Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kudalirana kwa Mayiko Kumene Kudzakupindulitseni

Kudalirana kwa Mayiko Kumene Kudzakupindulitseni

Kudalirana kwa Mayiko Kumene Kudzakupindulitseni

“Kuti kudalirana kwa mayiko pazinthu zosiyanasiyana kuyende bwino, m’pofunika kuti amphaŵi ndi olemera omwe zinthu ziziwayendera mofanana. Kudaliranaku kuyenera kuwapatsa anthu ufulu ndi chuma chomwe. Si kuyenera kubweretsa chuma ndiponso njira zolankhulirana zabwino zokha koma kuyeneranso kubweretsa chilungamo pakati pa anthu mosayang’ana nkhope.”—ANATERO MLEMBI WAMKULU WA BUNGWE LA UNITED NATIONS A KOFI ANNAN.

MONGA mmene Kofi Annan ananenera, kudalirana kwenikweni kwa mayiko kutamayenda bwino kungathandize kuti munthu aliyense wokhala padzikoli azisangalala. Koma zimene taona m’zaka zaposachedwapa sizikugwirizana n’komwe ndi mfundo imeneyi. Zinthu zaumisiri ndiponso zinthu zina ndi zina ndizo zatenga malo kwambiri kuposa ufulu wa anthu ndi chilungamo.

Vuto lalikulu ndi lakuti mayiko akulimbikira kuti pakhale kudalirana pazachuma n’cholinga chopezerapo ndalama. Chifukwa choganizira kwambiri za kupeza phindu nthaŵi zambiri saganizira n’komwe za anthu osauka ndiponso anthu ena amene ali pamavuto kapenanso saganizira zatsogolo la dziko lathuli. Dr. David C. Korten anathirira ndemanga kuti, “Malonda a padziko lonse n’ngosayang’aniridwa bwino ndipo amachitidwa makamaka ndi mabungwe azamalonda amene ndalama amaiona ngati chinthu chofunika kwambiri motero malondaŵa sangakhazikike kwenikweni . . . ndipo akusaukitsa anthu m’njira zambiri osati kusoŵa ndalama kokha.”

Kodi mayiko padzikoli adzatha kuyendetsa chuma padziko lonse m’njira imene idzakhale yachilungamo kwa anthu onse? Zimenezo n’zokayikitsa. Pakali pano, mayiko aona kuti n’kovuta kuthetsa mavuto ena alionse apadziko lonse, kaya mavuto a umbanda wapadziko lonse, kutentha kwa dziko, kapena umphaŵi wapadziko lonse. Annan anafotokoza kuti, “M’pofunika kuti mayiko onse agwirizane pothandizana kuchita ntchito zopindulitsa anthu onse padzikoli, koma njira zimene zilipo m’mayiko odalirana amasiku anoŵa zothandizira kuti zimenezi zitheke sizinafikepo n’komwe ayi.”

Njira zapadziko lonse zothetsera mavuto apadziko lonse si ndizo zokha zimene zikufunika. Gulu la anthu amene anasankhidwa kuti aone za kulamulira anthu padziko lonse * linavomereza kuti dzikoli likufunikanso makhalidwe abwino. Lipoti la gululi linati, “Popanda mwambo padziko lonse, mikangano ya padziko lathuli ingawonjezeke; popanda utsogoleri, ngakhale mabungwe kapena njira zapamwamba zotani sizingayende bwino.”

Kodi anati ndi mwambo wotani wapadziko lonse umene uli wabwino? Lipotilo linati, “Anthu ayenera kuchitira ena zinthu zimene iwowo amafuna kuti anthu ena aziwachitira.” Yesu Kristu yemwe ndi mtsogoleri woposa mtsogoleri wina aliyense amene anakhalako padziko pano, anaphunzitsa anthu zakhalidwe limeneli zaka 2,000 zapitazo. (Mateyu 7:12) Koma zimene anaphunzitsazo n’zogwirabe ntchito panopa mofanana ndi nthaŵi imeneyo. N’zosakayikitsa kuti kudalirana kwa mayiko kutakhala kochokera pa mfundo imeneyo kungakhale kopindulitsa munthu wina aliyense. Kodi zimenezo zidzachitika n’komwe?

Njira Ina Yothetsera Mavuto Apadziko Lonse

Baibulo limaneneratu kuti njira yothetsera mavuto apadziko lonse posachedwapa idzagwirizanitsa anthu onse mopanda dyera kapena kugwiritsa ntchito ndalama kapenanso zaumisiri. Njira imeneyo idzatheka chifukwa ili ndi mphamvu ndiponso ili ndi njira zoyendetsera dziko lonse mokomera anthu onse. Yesu Kristu mwini wake ankaganiza za boma lapadziko lonseli pamene anaphunzitsa om’tsatira kupempherera ‘Ufumu wa Mulungu kuti udze ndiponso kuti kufuna kwa Mulungu kuchitidwe pansi pano.’—Mateyu 6:10.

Ufumu wa Mulungu, womwe ndi boma la kumwamba lolamulidwa ndi Yesu Kristu, lidzasonyeza chitsanzo cha mmene anthu apadziko lonse angakhalire amwambo watsopano, umene Yesuyo anaphunzitsa anthu adakali padziko lapansi. Anthu azidzachita zinthu chifukwa cha kukonda Mulungu ndiponso kukonda anzawo. (Mateyu 22:37-39) Maulosi ambirimbiri m’Baibulo amanena zimene boma limeneli lidzachite. Ponena za Wolamulira wake amene ali Yesu Kristu, Baibulo limalonjeza kuti: “Adzaweruza aumphaŵi mwachilungamo ndipo adzateteza ofatsa a m’dziko molungama.” (Yesaya 11:4, The New English Bible) Anthu achuma ndiponso amphamvu sadzadyera masuku pamutu anthu osauka. Yesu ‘adzachitira chisoni wosauka ndi waumphaŵi . . . Adzawombola moyo wawo ku chinyengo ndi chiwawa.’—Salmo 72:13, 14.

Mavuto okhudza zamalo adzakonzedwa nthaŵi yomweyo. Mmalo mwa zipululu zopanda zomera, “chipululu chidzakondwa, ndipo maluŵa adzamasula bwino m’malo ouma.” (Yesaya 35:1, Today’s English Version) Mmalo mokhala ndi zakudya zopereŵera, “m’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka.”—Salmo 72:16.

Ufumu wa Mulungu umagwirizanitsa anthu osiyanasiyana. Mulungu analonjeza kuti, “Ndidzawaika pamodzi ngati nkhosa za ku Bozira.” Iye ananenanso kuti, ‘Ndidzawasintha kuti alankhule chinenero choyera, kuti iwo onse anditumikire mogwirizana.’ (Mika 2:12; Zefaniya 3:9) “Chinenero choyera” chimenechi, chilinso ndi mfundo za kakhalidwe ndiponso kapembedzedwe kofanana ndipo chikugwirizanitsa anthu ngakhale panopa.

Chifukwa chakuti anthu angathe kuyenda padziko lonse, Mboni za Yehova zimakhala ndi misonkhano ikuluikulu yosiyanasiyana, yomwe imalimbikitsa kugwirizana kwa pakati pa anthu osiyana mitundu, mayiko ndiponso zikhalidwe. Misonkhano imeneyi imaikiradi umboni wa kugwirizana kumene kumakhudza mitima ndi maganizo, osangoti kokhudza zaumisiri ndiponso zamalonda. (Onani bokosilo.) Munthu wina wa ku Spain wa maphunziro azaumulungu amene anasonkhana nawo pamisonkhano yotereyi analemba kuti: ‘Ndinachoka pamsonkhanopo nditalimbikitsidwa kwambiri chifukwa cha nkhani za m’Malemba zimene zinakambidwa komanso chifukwa cha kugwirizana kwa anthu ameneŵa, makhalidwe awo apamwamba kwambiri ndiponso abwino.’

Mboni za Yehova zimatengerapo mwayi pa kugwirizana kwa mayiko zikamachita ntchito yolalikira uthenga wabwino wokhudza za Ufumu wa Mulungu. Mwachitsanzo Galamukani! imatembenuzidwa m’zilankhulo zokwana 87 ndi otembenuza ambirimbiri padziko lonse pogwiritsa ntchito makompyuta ndiponso mauthenga odzera pamakompyuta. Zida ngati zimenezi zimathandiza Mboni za Yehova kuti ntchito yawo yophunzitsa Baibulo ikhaledi ya padziko lonse. Indedi, zida zothandiza kuti mayiko akhale odalirana m’njira zosiyanasiyana zingathe kugwiritsidwa ntchito m’njira zothandiza komanso zowononga.

Moteronso, m’malo moyambitsa mavuto, monga zachitikira chifukwa cha kudalirana kwa mayiko, boma la padziko lonse lokhazikitsidwa ndi Mulungu lidzapereka njira zothetsera mavutowo. Palibenso chilichonse chingatikayikitse pa ulamuliro wakumwamba umenewu. Mulungu akulonjeza kuti, “Ndilenga dziko lapansi latsopano; ndipo zinthu zakale sizidzakumbukika. . . Khalani inu okondwa ndi kusangalala ku nthaŵi zonse ndi ichi ndichilenga.” (Yesaya 65:17, 18) “Dziko latsopano” la Mulungu lidzapindulitsadi anthu padziko lonse.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Gululi, limene lili ndi atsogoleri 28 otchuka padziko lonse, linalemba lipoti lalitali m’chaka cha 1995 la mutu wakuti, “Mgwirizano Wathu Padziko Lonse,” ndipo mu lipotilo analembamo zimene akuganiza kuti maboma apadziko lonse asinthe n’cholinga choti aziyendetsa bwino zinthu.

[Bokosi patsamba 28]

TINGATHE KULANKHULANA MOSAVUTA KOMA SITIGWIRIZANA

Ngakhale kuti zaumisiri zathandizapo kuti anthu tizilankhulana mosavuta padziko lonse, anthu sakugwirizanabe. Ma TV, maselura ndiponso maintaneti athandiza anthu kuti azilankhula mosavuta koma osati kuwagwirizanitsa. Kugwirizana pazachuma ndiponso kutha kwa kukangana kwa Mayiko amphamvu kwambiri kwachepetsa nkhondo zimene mayiko ankachita, koma nkhondo zoopsa zapachiŵeniŵeni zikupitirizabe kupha ndiponso kupundula anthu ambirimbiri chaka chilichonse.

N’chifukwa chiyani zimenezi zikuchitikabe? N’chifukwa chakuti palibe chizindikiro chilichonse chosonyeza kuti chidani cha mafuko a anthu, mitundu ndiponso magulu a zipembedzo, chomwe nthaŵi zambiri chimayambitsa nkhondo zapachiŵeniŵeni chikutha. Komanso malonda apadziko lonse ndiponso magulu a umbanda amachititsa kuti pakhale zida zankhondo zambiri zotsika mtengo mwakuti magulu omenyana amakhala achikwanekwane. Zipangizo zaumisiri zoyendera magetsi sindizo zimene zingabweretse mgwirizano weniweni. Ndiponso chuma chimene chimabwera pazamalonda sichingalimbikitse kuti anthu akhale achilungamo.

M’njira zina, kudalirana kwa mayiko pazachuma kungapangitse kusagwirizana. Chuma chikapanda kuyenda bwino m’dziko, anthu osauka angathe kugwiritsidwa ntchito mosavuta ndi anthu andale ankhanza amene amati akaona kuti anthu akudandaula ndi umphaŵi amapezerapo mwayi wokwaniritsa zolinga zawo powanyengerera. Kodi njira yothetsera mavutoŵa n’njotani? Chikalata cha Human Development Report 1999 chinati, “Mpofunika kuti pakhale njira zatsopano zoyendetsera mayiko pawokha ndiponso dziko lonse, ndipo njirazi makamaka zikhale zothandiza anthu kuchitira zinthu pamodzi ndiponso zikhale zachilungamo.” Zimenezi ndizo zimene kwenikweni Ufumu wa Mulungu udzachite.

[Chithunzi patsamba 29]

Ntchito ya Mboni za Yehova yophunzitsa anthu Baibulo yathandiza kuti anthu osiyanasiyana akhale ogwirizana