Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Peŵani Msampha wa Kutchova Njuga

Peŵani Msampha wa Kutchova Njuga

Peŵani Msampha wa Kutchova Njuga

“Sindinadwaleko chifukwa cha njuga, ndipo nthaŵi zonse ndinkaikiratu padera ndalama zotchovera njuga. Koma kunena zoona nthaŵi zonse ndikamachita mpikisano, ndinkasankha manambala amene ndinkaona kuti ndi opatsa mwayi.”—Anatero Linda.

ANTHU ambiri otchova njuga amayamba kukhulupirira kuti pali manambala enaake amwayi, kapenanso amakhulupirira zithumwa zopatsa mwayi. Mwina iwowo amaona kuti sikuti amakhulupirira tizikhulupiriro timeneti ndi mtima wonse, komabe amatigwiritsira ntchito nthaŵi zonse.

Anthu ena otchova njuga amafika mpaka popemphera kwa Mulungu kuti awathandize kuwina. Koma zimene zinalembedwa m’Baibulo zimasonyeza kuti Mulungu amadana ndi anthu amene amati amamulambira komano ‘n’kumakonzera gome mulungu wamwayi.’ (Yesaya 65:11) Inde Mulungu amadana ndi zochitika zimene zimalimbikitsa anthu kukhala ndi tizikhulupiriro tachabechabe ta mwayi wosadziŵika bwino. Njuga payokha imalimbikitsa anthu kukhala ndi tizikhulupiriro topanda pake todziŵa eni akewo basi.

Njuga imalimbikitsanso kwambiri kukonda ndalama mosachita manyazi. Masiku ano anthu ambiri saganizira zinthu zauzimu mwakuti ndalama zangosanduka kamulungu kamene, ndipo njuga ndiyo njira imene yatchuka yolambirira kamulungu kameneka. Matchalitchi atsopano asanduka nyumba zapamwamba zotchovera njuga, ndipo pano anthu ayamba kukhulupirira kuti kusirira n’kwabwino. Ofufuza apeza kuti anthu ambiri amene amapita kumalo otchovera njuga amanena kuti amapita kumeneko osati chifukwa chokasangalala kapena kukangopezekako, koma chifukwa chakuti amafuna kuwina “ndalama zambiri.” Komatu Baibulo limachenjeza kuti: “Muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pandalama; chimene ena pochikhumba, anasochera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zoŵaŵa zambiri.”—1 Timoteo 6:10.

Pa 1 Akorinto 6:9, 10, Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti: “Musasocheretsedwe . . . opembedza mafano . . . kapena osirira . . . sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu.” Kusirira sikuti ndi khalidwe loipa chabe, komanso ndi matenda auzimu oopsa, komabe ndi ochizika.

Anapeza Mphamvu Zowathandiza Kuti Asinthe

Kazushige, amene tam’tchula m’nkhani yoyamba ija anakumbukira kuti: “Ndinayesa kambirimbiri kusiya njuga. Ndinazindikira kuti banja langa silinkayenda bwino chifukwa ineyo ndinkatchova njuga ndi anzanga kumpikisano wa mahatchi. Nthaŵi zonse ndalama zimene ndinkawina ndinkaziluzanso. Ndinafika poluza ndalama zonse zimene mkazi wanga anasunga ali woyembekezera pokonzekera kubadwa kwa mwana wathu wamwamuna wachiŵiri, ndipo mpaka ndinayamba kutenga ndalama za kuntchito n’kumakatchovera njuga. Mapeto ake ndinadzichotsera ulemu wanga wonse. Nthaŵi zambiri mkazi wanga ankangolira n’kumandipempha kuti ndisiye njuga koma ayi ndithu ndinalephera kutero.”

Kenaka Kazushige anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Iye tsopano akunena kuti: “Ndikamaŵerenga Baibulo kwambiri, ndimalimbanso mtima kwambiri kuti kuli Mulungu ndiponso kuti ndingapindule pomumvera. Ndinatsimikiza kuti mwamphamvu imene Mulungu amapereka, ndidzatha kusiya njuga. Ndinadabwa kuona kuti sindinangosiya njugayo basi koma ndinayambanso kudana nayo. Pano ndimati ndikamaganizira mavuto amene banja langa linkakumana nawo chifukwa cha khalidwe langali, mtima umandipweteka kwambiri. Ndimathokoza Yehova Mulungu kwambiri chifukwa chondithandiza kusiya khalidwe langa lotchova njuga ndiponso kundithandiza kukhala ndi moyo wolongosoka!”—Ahebri 4:12.

John, amene tam’tchulanso m’nkhani yoyamba ija, nayenso anayamba kuphunzira Baibulo. Iye pokumbukira anati: “Kuphunzira Baibulo kunandithandiza kuonanso bwino zochita zanga. Ndinazindikira kwa nthaŵi yoyamba kuti kutchova njuga kunali kundiwononga ineyo komanso banja langa. Ndinaona kuti kumalimbikitsa anthu kukhala ndi khalidwe losaganizira ena ndiponso laumbombo, omwe ndi makhalidwe amene Yehova amadana nawo. Nditapitiriza kuphunzira, kukonda Yehova kunandipatsa mphamvu zimene zinandithandiza kusiya njuga. Ndinayamba njuga chifukwa chakuti ndinkafuna moyo wabwino. Popeza kuti tsopano ndinasiya njuga ndipo ndikutumikira Yehova mosangalala, moyo umene ndinkaulakalakawo ndaupeza ndithu.”

Mkazi wa John, Linda, nayenso anaganiza zosiya njuga. Iye anati: “Zinali zovuta kwambiri. Koma ineyo ndi mwamuna wanga titayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, ndinaphunzira kusalimbana ndi zinthu zosafunika kwenikweni m’moyo. Sikuti ndinangophunzira kukonda zinthu zimene Mulungu amakonda koma ndinaphunziranso kudana ndi zimene amadana nazo, ndipo kusirira kwamtundu uliwonse kuli m’gulu limeneli la zinthu zimene amadana nazozo. Moyo wanga panopo n’ngolongosoka komanso ndimakhala ndi ndalama zambiri kuposa kale.”—Salmo 97:10.

Mukayamba kum’konda kwambiri Yehova Mulungu, inunso mungathe kupeza mphamvu ndiponso nzeru zokuthandizani kuti mupeŵe msampha wa njuga. Mukatero mungathe kusamalira bwino chuma chanu, maganizo anu, ndiponso moyo wanu wauzimu. Motero mungadzadzionere nokha kuti mawu olembedwa pa Miyambo 10:22 ndi oona. Mawu ameneŵa amati: “Madalitso a Yehova alemeretsa, sawonjezerapo chisoni.”

[Mawu Otsindika patsamba 11]

Kusirira si khalidwe loipa chabe, ndi matendanso auzimu oopsa

[Bokosi/Zithunzi patsamba 9]

Mgwirizano Winawake wa Njuga ndi Zamizimu

M’lipoti lopita ku bungwe la National Gambling Impact Study Commission, ofufuza a ku yunivesite yotchedwa Duke ananena mfundo zosonyeza kuti pali mgwirizano winawake pakati pa kunenerera njuga ndi kukhulupirira zamizimu. Lipotilo linati: “Zinthu zambiri zonenerera [mipikisano] zimalimbikitsa kuti anthu azikonda kwambiri chuma . . . Komatu sikuti zimalimbikitsa kupeza chumachi pogwira ntchito mwachamuna kapena mwakhama koma pokhulupirira zamizimu ndi zamatsenga, zimene maziko ake ndi zinthu zongoganizira, maloto ndiponso tizikhulupiriro topanda umboni weniweni. Ndipo woyang’anira mpikisano aliyense amadziŵa kuti makasitomala ake ambiri akamachita mpikisanowo amadalira tizikhulupiriro tawo tinatake, maere, asing’anga, ndiponso mabuku okhala ndi manambala ogwirizana ndi mayina, masiku, ndiponso maloto. M’malo mowauza anthu mosabisa kuti nambala iliyonse ingathe kukasankhidwa ndiponso kuti pamipikisano inayake kusankha manambala otchuka kungachititse kuti munthuyo agaŵane mphoto yake ndi anthu ena, mabungwe ochita mipikisanowo amangolimbikitsa anthu ochita mipikisanoyo kusankha (ndiponso kusasintha) manambala amene amawakhulupirirawo.

[Zithunzi patsamba 10]

“Kukonda Yehova kunandipatsa mphamvu zimene zinandithandiza kusiya njuga.”—Anatero John

“Moyo wanga panopo n’ngolongosoka komanso ndimakhala ndi ndalama zambiri kuposa kale.”—Anatero Linda

[Zithunzi patsamba 10]

“Ndinadabwa kuona kuti sindinangosiya njugayo basi koma ndinayambanso kudana nayo.”—Anatero Kazushige