Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kulimbikitsa Amene Akulira Maliro

Kulimbikitsa Amene Akulira Maliro

Kulimbikitsa Amene Akulira Maliro

ZOOPSA zimene zigaŵenga zinachita pa September 11, 2001, ku New York City ndiponso ku Washington, D.C., zinachititsa nthumanzi anthu ambiri padziko lonse lapansi. Anthu masauzande ambiri anafa tsiku limodzi lokha, kuphatikizaponso amunamuna ambirimbiri ozimitsa moto, apolisi, ndi azachipatala.

Chichitikireni zimenezo, Mboni za Yehova zayesetsa mogwirizana kulimbikitsa anthu amene okondedwa awo anafa pa zoopsazo. Zachita zimenezi n’cholinga ‘chowakhazikitsa mtima pansi amene ataya mtima’ ndi ‘kutonthoza mtima onse amene akulira maliro.’—Yesaya 61:1, 2.

Mboni za Yehova zaona kwa zaka zambiri kuti anthu akaferedwa okondedwa awo amati akakhala amakonda kudzifunsa mafunso amene ali m’munsiwa. Baibulo limayankha mafunsoŵa. Bwanji osadziŵerengera nokha m’Baibulo lanu malemba amene asonyezedwa pamunsipa kuti muone?

Kodi nthaŵi ya kufa kwa munthu anaikonzeratu?

Pa Mlaliki 9:11, Baibulo la New World Translation limati ‘nthaŵi ndi zochitika za mwadzidzidzi’ zimawagwera anthu kapena kuti zochitika “mwangozi,” malingana ndi Baibulo la New English Bible. Ngati imfa ya munthu anaikonzeratu, n’chifukwa chiyani Baibulo limatilimbikitsa kuchita zinthu mosamala kuti tipeŵe ngozi?—Mwachitsanzo, onani lemba la Deuteronomo 22:8.

N’chifukwa Chiyani Timafa?

Anthu aŵiri oyambirira, Adamu ndi Hava, anawaika m’paradaiso wa padziko lapansi. Akanakhalabe omvera sibwenzi anthu akufa chifukwa chakuti mapeto ake a kusamvera anali imfa. (Genesis 1:28; 2:15-17) N’zomvetsa chisoni kuti Adamu ndi Hava sanamveredi Mlengi wawo. Ndiye chifukwa cha kusamverako, iwo analandira mphoto ya zimene anachitazo, ndiyo imfa. Pakuti anthu onse anachokera kwa Adamu ndi Hava, onse anabadwa ali ndi uchimo ndiponso amafa. Baibulo limalongosola kuti: “Uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi [Adamu], ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.”—Aroma 5:12.

Kodi anthu akufa amakhala motani?

Adamu atapanduka, Mulungu anati: “Udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti mmenemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.” (Genesis 3:19) Motero tikati munthu wafa ndiye kuti sakuthanso kumva chilichonse, ndithudi munthuyo kumakhala kulibe. Baibulo limati: ‘Amoyo adziŵa kuti tidzafa; koma akufa sadziŵa kanthu bi.’ (Mlaliki 9:5) Baibulo limanenanso kuti munthu akafa, ‘abwerera kumka ku nthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.’Salmo 146:3, 4.

Kodi tilibe moyo wina kapena mzimu umene sufa munthu akamwalira?

Baibulo limaphunzitsa momveka bwino kuti moyo ndiwo munthuwe, osati chinachake chovuta kufotokoza chimene sichifa mukamwalira. (Genesis 2:7; Miyambo 2:10; Yeremiya 2:34) Pakuti zinthu zili choncho, tinganene kuti munthu akafa, moyo kapena mzimu umakhala utafa. Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti: “Moyo [umene uli munthuyo] wochimwawo ndiwo udzafa.”—Ezekieli 18:4.

Kodi Tingayembekeze Chiyani za Amene Anafa?

Baibulo limavumbula kuti n’cholinga cha Mulungu kudzapatsanso moyo anthu akufa powaukitsira m’dziko lapansi la paradaiso, limene silidzakhalanso ndi matenda ndiponso imfa. Yesu anati: “Ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira.”—Yohane 5:28, 29; Chivumbulutso 21:1-4.

Posimba za mnzake Lazaro amene anali atangomwalira kumene, Yesu anayerekezera imfa ndi tulo. (Yohane 11:11-13) Ndiponso Yesu atamuukitsa, Lazaroyo sananenepo chilichonse chosonyeza kuti anali kumalo ena ake ozunzirako anthu ochimwa kapena malo ena ake amtendere okhaokha panthaŵi yochepa imene anafa. (Yohane 11:37-44) Izi sizodabwitsa, chifukwa chakuti akufa sadziŵa kanthu kalikonse. Samva kuwawa koma amangodikirira “nthaŵi” yodzaukitsidwa. Koma mfundo yofunika kwambiri n’njakuti chifukwa chakuti Yesu anaukitsa Lazaro timadziŵa kuti akufa angathe kukhalanso ndi moyo. Inde, pochita chozizwitsa chimenechi Yesu anasonyeza pang’ono chabe zimene zidzachitike padziko lapansi Ufumu wa Mulungu ukamadzalamulira. (Machitidwe 24:15) Koma ndiye n’zolimbikitsa kwambiritu kwa anthu amene okondedwa awo akufa m’nthaŵi zodzaza ndi mavuto zino!