Kodi Muyenera Kudalira Manambala Pazochita Zanu?
Kodi Muyenera Kudalira Manambala Pazochita Zanu?
KODI tikaona zimene sayansi imanena ndiponso tikaganizira mozama timaona kuti kukhulupirira manambala n’kwanzeru? Kodi manambala ndi amene ali ndi zinsinsi zonse zokhudza mmene moyo wathu udzayendere? Kodi muyenera kukonza tsogolo lanu mogwirizana ndi zimene anthu okhulupirira manambala amapeza ndiponso amalosera?
Mfundo imodzi imene anthu okhulupirira manambala akhala akulephera kuisamalira n’njakuti anthu a mitundu yosiyanasiyana amagwiritsira ntchito makalendala awoawo. Mwachitsanzo, bwanji ngati munthu akukhala kumene amagwiritsira ntchito kalendala ya chitchaina? Tatiyeni tione deti limene talitchula m’nkhani yathu yoyamba ija la pa September 11, 2001. Malingana ndi kalendala ya chitchaina imene zaka amaziika m’magulumagulu, limeneli linali tsiku la 24 la mwezi wa 7 wa chaka cha 18 cha m’gulu la nambala 78. Tsiku lomweli pakalendala ina ya chiroma angalitchule kuti linali August 29, 2001. Pa kalendala ya chisilamu, tsikuli linali pa 22 mwezi wa Jumada wachiŵiri chaka cha 1422, ndipo pa kalendala ya chihebri linali 23 Eluli 5761. Kodi zingatheke bwanji kuti manambala a deti limene limalembedwa m’njira zosiyanasiyana chonchi akhale ndi chinsinsi chinachake? Mfundo inanso nayi: Nthaŵi zambiri maina a zinthu amalembedwa mosiyana m’zinenero zosiyanasiyana. Mwachitsanzo zilembo za dzina la m’Chingelezi lakuti John akaliŵerengetsera mogwirizana ndi zokhulupirira manambala amapeza 2, koma zilembo za dzina lomweli lomwe m’Chispanya amati Juan akaziŵerengetsera amapeza 1.
N’zoona kuti zinthu zambiri m’chilengedwechi timatha kuzimvetsa bwinobwino pogwiritsira ntchito njira zinazake za masamu. Njira zimenezi anthu angathe kuziyesa ngati zilidi zoona ndiponso angathe kusonyeza mmene zimagwirira ntchito. Koma nkhani yake si imeneyi yakuti dzina lanu linakonzedwa kuti likhale logwirizana ndi tsiku limene munabadwa ndiponso ndi manambala enaake kotero kuti muzitha kudziŵa zimene zikuchitikireni m’moyo wanu.
Apa n’zosachita kufunsa kuti n’kusaganiza bwino kukhulupirira kuti manambala amalosera zinthu molondola, pamene tikudziŵa bwinobwino kuti manambala amasintha mosiyanasiyana malingana ndi zinthu monga makalendala ndi zilankhulidwe.
“Nthaŵi ndi Zochitika Zadzidzidzi”
Anthu ena amachita chidwi ndi zokhulupirira manambala chifukwa amafuna kuti azidziŵa zimene zili m’tsogolo mwawo. Koma Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti moyo wamunthu simungaudziŵiretu Mlaliki 9:11, NW) Inde, zinthu zambiri zimachitika mosayembekezeka. N’kosatheka kuyesa kudziŵiratu zinthu zamwadzidzidzi zimenezi pogwiritsa ntchito tsiku limene tinabadwa kapena pochita masamu oŵerengetsera dzina lathu.
wonse ayi. Timaŵerenga kuti: “Amene athamanga kwambiri sapambana liŵiro, ngakhale amphamvu sapambana nkhondo, ngakhalenso anzeru sapeza zakudya, ngakhale ozindikira sapeza chuma, ndipo ngakhale aja amene ali ndi chidziŵitso sapeza chiyanjo, chifukwa nthaŵi ndi zochitika zadzidzidzi zimawagwera iwo onse.” (Taganiziraninso chitsanzo china ichi: Polimbikitsa anthu kukhala owoloŵa manja, Baibulo limanena kuti: ‘Ponya zakudya zako pamadzi; udzazipeza popita masiku ambiri. Gawira asanu ndi aŵiri ngakhale asanu ndi atatu; pakuti sudziŵa choipa chanji chidzaoneka pansi pano.’ (Mlaliki 11:1, 2) Nthaŵi zambiri anthu satha ndipo sangathe n’komwe kudziŵiratu masoka am’tsogolo. Motero pulofesa wina wa masamu dzina lake Underwood Dudley analemba izi pankhani ya anthu okhulupirira manambala: “Savomereza kuti zinthu zina zimangochitika mwamwayi. Zinthu zodabwitsa kwambiri zimatha kungochitika zokha basi.”
N’zoona kuti anthu okhulupirira manambala amanena zinthu zina zimene zimatha kuchitikadi. Kodi chimachitika n’chiyani kuti zitero? Nthaŵi zina, zinthu zimene amanenazo zimakhala kuti zangokumanizana ndi zochitikazo basi. Ndiponsotu zimene anthuŵa amanena sizikhala zatchutchutchu motero zingathe kutanthauza zinthu zosiyanasiyana. Koma pali chinthu china chofunika kwambiri choyenera kuchiganizira.
Kodi ndi Njira Ina Yowombezera?
Baibulo silichita kutchula mawu akuti kukhulupirira manambala. Koma limalongosola nkhani Estere 3:7, Baibulo la Malembo Oyera.
ya Hamani, amene anali munthu wa mtundu wa a Amaleki yemwe anakonza chiwembu choti apheretu Ayuda onse okhala ku Perisiya zaka za m’ma 600 Nyengo Yathu Ino isanakwane. Nkhaniyo imati: ‘Anayesa maula [mayere, NW] pa maso pa Hamani kuti adziŵe za tsiku lililonse ndi za mwezi uliwonse mpaka pa mwezi wachikhumi ndi chiŵiri, ndiwo mwezi wa Abdara.’—Kale kuchita mayere inali njira yovomerezeka kutsatira pogamula nkhani zikuluzikulu. * (Numeri 26:55) Koma Hamani ankachita mayere powombeza maula, zimene zili zoletsedwa m’Baibulo. Lemba la Deuteronomo 18:10-12 limanena kuti Mulungu amanyansidwa ndi aliyense “wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga. Kapena wotsirika, kapena wobwebweta, kapena wopenduza . . . Popeza aliyense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye.”
Baibulo limati kuwombeza maula ndiponso kugwiritsira ntchito mphamvu zamizimu n’kogwirizana ndi kukhulupirira mizimu. Mizimu yoipa ingathe kuyendetsa zinthu kuti zigwirizane ndi mmene iyoyo ikufunira. Kaya kuti zimenezo ndizo zingakhale zitachitikadi pa nthaŵi inayake kapena ayi, mfundo n’njakuti: Mulungu amadana ndi kukhulupirira mizimu, ndipo kutero kungam’pangitse munthu kuyamba kulamuliridwa ndi mizimu yoipa.—1 Samueli 15:23; Aefeso 6:12.
Kukhulupirira manambala n’kosagwirizana ngakhale pang’ono ndi sayansi, ndipo mfundo zake n’zosamveka n’komwe kwa munthu woganiza bwinobwino. Mfundo yoyenera kuigwira apa n’njakuti, popeza kuti kukhulupirira manambala ndi njira ina yowombezera maula, ndiye kuti n’njosemphana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. Choncho kukhulupirira manambala si njira imene ingakupindulitseni m’moyo wanu kapena kukukonzerani tsogolo lanu.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 12 Pochita mayere, ankatenga tinthu ting’onoting’ono monga timiyala kapena timitengo n’kutikulunga m’chovala kapena kutiika m’chikho. Kenaka ankatipukusa zolimba. Ndiyeno ankatolapo kanthu kamodzi ndipo mwini wa kanthuko ndiye amene ankamusankha.
[Bokosi patsamba 22]
KUSIYANASIYANA KWA MAKALENDALA KUMACHITITSA KUTI MFUNDO ZA OKHULUPIRIRA MANAMBALA ZIKHALE ZOSAMVEKA N’KOMWE
YATHU September 11, 2001
YA CHITCHAINA tsiku la 24 la mwezi wa 7 wa chaka cha 18 cha
m’gulu la nambala 78.
YA CHIROMA August 29, 2001
YA CHISILAMU 22 Jumada wachiŵiri 1422
YA CHIYUDA 23 Eluli 5761
[Bokosi/Zithunzi patsamba 23]
KODI NYENYEZI ZA MWEZI UMENE MUNABADWA N’ZODALIRIKA?
“Nthaŵi zina mumamasuka kwambiri mukakhala ndi anthu, koma nthaŵi zina mumamangika. Mumaona kuti si chinthu chanzeru kuwamasukira kwambiri anthu amene simukuwadziŵa. Mumaganiza panokha ndipo mumafuna mupeze kaye umboni wa chinthu chinachake musanafike potengeka kuti mukhulupirire chinthucho. Mumakonda zinthu zosiyanasiyana m’moyo, ndipo simusangalala mukapatsidwa malamulo ambirimbiri okuletsani kuchita zinthu. Muli ndi luso losiyanasiyana koma simunafikepo poligwiritsa ntchito mokwanira. Mumadzimvera chisoni kwambiri mukapanda kuchita bwino zinthu ndiponso mukakanika kuchita zinthu.”
Kodi mawu amenewo akukhala ngati akunena inuyo? Ngati ndi choncho, n’kutheka kuti pamawu amenewo inuyo mukungoganizirapo mawu amene akunena zinthu zimene zimakuchitikirani. Komansotu mawu ambiri amene ali pamwambaŵa akunena zinthu zimene zimachitikira anthu ambirimbiri. Motero, anthu oŵerenga mawuŵa angasankhe mawu okhawo amene akuona kuti akukhudza iwowo n’kusiya enawo. Buku la mutu wakuti Why Do Buses Come in Threes—The Hidden Mathematics of Everyday Life, linati: “Ofufuza apeza kuti patsamba losonyeza zimene nyenyezi zikulosera akachotsapo zizindikiro zoimira mwezi umene munthu anabadwa, anthu amalephera kupeza ndime imene payenera kukhala zizindikiro za mwezi wawo, koma akaikapo zizindikirozo anthuwo amakhulupirira kuti zimene zalembedwa pamwezi wawowo n’zimene zili zogwirizanadi ndi iwowo.”
[Bokosi patsamba 24]
MANAMBALA OPHIPHIRITSIRA A M’BAIBULO
Manambala enaake m’Baibulo ali ndi matanthauzo ophiphiritsira, komatu matanthauzo ameneŵa amangokhudza nkhani za m’Malemba zimene akupezekamozo basi. Mwachitsanzo zinayi zimatanthauza chinthu chokwanira m’njira iliyonse kapena chokhudza wina aliyense. Mfundo imeneyi imapezeka m’mawu ngati akuti “madera anayi a dziko lapansi” ndi “mphepo zinayi za mlengalenga.” (Yesaya 11:12; Danieli 8:8) Nthaŵi zina sikisi amaimira chinthu chopereŵera m’njira inayake. N’zochititsa chidwi kuti nambala imene buku la Chivumbulutso linapatsa ulamuliro wa Satana wa padziko lapansi pano ndi ‘nambala ya munthu’ imene ili 666. (Chivumbulutso 13:18) Nambalayi ili ndi ma sikisi atatu, kutsimikizira kuti gulu lauchinyama limeneli n’lopereŵereratu kwenikweni. Seveni akagwiritsidwa ntchito mophiphiritsira, amaimira kukwanira kwenikweni. (Levitiko 4:6; Ahebri 9:24-26) Manambala ameneŵa ndiponso ena ophiphiritsira amene agwiritsidwa ntchito m’Malemba amadziŵika zimene akutanthauza kuchokera pankhani zaulosi zimene zili ndi manambalawo.
Ngakhale kuti Malemba amasonyeza kuti manambala enaake n’ngofunika m’njira inayake yapadera, Baibulo silitilimbikitsa kuti tizigwirizanitsa zilembo za mawu enaake ndi manambala pofuna kutulukira zinthu zinazake zachinsinsi.
[Chithunzi patsamba 24]
Hamani anawombeza maula pofuna kusankha tsiku lochitira chiwembu chopheratu mtundu wathunthu wa anthu