Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Akristu Ayenera Kulalikira Anthu Ena?

Kodi Akristu Ayenera Kulalikira Anthu Ena?

Lingaliro la Baibulo

Kodi Akristu Ayenera Kulalikira Anthu Ena?

N’KUTHEKA kuti kumene munakulira kapena mwambo wakwanu umati si bwino kukambirana zachipembedzo ndi anthu abanja lina kapena atchalitchi china. Chifukwa cha mfundo imeneyi, zikhoza kukuipirani ngati munthu wina atafika panyumba panu mwadzidzidzi ali ndi Baibulo m’manja. Anthu ena amaipidwa ndi zimenezi chifukwa choganizira zakuti chipembedzo chili ndi mbiri yochita zinthu zachiwawa ponamizira kuti chikufuna kupulumutsa anthu.

Mbiri ya mayiko ambiri imasonyeza kuti anthu ambiri anatembenuka chifukwa choopa kuti angaphedwe, koma osati chifukwa chokonda Kristu. Anthu ambiri anakabisala, kuthaŵa kwawo ndiponso dziko lawo, mwinanso kufa kumene, ena mpaka anawotchedwa ali pamtengo, pokana kutembenuka kuti atsatire chipembedzo cha anthu amene ankawazunzawo.

Malemba ouziridwa a m’Baibulo savomereza kutembenuza anthu mowaumiriza choncho. Kodi ndiye kuti si bwino kuuzako ena zimene mumakhulupirira m’chipembedzo chanu? Baibulo lomwelo limayankha zimenezi.

Kuphunzitsa ndi Mphamvu

Taganizirani kaye chitsanzo cha Yesu Kristu. Iye anali mphunzitsi waluso amene anawapangitsa anthu amene anali kumumvetsera kusintha zochita zawo. (Yohane 13:13, 15) Ali pa Ulaliki wa Paphiri, anaphunzitsa zinthu zosavuta kumvetsa koma zogwira mtima kwambiri. Zimene zinachitika chifukwa cha kuphunzitsa kwake n’zakuti anthu amene ankamumvetsera “anazizwa ndi chiphunzitso chake: pakuti anawaphunzitsa monga mwini mphamvu.” (Mateyu 7:28, 29) Patha zaka pafupifupi 2,000 chichitikireni zimenezo, koma anthu amene amafufuza zimene Yesu anaphunzitsazo akusinthabe zochita zawo m’moyo. Potsimikizira mfundo imeneyi, Pulofesa Hans Dieter Betz ananena kuti “mphamvu ya Ulaliki wa Paphiri imafika patali kwambiri osati ku Chiyuda ndi Chikristu kokha ayi, imakhudzanso ngakhale chikhalidwe cha Chizungu.”

Atangotsala pang’ono kukwera kumwamba, Yesu anapereka lamulo limene linatsimikizira kuti akamwalira ntchito yophunzitsa imene anaiyambitsa idzapitirira ndipo idzafika kutali. (Yohane 14:12) Analangiza ophunzira ake kuti apite kwa anthu a mitundu yonse, “ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse” zimene anali atawalamula kuti achite. Yesu anafotokoza momveka bwino cholinga chachikulu cha ntchito imeneyi poyamba n’kunena kuti: ‘Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu.’—Mateyu 28:19, 20; Machitidwe 1:8.

Onaninso chitsanzo cha mtumwi Paulo. Iye atatembenuka kukhala Mkristu, sanachite manyazi kuuzako ena za chikhulupiriro chatsopano chimene anali atapeza. (Machitidwe 9:17-19, 22) Paulo ankakonda kulankhula m’masunagoge ndiponso ‘kutsimikiza, kuti kunayenera Kristu kumva zowawa, ndi kuuka kwa akufa.’ Mwaluso kwambiri, iye “ananena ndi iwo za m’Malemba” n’cholinga ‘chokopa Ayuda ndi Ahelene.’ Buku lina lotanthauzira mawu limati mawu a Chigiriki amene anawagwiritsa ntchito ponena kuti ‘kukopa’ amatanthauza kuti “kum’sintha munthu maganizo mwanjira yom’pangitsa kumvetsa zinthu zinazake kapena kum’sintha kukhala ndi makhalidwe abwino.” Chifukwa chakuti Paulo analankhula ndi anthu mwanjira yokopa, iye ‘anakopa ndi kutembenuza anthu ambiri.’—Machitidwe 15:3; 17:1-4, 17; 18:4; 19:26.

Kodi N’kuumiriza Kapena N’kukopa?

Masiku ano, mawu akuti “kutembenuza” akhala akuwagwiritsa ntchito ponena za kutembenuza munthu pochita kumuumiriza mwanjira inayake. Baibulo silivomereza kuchita zimenezi. Koma limaphunzitsa kuti anthu analengedwa ndi ufulu ndiponso udindo wosankha zimene akufuna kuchita m’moyo wawo. Anthu alinso ndi ufulu wotere pankhani ya kulambira Mulungu.—Deuteronomo 30:19, 20; Yoswa 24:15.

Yesu anaona kufunika kwa ufulu wochokera kwa Mulungu umenewu posagwiritsa ntchito mphamvu zake zapamwamba kuumiriza munthu wina aliyense kuti avomereze zonena zake. (Yohane 6:66-69) Iye anawalimbikitsa anthu amene ankamumvetsera polankhula mfundo zomveka bwino, zitsanzo, ndiponso mafunso om’pangitsa munthu kuganiza, ndipo zonsezi anazichita n’cholinga choti anthuwo awafike pamtima. (Mateyu 13:34; 22:41-46; Luka 10:36) Yesu anawaphunzitsa ophunzira ake kuti nawonso aziona kuti anthu enanso ali ndi ufulu wawo.—Mateyu 10:14.

N’zoonekeratu kuti Paulo anatengera chitsanzo cha Yesu pautumiki wake. Paulo anakopa anthu amene ankamumvetsera ponena mfundo zomveka bwino za m’Malemba, koma anaganiziranso maganizo a anthu ena pankhaniyi. (Machitidwe 17:22, 23, 32) Iye anamvetsa kuti chimene chiyenera kutilimbikitsa kutumikira Mlengi wathu momasuka ndicho kum’konda Mulungu ndi Kristu. (Yohane 3:16; 21:15-17) Choncho, zimene tingafune kuchita pankhaniyi, ndi nkhani ya kadziŵa mwini.

Nkhani ya Kadziŵa Mwini

Anthu oganiza bwino akamaganizira zinthu zikuluzikulu zoti achite m’moyo wawo, monga nyumba yoti agule, malo oti akagwire ntchito ndiponso mmene angalerere ana awo, sachita zinthuzi mopupuluma. Mwina angayambe afufuza bwino kaye zimene akuganizira kuti angachite, n’kusinkhasinkha zimene apeza pakufufuzako, ndipo mwinanso sangalephere kufunsa ena kuti awathandize maganizo. Akamaliza kuchita zonsezi mpamene angaganize zochita zimene akufunazo.

Palibenso nkhani ina m’moyo imene ili yofunika kukhala ndi nthaŵi ndiponso khama lalikulu kuposa nkhani ya kusankha mmene tiyenera kupembedzera Mulungu. Zimene tingasankhezo zimakhudza mmene tikukhalira panopa, ndipo chofunika kwambiri n’chakuti zimakhudzanso moyo wosatha umene tingadzapeze m’tsogolo. Akristu a ku Bereya a m’zaka 100 zoyambirira za m’nyengo yathu ino anaimvetsa kwambiri mfundo imeneyi. Ngakhale kuti mtumwi Paulo anali atawauza momveka bwino za uthenga wabwino, iwo anafufuzabe Malemba mosamalitsa tsiku lililonse kuti atsimikize ngati zimene anali kuwaphunzitsazo zinalidi zoona. Motero, “ambiri a iwo anakhulupira.”—Machitidwe 17:11, 12.

Masiku ano, Mboni za Yehova zimapitiriza kugwira ntchito yophunzitsa ndi kupanga ophunzira imene Yesu analinganiza. (Mateyu 24:14) Iwo sanyoza ufulu wa anthu ena wokhala ndi chipembedzo chawo. Koma tikanena nkhani youzako ena zachikhulupiriro chawo pankhani yachipembedzo, iwo amatsatira zitsanzo zimene zili m’Baibulo. Amanena mfundo zoona zochokera m’Malemba pochita ntchito imene iwo amaona kuti ndi ntchito yopulumutsa moyo.—Yohane 17:3; 1 Timoteo 4:16.