Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chakudya Chopatsa Thanzi N’chosasoŵa

Chakudya Chopatsa Thanzi N’chosasoŵa

Chakudya Chopatsa Thanzi N’chosasoŵa

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU MEXICO

ANGÉLICA amene m’banja mwawo alipo anthu okwanira khumi ankakhala m’tauni inayake yaing’ono m’boma la Oaxaca, ku Mexico. Iwo anali amphaŵi, ndipo chakudya chawo chinali zitumbuwa, nyemba, msuzi wothira tsabola wa kamphiripiri, phala la mpunga lamadzimadzi, zimimina ndiponso tiyi. Angélica ananena kuti, “Tinakula mokwinimbira, ndipo tinali oonda kwambiri. Tinkangodwaladwalanso m’mimba, tinkakhalanso ndi tizilombo tina tolumaluma m’thupi ndiponso chimfine.”

Angélica pamodzi ndi onse a m’banja mwawo anaganiza zosamukira kumzinda wotchedwa Mexico City pofuna kukapeza ntchito imene ikanachepetsa umphaŵi wawowo. Iye akukhulupirira kuti chakudya chawo chili bwinopo tsopano chifukwa chakuti amadya zinthu monga mkaka, mazira, nyama, mkaka wamafuta okhathamira, masamba osiyanasiyana ndiponso zakudya zina zosiyanasiyana zopangidwa ku fakitale. Koma kodi anayambadi kudya chakudya chopatsa thanzi?

Kodi Vuto la Kusadya Bwino N’lofala Motani?

Padziko lonse n’kutheka kuti anthu okwana 800 miliyoni angadzafe chifukwa chosoŵa zakudya zamagulu m’thupi. Bungwe la World Health Organization (WHO) linalemba lipoti m’chaka cha 1998 lakuti pafupifupi theka la ana amene amafa pakati pa ana azaka zosapitirira zisanu amafa chifukwa cha vuto losoŵa zakudya zamagulu m’thupi mwawo. Ngakhale ena amene amapulumuka, nthaŵi zambiri amakhala onyentchera.

Komanso panthaŵi yomweyomweyo, akuti pali anthu okwana 800 miliyoni amene mwina adzafa chifukwa cha kudya mopitirira muyeso. Kudya kwambiri kukhoza kudwalitsa munthu matenda okhalitsa onga kunenepa mopitirira muyeso, kutsekeka mitsempha chifukwa cha mafuta ambiri, kuthamanga kwa magazi, matenda ashuga, kuwonongeka chiwindi ndiponso mitundu yosiyanasiyana ya kansa. Mwachidule, bungwe la World Health Organization linati: “Motero vuto la kusadya bwino limaphatikizaponso mavuto ena ambiri, monga kudya mopereŵera, kusoŵeka kwa mbali inayake ya chakudya chamagulu m’thupi komanso kudya mopitirira muyeso; ndipo kumapha, kumawononga thupi, kumagodomalitsa, kumapundula, kumayambitsa khungu ndipo kumalepheretsa anthu ambiri kutukuka padziko lonse.”

N’kutheka kuti m’dziko limodzi lomwelo anthu ena angakhale onyentchera ndipo ena onenepa mopitirira muyeso. M’nyumba imodzi yomweyo, mungakhale ana ena odwala matenda opereŵera zakudya m’thupi komanso mungakhale akuluakulu amavuto okhalitsa a kunenepa mopitirira muyeso. Nthaŵi zina zimatheka kuti munthu mmodzimodzi yemweyo amene anali wonyentchera adakali mwana amadzakhala wonenepa kwambiri atakula. Zimenezi zimatha kuchitikira anthu amene asamuka kuchoka kumudzi kupita kutauni.

Anthu ambiri samvetsa kuti thanzi lawo limawonongeka ngati sadya bwino. Mwina n’chifukwa chakuti vuto limene limabwera chifukwa chosadya zakudya zamagulu silionekera msanga. Koma chakudya chamagulu chimateteza matenda ambiri. Ndipotu bungwe la WHO limati mwina anthu okwana 40 pa 100 alionse amene amadwala kansa sibwenzi akudwala matendaŵa ngati akanamadya chakudya chamagulu ndiponso akanamachita maseŵera olimbitsa thupi. Koma kodi mungatani kuti chakudya chanu chikhale chamagulu?

Zimene Mungachite Kuti Chakudya Chanu Chikhale Chamagulu

Anthu ena amaona kuti kwenikweni chakudya chili m’magulu atatu. Gulu loyamba limakhala ndi zakudya monga chimanga, tirigu, mpunga, mapira ndi mcheŵere komanso zakudya monga mbatata, chinangwa, chilazi ndi zakudya zina zotere. Zakudya zopatsa mphamvu zimenezi zimalimbitsa thupi mofulumira. Gulu lachiŵiri limakhala ndi zakudya monga nyemba, soya, nandolo, nsawawa, kamumpanda, ndi zakudya zina monga nyama, nsomba, mazira, ndi mkaka komanso zakudya zopangidwa kuchokera ku mkaka. Zakudya zimenezi zimathandiza kumanga thupi, kuwonjezera magazi ndiponso zili ndi mavitamini enanso ambiri othandiza m’thupi. Gulu lachitatu ndi la zipatso ndi ndiwo za masamba. Zakudya zimenezi zimakhala ndi mavitamini ofunika kwambiri m’thupi. Zimathandizanso pogaya zakudya m’thupi ndiponso potipatsa mphamvu, ndipo ndi zokhazi zimene zili ndi vitamini C wachibadwa.

Dr. Héctor Bourges, yemwe ndi mkulu wa bungwe loona za chakudya chamagulu la Salvador Zubirán National Institute of Nutrition (INCMNSZ) ku Mexico, anati chakudya chabwino chiyenera kukhala chamagulu onse atatu, chokwanira ndiponso chopatsa thanzi. Iye anati ndibwino kuti pachakudya chathu “pasamalephere kupezeka chakudya china chochokera kumagulu onse atatu koma tizichita kasinthasintha wa zakudya za m’gulu lililonse, komanso tizizisinthasintha kaphikidwe kake.”

Tangoganizirani nkhani iyi ya María. Iye pamodzi ndi anthu a m’banja mwawo ankakhala m’mudzi winawake wotchedwa Atopixico, m’dziko la Hidalgo ku Mexico. Iwo anali amphaŵi adzaoneni, ndipo chakudya chimene ankadya nthaŵi zambiri chinali zitumbuwa, nyemba, samusa ndi tsabola wakamphiripiri. Mosiyana ndi banja la Angélica uja tam’tchula poyamba paja, banjali linkadyanso mphonda, zakudya zina zangati mavwende, bowa, ndiponso ndiwo zina zakutchire, ndipo zambiri mwa zimenezi zimatengedwa kumidzi. Kaŵirikaŵiri iwo ankayesetsa kupeza zipatso zosiyanasiyana nyengo yake ikakwana. Khama lawolo linawathandiza kuti akhale athanzi.

Dr. Adolfo Chávez, yemwe ndi mkulu wa dipatimenti ya maphunziro a chakudya chathanzi m’bungwe la INCMNSZ anati ndibwino kudya ndiwo zankhwiru pamodzi ndi zakudya zina, osati kuti zimenezi pazokha ndizo zizikhala ndiwo za chakudyacho ayi. Mwachitsanzo, mukhoza kuphika ndiwo zosakaniza timazira ndi mbatatesi, ndiwo zamasamba kapena nyemba. Dr. Chávez anati, “Kutereku n’kumene [pamaphunziro a] zakudya zopatsa thanzi amakutcha ‘kutupitsa zakudya.’” Komabe ndibwino kuonetsetsa kuti: Nthaŵi zonse mwatsuka bwinobwino zipatso ndiponso ndiwo zamasamba, makamaka zimene mukufuna kudya zili zosaphika.

Chakudya chiyeneranso kuti chikhale chokomera munthu wina aliyense, ndipo zinthu monga zaka, kaya kuti munthuyo ndi wamkazi kapena wamwamuna, ndiponso mmene amakhalira m’moyo wake muyeneranso kuziganizira. Akakhala anthu aakulu, ena amaona kuti ndibwino kudya zipatso kapenanso ndiwo zamasamba zokwanira akamadya, ndipo pazipezekanso zakudya zopatsa mphamvu ndi zina za m’gulu la nyemba. Anthu ena amati ndibwino kusadya kwambiri nyama, koma muzidya nsomba, nyama ya nkhuku yochotsa chikopa, ndiponso nyama yopanda mafuta ambiri. Akutinso ndibwino osadya zakudya zamafuta ndiponso zotsekemera kwambiri.

Ngakhale anthu amene amakhala m’mayiko osauka komanso ali paumphaŵi, nthaŵi zina akhoza kumadya chakudya chamagulu. Angatero motani? Angatero posankha zakudya zopatsa thanzi ndi kuzisakaniza pamodzi, kudya zakudya monga mtakula wosakaniza ndi nyemba. Pogwiritsa ntchito kanyama kapena timazira kuti chakudya chikomerekomere ndi kupatsa thanzi. Posalekerera ndiwo zamasamba zimene zimamera m’dera lanulo ndipo pomadya zipatso za panyengo imeneyo.

Mlengi wathu amachititsa kuti ‘chakudya chichokere m’nthaka’ kuti anthu azichidya. (Salmo 104:14) Pa Mlaliki 9:7, Baibulo limati: “Tiye, idya zakudya zako mokondwa.” Mosakayikira konse, tikachita zinthu mosamala ndiponso mwanzeru, tikhoza kupindula ndi chakudya chopatsa madyo ndiponso chopatsa thanzi chimene Mlengi wathu watipatsa.

[Chithunzi patsamba 11]

GULU LOYAMBA: zakudya zam’gulu la chimanga, mapira, mbatata, chinangwa ndi zina zotere

[Chithunzi patsamba 11]

GULU LACHIŴIRI: zakudya zam’gulu la nyemba, nyama, nsomba, mazira, ndiponso mkaka ndi zina zopangidwa kuchokera ku mkaka

[Chithunzi patsamba 11]

GULU LACHITATU: zipatso ndi ndiwo zamasamba