Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Nthaŵi Imene Ukapolo Udzathe!

Nthaŵi Imene Ukapolo Udzathe!

Nthaŵi Imene Ukapolo Udzathe!

UFULU! Pali mawu ochepa chabe amene amamveka okoma m’mitima ya anthu kuposa mawu ameneŵa. Ufulu anthu aumenyera nkhondo n’kuuvutikira, ena anangokhalira zomwezi moyo wawo wonse ndipo ena afera zomwezi. Komabe, n’zomvetsa chisoni kuti ambiri akhala akutero koma osaona kusintha kwenikweni. Kodi pali chinthu chimene chingatilimbitse mtima kuti anthu adzachokadi muukapolo n’kukhala aufulu, chinthu chimene sichidzagwiritsa anthu fuwa lamoto? Inde chilipo.

Mtumwi Paulo anauziridwa kulemba lonjezo la Mulungu lakuti: “Cholengedwa chomwe chidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi, ndi kuloŵa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:20, 21) Koma kodi tingatsimikize bwanji kuti Mulungu adzabweretsadi “ufulu waulemerero” wotero? Njira imodzi ndiyo ya kufufuza mmene Mulungu ankachitira zinthu ndi anthu kumbuyoku.

Baibulo limati, ‘Pamene pali Mzimu wa Yehova pali ufulu.’ (2 Akorinto 3:17) Inde, Mzimu wa Mulungu, kapena kuti mphamvu yake imene imagwira ntchito, ndi yamphamvu kwambiri. Kwa nthaŵi yaitali iye wakhala akuigwiritsa ntchito mphamvu yakeyo kubweretsa ufulu. Watero motani? Tisaiwale kuti paja pali mitundu ya ukapolo yambirimbiri. Takambirana kale za mtundu wina woipitsitsa, umene anthu amphamvu amagwira ukapolo anthu ofooka mowakakamiza ndiponso mwankhanza. Koma tatiyeni tione mitundu ina ya ukapolo.

Anthu angadzisandutse okha akapolo a zizoloŵezi zosiyanasiyana zimene zimavuta kwambiri kuzisiya. Anthu angathenso kukhala akapolo a mabodza ndiponso chinyengo zimene zikhoza kuwaloŵetsa muukapolo wa ziphunzitso zonama. Ukapolo wina wovuta kwambiri kuudziŵa ndiwo umene umavutitsa munthu wina aliyense, kaya timaudziŵa kapena ayi, ndipo zimene umachita n’zakupha. Komabe, tinenepo apa kuti ngakhale tikutchula mitundu yosiyanasiyana ya ukapolo m’nkhaniyi, sikuti tikuitenga mitundu yonseyo kuti n’njofanana ayi. N’njosiyana kwambiri. Komabe ngakhale zili choncho, mitundu yonseyi n’njofanana m’njira imodzi yakuti m’kupita kwa nthaŵi, Mulungu waufulu adzatsimikizira kuti wawachotsera anthu zosautsa zonse zobwera chifukwa cha mitundu yonseyi ya ukapolo.

Zizoloŵezi Zovuta Kusiya Zikam’sandutsa Munthu Kapolo

Taonani mmene buku lakuti When Luck Runs Out limafotokozera khalidwe la kutchova juga likafika povuta kusiya. Limati: ‘Ndi vuto limene limam’chititsa munthu kukhala ndi chilakolako champhamvu mwakuti amalephera kuugwira mtima akafuna kutchova juga. Chilakolako chimenechi sichitherapo ndipo chimamka chikula kwambiri n’kusanduka chinthu chofunika kwambiri kwa munthuyo. . . mpaka pamapeto chimam’lowerera ndipo nthaŵi zambiri chimawononga ndi kusokonezeratu zinthu zonse zofunika kwambiri m’moyo wa munthuyo.’ Palibe munthu amene amadziŵa kuti pali anthu angati amene anasanduka akapolo a kutchova juga. M’dziko la United States lokha, akuti mwina alipo okwana 6 miliyoni.

Kumwa kwambiri mowa kukhozanso kum’sokoneza kwambiri munthu, mwinanso kuposa pamenepa, ndipo m’madera ambiri limeneli ndilo vuto lofala kwambiri. M’dziko lina lalikulu, pafupifupi theka la anthu aamuna onse aakulu amavutika ndi mavuto ena obwera chifukwa cha uchidakwa. Ricardo, yemwe anali chidakwa zaka 20 zapitazo anafotokoza zimene zimachitika munthu akakhala chidakwa chenicheni ponena kuti: “Umati ukangodzuka, umangofuna moŵa pofuna kuthetsa matsire, kuiwala mavuto, kapena kuti ulimbe mtima mokwanira pochita zinthu. Umangokhalira kuganiza za mowa basi, komano umayesetsa kuti mwiniwakewe kapena anthu amene amakudziŵa aziganiza kuti uli bwinobwino.”

Si mowa wokha umene umawavuta anthu kusiya n’kuwasandutsa akapolo. Padziko lonse, pali anthu mamiliyoni ambirimbiri amene amagwiritsa ntchito mankhwala oletsedwa ozunguza bongo. Komanso, anthu oposa biliyoni imodzi amasuta fodya, ndipo mufodyamo mumapezeka mankhwala omwe ali m’gulu la mankhwala ovuta kwambiri kuwasiya. Anthu ambiri amalakalaka kwambiri atasiya kusuta fodya, koma amaona kuti anasanduka akapolo ake. Kodi Yehova wasonyeza kuti ndiye angamasuledi anthu kuukapolo wamphamvu wosiyanasiyanawu? *

Taganizirani chitsanzo cha Ricardo. Iye anafotokoza kuti: “Pafupifupi zaka khumi zapitazo, ndinazindikira kuti mowa ukundilamulira. Unkandisokonezera ukwati, ntchito, ndiponso banja langa, ndipo ndinaona kuti sindikanatha kuthetsa mavuto angaŵa pokhapokha nditaleka mowawo. Pophunzira Baibulo, ndinaphunzira kuti anthu amene amamwa mowa kwambiri amasauka zenizeni, ngakhalenso kusauka mwauzimu. (Miyambo 23:20, 21) Ndinkafuna kuti ndizikondana ndi Mulungu, ndipo mapemphero anga ochokera pansi pamtima opempha thandizo la Mulungu anandithandiza kuti ndisamachite zinthu modzinamiza ndekha. Munthu wina anaphunzira nane Baibulo ndipo anasandukadi mnzanga weniweni. Ndikayamba kuchita mphwayi, sankaipidwa nane, koma ankalimbikira kundiuza mwachifatse njira imene Mulungu amafuna kuti Akristu aziitsatira.”

Poyerekeza ndi kale, Ricardo amaona kuti anamasulidwa kuukapolo umene anali nawo. Amavomereza kuti poyamba nthaŵi zina ankachita mphwayi. Iye anati: “Koma ngakhale kuti panali zovuta zimenezo, chimene chinandithandiza ndicho cholinga changa chotumikira Yehova mokhulupirika, komanso mkazi wanga ndi Akristu anzanga ena anandithandizanso. Ndikungodikira nthaŵi imene Mulungu analonjeza kuti ‘aliyense sadzanena kuti, “Ine ndidwala’’ ’ ndipo uchidakwa udzaiwalikiratu. Pakalipano, ndizilimbikirabe tsiku lililonse kuti thupi langa likhale “nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu.”—Yesaya 33:24; Aroma 12:1.

Padziko lonse anthu ambirimbiri adzionera okha mmene Mulungu amathandizira pamene anali kuyesetsa kusiya zinthu zosiyanasiyana zovuta kuzisiya. Inde tisakane kuti avutika kwambiri chifukwa cha ukapolo wodzipatsa okha, mwina mpaka kugwa m’mavuto kapena m’mayesero osiyanasiyana. Komabe, iwo aona kuti Yehova ndi wodekha kwambiri, Womasula anthu kuukapolo. Ndi wofunitsitsa kuthandiza ndiponso kulimbikitsa anthu onse amene akufunadi kuti am’tumikire.

“Choonadi Chidzakumasulani”

Bwanji za ukapolo wa mabodza ndiponso chinyengo? Yesu Kristu amatitsimikizira kuti tikhoza kumasuka ku zinthu zimenezi. Iye anati: “Ngati mukhala inu m’mawu anga, muli akuphunzira anga ndithu; ndipo mudzazindikira choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.” (Yohane 8:31, 32) Panthaŵi imene ankanena zimenezi, n’kuti anthu ambiri amene ankam’mvetsera ali paukapolo wa malamulo okhwima a miyambo ya Afarisi. M’paketu kuti Yesu ananena za atsogoleri amatchalitchi a nthaŵi imeneyo kuti: “Amanga akatundu olemera ndi osautsa ponyamula, nawasenza pamapewa a anthu; koma iwo eni okha safuna kuwasuntha amenewo ndi chala chawo.” (Mateyu 23:4) Zimene Yesu anaphunzitsa zinamasula anthu kuukapolo woterowo. Iye anaulula poyera mabodza amatchalitchi, mpaka kutchula kumene mabodzawo amachokera kwenikweni. (Yohane 8:44) Ndipo mmalo monena mabodza, iye ananena zoonadi n’kusonyeza poyera zinthu zabwino zimene Mulungu amafuna kuti anthu onse achite.—Mateyu 11:28-30.

Monga ophunzira a Yesu, anthu ambirimbiri masiku ano akuona kuti pothandizidwa ndi Mulungu akhoza kumasuka kusiya mabodza a kupembedza ndiponso miyambo yonama imene yawasandutsa akapolo. Anthuwo akaphunzira choonadi chotsitsimula chochokera m’Baibulo, amaona kuti amasuka posakhalanso ndi mantha osautsa a kuopa akufa, posavutikanso maganizo chifukwa choopa moto wosatha wa kuhelo, ndiponso amamasuka posavutika ndi kulipira akuluakulu a m’matchalitchi amene amauza anthu kuti akuimira Kristu, koma chonsecho Kristu ananena kuti: “Munalandira kwaulere, patsani kwaulere.” (Mateyu 10:8) Komanso tatsala pang’ono chabe kupeza ufulu wina woposa ngakhale pamenepa.

Ukapolo Wovuta Kwambiri Kuudziŵa

Taonani mmene Yesu anafotokozera za mtundu wina wa ukapolo wovuta kuudziŵa, umene tautchula kale womwe umakhudza munthu aliyense padzikoli, kaya akhale wamwamuna, wamkazi kapenanso wamng’ono. Iye anati: “Indetu, indetu, ndinena kwa inu kuti yense wakuchita tchimo ali kapolo wa tchimolo.” (Yohane 8:34) Ndani amene anganene kuti sanachitepo tchimo? Ngakhale mtumwi Paulo anavomereza kuti: “Chabwino chimene ndichifuna, sindichichita; koma choipa chimene sindichifuna, chimenecho ndichichita.” (Aroma 7:19) Ngakhale kuti palibe munthu aliyense amene angadzimasule muunyolo wa uchimo, sindiye kuti basi palibenso kuchitira mwina.

Yesu anawatsimikizira ophunzira ake kuti: “Ngati Mwana adzakuyesani inu aufulu, mudzakhala mfulu ndithu.” (Yohane 8:36) Kukwaniritsidwa kwa lonjezo limeneli kudzatanthauzadi ufulu weniweni kuchoka muukapolo umenewu umene uli woipitsitsa. Kuti timvetse mmene tingachokere muukapolowu, choyamba tiyenera kuona mmene tinayambira kusanduka akapolo.

Baibulo limaulula kuti pamene Mulungu analenga anthu, iwo anali ndi ufulu wosankha zimene akufuna kuchita, ndipo analibe mtima womangofuna kuchita zinthu zochimwa. Koma mwana wina wauzimu wa Mulungu wadyera anafuna kugwiritsa ntchito mphamvu zake kwa anthu, popanda kuganizira zamavuto amene anthuwo angadzakhale nawo chifukwa cha zimenezi. Pofuna kuti achitebe zimenezi, mngelo wopandukayu, yemwe anadzatchedwa kuti Satana Mdyerekezi, anapangitsa kuti Adamu ndi Hava omwe ndi makolo athu oyambirira alakwire Mulungu. Adamu ataphwanya dala malangizo omveka bwino a Mulungu, iye anasanduka wochimwa komanso anapatsira ana ake onse kupanda ungwiro ndiponso imfa. (Aroma 5:12) Kenaka Satana anasanduka ‘mkulu wa dziko lapansili,’ ndipo ‘uchimo wakhala ukuchita ufumu pakati pa anthu onse muimfa.’—Yohane 12:31; Aroma 5:21; Chivumbulutso 12:9.

Kodi tingamasulidwe bwanji? Pokhala otsatira a Yesu, tikhoza kupindula chifukwa cha nsembe ya imfa ya Kristu imene ili ndi mphamvu ya ‘kuwononga iye amene anali nayo mphamvu ya imfa, ndiye Mdyerekezi’ ndiponso ‘kumasula iwo onse amene, chifukwa cha kuopa imfa, m’moyo wawo wonse anamangidwa ukapolo.’ (Ahebri 2:14, 15) Tangoganizirani kuti anthu adzamasuka kuukapolo wauchimo ndiponso imfa! Kodi si zosangalatsa kuganizira zoti tidzakhala ndi ufulu wotero?

Nanga bwanji za mtundu wa ukapolo umene tafotokoza poyamba paja? Kodi ukapolo woumiriza anthu kuchita zimene sakufuna uja udzatha n’komwe?

Mfundo Yolimbitsa Mtima Kwambiri

Ndithudi, tisakaike kuti ukapolo woipa choncho udzathetsedwa. Chifukwa chiyani? Tangoganizirani izi: Yehova Mulungu ndiye amene anatsogolera anthu pa ulendo waukulu kwambiri m’mbiri yonse wochoka muukapolo. Nkhani yakale imeneyi mwayenera kuti mukuidziŵa bwino.

Mtundu wa Aisrayeli unasandutsidwa akapolo ndi Aigupto, pomawaumiriza kugwira ntchito yakalavula gaga ndiponso kuchitidwa nkhanza kwambiri. Iwo analirira Mulungu kuti awathandize, ndipo iye poti ndi wachifundo kwambiri, anawamvera n’kuwathandiza. Pogwiritsa ntchito Mose ndi Aroni kuti azimulankhulira, Yehova analamula kuti Farao wa ku Igupto awalole Aisrayeli kupita kukakhala aufulu. Kangapo konse, mfumu yoyerekedwayo inakana, ngakhale pamene Yehova anabweretsa m’dzikomo miliri yowononga yotsatizanatsatizana. Kenaka pamapeto pake, Mulungu anamuonetsa Farao chimene chinameta nkhanga mpala. Kenaka Aisrayeli anapeza ufulu!—Eksodo 12:29-32.

Imeneyi ndi nkhani yochititsa chidwi kwambiri, eti? Komabe mukhoza kudabwa kuti nanga bwanji Mulungu osachitanso chimodzimodzi panopa. Bwanji sanaloŵerere pazochita za anthu n’kuthetsa ukapolowu? Musaiwaletu kuti Yehova si ndiye ‘mkulu wa dziko lapansili,’ koma ndi Satana. Chifukwa cha kuderera kumene kunachitika kumbuyoku mu Edene, Yehova walola kuti Mdani woipa kwambiri ameneyu alamulire kwa nthaŵi yochepa chabe. Ukapolo, kupondereza ena ndiponso nkhanza n’zizindikiro chabe zakuti Satana akulamulira. Chifukwa cha Satanayu, ulamuliro wa anthu waoneka kuti ndi wosautsa anthu ena. Baibulo limangonena nkhaniyi mwachidule ponena kuti: “Wina apweteka mnzake pom’lamulira.”—Mlaliki 8:9.

Koma kodi zimenezi zichitika kwanthaŵi yaitali bwanji? Baibulo limafotokoza kuti tili ‘m’masiku otsiriza,’ nthaŵi imene dyera ndiponso umbombo uli wochuluka kwambiri. (2 Timoteo 3:1, 2) Apa ndiye kuti posachedwapa Ufumu wa Mulungu, umene Yesu anatiphunzitsa kuupempherera, udzabweretsa dziko lokhala ndi anthu olungama amene sadzalola kuti pakhale ukapolo. (Mateyu 6:9, 10) Yesu Kristu, yemwe ndi Mfumu yoikidwa ndi Mulungu, sadzalekerera kena kalikonse kokhudzana ndi ukapolo mpaka pamene adzam’chotseretu mdani wotsiriza, imfa.—1 Akorinto 15:25, 26.

Tsiku limenelo likadzafika, anthu okhulupirika adzaona kuti kumasuka kwa anthu a Mulungu kuukapolo m’dziko la Igupto kunali kungosonyeza pang’ono chabe za ufulu wochuluka kwambiri wam’tsogolowu. Inde, nthaŵi yake ikadzakwana, “cholengedwa chomwe chidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi, ndi kuloŵa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.”—Aroma 8:21.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 M’zaka 100 zoyambirira za m’nyengo yathu ino, anthu ankakonda kudya kapena kumwa kwambiri pamapwando aakuluakulu achiroma. Choncho, Akristu ankachenjezedwa kuti asalole kuti zakudya kapena zina zilizonse zotere ziwasandutse akapolo.—Aroma 6:16; 1 Akorinto 6:12, 13; Tito 2:3.

[Chithunzi patsamba 23]

M’dziko la United States lokha, akuti mwina muli anthu okwana 6 miliyoni amene ali akapolo a kutchova njuga

[Zithunzi patsamba 23]

Anthu ambirimbiri anasanduka akapolo a mankhwala ozunguza bongo, mowa ndiponso fodya

[Zithunzi pamasamba 24, 25]

Monga Ricardo, anthu ambirimbiri aona kuti Mulungu wawathandiza kusiya zinthu zovuta kuzisiya

[Zithunzi patsamba 26]

Monga mmene Aisrayeli akale anamasulidwira kuukapolo, posachedwapa olambira Mulungu oona adzakhala ndi ufulu wochuluka kuposa umenewo