Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kutchova Njuga Kwatenga Malo Padziko Lonse

Kutchova Njuga Kwatenga Malo Padziko Lonse

Kutchova Njuga Kwatenga Malo Padziko Lonse

JOHN amene anakulira ku Scotland, ankalakalaka atachita mphumi yopambana pampikisano. Iye anati: “Tsiku lililonse ndinkagula tikiti ya mpikisano. Tikitiyo inali yotsika mtengo kwambiri, ndipo zinkandilimbitsa mtima kuti tsiku lina ndidzapeza zinthu zonse zimene ndimafuna.”

Kazushige, amene amakhala ku Japan, ankakonda mpikisano wokwera mahatchi. Iye anakumbukira kuti: “Ndinkasangalala kwambiri kubetcherana ndalama ndi anzanga pakakhala mpikisano wa mahatchi, ndipo nthaŵi zina ndinkawina ndalama zambiri zedi.”

Linda amene amakhala ku Australia ananena kuti: “Ndinkakonda kwambiri maseŵera enaake amakadi obetcherana ndalama otchedwa bingo. Pa sabata imodzi yokha ndinkawononga ndalama zokwana madola mpaka 30, chifukwa cha chizoloŵezi chimenechi, koma ndinkangokomedwa ndi kuwinako.”

John, Kazushige, ndi Linda, ankaona kuti kutchova njuga kulibe vuto lenileni. Anthu ochuluka zedi padziko lonse amaganizanso chimodzimodzi. Anthu ena a ku America atafunsidwa m’chaka cha 1999 kuti alankhule mmalo mwa ena onse m’dzikolo za kutchova njuga, panapezeka kuti anthu aŵiri pa anthu atatu alionse a kumeneko amaona kuti kutchova njuga n’kwabwino. M’chaka cha 1998, anthu a ku America otchova njuga anawononga ndalama zokwana madola 50 biliyoni potchova njuga m’njira yololedwa ndi lamulo ndipotu ndalama zimenezi n’zoposa ndalama zonse zimene anawononga poonerera mafilimu, kugula makaseti anyimbo, kuonerera zamaseŵera, kupita kumalo azionetsero, komanso maseŵera a pavidiyo.

Atafufuza posachedwapa anapeza kuti, pachaka chimodzi, pafupifupi anthu 8 pa anthu 10 alionse a ku Australia anatchovako njuga nthaŵi inayake, ndipo anthu 4 pa anthu 10 alionse ankatero mlungu uliwonse. M’dziko limenelo, anthu aakulu ambiri pachaka amawononga ndalama zokwana madola 400 (a ku America) potchova njuga, zimene zili ndalama zopitirira theka la ndalama zimene anthu a ku Ulaya ndi ku America amawononga, motero zimenezi zikutanthauza kuti anthu a ku Australia ndiwo amakonda kwambiri kutchova njuga.

Anthu ambiri a ku Japan amakonda kwambiri maseŵera enaake oponyerana kampira patebulo otchedwa pachinko ndipo pachaka amawononga ndalama zokwana madola 240 biliyoni pobetcherana pa maseŵeraŵa. Ku Brazil anthu amawononga ndalama zokwana mpaka 4 biliyoni pachaka potchova njuga, ndipo zambiri mwa ndalamazi amagulira matikiti a mpikisano. Koma sikuti ndi anthu a ku Brazil okha amene amakonda mipikisano. Magazini yotchedwa Public Gaming International posachedwapa inanena kuti mwina “pali mipikisano yokwana 306 m’mayiko 102.” Indedi kutchova njuga kwatenga malo padziko lonse ndipo ena amati kumapindulitsa anthu kwambiri.

Sharon Sharp, yemwe amaimira bungwe la Public Gaming Research Institute, ananena kuti ku United States, kuchokera m’chaka cha 1964 mpaka 1999, ndalama zimene anthu amapata m’mipikisano yotere “zinakwana madola mabiliyoni 125 a ndalama zimene boma linkaika padera chaka n’chaka, ndipo zambiri mwa ndalamazi anazipeza m’chaka cha 1993.” Zambiri mwa ndalama zimenezi anaziika padera kuti zigwiritsidwe ntchito pophunzitsa anthu, kukonza malo aboma osungirako zachilengedwe, ndiponso malo ochitirako zamaseŵera. Makampani a malo ochitirako njuga amapezetsanso ntchito anthu ambiri, ndipo ku Australia kokha makampaniŵa amalemba ntchito anthu pafupifupi 100,000 m’mitundu ya njuga yokwana 7,000.

Motero, anthu okonda njuga amanena kuti maseŵera a njuga ololedwa ndi boma n’ngosangalatsa komanso amapezetsa anthu ntchito, amathandiza polipira ndalama zamisonkho, ndiponso amatukula madera amene akutsalira pazachuma.

Motero anthu ambiri angafunse kuti, ‘Nangano kutchova njuga kuli ndi vuto lanji?’ Yankho la funso limeneli, limene lili mu nkhani yotsatirayi, mwina lingasinthe maganizo anu pa nkhani ya kutchova njuga.

[Chithunzi patsamba 3]

John

[Chithunzi patsamba 3]

Kazushige

[Chithunzi patsamba 3]

Linda