadera muulosi wina wa m’Baibulo wokhudza “masiku otsiriza” a nthaŵi ino. Baibulo la The Amplified Bible limati panthaŵi imeneyo, anthu adzakhala “omva zaokha, okonda ndalama,” ndiponso “opanda chisoni.” (2 Timoteo 3:1-5) Ulosi umenewu pamodzi ndi mawu a Yesu onena za mapeto a nthaŵi ino, umapereka umboni womveka bwino wakuti tikuyandikira nthaŵi imene Mulungu adzachititse kuti anthu ovutika maganizo, adzapumule kumva zowawa ndi zovutitsa zosiyanasiyana zamasiku ano, kuphatikizapo zivomezi zazikulu.—Salmo 37:11.
Kodi mungakonde kudziŵa zambiri zokhudza chiyembekezo cha m’Baibulo chimenechi? Pezani Mboni za Yehova zakwanuko, kapena lemberani kalata ku adiresi yoyenera imene ili patsamba 5.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 3 Anthu ena amanena kuti nkhani iliyonse yokhudza kuchuluka kwa zivomezi kwenikweni imakhalapo chifukwa chakuti sayansi yapita patsogolo, motero nthaŵi zambiri dziko likagwedezeka anthu amadziŵa.