Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Amene Ndimagona Naye M’chipinda Chimodzi Ali Wovuta Kwambiri?

N’chifukwa Chiyani Amene Ndimagona Naye M’chipinda Chimodzi Ali Wovuta Kwambiri?

Achinyamata Akufunsa Kuti . . .

N’chifukwa Chiyani Amene Ndimagona Naye M’chipinda Chimodzi Ali Wovuta Kwambiri?

“Ndine waukhondo kwambiri. Koma ndikafika m’nyumba, ndimapeza mnzanga amene ndimagona naye m’chipinda chimodzi ali kwala pansi akuonera TV kapena akuŵerenga, chimanga chokazinga chili mbwee. Nthaŵi zonse popita kunyumba, ndimadziŵiratu zimene ndikapeze m’nyumbamo, ndipo chamumtima ndimangodandaula poganizira kuti ndikaloŵa m’chinyumba choterecho.”—David.

“Mnzanga amene ndimagona naye m’chipinda chimodzi anamulekerera kwambiri. Ndikukhulupirira ankaganiza kuti mwina pali wantchito. Ndipo nthaŵi zonse amafuna kuti zinthu zichitike mmene iye akufunira.”—Renee. *

NKHANI ina mu nyuzipepala ya U.S. News & World Report inati: “Kukhala ndi munthu wachilendo wazake kungatiphunzitse . . . kulolera. Koma nthaŵi zambiri kuphunzirako kumakhala koŵaŵa.” Amene anakhalako m’chipinda chimodzi ndi munthu wina angavomereze zimenezi.

Ophunzira ambiri a ku yunivesite amagona aŵiriaŵiri kuti asamawononge ndalama zambiri pa maphunziro. Achinyamata ena pofuna kudziimira paokha amachoka kwa makolo awo kukakhala ndi munthu wina. Achinyamata ambiri achikristu amapeza wokhala naye n’cholinga chochita zinthu zauzimu. (Mateyu 6:33) Amaona kuti kupeza wina wothandizana naye kugula zinthu zofunika pamoyo kumawathandiza kukhala atumiki a Ufumu a nthaŵi zonse. Nthaŵi zina, kugona chipinda chimodzi ndi wina ndiwo moyo wa amishonale ndiponso wa amene amatumikira m’maofesi a nthambi za Mboni za Yehova. *

Atolankhani a Galamukani! analankhula ndi achinyamata angapo amene anagonapo m’chipinda chimodzi ndi munthu wina. Onse anati kukhala ndi munthu wina sikothandiza pankhani yolipirira nyumba yokha ayi koma amakhalanso mnzako, wokambirana naye zakukhosi ndi wochitira naye zinthu pamodzi. Lynn anakumbukira kuti: “Tisanakagone tinkakonda kukamba nkhani zathu zachitsikana kapena tinkaonera kanema.” Renee anati: “Chinanso n’chakuti munthu amene umagona naye amakulimbikitsa. Nthaŵi zina kupeza zofunika pamoyo, kulipira mabilu ako onse, ndiponso kulalikira kumakoma ukakhala ndi wokulimbikitsa.”

Komabe, kugona chipinda chimodzi ndi munthu wina, makamaka amene simunamuonepo, n’kovuta kwambiri. Nyuzipepala ya U.S.News & World Report inati pankhani ya moyo wa ku koleji: “Ngakhale kuti masukulu ambiri amayesetsa kuti anthu ogonera chipinda chimodzi azikhala oyenerana, pamakhalabe mavuto ambiri zedi.” Inde, pakoleji anthu ogonera chipinda chimodzi amakangana mpakana kumenyana kumene. Moti pa Intaneti pali malo amene ophunzira amadandaula poyera mavuto awo osaneneka amene amapeza chifukwa cha anzawo ogona nawo. N’chifukwa chiyani nthaŵi zambiri kugona chipinda chimodzi ndi munthu wina kumavuta?

Kukhala ndi Munthu Wosam’dziŵa

Mark anati: “Kukhala ndi munthu wosam’dziŵa si kosangalatsa kwenikweni. Mwina sudziŵa n’komwe kuti khalidwe lake n’lotani.” Kungodziŵa kuti uzikhala ndi munthu amene zochita zake si zofananako ndi zako kapena n’zosiyaniranatu, kumadetsa nkhaŵa kwambiri. Ndi zoonadi kuti Akristu amafanana pa zinthu zambiri ndiponso angakambirane nkhani zambiri. Komabe, David anavomereza kuti: “Kugona chipinda chimodzi ndi munthu wina kun’kandiopsa zedi.”

Koma mwamwayi David anamuika ndi munthu amene anakula monga iyeyo. Koma si onse amene amayeneranadi. Mark anati: “Amene ndinkakhala naye poyamba, sankalankhulalankhula. Mukamakhala anthu aŵiri m’chipinda chimodzi, mumafuna kucheza kwambiri. Koma iye sankalankhula. Zinayamba kundinyansa.”

Kusiyana kochokera kumabweretsanso mavuto ena. Lynn anati: “Ukayamba kukhala pawekha, umafuna kuchita zofuna zako. Komano umadzazindikira kuti pali anthu ena ofunika kuwaganizira.” Ndithudi, mukachoka kunyumba kwanu komwe mumakhala mtima uli m’malo mungasokonezeke maganizo kwambiri kuona mmene anthu ena amaonera zinthu.

Mukakula Mosiyana Mumachita Zinthu Mosiyananso

Chinthu chachikulu kwambiri pankhani imeneyi ndi mmene makolo anu anakuphunzitsirani kapena ngati sanakuphunzitseni. (Miyambo 22:6) Mnyamata wina wotchedwa Fernando anati: “Ndine waukhondo, koma amene ndinkagona naye anali wauve. Mwachitsanzo, pankhani ya koika zovala: iye ankakonda kungoponya zinthu paliponse. Koma ine ndinkakonda kukoloweka zinthu bwinobwino.” Nthaŵi zina kusiyana kwa mmene mumachitira zinthu kumachita kunyanyira.

Renee anati: “Ndinakhalapo ndi mnzanga wina amene chipinda chake chinkaoneka ngati dzala loponyako zinyalala. Ndinakhalaponso ndi ena amene sankapukuta patebulo akadya kapena ankangosiya mbale zosatsuka zili bii kwa masiku aŵiri kapena atatu.” Inde, tikanena za ntchito ya panyumba ena amene timagona nawo amafanana ndi amene akunenedwa pa Miyambo 26:14 kuti: “Monga chitseko chikankhikira pa zitsulo za pamphuthu, momwemo waulesi agubuduka pakama pake.”

Komanso, kugona ndi munthu waudongo wochita kunyanyira sikosangalatsanso. Mtsikana wina dzina lake Lee anati amene ankakhala naye m’chipinda chimodzi: “Ankafuna kuti m’chipindacho azikonzamo ola lililonse. Sikuti ineyo ndine wauve ayi, koma nthaŵi zina ndinkasiya zinthu monga mabuku pabedi. Ndipo iye ankafuna kuti andisiyitse khalidwe limeneli.”

Anthu ogonera limodzi angakhalenso osiyana maganizo pa mmene amaonera ukhondo. Mark anati: “Amene ndimagona naye amadzuka mochedwa kwambiri. Amangopita pampopi n’kunyowetsa tsitsi lake, basi akatero wapsa ulendo.”

Kusiyana chikhalidwe ndiponso zochitika kumakhudza nyimbo ndi zosangalatsa zimene timakonda. Ponena za amene amagona naye Mark anatinso “timakonda nyimbo zosiyana.” Komabe ngati mumalemekezana, kusiyana kumeneko mungapindule nako, mwinanso kungakuthandizeni nonse kuphunzira kukonda zinthu zina. Koma nthaŵi zambiri, kusiyana kumeneku kumabweretsa mikangano. Fernando anati: “Ndimakonda nyimbo za ku Spain, koma mnzanga amene ndimagona naye amangokhalira kuzinyoza.”

Vuto la Telefoni

Nkhani ya kugwiritsa ntchito telefoni ndi nkhani yaikulu imene imakanganitsa anthu. Mark anati: “Ndimafuna kugona msanga, koma mnzangayo amangolankhula patelefoni mpaka usiku kwambiri. Munthu umafika pena poti zimayamba kukupweteketsa mtima.” Lynn nayenso anakumbukira kuti: “Nthaŵi zina anzake a mnzangayo ankaimba telefoni nthaŵi ya 3 kapena 4 koloko m’bandakucha. Ngati iye kulibe, ndinkadzuka kukayankha telefoniyo.” Nanga anathetsa bwanji vutoli? “Tinagwirizana kuti aliyense apeze telefoni yake.”

Komabe, si achinyamata onse amene angakwanitse kuti aliyense akhale ndi telefoni yake, choncho ambiri amagwiritsa ntchito telefoni imodzi. Zimenezi zingayambitse mavuto ena aakulu zedi. Renee anakumbukira kuti: “Wina amene ndinkagona naye anali ndi chibwenzi, ndipo nthaŵi zambiri ankalankhula pa telefoni kwanthaŵi yaitali. Mwezi wina bilu ya telefoni inakwana madola oposa 90. Anati tigaŵane biluyo, popeza n’zimene tinagwirizana kuti bilu ikabwera tizigaŵana pakati.”

Nkhani ya kupeza mpata wotha kuimba telefoni imakhalanso yovuta. Lee anakumbukira kuti: “Amene ndinkagona naye anali wamkulu pomuyerekezera ndi ine. Ndipo tinali ndi telefoni imodzi yokha. Nthaŵi zonse ndinkalankhula patelefoni chifukwa ndinali ndi anzanga ambiri. Koma mnzangayo sankanena kanthu. Ndinkaganiza kuti akafuna kuimba telefoni, andiuza. Tsopano ndadziŵa kuti sindinali kumuganizira.”

Nthaŵi Yokhala Pawekha Imasoŵa

David anati: “Tonse timafuna nthaŵi yokhala patokha. Nthaŵi zina, ndimangofuna kupuma basi, kungokhala phee.” Koma, ngati ukukhala ndi munthu wina nthaŵiyi imasoŵa. Mark anavomereza kuti: “Nthaŵi zina ndimafuna kukhala pandekha. Choncho chimene chimandisoŵetsa mtendere kwambiri n’chakuti sindipeza nthaŵi yokhala pandekha. Ine ndi mnzanga amene ndimagona naye timachoka ndi kufika pakhomo nthaŵi yofanana. Choncho zimandivuta kupeza nthaŵi yokhala pandekha.”

Ngakhale Yesu Kristu nthaŵi zina ankafuna nthaŵi yokhala payekha. (Mateyu 14:13) Choncho zimasoŵetsa mtendere ngati mukulephera kuŵerenga, kuphunzira kapena kusinkhasinkha chifukwa chakuti mukukhala ndi munthu wina. Mark anati: “Kuŵerenga kumavuta chifukwa nthaŵi zonse wina amakhala akuchita zinazake m’chipinda mwathumo. Amaitana anzake, amakhala akulankhula patelefoni, kuonera TV kapena kumvera wailesi.”

Komabe, ngakhale kulolerana ndi amene mumagona naye kuli kovuta bwanji, dziŵani kuti achinyamata ambiri apindula nako. Nkhani zotsatira nkhani ino zidzafotokoza njira zina zimene zingathandize kuti mupindule kwambiri ndi amene mumagona naye m’chipinda chimodzi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Tasintha mayina ena.

^ ndime 6 Ngakhale kuti nkhaniyi ikulangiza achinyamata, ingathandizenso achikulire amene akugona m’chipinda chimodzi ndi munthu wina chifukwa cha mavuto ena, monga umasiye.

[Chithunzi pamasamba 16, 17]

Kukonda nyimbo zosiyana kungabweretse mavuto

[Chithunzi patsamba 18]

Kusaganizirana kungayambitse mikangano