Ndinapita Padera
Ndinapita Padera
LOLEMBA pa April 10, 2000, kunja kunali dzuŵa ndipo linali tsiku lotentha motero ndinaganiza zochokapo kuti ndikachite zina n’zina. Ndinali nditakwanitsa miyezi inayi ndili ndi pathupi, ndipo ngakhale kuti sindinkamva bwino m’thupi, ndinkasangalala popondapondako panja kuti ndipitidwe mphepo. Kenaka ndikudikirira pamzere kuti ndilipire zinthu zimene ndinali nditanyamula m’golosale, ndinayamba kumva kuti zinthu sizili bwino.
Ndinatsimikiza nditafika kunyumba kuti sizinali bwinodi. Ndinkatuluka magazi, ndipo zimenezi zinandichititsa mantha kwambiri chifukwa mimba imeneyi inali yachitatu ndipo zoterezi zinali zisanandichitikirepo kumbuyoku! Ndinaimbira telefoni adokotala, koma anati ndidikire kaye mpaka tsiku lotsatira chifukwa ndinali nditagwirizana nawo kale kuti ndidzaonana nawo tsiku limenelo. Ine ndi mwamuna wanga tisanapite kukagoneka ana athu aŵiriwo, tinapemphera kaye kuti Yehova atilimbitse mtima pa china chilichonse chimene chingatichitikire. Kenaka, patatha kanthaŵi ndithu, ndinagona tulo.
Koma cha m’ma 2 koloko usiku, ndinadzuka chifukwa cha ululu wosaneneka. Kenaka pang’ono ndi pang’ono ululuwo unazizira koma pamene ndinkati ndibenso katulo, ululuwo unayambiranso ndipo panthaŵi imeneyi unkati ukazizira nthaŵi yomweyo umayambiranso. Magazi aja anayambanso kutuluka ambiri, kenaka ndinazindikira kuti matenda anali atandiyamba. Ndinayamba kuunguzaunguza m’mutu mwanga ngati ndinali nditalakwitsa chinachake kuti zimenezi zichitike, koma sindinachipeze n’komwe.
Pokwana 5 koloko mmaŵa, ndinangodziŵiratu kuti ndifunika ndipite kuchipatala. Ine ndi mwamuna wanga titafika kuchipatalako, tinakhazikitsa mitima yathu pansi chifukwa chakuti anthu amene anatilandira anali anthu achifundo kwambiri, odziŵa kuthandiza anthu ndiponso omvetsa zinthu amene anali m’chipinda cha anthu odwala kwambiri. Kenaka patapita maola aŵiri, dokotala uja anatiuza nkhani imene tinkachita nayo nthumanzi kwambiri yakuti: Ndinali nditapita padera.
Chifukwa cha zimene zimandichitikira zija, ndinali nditakonzeka ndithu kuuzidwa zimenezi, choncho nkhaniyi sinandidzidzimutse kwambiri. Chinanso n’chakuti mwamuna wanga anali nane nthaŵi yonseyi ndipo ankandilimbitsa mtima kwambiri. Komano pakuti timabwerera kunyumba popanda mwana m’manja tinali ndi nkhaŵa yakuti nanga ana athu aŵiri, Kaitlyn yemwe ndi mtsikana wazaka zisanu n’chimodzi ndiponso David yemwe ndi mnyamata wazaka zinayi tikawauza chiyani.
Kodi Ana Athu Tiwauza Chiyani?
Ana athu anapita kukagona akudziŵa kuti chinachake sichili bwino, nanga kodi tiwauza bwanji kuti yemwe akanakhala mchimwene kapena mchemwali wawo anali atamwalira? Tinaganiza kuti tingonena zoona zokhazokha mosabisa mawu. Amayi anga anatithandiza pankhani imeneyi powauza anawo kuti ifeyo sitibwera ndi mwanayo kunyumba. Titafika, anawo anatithamangira ali ndi chimwemwe chosaneneka n’kufikira kutikupatira kwabasi. Chinthu choyambirira kufunsa chinali chakuti, “Kodi mwanayo ali bwino?” Ine sindinathe kuyankha, koma mwamuna wanga ndiye anayankha atatigwira kwambiri tonsefe n’kunena kuti: “Mwanayo wafa.” Tinagwirana tonse n’kuyamba kulira, ndipo kulirako kunathandiza kuti mitima yathu iyambe kukhala pansi.
Komabe sitinkadziŵa n’komwe mmene zidzawakhudzire ana athuwo m’tsogolo. Mwachitsanzo, patapita pafupifupi milungu iŵiri nditapita padera, kumpingo wathu wa Mboni za Yehova analengeza kuti Mboni ina yachikulire
yemwenso anali mnzathu kwambiri wamwalira. David amene ali ndi zaka zinayi anayamba kusisima mosatonthozeka, motero mwamuna wanga anam’nyamula kupita naye panja. Atakhazikitsa mtima wake pansi, David anafunsa kuti adziŵe chifukwa chimene mnzakeyo anafera. Kenaka anafunsanso chifukwa chake mwana wakwawo anafera. Kenakanso anafunsa bambo ake kuti: “Kodi inunso mudzafa?” Ankafuna kudziŵanso chifukwa chake mpaka panopa Yehova Mulungu sanamuwonongeretu Satana kuti ayambe “kukonza zinthu kuti zikhale bwino.” Kunena zoona, ife tinangoti kukamwa yasa podabwa ndi zimene mwana wamng’onong’onoyu anali kuganiza.Nayenso Kaitlyn anafunsa mafunso ambiri. Ankati akamaseŵera ndi zidole zake, nthaŵi zambiri ankayeseza kuti chidole china chikudwala ndipo zidole zina zimakhala ngati ndizo anthu odwazika matendawo kapena kuti achibale. Anapanga chikatoni chinachake kukhala chipatala cha zidolezo ndipo pakapita kanthaŵi ankayerekeza ngati chidole china chamwalira. Tinkapeza mipata yambiri yophunzitsa ana athu malangizo ofunika kwambiri pamoyo komanso mmene Baibulo lingatithandizire kupirira ziyeso chifukwa cha mafunso amene iwo ankafunsa ndiponso maseŵera amene ankachita. Tinawakumbutsanso za cholinga cha Mulungu chodzapanga dziko lapansi kukhala paradaiso wokongola, yemwe adzakhale opanda matenda ena alionse ndiponso chowawa china chilichonse, ngakhale imfa imene.—Chivumbulutso 21:3, 4.
Chimene Chinandilimbikitsa Nditapita Padera
Poyamba nditabwerera kunyumba kuchoka kuchipatala, mtima wanga unangoti zii ndiponso mutu wanga unasokonekera. Zinthu zoti ndichite zinangoti pwirikiti, ndipo ndinasoŵa poyambira. Ndinaimbira telefoni anzanga angapo amene anakumanapo ndi zotere ndipo anandilimbikitsa kwambiri. Mnzathu wina wapamtima anatitumizira maluŵa osonyeza kuti zinam’khudza kwambiri ndipo anadzipereka kutenga ana athu kuti akacheze nawo madzulo. Ndinayamikira kwambiri chifukwa cha kukoma mtima kwake komanso potithandiza.
Ndinaika bwinobwino zithunzi m’chibuku choikamo zithunzi. Ndinanyamula m’manja zovala zimene tinagula kuti azidzavala mwana wathuyo n’kumangoziyang’ana. Zovala zokhazi n’zimene zinali kundikumbutsa za mwana wanga amene anapitirirayo. Panatenga masabata angapo ndikumangovutika kwambiri ndi maganizo. Masiku ena ndinkangokhalira kulira, ngakhale kuti achibale ndiponso anzanga anali kundilimbikitsa kwambiri. Nthaŵi zina ndinkangoona ngati ndiyamba misala. Makamaka zinkandivuta kwambiri kukhala pakati pa anzanga amene anali ndi pathupi. Poyamba ndinkaganiza kuti mayi akapita padera silikhala vuto “losautsa” kwenikweni m’moyo mwake. Ha, n’kanadziŵa sin’kanatero! *
Chikondi Chawo Ndicho Chinandilimbikitsa Kwambiri
M’kupita kwa nthaŵi ndinayamba kuiwalako komanso zinthu zachikondi zimene mwamuna wanga ndiponso Akristu anzanga ankandichitira zinandilimbikitsa kwambiri. Mlongo wina anaphika chakudya n’kubwera nacho kunyumba kwathu. Mkulu wina wa kumpingo pamodzi ndi mkazi wake anabweretsa maluŵa ndiponso makadi osonyeza chikondi chawo ndipo anakhala nafe madzulo onse. Tinkadziŵa kuti anali otanganidwa kwambiri, choncho tinayamikira kwambiri chifukwa choti iwo anatiganizira. Anzathu ena ambiri anatitumizira makadi kapena maluŵa osonyeza chikondi chawo. Mawu ochepa chabe akuti “Timakuganizirani” ankatilimbikitsa kwambiri! Munthu wina wa kumpingo kwathu anatilembera uthenga wakuti: “Moyo timauona monga mmene Yehova amauonera, kuti ndi chinthu chofunika kwambiri. Ngati iye amadziŵa mpheta ikagwa, ndithudi ndiye kuti amadziŵanso mwana amene adakali mluza akafa.” Msuweni wanga analemba kuti: “Anthufe timadabwa kwambiri kuti kaya zimakhala bwanji kuti mpaka munthu abadwe n’kukhala ndi moyo, ndipo timadabwanso chimodzimodzinso mwana akabadwa ali wakufa.”
Nthaŵi inayake ndili ku Nyumba ya Ufumu patatha masabata angapo, chinachake chinandibwerera kumtima chofuna kulira ndipo ndinaona kuti panalibenso kuchitira mwina koma kungonyamuka basi msonkhano usanayambe. Anzanga apamtima aŵiri amene anaona kuti misozi yalengeza m’maso mwanga ananditsatira pamene ndinkatuluka n’kumapita m’galimoto ndipo anakakhala nane limodzi, ndiyeno n’kundigwira dzanja kenaka n’kumandichitira tinthabwala. Patangopita kanthaŵi kochepa chabe, tonse atatufe tinabwereranso. N’zosangalatsatu kukhala ndi ‘anzako oumirira kuposa mbale!’—Miyambo 18:24.
Nkhani yangayi itamveka patali, ndinali wodabwa podziŵa kuchuluka kwa Mboni zinzanga zimene zinakumanapo ndi tsoka lofanana ndi langali. Ngakhale ena amene poyamba sindinkadziŵana nawo bwinobwino anandipepesa ndiponso kundilimbikitsa. Chifukwa cha mmene anandithandizira ndili pa mavuto, anandikumbutsa mwambi wa m’Baibulo wakuti: “Bwenzi limakonda nthaŵi zonse; ndipo mbale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka.”—Miyambo 17:17.
Chilimbikitso Chochokera M’Mawu a Mulungu
Tsiku la Chikumbutso cha imfa ya Kristu linafika patatha sabata imodzi nditapita padera. Tsiku lina madzulo tikuŵerenga nkhani za m’Baibulo zokhudza masiku otsiriza a Yesu, zinangondibwerera m’mutu kuti: ‘Yehova amadziŵa mmene zimapwetekera ukaferedwa. Paja nayenso anaferedwapo mwana!’ Chifukwa chakuti Yehova ndi Atate wathu wakumwamba, nthaŵi zina ndimaiŵala kuti iye amamvetsa ndiponso kuti amamvera chisoni atumiki ake, aamuna ndi aakazi omwe. Nthaŵi imeneyo ndinachita kumva kuti mtima wanga wakhazikika. Ndinaona kuti Yehova amandikonda kwambiri kuposa mmene ndinkaonera kumbuyoku.
Mabuku ofotokoza za m’Baibulo, makamaka a Nsanja ya Olonda ndiponso a Galamukani! a m’mbuyomu amene analongosola nkhani zokhudza kuferedwa wokondedwa wanu anandilimbikitsanso kwambiri. Mwachitsanzo, nkhani za mu Galamukani! ya February 8, 1988, za mutu wakuti “Kuyang’anizana ndi Kutaika kwa Mwana” zinandithandiza kwambiri, monganso bulosha lakuti Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira. *
Kutha kwa Chisoni
M’kupita kwa nthaŵi, ndinaona kuti ndayamba kuiwalako, popeza kuti ndinkatha kuseka popanda kuganiza zambiri ndipo ndinkatha kulankhula ndi anzanga popanda kutchulako za mwana wanga amene anapitirirayo. Ngakhale zinali choncho, nthaŵi zina ndinkagwidwa chisoni kwambiri ndikaona anzanga amene anali asanamve kuti ndinali nditapita padera kapena ku Nyumba yathu ya Ufumu kukafika banja lina lokhala ndi mwana wakhanda.
Kenaka tsiku lina mmaŵa ndinadzuka ndili bwinobwino popandanso maganizo aja. Ngakhale panthaŵi imene ndinali ndisanatsegule maso, ndinaoneratu kuti zonse zatha tsopano, ndipo ndinali pamtendere umene ndinausoŵa kwa miyezi yambiri. Komabe nditatenganso pathupi patapita pafupifupi chaka chathunthu kuchokera pamene ndinapita padera, maganizo oti mwina ndikhoza kupitanso padera anandifikira. Koma n’zokondweretsa kuti ndinabereka mwana wamwamuna wathanzi m’mwezi wa October m’chaka cha 2001.
Chisoni chimandigwirabe chifukwa cha mwana amene ndinapititsa padera. Komabe nkhani yonseyi yachititsa kuti ndiziyamikira kwambiri moyo, banja langa, Akristu anzanga ndiponso Mulungu amene amatilimbikitsa. Zimene zinandichitikirazi zatsimikizira choonadi chogwira mtima chakuti Mulungu satenga ana athu koma kuti ‘nthaŵi ndi zochitika zamwadzidzidzi zimatigwera tonsefe.’—Mlaliki 9:11.
Ndimafunitsitsa kwambiri kudzakhalapo Mulungu akamadzathetsa chisoni chonse, kulira ndiponso chowawitsa chilichonse, ngakhalenso kupweteka ndi chisoni chobwera munthu akapita padera! (Yesaya 65:17-23) Kenaka anthu onse omvera adzakhoza kunena kuti: “Imfawe, chigonjetso chako chili kuti? Imfawe, mbola yako ili kuti?”—1 Akorinto 15:55; Yesaya 25:8.—Munthu wina anatitumizira nkhaniyi.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 13 Malinga ndi zimene akatswiri anafufuza zikusonyeza kuti anthu akapita padera zimawakhudza mosiyanasiyana. Anthu ena mutu wawo sugwira, ena amataya mtima, komanso ena amachita chisoni kwambiri. Ofufuza amati kulira n’kwachibadwa ndipo kumathandiza munthu kuiwala msanga pakachitika vuto linalake, monga kupita padera.
^ ndime 20 Ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Bokosi patsamba 29]
Kuchuluka kwa Anthu Opita Padera Ndiponso Zifukwa Zake
“Ofufuza amasonyeza kuti kuyambira amayi 15 mpaka 20 pa 100 alionse amene amawapeza kuti ali ndi pathupi mapeto ake amapititsa padera. Koma tsoka lalikulu loti wina angapititse padera limakhalapo pakangopita masabata aŵiri oyambirira mkazi akaima, ndipo imeneyi ndi nthaŵi imene azimayi ambiri samadziŵa n’komwe kuti ali m’pathupi,” linatero buku lotchedwa The World Book Encyclopedia.” Buku linanso linati amayi oposa “80 pa 100 alionse amapita padera m’kati mwa miyezi itatu yoyambirira ali ndi pathupi,” ndipo akuti n’kutheka kuti amayi osachepera theka lawo amapititsa padera chifukwa chakuti chinachake m’kati mwa mluza chimakhala chitapangika udyo. Si kuti mluzawo umapangika udyo chifukwa chakuti amayi kapena abambo a mwanayo ali ndi vuto m’thupi mwawo.
N’kuthekanso kuti mayi angapititse padera chifukwa chakuti sali bwino m’thupi. Madokotala amati kusokonezeka kwamphamvu zinazake za m’thupi, mphamvu yoteteza thupi kumatenda, matenda opatsirana ndiponso mavuto a m’chibelekero ndiwo amachititsa kuti mayi apititse padera. Matenda okhalitsa monga matenda a shuga (mukapanda kusamala nawo) ndiponso matenda a kuthamanga kwa magazi angachititsenso mayi kupititsa padera.
Malinga n’kunena kwa akatswiri, akuti si kuti mayi angapititse padera chifukwa chochita maseŵera olimbitsa thupi, kunyamula zinthu zolemera kapena kugonana. M’povuta kuti kugwa, kumenyedwa pang’ono ndi chinachake kapena kudzidzimutsidwa kungachititse mayi kupita padera. Buku lina linati: “M’povuta kuti mluza uvulale, pokhapokha ngati mayiyo wavulala modetsa nkhaŵa.” N’zoonekeratu apa kuti mimba imaikiradi umboni wakuti inapangidwa ndi Mlengi wanzeru ndiponso wachikondi!—Salmo 139:13, 14.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 31]
Mmene Achibale Ndiponso Anzanu Angathandizire
Nthaŵi zina wachibale kapena mnzathu akapita padera, mawu kapena chochita chimasoŵa. Anthu amakhudzidwa mosiyanasiyana akapita padera, choncho palibe njira imodzi yokha yowalimbikitsira ndiponso kuwathandizira. Komabe taonani malangizo otsatiraŵa. *
Zinthu zoyenera kuchitapo kuti muwathandize:
◆ Dziperekeni kuyang’anira ana awo amene ali aakulupo.
◆ Phikani chakudya n’kukachipereka kubanja limene laonekeredwa vutoli.
◆ Alimbikitseninso bambo a mwana amene wafayo. Bambo wina ananena kuti, “makampani sapanga makadi olimbikitsa azibambo amene ali m’mavuto otere.”
Zinthu Zothandiza Zimene Munganene:
◆ “Pepani kwambiri, ndamva kuti mwapita padera.”
Mawu okhaŵa akhoza kuthandiza kwambiri ndipo akhoza kukhala poyambira kulimbikitsa mayiyo.
◆ “Kulira sikulakwa.”
M’kati mwa masabata oyambirira mwinanso ngakhale miyezi imene, misozi siichoka m’maso mwa mayi akapita padera. M’tsimikizireni mayiyo kuti simukumuona ngati ndi munthu wosalimba mtima chifukwa chakuti akuchita kulira moonetsera.
◆ “Ndikuzondaninso sabata yamaŵa.”
N’kutheka kuti pamasiku oyambirira, anthu amene aonekeredwa vutoli pamakhala anthu ambiri odzawaona, koma m’kupita kwa nthaŵi, chisoni chawo chisanathe kwenikweni, akhoza kuona ngati anthu ena awaiŵala. Ndiye ndibwino kuti iwowo adziŵe zoti mukuwaganizirabe. Akhoza kukhalabe ndi chisoni kwa masabata angapo kapena miyezi imene. Mwina chisonichi chimadzayambanso mayiyo akatenga pathupi pena.
◆ “Choti ndinene kwenikweni chikundisoŵa.”
Kunena mawu amenewo kuli bwino kusiyana n’kungokhaliratu duu. Kunena kwanu mawu ameneŵa kochokera pansi pamtima komanso kukazonda woferedwawo zimasonyeza kuti zakukhudzanidi.
Zosayenera kunena:
◆ “Mukhoza kuberekaso mwana wina.”
Zimenezi zingakhaledi zoona, koma zikhoza kuoneka ngati n’kusoŵa chifundo. Si kuti makolo ake amafuna kuti akhale ndi mwana winayo ayi, iwo amafuna mwana yemweyo amene wapitirirayo. Asanayambe kuganiza zoti akhale ndi mwana wina, makolowo angafunike kulira kaye maliro a mwana amene wapitirirayo.
◆ “N’kutheka kuti mwanayo mwina anali ndi matenda enaake asanabadwe.”
Mawu ameneŵa angakhaledi oona, koma si mawu olimbikitsa ayi. Amayi a mwanayo amati akakhala, m’maganizo mwawo amangoti anyamula mwana wamoyo ndithu.
◆ “Koma zakhalabe bwino pang’ono popeza kuti simunam’dziŵe kwenikweni mwanayo. Zikanakhala zopweteka kwambiri mwanayo akanadzamwalira m’tsogolo.”
Azimayi ambiri amayamba msanga kugwirizana kwambiri ndi mwana wawo mwanayo asanabadwe n’komwe. Ndiye mwana woteroyo akapitirira, nthaŵi zambiri mayiyo amamva chisoni kwambiri. Chisoni chimenechi chimakulanso kwambiri chifukwa chakuti palibe munthu wina aliyense amene anali “kudziŵa” mwanayo ngati mmene amayi ake anali kum’dziŵira.
◆ “Chachikulu n’chakuti muli ndi ana ena.”
Makolo amene akulira mwana wawo, kumva mawu ameneŵa kungafanane n’kuuza munthu winawake amene waduka mkono kapena mwendo kuti: “Chachikulu n’chakuti mwatsala ndi mkono kapena mwendo wina.”
Inde, n’zoona kuti tiyenera kudziŵa kuti munthu aliyense ngakhale wabwino chotani, nthaŵi zina amanena zinthu zosayenera. (Yakobo 3:2) Choncho, azimayi ozindikira amene anapita padera afunika kuonetsa chikondi cha Chikristu ndipo sayenera kusunga chakukhosi anthu osadziŵa kulankhula bwino akamanena mawu osayenera pofuna kuwalimbikitsa.—Akolose 3:13.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 36 Malangizoŵa tawatenga m’buku lakuti A Guide to Coping With Miscarriage, limene linalembedwa ndi gulu lothandiza anthu amene anapita padera lotchedwa Miscarriage Support Group la mumzinda wa Wellington, ku New Zealand.