Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Sayansi ndi Chipembedzo Zikulimbana

Sayansi ndi Chipembedzo Zikulimbana

Sayansi ndi Chipembedzo Zikulimbana

“Kodi tingalakwitse titanena kuti chipembedzo kwenikweni chili ngati matenda opatsirana a m’maganizo?”—Anafunsa choncho katswiri wa sayansi ya zinthu zamoyo Richard Dawkins.

NTHAŴI zina anthu amaganiza kuti chipembedzo ndi sayansi sizingagwirizane ngakhale pang’ono. Ena amaona kuti ndi zinthu zimene zikulimbana kwambiri mwakuti zimaoneka ngati kuti china chingayende bwino pokhapokha chinzakecho chitalekeratu kugwira ntchito.

Pali anthu ena asayansi, monga wasayansi ya zamankhwala wina dzina lake Peter Atkins, amene amaona kuti “n’zosatheka” kugwirizanitsa chipembedzo ndi sayansi. Atkins ananena kuti “n’kupanda nzeru kukhulupirira kuti Mulungu (ndiye analenga chinthu chinachake, ndipo kunena kuti ndiye analenga zinthu zonse) n’kupusa kwenikweni.”

Ndiye palinso anthu achipembedzo amene amanena kuti sayansi ndiyo yachititsa kuti anthu akhale osakhulupirira chipembedzo. Anthu oimba mlandu sayansiŵa amakhulupirira kuti sayansi yamasiku ano n’njosocheretsa; inde imanena zoona, komano imasokoneza chikhulupiriro cha anthu posinjirira zoonazo. Mwachitsanzo, katswiri wa sayansi ya zinthu zamoyo dzina lake William Provine ananena kuti chiphunzitso chakuti zinthu zamoyo sizinachite kulengedwa koma zinangokhalapo zokha chimasonyeza kuti “palibe maziko enieni a makhalidwe abwino, ndiponso kuti moyo ulibe ntchito yeniyeni.”

Komabe, pakhalanso kulimbana chifukwa cha nkhani zina zabodza kapena zosatsimikizirika zochokera ku mbali zonse ziŵirizi. Kwa zaka mazana ambiri, atsogoleri achipembedzo akhala akuphunzitsa nthano zopanda umboni ndiponso ziphunzitso zolakwika zimene zili zotsutsana ndi zimene asayansi apeza masiku ano ndiponso zimene sizili zochokera m’Malemba ouziridwa. Mwachitsanzo, tchalitchi cha Roma Katolika chinadzudzula Galileo chifukwa chakuti ananena zoona atapeza kuti dziko ndilo limazungulira dzuŵa. Zimene Galileo ananenazo sizotsutsana ndi Baibulo ngakhale pang’ono, koma zinali zotsutsana ndi zimene tchalitchicho chinkaphunzitsa panthaŵiyo. Komanso nawo asayansi amalakwa akamaphunzitsa anthu zinthu zosatsimikizika kuti zamoyo zinachita kusanduka kuchokera ku zinthu zopanda moyo popanda kulengedwa ndi Mulungu ngati kuti n’zoona. Iwo amanyoza kukhulupirira zachipembedzo kuti n’kusadziŵa zasayansi.

Motero, kodi n’zotheka kugwirizanitsa mfundo zasayansi ndi zachipembedzo? Inde, n’zotheka ndithu. Kwenikweni mfundo zasayansi zimene zinatsimikiziridwa zimagwirizana, osati kutsutsana, ndi mfundo zachipembedzo choona.

[Chithunzi pamasamba 2, 3]

Galileo anaphunzitsa sayansi yoona, zimene zinachititsa kuti tchalitchi chake chimudzudzule