Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Anthu Akuchoka M’zipembedzo Zodziŵika Bwino?

N’chifukwa Chiyani Anthu Akuchoka M’zipembedzo Zodziŵika Bwino?

N’chifukwa Chiyani Anthu Akuchoka M’zipembedzo Zodziŵika Bwino?

ZIPEMBEDZO ZIMENE ZIMATI zimagwiritsa ntchito ziphunzitso za Yesu Kristu zili ndi anthu okwana 1.7 biliyoni. Akuti Matchalitchi Achikristu ndiwo ali ndi anthu ochuluka kwambiri padziko lonse, mpaka kuposa zipembedzo zodziŵika bwino monga, Chibuda, Chihindu, ndi Chisilamu. Komabe, malipoti akusonyeza kuti m’mayiko ambiri amene amati ndi achikristu, mphamvu ya matchalitchiŵa pa anthu awo yayamba kuchepa.

Anthu osiyanasiyana akuchoka m’matchalitchi awo. Ronald F. Inglehart, wofufuza wa pa Yunivesite ya Michigan amenenso ndi woyang’anira bungwe lina lofufuza zinthu la World Values Survey anati, m’mayiko olemera chipembedzo chikutha mphamvu. Magazini ya Bible Review inagwira mawu a munthu ameneyu, akuti: “Kuwonjezera pa kuchepa kwa chiŵerengero cha anthu amene amapita ku tchalitchi mlungu uliwonse, mayiko a ku Latin America tsopano akutumiza amishonale kukapulumutsa anthu m’mayiko amene ankawachita utsamunda.” Ananenanso kuti, “chipembedzo chaloŵa pansi” kwabasi m’mayiko ena a kumpoto kwa Ulaya. Ku Norway ndi Denmark, anthu asanu okha pa anthu 100 alionse ndi amene amapita ku tchalitchi mokhazikika. Ku Sweden pa anthu 100 alionse pamakhala anayi okha ndipo ku Russia ndi anthu aŵiri okha.

Malipoti a ku Germany akusonyeza kuti kuyambira chaka cha 1984 mpaka 1993, anthu amene analembetsa ku Katolika, ndipo amapita ku tchalitchi mokhazikika achepa, kuchoka pa 25.3 peresenti kufika pa 19 peresenti. Pofika mu 1992, Apulotesitanti anayi okha pa 100 alionse ndi amene anali kupita kumapemphero Lamlungu lililonse. Mu 1999, magazini ya Christianity Today inanena kuti: “Ku Germany munthu mmodzi yekha pa anthu khumi alionse ndi amene amapita ku tchalitchi mlungu uliwonse.”

Ponena za kuchepa kwa anthu okhulupirira ku Britain, nyuzipepala ya The Guardian inati: “Chikristu chisanafikepo pomvetsa chisoni kwambiri ngati mmene chachitiramu.” Nkhaniyo inati “kuyambira 1950 mpaka 2000 zinali zaka zovuta kwambiri kwa ansembe ndi akulu a mpingo.” Ponena za lipoti lapadera la ku United Kingdom, nyuzipepalayo inasonyeza kuti si achinyamata okha amene akuchoka m’zipembedzo zodziŵika komanso achikulire. Inanenanso kuti: “Anthu achikulire akusiya kukhulupirira Mulungu akamakalamba. Zimene ofufuza apeza posachedwapa potsimikizira zimenezi zikhumudwitsa matchalitchi a ku Britain amene ali ndi vutoli, amene panopo amaona anthu achikulire kuti ndiwo mizati ikuluikulu ya mipingo yawo imene ikumka ichepa pang’onopang’ono.”

Zinthu zimenezi sizikuchitika ku Ulaya kokha, zikuchitikanso m’mayiko ena. Mwachitsanzo, magazini ya ku Canada ya Alberta Report inanena kuti dzikoli lili ndi vuto la “kusiya kukhulupirira ndi kulambira m’zipembedzo zodziŵika bwino” ndiponso kuti “anthu a ku Canada amene akutsatira malingaliro awoawo pankhani ya Mulungu osati malamulo oikidwa achipembedzo, ndi ochuluka kuŵirikiza katatu poyerekezera ndi anthu a ku Britain a malingaliro ofananawo.

Anthu ambiri amaona kuti kupita ku tchalitchi sikuwathandiza mwauzimu. Malinga ndi magazini ya ku Canada ya Maclean’s, Ayuda ndi Akatolika amene anawapeza kunyumba ya a monke achihindu ku Himalaya, omwe anafunsidwa ananena motere zakukhosi kwawo: “Sitikukhutitsidwanso ndi kumangotsatira miyambo yopanda tanthauzo lililonse.” Inde, ngakhale kuti akhala akupita kutchalitchi mokhulupirika kwa zaka zambiri, ena amadzifunsa kuti, “Kodi kutchalitchi ndaphunzirako chiyani? Kodi kupita ku tchalitchi kwandithandiza kugwirizana ndi Mulungu?’ N’zosadabwitsa kuti, Gregg Easterbrook amene amalemba mabuku, ananena kuti, “Kumaiko aazungu, m’nthaŵi yathu ino anthu ayamba kusoŵa kwambiri chuma chauzimu osati chuma chenicheni.”

N’zoona kuti pali mayiko ochuluka amene muli anthu ambiri omwe amapita kutchalitchi. Komabe, kupita kutchalitchi sikutanthauza kuti amatsatira mokhulupirika ziphunzitso zake. Mwachitsanzo, nyuzipepala ya ku Australia ya The Age inanena kuti ku kumayiko aazungu, “Akristu amene amachita zimene chipembedzo chawo chimaphunzitsa akuchepa kwambiri. M’madera ambiri ku Africa, Asia ndi Latin America, kwa anthu ambiri Chikristu ndi njira yongobisalirako kuti azitsatirabe zikhulupiriro zowasangalatsa za mtundu wawo kapena gulu lawo, zimene sizigwirizana n’komwe ndi ziphunzitso zovomerezeka zachikristu. Ziphunzitsozi nthaŵi zambiri zimasutsana ndi zikhulupiriro zawozo, ndipo zinachotsedwa kalekale m’chikristu.”

N’chifukwa chiyani anthu ambiri, achinyamata ndi achikulire omwe akuchoka m’matchalitchi awo? Zikuoneka kuti chifukwa chachikulu ndicho kukhumudwa.

Mbiri Yoipa ya Chipembedzo

Nyuzipepala ya The Guardian inanena izi: “Tchalitchi cha Roma Katolika chili ndi mbiri yoipa yogwirizana ndi zoipa zonse zochitidwa ndi ndale zankhanza za chifasizimu m’zaka za m’ma 1900. Chinayamikira Kazembe Franco atapambana nkhondo ya pachiŵeniŵeni ya ku Spain ndipo posachedwapa chathandizanso Kazembe Pinochet.” Nyuzipepala yomweyi inanenanso kuti Papa Pius XII, yemwe anali Papa panthaŵi ya nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse, “anali wofunitsitsa kugwirizana ndi [Hitler] popeŵa ntchito zovuta monga kuletsa chipani cha Nazi kupulula anthu.”

Nyuzipepala ya The Age inanena kuti: “Nthaŵi zambiri Chikristu chimanena zabodza. Akristu alephera kukhala mwamtendere ndi mogwirizana. . . . Umboni wake ndiwo Nkhondo zambiri zolanda anthu zinthu n’kuwagonjetsa, zimene akhala akuzilungamitsa ponena kuti cholinga chawo chinali kutembenuza anthu kuti akhale Akristu. N’zoona kuti chikhulupiriro, chiyembekezo ndi chikondi ndi mikhalidwe yachikristu yofunika kwambiri, koma anthu amene amati amayesetsa kukhala ndi mikhalidwe imeneyi ndi amenenso sakhulupirira mofanana ndi amene si Akristu n’komwe, ndipo mwinamwake safuna kuthandiza anzawo kuposanso amene si Akristu. . . . Linali dziko lachikristu limene linapululitsa anthu pansi pa chipani cha Nazi ndipo ndi dzikonso lachikristu limene linaphulitsa mabomba a nyukiliya ku Japan.”

Ena anganene kuti Matchalitchi Achikristu akhala akulimbikitsa mikhalidwe yabwino monga kugwiritsa ntchito zinthu mwanzeru, kulimba mtima, kudziletsa, ndi chilungamo. Komabe, nyuzipepala ya The Age inanena kuti: “Akristu ku Ulaya, North America ndi ku Australia ndiwo akudyerera kwambiri zinthu zosiyanasiyana zapadzikoli ndipo akupitirizabe kuchenjeretsa anzawo. Ndipo pofuna kukwaniritsa zokhumba zawo iwo akuchita nkhanza ndi kuwononga mayiko ochepa mphamvu amene ayandikana nawo.”

Ponena za tsogolo la Matchalitchi Achikristu nyuzipepala ya The Age inapitiriza kunena kuti: “Popanda njira ina yoyendetsera bwino zinthu, Chikristu sichingakhalenso champhamvu monga chinalili zaka mazana zapitazo. Izi zingakhale zabwino kapena zoipa, malingana ndi mmene munthu aliyense payekha angazionere. Koma n’zimene zidzachitikire Chikristu zaka zikubwerazi.”

Ndiyeno chifukwa cha kutha mphamvu kwa zipembedzo padziko lapansi, anthu ambiri akuchoka m’matchalitchi odziŵika bwino. Koma kodi zipembedzo zina zimene amapeza zimathetsadi vuto lawo? Kodi zimathandizadi?

[Zithunzi patsamba 23]

Miyambo yokhala ndi zinthu zambirimbiri zokopa imasiya anthu ambiri ali ndi njala yauzimu

[Chithunzi patsamba 23]

Anthu ambiri achoka m’zipembedzo zodziŵika bwino chifukwa zimalimbikitsa nkhondo ndi ulamuliro wankhanza

[Mawu a Chithunzi]

chithunzi: age fotostock