Tikukuitanani ku Msonkhano Wachigawo wa “Olengeza Ufumu Achangu”
Tikukuitanani ku Msonkhano Wachigawo wa “Olengeza Ufumu Achangu”
KU MALAŴI kokha, kudzachitika misonkhano 27 yotereyi. Woyamba udzachitika pa August 9 mpaka pa August 11, ndipo womaliza udzachitika kumayambiriro kwa September. N’zosakayikitsa kuti umodzi mwa misonkhano ya masiku atatu imeneyi, imene kaŵirikaŵiri imachitika kuyambira Lachisanu mpaka Lamlungu, udzachitikira mumzinda wa kufupi ndi kwanuko.
M’malo ambiri, msonkhanowu udzayamba ndi nyimbo nthaŵi ya 9:30 m’maŵa. Patsiku loyamba nkhani ya malonje ikadzatha padzabwera nkhani imene adzafunse mafunso anthu ena olengeza Ufumu. Kenaka pambuyo pa nkhani yakuti “Kondwerani ndi Yehova” ndiponso yakuti “Khalani Oyamikira” tidzamaliza chigawo cham’maŵachi ndi nkhani yaikulu yakuti, “Changu cha Olengeza Ufumu Chinakolezeka.”
Lachisanu, chigawo chamadzulo chidzakhala ndi nkhani yosiyirana ya mbali zitatu, ya mutu wakuti, “Ulosi wa Mika Umatilimbikitsa Kuti Tiyende M’dzina la Yehova,” kenaka chidzakhalanso ndi nkhani ina yakuti “Khalanibe Oyera mwa Kutchinjiriza Mtima Wanu” ndiponso yakuti “Peŵani Chinyengo.” Potsiriza pake, anthu adzathandizidwa kwambiri pa za utumiki wachikristu m’nkhani yotsirizira pa tsikuli yakuti, “Lambirani Mulungu Woona Yekha.”
Chigawo cha Loŵeruka m’maŵa chidzakhala ndi nkhani yosiyirana ya mbali zitatu ya mutu wakuti “Olengeza Ufumu Amene Amalemekeza Utumiki Wawo.” Nkhani zimene zidzatsatire zidzakhala zolimbikitsa ndipo zidzakhala ndi mitu yakuti “Chifukwa Chomwe Tiyenera ‘Kupempherera Kosaleka’” ndiponso “Kukambirana Nkhani Zauzimu Kumalimbikitsa.” Pulogalamu yam’maŵa idzatha ndi nkhani yonena za kudzipatulira ndiponso za ubatizo, kenaka anthu oyenerera adzakhala ndi mpata wokabatizidwa.
Chigawo chamadzulo pa Loŵeruka chidzakhala ndi nkhani yosiyirana yotsiriza pamsonkhanowu ya mbali zitatu ya mutu wakuti, “Chikhulupiriro Chathu Chimayesedwa ndi Mayesero Osiyanasiyana.” Nkhani zitatuzi zidzathandiza Akristu kuti athe kulimbana ndi mavuto obwera chifukwa chosaloŵerera m’ndale. Pulogalamu ya Loŵeruka idzatha ndi nkhani yapadera kwambiri pa msonkhanowu ya mutu wakuti, “Yandikirani kwa Yehova.”
Pulogalamu ya m’maŵa Lamlungu idzakhudza kwambiri achinyamata, ndipo idzayamba ndi nkhani yakuti “Kodi Mumakhulupirira Yehova?” ndiponso yakuti “Achinyamata—Konzani Tsogolo Lanu ndi Gulu la Yehova.” Nkhani yachiŵiriyi idzakhala ndi mbali ya mphindi 20 yofunsa achinyamata ena mafunso ena ndi ena. Kenaka padzakhala seŵero losimba za Yeremiya, amene anakana atasankhidwa kukhala mneneri ponena kuti, ‘ndine mwana,’ ndipo ochita seŵeroli adzavala zovala zogwirizana ndi za nthaŵi yakaleyo. (Yeremiya 1:6) Pambuyo pake padzakhala nkhani yogogomezera uthenga wa m’seŵerolo. Pulogalamu ya kumadzulo idzakhala ndi nkhani ya anthu onse, yakuti “Maonekedwe a Dzikoli Akusintha.”
Ndithu mudzapindula kwambiri mwauzimu m’moyo wanu mukadzabwera masiku atatu onseŵa. Kuti mudziŵe kumene misonkhanoyi idzachitikire chakwanuko, kafunseni ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova ya kwanuko kapena lemberani kalata kwa ofalitsa a magazini ino.