Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndinali Wandale Tsopano Ndinasanduka Mkristu Wosakhudzidwa N’zandale

Ndinali Wandale Tsopano Ndinasanduka Mkristu Wosakhudzidwa N’zandale

Ndinali Wandale Tsopano Ndinasanduka Mkristu Wosakhudzidwa N’zandale

YOSIMBIDWA NDI LADISLAV ŠMEJKAL

Mlandu wanga utazengedwa, anakanditsekeranso m’ndende. Nthaŵi yomweyo, ndinayamba kumuuza mnzanga yemwe anali zipinda ziŵiri pamwamba pa chipinda chomwe ine ndinali mmene zonse zayendera mwanjira yachinsinsi yongogogoda khoma popanda kutulutsa mawu alionse. Iye anali tcheru kufuna kumva kuti andipatsa chilango chotani.

Ndinagogoda pomuuza kuti, “Alamula kuti ndikhale m’ndende zaka 14.”

Sanakhulupirire. Choncho anafunsa kuti: “Wati miyezi 14?”

“Ayi, ndati zaka 14,” ndinayankha motero.

ZIMENEZI zinachitika m’chaka cha 1953 m’dziko la Czechoslovakia (limene masiku ano amalitcha kuti Czech Republic). Panthaŵi imeneyo n’kuti ndili wandale wofuna kusintha zinthu wa zaka 19. Ife amene tinkalimbana ndi chipani chimene chinkalamulira cha Communist Party panthaŵi imeneyo, tinkafalitsa maganizo athu polemba makalata onyoza chipanicho n’kuwagaŵa kwa anthu. Anagamula kuti zimene tinkachitazo zinali kuukira boma, n’chifukwa chake ndinalandira chilango chokhala m’ndende nthaŵi yaitali.

Anali atanditsekera kale m’ndendemo pafupifupi kwa chaka chathunthu mlandu wanga asanauzenge. Asanawazenge mlandu wawo akaidi, ankawatsekera m’zipinda za anthu aŵiriaŵiri, ndipo nthaŵi ndi nthaŵi ankawatenga atawamanga kumaso kuti akawafunse mafunso. Tikakhala m’zipinda zathuzo, sankatilola kulankhula, choncho tinkangonong’onezana kapena kungogwiritsa ntchito njira yogogoda khoma ija.

Sizinanditengere nthaŵi yaitali kuzindikira kuti akaidi ambiri m’ndendeyo anali Mboni za Yehova. M’ndende yathuyi akaidi ankakonda kuwasinthasintha zipinda mwina mwezi uliwonse kapena pamiyezi iŵiri iliyonse. Ndinakondwa pamene anadzandiika pamodzi ndi wa Mboni chifukwa chakuti Baibulo linkandisangalatsa. Patapita kanthaŵi, ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboniwo.

Ngakhale kuti tinalibe Baibulo kapena buku lililonse lofotokoza za m’Baibulo, ndikukhulupirira tikhoza kunena kuti kukambirana kwathu kunali kuphunzira Baibulo. Ponena mosapita m’mbali, panthaŵiyi n’kuti ndisanaonepo Baibulo chibadwireni. Koma tinkatha kukambirana, chifukwa wa Mboniyu ankafotokoza nkhani za m’Baibulo zimene ankakumbukira ndipo ine ndinkalemba zimene ankanenazo. Zonsezi zinkachitika titakhala mogundizana kwambiri n’kumanong’onezana.

Zinthu zokha zimene tinali nazo zinali mapepala a kuchimbudzi ndi chipeso. Ndinagwiritsa ntchito chipesocho kulembera mfundo zina pa mapepalawo. Malemba ambiri amene tinkakambirana ndinangowaloŵeza pamtima. Mboni zimene zinaphunzira nane zinandiphunzitsanso nyimbo za Ufumu. Mboni ina inandiuza kuti: “Panopa uli m’ndende chifukwa cha mlandu wokhudza zandale, koma m’tsogolomu ukhoza kudzamangidwa chifukwa choti uli m’gulu la Mboni za Yehova.”

Pomalizira pake, atandifunsa mafunso ambirimbiri, mlandu wanga unazengedwa kenaka anandipititsa ku ndende ina kufupi ndi tauni yotchedwa Jáchymov, kokagwira ntchito yakalavula gaga. Apa, n’kuti nditakhutira kale kuti tsiku lina ndidzakhala wa Mboni za Yehova basi.

Ndinakhala Zaka Zambiri Ndili M’ndende

Nditafika ku kampuyo kumene ankakumbako miyala inayake yotchedwa uranium, ndinafulumira kufunafuna anthu amene anali Mboni. Koma posakhalitsa ndinauzidwa kuti anawapititsa kwina. Komabe mmodzi wa m’gululi sanapite nawo chifukwa chakuti ankadziŵa bwino zophikaphika. Iye anandibwereka Baibulo linalake lakale kwambiri limene linadutsa mwambiri chifukwa cholibisabisa. Choncho ndinaŵerenga malemba amene ndinali nditawaloŵeza pamtima. Chamumtima ndinkangoti, ‘Sizikusiyana n’komwe ndi zimene abale aja anandiphunzitsa.’

Patatha mwinamwake mwezi umodzi, anandisamutsira ku kampu ina yotchedwa Bytiz, kufupi ndi tauni ya Příbram. Ndinakumana ndi anthu ena amene anali Mboni kumeneko. Tili ku Bytiz, nthaŵi zonse tinkalandira mabuku ofotokoza za m’Baibulo amene ankafika mwanjira yozembetsa. Ngakhale kuti akuluakulu a pa kampupo ankayesetsa kufufuza kuti adziŵe mmene tinkalandirira mabukuwo, iwo analephera kupeza njira yake. Panali akaidi okwana mpaka 14 omwe ankachitira umboni kwa ena mwakhama. Obatizidwa analipo asanu ndi aŵiri, ndipo asanu ndi aŵiri enawo anali ngati ine ndemwe, anthu omwe anayambira kundendeko kugwirizana ndi zimene anthu a m’gulu la Mboni amakhulupirira.

Ambirife tinkafuna kuonetsa kudzipereka kwathu kwa Mulungu mwa kubatizidwa. Koma chifukwa chosoŵa madzi, kapena ndingonena mwatchutchu kuti, chifukwa chosoŵa chinthu choti n’kuikamo madzi okwanira kubatiza munthu, kunali kovuta kwambiri kuti munthu amizidwe. Choncho, anthu ambiri m’masiku amenewo ankangodikira kuti adzabatizidwa akadzatuluka m’ndendemo. Komabe ku kampu ya ku Bytiz anamangako nsanja zimene zinkaloŵetsa mphepo m’migodi. Cha m’ma 1955, ambiri pagulu lathu tinabatizidwa m’thanki yaikulu yamadzi ogwiritsidwa ntchito pa imodzi ya nsanjazo.

Patatha zaka zochepa chabe, m’chaka cha 1960 mwezi wa March, wapolisi amene ankayang’anira akaidi omwe milandu yawo inkakhudzana ndi ndale anandiitana. Iye ananena kuti ngati nditamuuza zimene akaidi ena akuchita, akhoza kukonza zondichepetsera masiku anga okhala m’ndende. Nditakana kuchita zimenezo, anayamba kundilalatira monyoza kwambiri. Iye anakalipa mokuwa amvekere, “Wakana wekha mwayi woti umasuke. Ndionetsetsa kuti usadzapitenso kwanu! Udzafera mom’muno.” Komabe patangotha miyezi iŵiri, boma linakhululukira onse amene anamangidwa pa zifukwa zangati za ine ndipo patatha zaka zisanu ndi zitatu ndili m’ndende, ndinabwerera kwathu.

Ndinapeza Kaufulu kwa Nthaŵi Yochepa Chabe

Kuyambira mwezi wa April m’chaka cha 1949 mpaka panthaŵiyo n’kuti ntchito ya Mboni za Yehova ili yoletsedwa ku Czechoslovakia, choncho sindinaone kusiyana kwake kotumikira Mulungu panthaŵi imeneyi imene ankati ndili pa ufulu ndi kum’tumikira pamene ndinali m’ndende. Tsopano atandimasula, ndinakumana ndi vuto linanso. Nthaŵi imeneyo ankati mwamuna aliyense wa m’dzikolo kaya afune kaya asafune, ayenera kupita kunkhondo kwa zaka ziŵiri.

Amuna ena amene ankagwira ntchito m’mabungwe ena aboma sankapita nawo kunkhondoko. Mwachitsanzo, onse amene ankagwira ntchito m’migodi ya malasha sankapita kunkhondoko. Popeza kuti ndinali nditagwirako ntchito ya m’migodi, ndinapeza ntchito pa mgodi wina wa malashawo. Kumeneko anandilandira ndi manja aŵiri. Iwo anandiuza kuti: “Usadandaule n’zopita kunkhondo. Kukuthandiza kuti usapite kunkhondo si nkhani kwa ife.”

Patangotha miyezi iŵiri, nditalandira chikalata chondidziŵitsa zakuti kaya ndikufuna kapena ayi, ndiyenera kupita kunkhondo, kachiŵirinso akuluakulu a pam’godiwo ananditsimikizira kuti: “Usadandaule, mwina anthu amenewo angolakwitsa. Tiwalembera kalata ndipo nkhani imeneyo itheratu.” Koma zinthu sizinatero ndithu. Patapita nthaŵi ndithu, bwana wina anabwera kudzandipepesa akunena kuti: “Pepa ambwana, aka n’koyamba kuchitika zoterezi, ndiyetu basi uyenera kupita kunkhondo.” Koma ine poganizira za chikhulupiriro changa pankhani yopita kunkhondo, ndinakana kupita ndipo anandimanga n’kundipititsa kundende ina ya asilikali ankhondo imene siinali kutali kwambiri.—Yesaya 2:4.

Kuzengedwa Mlandu

Atandimanga m’tauni ya Kladno m’chaka cha 1961, anayesetsa kundinyengerera kuti ndikhale msilikali wankhondo. Mkulu wina wa asilikali anaitanitsa msonkhano. Anapita nane m’chipinda chochitiramo misonkhano momwe munali chitebulo chachikulu chozungulira chokhala ndi zimipando zachikopa zawofuwofu. Posakhalitsa akuluakulu anayamba kuloŵa n’kukhala mozungulira chitebulocho. Wamkulu wawoyo anandidziŵitsa munthu aliyense pagululo. Kenaka anakhala pansi n’kunena kuti: “Tsopano tatiuzatu za chikhulupiriro chakocho.”

Nditapemphera msangamsanga mosatulutsa mawu, ndinayamba kulankhula kwa anthuwo omwe anali tcheru pofuna kumva kuti ndinena zotani. Posakhalitsa nkhani imene tinkakambirana inafika pa nkhani yonena kuti zamoyo zinachita kusanduka, ndipo ena ananena kuti sayansi inatsimikizira kuti zimenezo n’zoona. Ndili ku kampu yomwe ndinali poyamba ndinaphunzira kabuku konena za nkhani imeneyi kamutu wakuti Evolution Versus the New World. * Choncho akuluakuluwo anadabwa kuti ndikutulutsa mfundo zotsimikizira kuti chiphunzitso chakuti zamoyo zinachita kusanduka n’chopanda umboni.

Kenaka msilikali wina wakaudindo kake ndithu yemwe n’zosachita kufunsa kuti anali Mkatolika, analoŵererapo. Iye anandifunsa kuti, “Namwali Mariya umamuona bwanji? Ndipo nkhani ya Misa yoyera umati nayo bwanji?” Ndinam’yankha mafunso akewo kenaka n’kunena kuti: “Bwana, ndikuona kuti ndinu munthu wokhulupiriradi, chifukwa mafunso anu akusiyana ndi a ena onseŵa.”

“Ayi ndithu, ndakaniratu zimenezo! Sindine munthu wokhulupirira ayi!” anakuwa motero pokanitsitsa kwa mtu wagalu. M’dziko la chikomyunizimu, anthu odziŵika kuti ndi Akristu sankalandira n’komwe ulemu kapena udindo uliwonse. Choncho titayankhana motero, msilikaliyo anangolekera anzakewo kuti azindifunsa ndipo iye sanapitilizenso kulankhula mawu ena aliwonse. Ndinasangalala kwambiri pokhala ndi mwayi umenewo wofotokozera anthuwo za chikhulupiriro cha Mboni za Yehova.

Mwayi Winanso Wochitira Umboni

Patangotha masiku ochepa chabe, anapita nane kunyumba ina ya asilikali mumzinda wotchedwa Prague ndipo asilikali ankandilondera. Msilikali woyamba amene anapatsidwa ntchito yondilondera anadabwa chifukwa cha chitetezo chapadera choterocho. Iye anandiuza kuti, “Aka n’koyamba kuti tizilondera munthu chonchi.” Choncho ndinam’fotokozera chifukwa chimene anandimangira. Izi zinam’chititsa chidwi kwambiri mwakuti anakhala pansi, mfuti yake ili pakati pa maondo ake n’kumamvetsera. Maola aŵiri atatha panabwera msilikali wina iye n’kuchokapo, ndipo nayenso anandifunsa mafunso omwewo kenaka tinayambanso kukambirana za m’Baibulo.

M’kati mwamasiku otsatira, ndinali ndi mwayi wolankhula ndi anthu amene ankandilondera ndiponso ndi akaidi anzanga asilikali ondilonderawo akandilola kutero. Alondawo anafika mpaka pomatsekulira akaidi kuti asonkhane pamodzi kuti tikambirane za m’Baibulo! Patapita kanthaŵi, ndinayamba kuda nkhaŵa kuti ufulu umene alondawo anali kundipatsa woti ndizilankhula ndi akaidi ena ukhoza kutulukira poyera ndipo zikadzatero mwina ndidzagwa nazo m’mavuto. Koma sizinaululike n’komwe.

Kenaka pomalizira pake, nthaŵi imene ankanditenga kupita nane kukhoti kuti mlandu wanga ukagamulidwe, anthu amene ndinawauza za chikhulupiriro changa ndi omwenso anandilimbikitsa. Anagamula kuti ndikhale m’ndende zaka ziŵiri, zomwe anaziwonjezera pazaka zisanu ndi chimodzi zomwe boma linatikhululukira zija. Ndiye kuti ndinali ndi zaka zisanu ndi zitatu zoyenera kuti ndikhale m’ndende.

Ndinkangoona kuti Mulungu Akundithandiza

Nthaŵi zambiri, akamandisamutsa kupita m’makampu ndiponso m’ndende zosiyanasiyana za ku Czechoslovakia, ndinkangoona kuti Mulungu akundithandiza. Nditafika kundende ya ku Valdice, woyang’anira ndendeyo anandifunsa chifukwa chimene anandipititsira kumeneko. Ndinam’yankha kuti, “Ndinakana kupita kunkhondo. Kumenya nawo nkhondo n’chinthu chosemphana ndi zimene ndimakhulupirira.”

Mokoma mtima iye anati: “Anthu onse akanakhala ndi maganizo otero bwenzi zinthu zili bwino kwambiri.” Koma atakhala kaye phee n’kuganiziranso zonena, iye anati: “Komabe, popeza kuti anthu ambiri saganiza choncho masiku ano, ndi bwino kuti tikukhaulitsebe!”

Anandiika m’dipatimenti yopanga zinthu zopangidwa ndi magalasi ndipo ntchito imene tinali kugwira m’dipatimenti imeneyi inali yowawa kwambiri. Mumvetse bwinobwino pamenepa kuti ngakhale kuti anagamula zakuti ndikhale m’ndende chifukwa chakuti ndinakana kupita kunkhondo monga wa m’gulu la Mboni za Yehova, anandiikabe m’gulu la akaidi omangidwa pazifukwa zandale ndipo motero, ankandipatsa ntchito zovuta kwambiri. Ntchito yodula magalasi n’kumapangira zinthu zoikapo nyali ndiponso zinthu zina zokongoletsera m’nyumba inali yowawa kwambiri chifukwa chakuti zinthu zimenezo sankafuna kuti zikhale ndi nthenya ina iliyonse. Nthaŵi zambiri, akaidi ankati akapereka zinthu zimene akonza bwinobwino, ankangoona kuti m’maŵa wake theka la zinthuzo zatulukiranso zitasweka kuti tizikonzenso. Choncho kunali kovuta kuti tizikwanitsa kupanga zinthu zokwanira ndendende zimene ankafuna panthaŵi imene ankaifunayo.

Tsiku limene ndinaloŵa m’dipatimenti imeneyi, ndinadikira kaye kuti ndionane ndi woyang’anira dipatimentiyi. Atafika, anayamba kulalatira akaidi omwe mwini wakeyo ankati sanali kugwira ntchito molimbika. Anadutsa pakati pa akaidi onsewo n’kufika pa ine n’kunena kuti: “Nanga iwe bwanji? Si ukugwira ntchito chifukwa chiyani?”

Ndinam’fotokozera kuti ndinali mlendo pakati pa akaidi ena onsewo. Anapita nane muofesi yake n’kundifunsa mafunso omwe aja ofuna kudziŵa kuti anandimangiranji. Nditamuuza zonse, iye anandifunsa kuti: “Ndiye kuti iweyo ndiwe wa Mboni za Yehova eti?”

Ndinam’yankha kuti: “Inde.”

Kenaka nkhope yake inasintha n’kunena kuti: “Usadandaule, tinali ndi a Mboni za Yehova ambiri pano. Onse timawapatsa ulemu chifukwa chakuti ndi anthu olimbikira ntchito ndiponso okhulupirika. Ndionetsetsa kuti uzigwira ntchito imene ungakwanitse.”

Ndinadabwa kwambiri ndi mmene woyang’anira ameneyu anasinthira. Ndinasangalala kwambiri chifukwa cha Yehova ndiponso okhulupirira anzanga omwe sindinawadziŵe amene anasiya mbiri yabwino ya Mboni za Yehova pa ndende imeneyo. Kunena zoona, nthaŵi yonseyo imene ndinakhala m’ndende ndinaona kuti Yehova anandithandiza.

Ngakhale zinthu zikandivuta motani, nthaŵi zonse sindinkakayika kuti tsiku lina ndidzakumana ndi abale anga achikristu basi. Ndikatero ndinkangowaona m’maganizo mwangamu akumwetulira mosangalatsa ndiponso akundilimbikitsa. Pakanapanda iwoŵa, zikanandivuta kwambiri kuti ndipirire ndili m’ndende.

Akaidi ambiri ankaoneka kuti sanali kuganizira china chilichonse kuposa kubwezera nkhanza zimene ankachitiridwa. Koma ine sindinaganizepo motero. Ndinazindikira kuti ndinali kuvutika chifukwa chakuti ndikumvera mfundo zolungama za Mulungu. Choncho ndinkadziŵa kuti patsiku lililonse limene ndinakhala m’ndende, Yehova ankandiwonjezera masiku osaŵerengeka a moyo wokoma m’dziko lake latsopano la Paradaiso.—Salmo 37:29; 2 Petro 3:13; Chivumbulutso 21:3, 4.

Ndikusangalala Kwambiri Chifukwa cha Madalitso Amene Ndili Nawo Panopa

M’chaka cha 1968 mwezi wa May, nditakhala m’ndende kwa zaka zoposa 15, anandimasula. Poyamba, ndinkachita manyazi kulankhula ndi anthu, ndipo izi sizachilendo kwa anthu amene akhala nthaŵi yaitali m’moyo wawo ali m’ndende n’kumangokhalira kuona anthu okhaokha ovala zovala zaukaidi kapena za ulonda. Koma abale anga achikristu anafulumira kundithandiza kuti ndizilalikira nawo, ndipotu panthaŵiyi n’kuti tidakali oletsedwabe.

Masabata ochepa chabe chindimasulireni, ndinakumana ndi Eva. Ngakhale kuti ankakhalira kulimbana ndi akwawo, iye pamodzi ndi mchimwene wake analimba mtima kwambiri kutsatira choonadi cha m’Baibulo pafupifupi zaka zitatu tisanaonane. Posakhalitsa tinayamba kumalalikira tili limodzi. Tinathandiza nawonso kupanga mabuku athu ofotokoza za m’Baibulo. Zimenezi tinkachita mobisa pogwiritsa ntchito makina osindikiza omwe anakwiriridwa pansi. Kenaka m’chaka cha 1969, mwezi wa November, tinakwatirana.

M’chaka cha 1970, Jana mwana wathu woyamba anabadwa. Patapita nthaŵi ndithu, ndinayamba kuyendera mipingo kumapeto kwa sabata iliyonse monga mtumiki woyendayenda wa Mboni za Yehova n’kumailimbikitsa kukonda zinthu za Mulungu. Ndili m’kati mogwira ntchito imeneyi m’chaka cha 1975, anandigwira n’kundipititsanso kundende. Koma panthaŵiyi ndinangokhalako kwa miyezi yoŵerengeka chabe. Ndipo m’chaka cha 1977, mwana wathu wamwamuna dzina lake Štěpán anabadwa.

Kenakano pa September 1, 1993 boma la Czech Republic linalola Mboni za Yehova kulembetsa mwalamulo kuti ndi chipembedzo. Chaka chotsatira mwana wathu wamkazi, Jana anakwatiwa ndi Dalibor Dražan, yemwe ndi mkulu mumpingo wa Chikristu. Ndipo m’chaka cha 1999, mwana wathu wamwamuna, Štěpán yemwe ndi mtumiki wotumikira, anakwatira Blanka yemwe amagwira nawo ntchito ya utumiki wanthaŵi zonse. Tonsefe tsopano tili m’gulu la abale ndi alongo amene ali m’mipingo imene ili ku Prague. Tonsefe tikuyembekeza mwachidwi nthaŵi imene dziko latsopano lidzabwere, koma makamaka ndikufunitsitsa kudzaona nthaŵi imene sikudzakhalanso ndende kwina kulikonse.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 24 Linafalitsidwa ndi Mboni za Yehova m’chaka cha 1950.

[Zithunzi patsamba 28]

Ndinkagwiritsa ntchito chipeso polemba mfundo za m’Baibulo

[Chithunzi patsamba 29]

Ku kampu ya Bytiz, komwe ananditsekera m’ndende kenaka n’kudzabatizidwa

[Chithunzi patsamba 31]

Tsiku la ukwati wathu

[Chithunzi patsamba 31]

Eva ndi ineyo, ndipo kudzanja lamanzereku kuli Štěpán ndi Blanka, ndipo kulamanja kuli Jana ndi Dalibor