Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chinthu Chofunika kwa Tonse

Chinthu Chofunika kwa Tonse

Chinthu Chofunika kwa Tonse

MUMAFUNIKA CHAKUDYA. Mumafunika madzi. Mumafunika mpweya. Mumafunika malo abwino okhala ndiponso okutetezani ngati kunja sikunache bwino. Izi ndi zinthu zofunika kwa tonsefe ndiponso kwa zamoyo zambiri za padziko pano. Komabe, pali chinthu chimodzi chofunika kwa anthu okha basi. Kodi ndicho chiyani?

Reginald W. Bibby wa ku Canada, yemwe ndi katswiri wa zachikhalidwe cha anthu analemba kuti: “Pali zinthu zimene anthu amafunika, zopezeka ku chipembedzo kokha basi.” Ndipo magazini ya American Sociological Review ya February 2000, inafalitsa nkhani imene inanena kuti: “Anthu sadzasiya kufuna kupembedza.”

Inde, m’mbiri yonse, anthu akhala akufuna kulambira. Kwa zaka mazana ambiri anthu ambiri aloŵa m’magulu achipembedzo kuti achite zimenezi. Koma masiku ano zinthu zasintha. M’mayiko ambiri olemera monga kumpoto kwa America ndi kumpoto kwa Ulaya, anthu ambiri zedi akuchoka m’matchalitchi awo. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti anthu adzasiyiratu kupembedza? Ayi, sizikutanthauza choncho.

Nyuzipepala ya ku Sweden ya Svenska Dagbladet inanena kuti: “Anthu akukokomeza kwambiri nkhani ya kutha kwa kupembedza.” Kodi n’chiyani chikutenga malo a matchalitchi amakolo? Nyuzipepalayi inapitiriza kunena kuti: “Masiku ano anthufe sitikhala ndi chipembedzo chathu chenicheni. Koma, timasankha zinthu zimene tikufuna m’zipembedzo zosiyanasiyana za padziko n’kukhala zikhulupiriro zathu. . . . Zingathe kukhala zinthu monga kuchiritsa ndi miyala ya mtengo wapatali ndiponso kuvala mikanjo ya Amonke achibuda. Mukatopa nazo ziphunzitso zimene munasankhazo, mungasankhe zina zomwe mungagwirizane nazo.”

Ofufuza zachikhalidwe cha anthu pankhani ya kupembedza amati chizoloŵezi chimenechi ndi “chipembedzo chawekha” kapena “chipembedzo chosaoneka.” Bibby, katswiri wa zachikhalidwe cha anthu amene wagwidwa mawu pamwambayo, anapeka mawu akuti “chipembedzo chogwirizana ndi zokonda za munthu.” Ena zikhulupiriro zimenezi amati ndi “zokomera munthu aliyense payekha.” Panopo m’mayiko ena amene Chikristu chinazika mizu, gulu lalikulu la chipembedzo ndi la anthu amene amapemphera paokha.

Onani zimene anapeza atafufuza m’dziko la Sweden, limene ndi limodzi mwa mayiko osapembedza kwambiri. Pa kufufuzapo anapeza kuti anthu aŵiri mwa anthu atatu alionse ankati ndi Akristu opembedza “paokha.” Ena ananena kuti: “Ndili ndi chikhulupiriro changa pankhani yachikristu,” “Sindimasuka m’tchalitchi,” “Sindikonda kupita kutchalitchi kukamvera zonena za azibusa,” kapena “Ndikhoza kupita m’chipinda changa n’kukapemphera pandekha.” Ambiri ankakhulupirira kuti munthu amakabadwanso kwinakwake akamwalira kapena kuti Mulungu analemberatu zimene zimachitikira anthu. Anthu ambiri anati amakhulupirira kuti pali mphamvu inayake ya Mulungu koma sangathe kuifotokoza.

Pa kufufuza kwinanso anapeza kuti anthu ambiri amaona kuti amapembedza bwino akapita kwinakwake n’kumakayang’ana chilengedwe. Mtsikana wina yemwe ndi mlimi anati: “Ine ndimaona kuti ukakhala kutchire, m’pamene umam’yandikira kwambiri Mulungu.” Munthu wina amene ankadziona kuti ndi wosapembedza atafunsidwa anati: “Ndikapita ku nkhalango, ndimaona ngati ndili m’kachisi wamkulu zedi. . . . Ndipo sindidziŵa amene amayang’anira kachisi ameneyu, koma ndimadziŵa kuti pali amene amayang’anira.” Ena anafotokoza kuti malo amene kuli zachilengedwe ndi malo oyera, opatulika kwa Mulungu ndiponso odzetsa nthumanzi ndipo amati kukhala m’malo ameneŵa kumawapatsa mphamvu, mtendere ndiponso kuwakhazika maganizo pansi. Mwachidule, wofufuza wina anamaliza lipoti lake motere: “Zili ngati kuti Mulungu anasamukira kutchire.”

Masiku ano zimenezi zafala m’mayiko ambiri padziko lapansi. Thomas Luckmann, katswiri wa ku America wa zachikhalidwe cha anthu pankhani ya chipembedzo, ananena kuti m’madera olemera anthu asiya kupembedzera m’tchalitchi ndipo ayamba “chipembedzo chogwirizana ndi moyo wawo.” Anthu amasankha mfundo zachipembedzo zoti azitsatira pa moyo wawo n’kuziphatikiza ndi mfundo zina zogwirizana ndi mmene iwowo amafunira kupembedza.

Mungafunse kuti, ‘Kodi zipembedzo zodziŵika bwinozi komanso matchalitchi zayamba kutha mphamvu? Ngati ndi choncho, chifukwa chiyani?’ Mafunso ameneŵa tikambirana m’nkhani yotsatira.

[Chithunzi patsamba 19]

Wofufuza wina anathirira ndemanga pa khalidwe la masiku ano lopembedza zachilengedwe ponena kuti: “Zili ngati kuti Mulungu anasamukira ku nkhalango”