Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuteteza Ndiponso Kuletsa Matenda a Kuthamanga kwa Magazi

Kuteteza Ndiponso Kuletsa Matenda a Kuthamanga kwa Magazi

Kuteteza Ndiponso Kuletsa Matenda a Kuthamanga kwa Magazi

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU BRAZIL

MARIAN anagwidwa nthumanzi kwambiri! Asakuyembekezera n’komwe, anangoyamba kutuluka kamfuno wochititsa mantha zedi. “Ndinkangoti ndifa basi,” amakumbukira choncho. Dokotala anamuuza kuti kamfuno wakeyo anali atayamba chifukwa cha matenda a kuthamanga (kwambiri) kwa magazi. “Komatu ine ndikuona kuti ndili bwinobwino,” anayankha choncho Marian. “Inde, anthu ambiri sadziŵa kuti ali ndi matenda a kuthamanga kwa magazi chifukwa chakuti saona zizindikiro zake,” anatero dokotalayo.

Nanga inuyo, kodi magazi anu akuyenda bwinobwino? Kodi zimene mumachita zingadzakudwalitseni matenda a kuthamanga kwa magazi? Kodi mungatani kuti magazi anu aziyendabe bwinobwino? *

Magazi ali ndi liŵiro lake limene amayendera akakhala m’mitsempha. Liŵiro limeneli amaliyeza pogwiritsa ntchito chilamba chinachake chimene chimafufuma akachipopera mpweya, ndipo amachikulunga kumtunda kwa dzanja n’kuchilumikiza kuchipangizo chinachake chimene chimaŵerengetsera mmene magaziwo akuyendera. Chipangizochi chimasonyeza manambala aŵiri. Mwachitsanzo chimatha kusonyeza kuti: 120/80. Nambala yoyambayo imasonyeza mmene magaziwo akuyendera malingana ndi mmene mtima ukugundira, ndipo yachiŵiriyo imasonyeza mmene magaziwo akuyendera pakanthaŵi kamene mtima umakhala zii ukangogunda kumene. Kuyenda kwa magazi amakuyeza poona kuchuluka kwa timadzi totchedwa mercury timene amatiika m’chipangizo choyezera thupi, ndipo amati magazi a munthu akuthamanga kwambiri ngati patapezeka kuti liŵiro la magaziwo laposa 140/90.

Kodi n’chiyani chimene chimapangitsa kuti magazi athamange? Tangoyerekezerani kuti mukuthirira dimba lanu. Mukatsegula mpope wa madzi kapena mukatseka pang’ono kukamwa kwa paipiyo, madziwo amatuluka mothamanga kwambiri. Ndi zimene zimachitikanso magazi akamayenda: Magaziwo akamayenda mofulumira kwambiri kapena njira yake ikamachepa mumtsempha zimapangitsa kuti magaziwo azithamanga kwambiri. Kodi matenda a kuthamanga kwa magazi amayamba bwanji? Pali zinthu zambiri zimene zimayambitsa matendaŵa.

Zinthu Zimene Simungathe Kuziletsa

Ofufuza anapeza kuti ngati munthu ali ndi achibale amene ali ndi matenda a kuthamanga kwa magazi, m’posavuta kuti nayenso adwale matendaŵa. Ofufuza anapeza kuti mapasa amene ndi ofanana ndendende amadwala kwambiri matendaŵa kuposa mapasa wamba. Ulendo wina, ofufuza ena ananena kuti “anapeza zinthu zina zotengera kumtundu zimene zimachititsa kuti magazi aziyenda mothamanga kwambiri m’mitsempha,” ndipo zonsezi ndizo zimatsimikizira kuti kutengera zakumtundu kumachititsanso munthu kukhala ndi matenda a kuthamanga kwa magazi. Akuti anthu ambiri amene amakhala ndi vuto la kuthamanga kwambiri kwa magazi kaŵirikaŵiri ndi anthu achikulire ndiponso amuna achikuda.

Zinthu Zimene Mungathe kupeŵa

Musamangodya zilizonse! Anthu ena mchere umatha kuwayambitsa matenda a kuthamanga kwa magazi; makamaka anthu odwala matenda a shuga, amene magazi awo amathamanga kwambiri, achikulire ndiponso anthu ena achikuda. Mafuta akamachuluka m’mitsempha mmene mumadutsa magazi amapangitsa kuti m’kati mwa mitsemphayo mukhale mafuta okhaokha ndipo zikatere njira yodutsa magaziwo imachepa, choncho magaziwo amawonjezera liŵiro lake. Anthu amene ali onenepa kwambiri angadwale mosavuta matenda a kuthamanga kwa magazi. Ofufuza ena anapeza kuti kudya kwambiri zinthu monga nthochi, nyemba, nyama, ndiponso mkaka, kapena zakudya zina zopangidwa ndi mkaka kukhoza kuchepetsa liŵiro la magazi.

Kusuta fodya kumachititsa kuchuluka kwa mafuta m’kati mwa mitsempha, matenda a shuga, matenda a mtima ndiponso sitiroko. Ndiyetu n’zoopsa kuti munthu wa matenda a kuthamanga kwa magazi azisutanso chifukwa akhoza kuyamba kudwala matenda a mtima. Ngakhale kuti pali umboni wosagwirizana, koma mankhwala amene amapezeka mu khofi, tiyi ndiponso mu zakumwa zina zoziziritsa kukhosi, akhozanso kuyambitsa matenda a kuthamanga kwa magazi. Komanso kukhala ndi maganizo ambirimbiri kapena kupanikizika ndi zinthu zinazake kungateronso. Chinanso n’chakuti asayansi amadziŵa kuti kumwa kwambiri kapena kumangokhala chiledzerere ndiponso kukhala munthu wosachitako maseŵera olimbitsa thupi kukhoza kuchititsa kuti magazi azithamanga.

Makhalidwe Okuthandizani Kukhala Athanzi

Kudikirira kuti mpaka muyambe mwadwala kaye matenda a kuthamanga kwa magazi mmalo moyambiratu kutsatira njira zothandiza kuti musadwale matendaŵa, n’kulakwitsa kwambiri. Ndibwino kumachita zinthu zokuthandizani kukhala wathanzi zinthu zisanafike poipa. Mukamachita zinthu mosamala panopa mapeto ake simudzavutika mtsogolomu.

Mfundo yachitatu yokhudza matenda a kuthamanga kwa magazi imene madokotala a ku Brazil anagwirizana inafotokoza makhalidwe ofunika kusintha pofuna kuti vuto la kuthamanga kwa magazi lichepe. Zimenezi n’zothandiza kwambiri kwa anthu amene ali ndi vutoli ngakhalenso amene ali bwinobwino.

Kwa anthu onenepa kwambiri, ofufuza anati ndibwino kuti azidya pang’ono zakudya zonse zamagulu, asamayambe kusala kudya pofuna kuti awonde mwamsanga, koma azilimbikira kuchita timaseŵera tolimbitsa thupi. Koma anati ndibwino kuti azingodya mchere wochepa kwambiri mwina wokwana sipuni yaing’ono imodzi yokha patsiku. * Izi zikutanthauza kuti ayenera kuthira mchere wochepa kwambiri pophika zakudya, komanso osamadya kwambiri zakudya zimene anazikonza kalekale n’kuzisunga, nyama yophikaphika n’kuisunga ili yozizira (monga soseji, ndi zina zotero) ndiponso zakudya zochita kuŵamba ndi moto. Akhozanso kuchepetsa kudya mchere wambiri posawonjezera wina m’mbale pa chakudya ndiponso poonetsetsa zimene analemba pazakudya zokonzakonza kale kuti anathira mchere wambiri bwanji.

Pamsonkhanowu ananenanso kuti ndibwino kudya kwambiri zakudya monga nthochi ndi zipatso zina n’zina zotere chifukwa chakuti zili ndi mphamvu inayake yothandiza “kuletsa matenda a kuthamanga kwa magazi.” Apa ndiye kuti chakudya chosakudwalitsa matendaŵa chiyenera kukhala “chakudya chimene chilibe mchere wambiri ndiponso chimene chili ndi mphamvu yochepetsa mchere,” monga nyemba, ndiwo zamasamba zosaphika kwambiri, nthochi, mavwende, karoti, tomato ndiponso malalanje. Komanso ndibwino osamwa kwambiri mowa. Ofufuza ena amasonyeza kuti amuna amene magazi awo amathamanga kwambiri ngati amamwa sayenera kumwa mowa wokwana mabotolo atatu amamililita 300 patsiku; ndipo akazi kapena anthu ochepa matupi kwambiri sayenera kumwa mowa wokwana mabotolo aŵiri.

Bungwe la Brazilian Consensus linatinso anthu akamachita maseŵera olimbitsa thupi amachepetsa vuto la kuthamanga kwa magazi ndipo potero akhoza kupeŵa matendaŵa. Kuchita timaseŵera tina tolimbitsa thupi, monga kungoyenda, kupalasa njinga ndiponso kusambira, kwa mphindi 30 mpaka 45, katatu kapena kasanu pasabata n’kothandiza kwambiri. * Zinthu zinanso zimene zimathandiza kuti mukhale ndi moyo wathanzi ndizo kusiya kusuta fodya, kuleka kudya zinthu zamafuta kwambiri ndi zotsekemera kwambiri komanso zinthu zimene zingayambitse vuto la matenda a shuga, kudya zakudya zokwanira zolimbitsa mafupa komanso zothandiza thupi kupeza mphamvu, kusachita zinthu zotopetsa kwambiri ndiponso zopatsa maganizo. Mankhwala ena akhoza kuyambitsa munthu kuthamanga magazi, monga mankhwala enaake om’patsa munthu chilakolako cha chakudya, ndiponso a mutu waching’alang’ala.

Ndithudi, ngati muli ndi vuto lothamanga kwambiri magazi, palibenso munthu wina kuposera dokotala amene angakupatseni malangizo a zinthu zimene muyenera kudya kapenanso zizolowezi zanu, malinga ndi zimene zikufunika m’thupi mwanu. Komabe mosaganizira zakuti kaya mukudwala matendaŵa kapena ayi, kuyambiratu kuchita zinthu zopeŵa matendaŵa n’kothandiza kwa anthu onse m’banja, osangoti kwa okhawo amene amathamanga kwambiri magazi. Marian uja amene tam’tchula pachiyambi pa nkhani ino, anasintha zochita m’moyo wake. Panopa amalandira mankhwala ndipo akukhala bwinobwino ngakhale kuti akudwalabe. Nanga inuyo bwanji? Poyembekeza nthaŵi imene anthu onse adzakhale ndi moyo wathanzi kwambiri ndiponso dziko limene “wokhalamo sadzanena, ‘Ine ndidwala,’” yesetsani kuchita zinthu zakuti magazi anu aziyendabe bwinobwino!—Yesaya 33:24.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Galamukani! siilamulira anthu kuti agwiritse ntchito njira inayake pofuna kuthetsa vutoli, pakuti imeneyi ndi nkhani ya kadziŵa mwini.

^ ndime 15 Kaonaneni ndi dokotala wanu kuti akuuzeni kuchuluka kwa mchere umene muyenera kudya ngati mukudwala matenda a kuthamanga kwa magazi kapena mtima, chiwindi, kapenanso impso ngati mukulandira mankhwala.

^ ndime 17 Kambiranani ndi dokotala wanu za ndondomeko yofunika yochita maseŵera olimbitsa thupi imene mungatsatire.

[Bokosi patsamba 14]

KULIMBANA NDI VUTO LA KUTHAMANGA KWA MAGAZI

1. Njira Zimene Zingathandize Kuletsa Vutoli

• Chitani zinthu zochepetsa thupi

• Musamadye mchere wambiri

• Muzidya zipatso zambiri zochepetsa mchere m’thupi

• Musamamwe kwambiri mowa

• Nthaŵi zonse muzichita maseŵera olimbitsa thupi

2. Njira Zina Zothandizanso

• Muzidya zakudya zambiri zamkaka ndiponso zakumwaimwa zowonjezera madzi m’thupi

• Muzidya zakudya zamasamba zambiri

• Muzichita zinthu zopumitsako thupi

3. Njira Zina za M’gulu Lomweli

• Musamasute fodya

• Musamadye zakudya zamafuta ambiri

• Musamadye zakudya zimene zingayambitse matenda ashuga

• Musamamwe mankhwala amene angachititse kuti magazi ayambe kuthamanga

[Mawu a Chithunzi]

Malangizoŵa achokera pamfundo yachitatu yokhudza matenda a kuthamanga kwa magazi imene madokotala a ku Brazil anagwirizana, yolembedwa m’magazini yotchedwa Revista Brasileira de Clínica & Terapêutica.

[Chithunzi patsamba 15]

Kukonda kuchita maseŵera olimbitsa thupi ndiponso kudya zakudya zopatsa thanzi kumathandiza kuteteza ndiponso kuletsa matenda a kuthamanga kwa magazi