Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tizilombo Tochotsa Nyansi Mogometsa

Tizilombo Tochotsa Nyansi Mogometsa

Tizilombo Tochotsa Nyansi Mogometsa

ZAKA zongopitirira 150 zapitazo, anthu anayamba kukonza njira zapamwamba zodutsamo zoipa ndiponso nyansi. Komabe apa n’kuti katswiri wina wochotsa nyansi alipo kale, ndipo katswiriyu ndi kanyerere kenakake ka m’dera lotentha la ku America.

Mtundu wapadera wa nyererezi zomwe zimakwana mwina miliyoni zimakhala kufunkha lalikulu pansi panthaka ndipo zimaduladula masamba a mitengo. Nyererezi zimakhala m’magulu n’kugaŵana ntchito zosiyanasiyana. Gulu lina limatolera masamba othothoka, ndipo lina limatafuna masambawo n’kuwasandutsa ngati chigwada. Nyerere zimene ntchito yawo ili yolima chakudya zimagwiritsa ntchito masambawo ngati manyowa opangitsa kuti m’funkhamo mumere bowa winawake umene nyererezo zimadya. Zimachotsanso chilichonse chimene chingafalitse matenda, monga tizilombo towononga, bowa wakupha, nyerere zakufa kapena zimene zatsala pang’ono kufa, ndiponso zinthu zowola. Koma kodi nyererezi zimachotsa bwanji zinyalala m’funkha mwawo?

Malingana ndi nyuzipepala ya The Independent, akuti asayansi ena a ku Britain ochokera pa yunivesite yotchedwa Sheffield anatulukira mmene nyererezi zimachotsera zinyalalazi. Kufupi ndi kumene kumakhala nyerere zolima zija kuli mafunkha ena aakulu kumene zimatayako zinyalala. Nyerere zimene zimagwira ntchito kumene kuli zinyalalazi zimangokhalira kutembenuza zinyalalazo kuti zonse ziwolerane, motero tizilombo toyambitsa matenda timafa. Nyerere zolima siziloŵa n’komwe m’mafunkha mmene muli nyansi. Zimangounjika zinyalalazo panjira, ndipo nyerere zonyamula zinyalala zija zimabwera n’kudzazitengapo. Njira yochotsera zinthu zoipa imeneyi imateteza matenda ena alionse amene angathe kugwira mtundu wa nyererezi.

Yehova Mulungu analenga tizilombo tokhala ndi nzeru zachibadwa komanso zaka 3,500 zapitazo anapatsa Aisrayeli malangizo othandiza. Kugwiritsa ntchito malangizo ameneŵa kunkathandiza kuti zakudya ndiponso madzi asamakhale ndi matenda, kunkaletsa kufalikira kwa matenda opatsirana, ndiponso kunkachititsa kuti nyansi zizikwiriridwa bwinobwino. Anthu akanapeŵa matenda ndiponso imfa zambirimbiri akanati azitsatira mfundo zimenezi!—Levitiko 11:32-38; Numeri 19:11, 12; Deuteronomo 23:9-14.