Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Apolisi Ali ndi Tsogolo Lotani?

Kodi Apolisi Ali ndi Tsogolo Lotani?

Kodi Apolisi Ali ndi Tsogolo Lotani?

TIKANAKHALA opanda apolisi mwina bwenzi zinthu zili zosokonekera kwambiri. Komabe ngakhale kuti apolisiwo tili nawo, kodi dziko lathuli ndi losaopsa? M’mizinda yambiri masiku ano, monganso mmene zilili kumidzi yambiri, anthu akuona kuti pali vuto lalikulu lokhudza chitetezo. Kodi tiyenera kuganiza kuti apolisi ndiwo angatipulumutse ku zigaŵenga ndiponso kwa a kabwerebwere? Kodi tiyenera kuganiza kuti apolisi ndiwo angapangitse kuti m’misewu mwathu mukhale mosaopsa? Kodi adzapambana pankhondo yolimbana ndi umbanda?

David Bayley anatchula maganizo ake m’buku lake lakuti Police for the Future. Iye anati: “Apolisi sathetsa umbanda. Ndithudi, tikhoza kuyerekezera apolisi ndi kansalu komangira pachilonda chosamva mankhwala. . . . Sitingadalire apolisi, kuti ndiwo angathetse umbanda pakati pa anthu ngakhale kuti amadzipereka kwambiri kuti atero.” Ofufuza anapeza kuti ntchito zitatu zikuluzikulu zomwe apolisi amagwira, monga kuyendera misewu, kuthamangira kwa anthu amene ayimba foni kuwauza zinthu zamwadzidzidzi ndiponso kufufuza anthu olakwira malamulo, sizithetsa umbanda. N’chifukwa chiyani zili choncho?

Kuyesa kuletsa umbanda powonjezera apolisi ambiri n’kongowonongetsa chuma. Anthu amene amalakwira malamulo alibe nazo ntchito zoti apolisi oyendera madera achuluka. Komanso ngakhale apolisi atamafulumira kufika pamalo enaake kudzathandiza akamva zinthu, si kuti anthu ambanda amaleka kuchita umbanda. Apolisi anenapo kuti mwina akapanda kufika pomwe pachitika zachisokonezo pasanathe mphindi imodzi, zimavuta kwambiri kum’gwira wosokonezayo. Zikuoneka kuti anthu ambanda amadziŵa kuti kaŵirikaŵiri apolisi safika msanga choncho kudzathandiza. Ngakhalenso ofufuza anthu olakwira malamulo sathandiza. Ngakhale apolisi ofufuza milandu akawapeza anthu olakwawo n’kukawatsekera kundende, si kuti kwenikweni zimenezi zimaletsa umbanda. Dziko la United States limatsekera m’ndende anthu opalamula milandu ambirimbiri kuposa dziko lina lililonse, koma anthu ambanda alikobe ochuluka kwambiri; pamene ku Japan komwe kuli anthu ochepa m’ndende, kulinso ambanda ochepa kwambiri. Ngakhalenso mabungwe monga magulu othandizana ndi apolisi sanafikebe pothandiza kwenikweni, makamaka m’madera mmene muli ambanda ochuluka. Njira zokhwima zimene amazikhazikitsa pofuna kuthana ndi milandu ina, monga kuzembetsa mankhwala ozunguza bongo kapena kuba, zimakhala zothandizako ndithu kwakanthaŵi, koma kenaka zimangofa.

Buku lakuti Police for the Future limati: “Mfundo yakuti apolisi sangathe kuthetsa umbanda siyenera kudabwitsa kwambiri anthu oganiza. Anthu ambiri amadziŵa kuti zimene zimachititsa kuti anthu aziphwanya lamulo ndi zochita za anthu zimene sizikhudzana ndi ntchito ya apolisi, komanso magulu onse oona zachilungamo.”

Kodi Chingachitike N’chiyani Patapanda Apolisi?

Kodi pakapanda apolisi amene akukuonani mumachita zinthu zotani? Kodi mumapezerapo mwayi wophwanya malamulo? N’zodabwitsa kuti anthu ambiri aulemu wawo ndiponso achuma ndithu amawononga mbiri ndi tsogolo lawo chifukwa chofuna kupeza zinthu mwachinyengo pantchito yawo yapamwamba. Nyuzipepala ya The New York Times posachedwapa inalemba kuti ‘anthu 112 anawapeza ndi mlandu wochita zachinyengo, omwe akuti anakonza zakuti abe ndalama za makampani enaake ochita za inshuwalansi ya magalimoto. Ena amene mlanduwu unawakhudza anali maloya, madokotala amatenda osiyanasiyana ndiponso wachiŵiri kwa wamkulu wina woyang’anira apolisi.’

Mlandu wina waukulu wokhudza zachinyengo posachedwapa unachititsa nthumanzi anthu amene amapereka thandizo la ndalama zoyendetsera ntchito yaluso la zojambulajambula pamene akuluakulu akale panyumba zogulitsirako malonda zotchedwa Sotheby’s ku New York ndiponso Christie ku London anawapeza ndi mlandu woika mitengo yazinthu yabodza. Nyumba zogulitsira malondazi ndiponso akuluakuluŵa akufunika kulipira ndalama zokwana madola 843 miliyoni zowakhaulitsira komanso zoti alipire anthu! Motero kusakhutitsidwa ndi ndalama kumachitika pakati pa anthu amaudindo alionse.

Zimene zinachitika mumzinda wa Recife ku Brazil, m’chaka cha 1997 pamene apolisi ananyanyala ntchito yawo zikusonyeza kuti anthu ambiri amaphwanya malamulo pakakhala kuti palibe owaletsa kutero. Za Mulungu siziwakhudza n’komwe pazochita zawozo. Iwo akhoza kuchepetsa kapena kulekeratu mwambo wabwino ndiponso chikhalidwe chabwino mosavuta. N’zosadabwitsa kuti apolisi m’mayiko ambiri akungopumphunthitsa manja awo pachabe pakati pa anthu amene amakonda kuchita zinthu zachisokonezo, kaya zing’onozing’ono kapena zikuluzikulu.

Koma anthu ena amamvera malamulo chifukwa chakuti amalemekeza olamulira. Mtumwi Paulo anauza Akristu a ku Roma kuti ayenera kumvera anthu amene Mulungu wawalola kuti azilamulira chifukwa chakuti amayesetsako ndithu kuthandiza anthu kuchita zinthu mwadongosolo. Pa za olamulira otereŵa iye analemba kuti: “Ndiye mtumiki wa Mulungu, kuchitira iwe zabwino. Koma ngati uchita choipa, opatu, pakuti iye sagwira lupanga kwachabe; pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu wakukwiyira ndi kubwezera chilango wochita zoipa. Chifukwa chake, kuyenera kuti mukhale omvera, sichifukwa cha mkwiyo wokha, komanso chifukwa cha chikumbumtima.”—Aroma 13:4, 5.

Kusintha Mmene Anthu Amakhalira

Mosakayikira ntchito ya apolisi imathandizadi kuti anthu ayambe kukhala bwino. M’dera linalake zikaonekeratu kuti achotsamo anthu onse ogulitsa mankhwala ozunguza bongo m’misewu ndiponso ochita zachiwawa, anthu amayamba kutsatira khalidwe labwino logwirizana ndi mmene zinthu zasinthira m’deralo. Koma kunena zoona, sikuti apolisi angathe kuwasintha kwenikweni anthu.

Kodi mumtima mwanu mungaganizireko za dera linalake limene anthu amalemekeza kwambiri malamulo mwakuti safunikira n’komwe apolisi? Kodi mungaganizireko dziko linalake limene anthu amaganizirana kwambiri mwakuti anthu oyandikana nawo amafunitsitsa kuthandiza anzawowo ndipo aliyense safunikira kuitana apolisi kuti adzam’thandize? Mwinatu zimenezi zikumveka ngati nkhambakamwa chabe. Koma mawu a Yesu awa, ngakhale kuti ankanena zankhani ina, akugwiranso ntchito pankhaniyi. Iye anati: “Ichi sichitheka ndi anthu, koma zinthu zonse zitheka ndi Mulungu.”—Mateyu 19:26.

Baibulo limafotokoza za nthaŵi ina m’tsogolo pamene anthu onse adzalamulidwe ndi boma limene Yehova Mulungu adzalikhazikitsa. Ilo limati: “Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu . . . udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse.” (Danieli 2:44) Pophunzitsa anthu onse okhulupirika za chikondi cha Mulungu, boma latsopano limeneli lidzasintha zochita za anthu zimene zimabweretsa umbanda. “Dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.” (Yesaya 11:9) Mfumu yoikidwa ndi Mulungu, Yesu Kristu, adzakwanitsa kuletsa zinthu zonse zachisokonezo. “Sadzaweruza monga apenya maso, sadzadzudzula mwamphekesera; koma ndi chilungamo adzaweruza aumphawi, nadzadzudzulira ofatsa a m’dziko mowongoka.”—Yesaya 11:3, 4.

Sikudzakhala ochita zachisokonezo kapena milandu. Apolisi adzakhala alibe ntchito. “Adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwaopsa.” (Mika 4:4) Ngati mukufuna kudzakhala m’gulu la anthu a mu “dziko latsopano” limene lafotokozedwa m’Baibuloli, ino ndiyo nthaŵi yofufuza zimene Mulungu walonjeza m’Mawu ake.—2 Petro 3:13.

[Mawu Otsindika patsamba 12]

Kodi mumtima mwanu mungaganizireko za dera linalake limene anthu amalemekeza kwambiri malamulo mwakuti safunikira n’komwe apolisi?

[Mawu Otsindika patsamba 12]

Sikudzakhala anthu ophwanya lamulo la boma kapenanso umbanda

[Bokosi/Chithunzi patsamba 11]

Apolisi Akulimbana ndi Zigaŵenga

Monga mmene zinthu zimene zinachitika pa September 11, 2001 mumzinda wa New York City ndiponso ku Washington, D.C. zinasonyezera, zikuoneka kuti zigaŵenga zolanda ndege ili m’mlengalenga, anthu ogwira anzawo ukaidi pazifukwa zandale ndiponso zigaŵenga zinanso zikuchititsa kuti apolisi azivutika kwambiri pofuna kuteteza anthu. Magulu apolisi apadera m’madera ambiri padziko lonse akhala akuphunzitsidwa kuloŵa mwamsangamsanga m’ndege imene yatera kuti wina asasokoneze n’komwe. Iwo aphunziranso maluso oloŵa m’zinyumba modzidzimutsa, pogwiritsa ntchito chingwe chochokera kudenga, kudumpha kudzera m’mawindo, ndiponso kuponya mabomba okomola komanso aphunzira kuponya tizitini tokhala ndi utsi wokhetsa misozi. Apolisi ophunzitsidwa chonchiŵa nthaŵi zambiri alimbana ndi kugonjetsa zigaŵenga popanda kuika pachiswe moyo wa anthu amene agwidwa ndi zigaŵengawo.

[Mawu a Chithunzi]

James R. Tourtellotte/U.S. Customs Service

[Chithunzi patsamba 12]

Zinthu zimene sizidzafunikanso m’dziko latsopano la Mulungu