Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chakumwa Chokonkha Kukhosi Chochokera ku Chitsamba Chachilendo

Chakumwa Chokonkha Kukhosi Chochokera ku Chitsamba Chachilendo

Chakumwa Chokonkha Kukhosi Chochokera ku Chitsamba Chachilendo

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU NIGER

KODI mumakonda kumwa zinazake zoziziritsa kukhosi kunja kukatentha? Mabanja ambiri a ku West Africa amakonda chakumwa chokonkha kukhosi chokopa m’maso, chokoma kwambiri, chopatsa thanzi ndiponso chamtengo wosaboola m’thumba komanso, chopangidwa kuchokera ku chitsamba. Chakumwachi amati dzina lake ndi bissap, ndipo chitsamba chokhala ndi maluŵa chimene amapangira chakumwachi chili m’gulu la therere lobala ndipo chimapezeka kumadera otentha. Chitsambachi chimatha kutalika kufika mpaka mamita aŵiri kapena kuposa. M’madera osiyanasiyana amadzala chitsambachi koma makamaka m’madera ouma amene amapezeka m’mayiko monga Niger, Mali ndiponso Senegal.

Mmene Amapangira Chakumwachi

Amatenga zakunja kwamaluŵa zodzaza supuni yaikulu imodzi n’kuziika m’madzi okwana pafupifupi wani lita. Akatero amaziŵiritsa pamoto kenaka n’kuzisiya kuti ziloŵererane bwinobwino kwa mphindi 15 kapena 20. Amasefa timaluŵa tija n’kutichotsa m’madzimo, ndipo amamwa chakumwacho ngati tiyi chidakali chamoto kapena chitazizira, mwina atathiramo shuga kapena opanda shuga. Koma lero tikufuna tipange chakumwa chozizira chimene ana angachikonde, choncho tithiramo shuga. Mabanja ena akamapanga chakumwa chimenechi amathiramonso tokometsera tinatake. Chakumwa chozizirachi, chooneka chofiira kwambiri amachiika m’timatumba tapulasitiki toonekera m’kati mwake, kenaka amatimanga kukamwa kwake. Apa ndiye kuti zonse zatha tsopano, kwangotsala n’kugaŵira ana amene ali ndi ludzu kuti akonkhe kukhosi! Anawo amaboola pakona pa kathumbako kwinaku ali mwee kusangalala ndi chakumwa chawo chapamtima. Inde, ena amakonda kumwera chakumwachi m’tambula.

Kuwonjezera pakukoma kwa chakumwachi, akuti chimathandizanso kwambiri m’thupi mwanu. M’chakumwachi mumapezeka zinthu zothandiza kulimbitsa mafupa, kuwonjezera magazi, chili ndi mavitamini A ndi C, ndi zinanso zambiri! Anthu ena amati chakumwachi chimathandizanso kuti munthu asadzimbidwe, azitha kutaya madzi mosavutikira, ndiponso chimathandiza kuti chiwindi chizigwira bwino ntchito yake. Inde chitsambachi n’chabwinodi, ndipo ndifetu okondwa kwambiri kuti ngakhale chili chokongola kwambiri ukamachiona, icho chimatipatsanso chakumwa chokonkha kukhosi chomwenso n’chopatsa thanzi kwambiri!

[Mawu a Chithunzi patsamba 31]

Chojambulidwa ndi Kazuo Yamasaki