Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Amavomereza Nkhondo?

Kodi Mulungu Amavomereza Nkhondo?

Lingaliro la Baibulo

Kodi Mulungu Amavomereza Nkhondo?

SITINGAKWANITSE n’komwe kuŵerengera nthaŵi zimene akuluakulu ankhondo, olamulira, ngakhalenso ansembe, akhala akulengeza kapena kusainira nkhondo m’dzina la Mulungu. M’chaka cha 1095, gulu la Matchalitchi Achikristu linayamba ulendo wopita kokalandanso “Mzinda Woyera” wa Yerusalemu pa Nkhondo Yoyamba ya Pakati pa Akristu ndi Asilamu, movomerezedwa ndi Papa Urban wachiŵiri. Koma asanachite zimene ankafunazo, Asilamuwo, amene ankakhulupirira kwambiri Allah mofanana ndi mmenenso Akristuwo ankakhulupirira Utatu, anamenya nkhondo molapitsa mpaka kupheratu anthu onse a m’gulu lina la Akristuwo.

M’mwezi wa August chaka cha 1914, mnyamata wina wa ku Germany analemba ali mu tenti yake ya kunkhondo kuti: “Ngati amene amatsogolera zochita za anthu alidi Mulungu, ndiye kuti amene ayenera kupambana pankhondoyi, ndi ifeyo basi. Ndipo ine sindikukayika n’komwe kuti Mulungu ndiyedi amatsogolera zochita za anthu.” M’mwezi womwewo, Mfumu Czar Nicholas yachiŵiri inatumiza gulu la asilikali a ku Russia lokathira nkhondo ku Germany, kwinaku ikulengeza kuti: “Kuchokera pansi pamtima ndikukufunirani zabwino zonse inu asilikali anga olimba mtima ndiponso anzanga ena onse amene akutithandiza kuti tipambane. Mulungu alinafe!”

Atawalimbitsa mtima motere, asilikali ochuluka zedi akhala akupita kunkhondo ndi chikhulupiriro chonse chakuti Mulungu ali mbali yawo. Anthu ambiri amaganiza kuti Mulungu amalola kumenyana kotere chifukwa amati kumenyanako n’kofunika kuti pakhale mtendere, ndipo amatinso umboni wa zimenezi ndi nkhondo zimene zinalembedwa m’Malemba Achihebri (amene anthu ambiri amati Chipangano Chakale). Kodi kutanthauzira kwawo Mawu a Mulungu n’kolondola?

Nkhondo za ku Israyeli Wakale

Yehova Mulungu analamula kuti Aisrayeli achite nkhondo kuti m’Dziko Lolonjezedwa musapezekenso Akanani omwe anali anthu ochita zinthu zoipa. (Levitiko 18:1, 24-28; Deuteronomo 20:16-18) Mulungu analanga anthu ochita zoipa m’masiku a Nowa pogwiritsa ntchito madzi ndiponso anawononga Sodomu ndi Gomora pogwiritsa ntchito moto, moteronso, iye anagwiritsa ntchito mtundu wa Aisrayeli kuti ukhale monga chida chake chophera anthu.—Genesis 6:12, 17; 19:13, 24, 25.

Baibulo limati Aisrayeli anamenya nkhondo zina polamulidwa ndi Mulungu, makamaka n’cholinga chothamangitsiratu adani amene akanatha kuwaukira m’tsogolo. Mtunduwo ukamvera Yehova, nkhondo zimene unali kumenya zinali kuwayendera bwino. (Eksodo 34:24; 2 Samueli 5:17-25) Koma kaŵirikaŵiri tsoka linkakhalapo Aisrayeli akalimba mtima kumenya nkhondo mosiyana ndi malangizo a Mulungu. Taganizirani zimene zinachitikira Mfumu Yerobiamu. Ponyalanyaza chenjezo limene anauzidwa mwachindunji ndi mneneri wina, iye anatumiza gulu lalikulu lankhondo kuti likachite nkhondo ya pachiŵeniŵeni youkira fuko la Yuda. Kumenyanako kutatha, n’kuti ankhondo a Yerobiamu okwanira 500,000 ataphedwa. (2 Mbiri 13:12-18) Ngakhale Yosiya amene anali mfumu yokhulupirika analoŵerera nkhondo yaŵeni, ndipo kuthamanga maganizo kotereku kunam’phetsa.—2 Mbiri 35:20-24.

Kodi nkhani zonsezi zikusonyeza chiyani? Zikusonyeza kuti m’dziko lakale la Aisrayeli, Mulungu ndiye anali kulamulira kuti kukhale nkhondo. (Deuteronomo 32:35, 43) Iye anali ndi zifukwa zake zimene ankafunira kuti anthu ake achite nkhondo. Ndipotu, zimene ankafunazo zinakwaniritsidwa kalekale. Komanso Yehova ananeneratu kuti anthu amene azidzam’tumikira mu “masiku otsiriza” ano “adzasula malupanga awo akhale zolimira  . . . ndipo sadzaphunziranso nkhondo.” (Yesaya 2:2-4) Apa n’zoonekeratu kuti munthu sanganene kuti nkhondo za m’Baibulo zimasonyeza kuti nkhondo zamakono n’zabwino, ndipo masiku ano palibe nkhondo zimene zikumenyedwa motsogoleredwa ndi Mulungu kapena mochita kulamulidwa naye.

Zotsatirapo za Kuphunzitsa kwa Kristu

Yesu ali padziko lapansi anasonyeza mmene tingathetsere chidani n’kukhala ndi chikondi chopanda mpeni kumphasa polamula kuti: “Mukondane wina ndi mnzake, monga ndakonda inu.” (Yohane 15:12) Iye anatinso: “Odala ali akuchita mtendere.” (Mateyu 5:9) Palembali, m’Chigiriki akamati “akuchita mtendere” amatanthauza zambiri, osangoti kukhala womasuka m’maganizo. Kwenikweni amatanthauza kulimbikira kuchita zinthu zosonyeza mtendere, kuchita khama kwambiri kufunira ena zabwino.

Pamene Yesu ankamangidwa, mtumwi Petro anayesetsa kuti amuteteze pogwiritsa ntchito chida chophera anthu. Koma Mwana wa Mulungu anam’dzudzula mwamphamvu pomuuza kuti: “Tabweza lupanga lako m’chimakemo, pakuti onse akugwira lupanga adzawonongeka ndi lupanga.” (Mateyu 26:52) Kodi Akristu a m’zaka za zana loyamba anawagwiritsa ntchito motani mawu amenewo? Taonani mawu otsatiraŵa amene anthu ena ananena.

“Titayang’ananso bwinobwino m’mabuku onse amene alipo, [zikusonyeza] kuti pofika nthaŵi imene Marcus Aurelius anakhalapo [kuyambira chaka cha 121 mpaka 180 C.E.], panalibe Mkristu amene anakhalapo msilikali wankhondo; ndipo panalibe msilikali wankhondo amene anapitiriza kugwira ntchito yake atatembenuka kukhala Mkristu,” zimenezi zinalembedwa m’buku la The Rise of Christianity.

Buku lakuti Our World Through the Ages linati, “Khalidwe la Akristu [oyambirira] linali losiyana kwambiri ndi khalidwe la Aroma. . . . Chifukwa Kristu anali atalalikira za mtendere, iwo anakana kukhala asilikali ankhondo.”

Aroma anapha ophunzira a Kristu ambiri chifukwa chakuti anakana kukhala m’gulu la asilikali a mfumu. N’chifukwa chiyani Akristuwo ankachita zinthu zimenezi zimene zinali zosemphana ndi maganizo a anthu ambiri? Chifukwa chakuti Yesu anawaphunzitsa kuti akhale ochita zamtendere.

Nkhondo Zamakono

Tangoganizirani mmene zinthu zikanaipira otsatira Kristu akanati azimenyana m’magulu ankhondo pofuna kuphana. Zoterezi sizikanagwirizana n’komwe ndi mfundo zachikristu. Ndithudi, anthu amene amamvera Mulungu amene analemba Baibulo sangavulaze munthu aliyense, ngakhale adani awo. *Mateyu 5:43-45.

N’zoonekeratu kuti Mulungu sadalitsa nkhondo zamakono zimene anthu amachita. Choncho, chifukwa chokhala anthu amtendere, Akristu enieni amalimbikitsa mtendere umene udzakhalepo padziko lonse mu Ufumu wa Mulungu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 17 Baibulo limati pali “Harmagedo,” imene imatchedwanso kuti “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse.” Imeneyi si nkhondo ya anthu ayi, koma ndi nkhondo yochita kusankha imene Mulungu adzawonongere anthu ochita zoipa okha. Motero anthu sayenera kuganiza kuti chifukwa chakuti kuli Harmagedo ndiye kuti nkhondo zamasiku ano n’zabwinonso kapena kuti Mulungu amadalitsa nkhondozi.—Chivumbulutso 16:14, 16; 21:8.

[Chithunzi patsamba 29]

Wansembe wachipembedzo cha Greek Orthodox akudalitsa asilikali ankhondo asananyamuke ulendo wawo wopita ku Kosovo pa June 11, 1999

[Mawu a Chithunzi]

Chithunzi cha U.S. National Archives

[Chithunzi patsamba 29]

Mkulu wa ankhondo, Francisco Franco wa ku Spain ataima ndi ansembe angapo achikatolika

[Mawu a Chithunzi]

AP Photo/Giorgos Nissiotis