Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ngozi Zapamsewu Sizingakuchitikireni?

Kodi Ngozi Zapamsewu Sizingakuchitikireni?

Kodi Ngozi Zapamsewu Sizingakuchitikireni?

“Ine ndili ndi mbiri yoyendetsa bwino magalimoto, choncho palibe chifukwa choti ndizikhala ndi nkhaŵa yoti ndingachite ngozi yapamsewu.” “Madalaivala amene ali achinyamata ndiponso osasamala ndiwo amachita ngozi.” Anthu ambiri amaganiza kuti sangachite n’komwe ngozi yapamsewu. Kodi inunso mumaganiza choncho? Kodi ngozi zapamsewu sizingakuchitikireni?

OFUFUZA ena amati ngati mumakhala m’dziko lotukuka, mwina sizingatheke kukhala moyo wanu wonse osachitako ngozi yapamsewu ngakhale n’kamodzi komwe. Anthu ambiri amaferatu pangozi zoterezi. Masiku ano ngozi zophetsa anthu zoposa theka la miliyoni zikuchitika chaka chilichonse. N’kutheka kuti anthu ambiri amene anafa chaka chathachi sankaganiza kuti zoterezi zingawachitikire n’komwe. Kodi n’chiyani chimene mungachite kuti musachite ngozi? Chachikulu n’kupeŵa basi. Taonani mmene mungapeŵere ngozi zimene zimachitika chifukwa cha kusinza ndiponso ukalamba.

Dalaivala Woyendetsa Galimoto Uku Akusinza

Akatswiri ena amati dalaivala woyendetsa galimoto uku akusinza sasiyana kuopsa kwake ndi dalaivala woyendetsa galimoto atakhuta mowa. Malipoti ambiri amasonyeza kuti kusinza poyendetsa galimoto kumachititsa kuti ngozi zichuluke kwambiri. Posachedwapa chikalata chotchedwa Fleet Maintenance & Safety Report chinanena kuti chaka chimodzi chokha, munthu mmodzi pa anthu 12 alionse oyendetsa galimoto ku Norway, ankasinza poyendetsa galimoto. Nyuzipepala ya ku Johannesburg, ku South Africa yotchedwa The Star, inanena kuti madalaivala oyendetsa galimoto atatopa kwambiri ndiwo amachititsa kuti pakhale ngozi imodzi pa ngozi zitatu zilizonse za magalimoto owombana. Nkhani zochokera kumayiko ena zikusonyeza kuti madalaivala kulikonse akumakhala otopa kwambiri. Kodi n’chifukwa chiyani madalaivala ambiri akuvutika ndi tulo?

Chifukwa chimodzi n’chakuti moyo wamasiku ano ndi wotanganitsa kwambiri. Magazini ya Newsweek inanena posachedwapa kuti n’kutheka kuti anthu a ku America “akugona mopereŵera ndi ola limodzi ndi theka usiku uliwonse poyerekeza ndi mmene ankagonera panthaŵi imene tinkaloŵa m’zaka za m’ma 1900, ndipo vutoli likuoneka kuti likumka likukulirakulirabe.” N’chifukwa chiyani zili chonchi? M’magaziniyi analembamo mawu a katswiri woona za kagonedwe kabwino dzina lake Terry Young, onena kuti: “Anthu amaona kuti kugona kulibe ntchito kwenikweni. Amaona ngati kuti munthu amasonyeza kuti ndi wotsogola akamalimbikira kugwira ntchito n’kumangogona pang’ono basi.”

Akuti anthu ambiri amafunika kugona kwa maola okwana kuyambira pa asanu ndi limodzi ndi theka kapena mpaka asanu ndi anayi usiku wonse. Akatswiri amati anthu amene sagona mokwanira, amakhala ndi tulo masana. Lipoti limene linafalitsidwa ndi bungwe la ku America loona zapamsewu lotchedwa AAA Foundation for Traffic Safety linati: “Ngakhale munthu atamagona mopereŵera ndi mphindi 30 kapena 40 usiku uliwonse kwa masiku asanu ogwira ntchito, iye angamakhale ndi tulo masana kwa maola atatu kapena anayi pofika Loŵeruka ndi Lamlungu, ndipo zimenezi zingam’chititse kumangosinza.”

N’kutheka kuti nthaŵi zina simungagone bwino usiku. Matenda a kusoŵa kwa tulo, kusamalira mwana wodwala, kapena zinthu zina zokuvutani zingakulepheretseni kupeza tulo. Zikatere, zikhoza kutheka kuti m’maŵa mwake mungayambe kusinza chiwongolero chili m’manja. Kodi muyenera kutani ngati zoterezi zitachitika?

N’kutheka kuti zimene anthu ambiri amaganiza kuti ndizo zothandiza monga kumwa khofi kapena tiyi, kutsegula zenera, kutafuna chingamu, kapena kudya chinachake chochititsa tsoo mkamwa sikungakuthetsereni tulo tanu. Pa zinthu zimene amati n’zothandizazi palibe n’chimodzi chomwe chimene chingathetse vuto lenileni. Chofunika apa n’kugona basi. Choncho bwanji osangogonako pang’ono? Magazini ya The New York Times inanena kuti: “Ngati munthu akungogona pang’ono chabe sayenera kugona mopitirira mphindi 30, ndipo akagona kuposa pamenepa, thupi lonse limafooka kenaka amagona tulo tofa nato ndipo zikatere kudzuka kumavuta.” Inde kugonako pang’ono kungachedwetse ulendo wanu, koma kungakupangitseni kukafika muli moyo.

Zimene mumakonda kuchita m’moyo mwanu zingachititse kuti muzisinza poyendetsa galimoto. Kodi mumakhala nthaŵi yaitali mukugwiritsira ntchito intaneti, kapena mumachedwa kugona usiku chifukwa choonerera TV? Kodi mumapita kokasangalala kumene anthu amachezera mpaka mbandakucha? Musalole kuti zizoloŵezi zoterezi zikusokonezereni tulo tanu. Nthaŵi inayake Mfumu yanzeru Solomo inalimbikitsa za kufunika ‘kopumulako pang’ono.’—Mlaliki 4:6, NW.

Oidziŵa Bwino Ntchitoyi Koma Ali Achikulire

Nthaŵi zambiri madalaivala achikulire ndiwo amakhala oidziŵa bwino ntchito yoyenda pamsewu. Komanso sachita zinthu zoika moyo pachiswe ndipo sachita zinthu zimene sangakwanitse. Komabe si kuti madalaivala achikulire sangakumane ndi ngozi zowombanitsa magalimoto. Ndipotu, akamakula m’pamene makamaka angachite ngozi zoterezi mosavuta. Magazini ya ku America yotchedwa Car & Travel inati: “Pa anthu 100 alionse akumeneko, pamapezeka anthu 9 okha amene ali ndi zaka zoposa 70, koma pa gululi amene amachita ngozi zoopsa zapamsewu amakhala 13 pa 100 alionse.” N’zomvetsa chisoni kuti ngozi zowombanitsa magalimoto oyendetsedwa ndi achikulire zikuchuluka.

Tamvani zimene gogo wina wachikazi amene ali ndi zaka 80 dzina lake Myrtle anaona. * Iye anayamba kuyendetsa galimoto zaka 60 zapitazo ndipo sanachitepo n’komwe ngozi yapamsewu. Komabe, monga mmene amachitira anthu ambiri, ukalamba wayamba kumuvutitsa, mwakuti wayamba kuona kuti tsiku lina akhoza kudzachita ngozi basi. Posachedwapa anauza olemba Galamukani! kuti: “Munthu ukamakalamba, ntchito iliyonse [ngakhale kuyendetsa galimoto] imasanduka chintchito chovuta kwambiri.”

Kodi iye anachitapo zotani kuti apeŵe kuchita ngozi yapamsewu? “Kwa zaka zonsezi ndakhala ndikumasintha zochita zanga kuti zizigwirizana ndi msinkhu wanga,” iye anatero. Mwachitsanzo, iye anachepetsa nthaŵi yake yoyendetsa galimoto, makamaka usiku. Kusintha pang’ono kumeneku kukum’thandiza kuti aziyendetsabe galimoto bwinobwino popanda kuchita ngozi.

Ngakhale zili zovuta kuvomereza, kukalamba kumam’bwezera m’mbuyo munthu aliyense. (Mlaliki 12:1-7) M’thupimu mumakhala tambiri totsinatsina, ndipo anthufe timayamba chidodo, komanso maso athu saonanso patali, ndipo zonsezi zimachititsa kuti munthu asayendetsenso galimoto bwinobwino. Komabe si kuti ukalamba paokha umam’lepheretsa munthu kuyendetsa galimoto. Chachikulu ndi mmene munthuyo amayendetsera galimotoyo. Tikamazindikira kuti thupi lathu likusintha n’kuyamba kumachita zinthu zotiyenera, tikhoza kumayendetsabe galimoto bwinobwino.

N’kutheka kuti inuyo simudziŵa n’komwe kuti maso anuwo akutha mphamvu. Munthu akamakula, satha kuona patali ndipo kuti aziona bwinobwino amafunika kuti kukhale kowala kwambiri. Kabuku kenakake konena za madalaivala achikulire kamutu wakuti The Older and Wiser Driver kamati: “Dalaivala wazaka 60 amafunika kuwala koŵirikiza katatu kuti aziona mofanana ndi wachinyamata wazaka zoyambira pa 13 mpaka 19, ndipo maso ake amachedwa kwambiri kuzoloŵera msanga malo amdima ngati anali powala.” Kusintha kwa maso athu kumeneku kungapangitse kuti kuyendetsa galimoto usiku kukhale kovuta.

Henry panopo ali ndi zaka 72 ndipo wakhala ndi mbiri yoyendetsa bwino galimoto kwa zaka zoposa 50. Mkati mwa zaka zimenezo, iye anayamba kuona kuti akamayendetsa galimoto usiku, kuwala kwa magetsi agalimoto zobwera kutsogolo kwake kunali kum’thobwa m’maso ndipo ankavutika kuti ayendetse bwinobwino. Atapita kukaonedwa maso ake, anauzidwa kuti ankafunika magalasi ena otha kuchepetsako mphamvu ya kuwalaku. Mwini wakeyo anati: “Panopa kuwala kumeneku si nkhaninso kwa ine.” Kusintha pang’ono chabe kunam’thandiza kwambiri kuti aziyendetsabe galimoto bwinobwino. Koma kwa anthu ena monga Myrtle, njira imene ingawathandize n’kungolekeratu kuyendetsa galimoto usiku.

Kukula kumam’lepheretsanso munthu kuganiza msanga zoti achite. Anthu achikulire angakhale anzeru ndiponso okhwima maganizo kuposa achinyamata. Komabe munthu amati akamakalamba, zimavutirapo kuti aone bwino zinthu zimene zikuchitika n’kuchitapo kanthu. Zimenezi zimachititsa kuti kuyendetsa galimoto kukhale kovuta kwambiri chifukwa chakuti magalimoto akamayenda amaloŵa m’maso ndiponso pamsewu pamachitika zinthu zosiyanasiyana. Munthu ayenera kuona mwamsanga zimene zikuchitikazo kuti asachite zinthu mwachidodo.

Magazini ya Car & Travel inanena kuti “kaŵirikaŵiri ngozi zoopsa kwambiri zimene madalaivala achikulire amachita zimakhala zoti dalaivalayo wangodutsa popanda kutsatira lamulo linalake.” N’chifukwa chiyani zimakhala choncho? Magazini yomweyi inapitiriza kunena kuti: “Zikuoneka kuti vutoli . . . limachitika pamphambano, dalaivala wachikulire akamati ayang’ane magalimoto a kudzanja lake lamanzere ndi lamanja asanaloŵe mumsewu waukulu.”

Kodi mungatani ngati simutha kuganiza msanga zoyenera kuchita? Samalani kwambiri mukamayandikira pamphambano za misewu. Ndi bwino kudzizoloŵeza kuyang’ananso kachiŵiri ngati kukubwera galimoto ina musanapitirize ulendo wanu. Makamaka muyenera kukhala wosamala kwambiri pokhota. Kukhota pamphambano n’koopsa kwambiri, makamaka mukamakhota poloŵa mumsewu umene uli ndi magalimoto amene akudutsa.

M’dziko la United States, ngozi zoopsa zokwanira 40 pa 100 zilizonse zimene madalaivala azaka zoposa 75 amachita pamphambano za misewu zimakhala zoti dalaivalayo anali kukhota kuloŵera cha kumanzere. Bungwe la AAA Foundation for Traffic Safety linauza madalaivala a m’dzikolo kuti: “Nthaŵi zina ndibwino kutsata njira yokhotera kumanja ngakhale maulendo atatu popeŵa kukhotera kumanzere.” Mukhoza kutengera mfundo imeneyo malinga ndi mmene magalimoto amayendera m’misewu kwanuko. Mukakonzeka bwinobwino, mungapeŵe mphambano zoopsa ndiponso zovuta kudutsapo.

Mfundo Yoyenera Kuiganizira

Kodi n’chiyani chimene chingakuthandizeni kudziŵa ngati ndinu dalaivala wabwino kapena ayi? Mwinatu mungapemphe mnzanu amene mumam’khulupirira kwambiri kapena wina wa m’banja mwanu kuti muyende naye ndipo akuuzeni ngati mumayendetsa bwino kapena ayi. Kenaka, mumvetsere mosamalitsa zonse zimene iye waonapo. Mukhozanso kuganiza zopita kumayeso oyendetsa galimoto. Masukulu ambiri amene amaphunzitsa kuyendetsa galimoto amaphunzitsanso zinthu zokhudza makamaka madalaivala achikulire. Mukabwereza kaŵiri kapena kangapo zinthu zoti zikanatha kukuchititsani ngozi yoopsa, dziŵani kuti mwayamba kusayendetsa bwino galimoto.

Kunena mosapita m’mbali, imafika nthaŵi imene njira yabwino imene ingakuthandizenidi ndiyo kungolekeratu kuyendetsa galimoto. Zimenezi zingakupwetekeni mtima kwambiri. Myrtle amene tam’tchula kale uja akudziŵa kuti posachedwapa tsiku lina adzangosiyiratu kuyendetsa galimoto. Pakuti tsikuli likuyandikira, iye anayamba kale kukonda kuyendetsedwa ndi anthu ena. Kodi iye amamva bwanji akamalekera munthu wina kuti azimuyendetsa? Iye anati: “Zimakhala bwino kumva mmene galimoto imakomera wina akamakuyendetsa iwe utangokhala phee.”

Mutaganizira nkhaniyi mozama, mwina nanunso mukhoza kukhala ndi maganizo omweŵa. Kupita kokagula zinthu, kutimaulendo tina n’tina, ndiponso kupita kwinakwake kumene mukufunikira komanso kumisonkhano kukhoza kukhala kosangalatsa kwambiri mukapitako ndi mnzanu. Mwina mungapite pa galimoto yanu yomweyo koma n’kumusiyira mnzanuyo kuti ayendetse. Kuyenda chonchi kungakhale kwabwinopo ndiponso kosangalatsa kusiyana ndi kuyenda nokha. Njira inanso ingakhale yokwera magalimoto olipiritsa ngati alipo. Dziŵani kuti si kuti anthu amakuonani kuti ndinu wofunika chifukwa choyendetsa galimoto. Makhalidwe anu ndiwo angachititse kuti a m’banja mwanu ndiponso anzanu, komanso Mulungu azikuonani kuti ndinu munthu wofunikadi.—Miyambo 12:2; Aroma 14:18.

Kaya ndinu wachikulire kapena wachinyamata, dalaivala woidziŵa bwino ntchito yake kapena wongoyamba kumene, ngozi zoopsa zapamsewu zikhoza kukuchitikirani. Dziŵani kuti kuyendetsa galimoto si chinthu chamaseŵera ayi. Muziyendetsa mosamala kuti mupeŵe kuwombana ndi galimoto ina. Mukatero, mukhoza kudziteteza inuyo ndiponso anthu ena pa maulendo onse amene mungadzayende.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 13 Maina amene ali mu nkhani ino tawasintha.

[Chithunzi patsamba 12]

Tsimikizirani kuti thupi lanu lapuma bwinobwino pogona mokwanira

[Chithunzi patsamba 13]

Kugonako pang’ono kukhoza kuchedwetsa ulendo koma kungapulumutse moyo wa anthu

[Chithunzi patsamba 13]

Madalaivala achikulire ndiwo amene amaidziŵa bwino kwambiri ntchito koma amakumana ndi mavuto apadera

[Chithunzi patsamba 14]

Kupita kwinakwake ndi mnzanu n’kothandiza kwambiri