Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kukhala M’dziko Lokonda Kutaya Zinthu

Kukhala M’dziko Lokonda Kutaya Zinthu

Kukhala M’dziko Lokonda Kutaya Zinthu

ANTHU ku mayiko olemera amataya zinyalala zankhaninkhani. Mwachitsanzo, taganizani za kuchuluka kwa zinyalala zotayidwa chaka chilichonse ku United States. Akuti ‘kulemera kwake kungafanane ndi kulemera kwa madzi odzaza mayiwe okwana 68,000, lililonse lotalika mamita 50.’ Zaka zingapo zapitazo, akuti anthu a mumzinda wa New York City mokha, chaka ndi chaka ankataya zinyalala zoti zingakwirire malo enaake aakulu okongola kwambiri mu a mzindawu otchedwa Central Park, ndi mamita anayi! *

M’posadabwitsa kuti dziko la United States alitcha kuti ndi “chitsanzo chochenjeza madera ena onse a dziko lapansi” pankhani ya “kugula zinthu ndi kukonda kuzitaya.” Komatu si dziko lokhali komwe kukuchitika zoterezi. Anthu akuganizira kuti zinyalala zomwe anthu a ku Germany amataya pachaka zingadzaze sitima ya pamtunda, yaitali kuchoka kulikulu la dzikolo ku Berlin, kukafika kugombe la Africa, womwe ndi mtunda wa makilomita 1,800. Ndipo nthaŵi inayake ku Britain akuti pachaka mabanja ambiri omwe munali anthu anayi anali kuwononga mapepala opangidwa kuchokera ku mitengo yokwana isanu ndi umodzi.

Mayiko omwe akutukuka kumene nawonso amataya zinyalala zochuluka koopsa. Magazini ina yodziŵika bwino inanena kuti: “Nkhani yomvetsa chisoni kwambiri ndi yakuti ambiri mwa anthu sikisi biliyoni a padziko lapansi pano akuyambanso kutaya zinyalala zochuluka monga zimene dziko la United States ndi mayiko ena otukuka amataya.” Inde, kaya tifune kapena tisafune, ambiri mwa ife lerolino tili m’gulu la anthu okonda kutaya zinthu.

Ndi zoona kuti anthu sanayambe lero kutaya zinthu. Komatu, masiku ano zakudya ndiponso zinthu za m’zitini ndi m’mapepala zafala kwambiri kusiyana ndi mmene zinalili zaka zapitazi, chotero zikutiro zomwe zinapangidwa kuti akatha kuzigwiritsira ntchito zizitayidwa zangoti mbwee kulikonse. Komanso manyuzipepala, magazini, mapepala otsatsa malonda, ndiponso mabuku achuluka koopsa.

Chinanso n’chakuti dzikoli latukuka kwambiri pankhani za mafakitale ndiponso za sayansi motero layambitsa mitundu yatsopano ya zinyalala. Nyuzipepala ya Die Welt, ya ku Germany, inati m’mayiko a m’bungwe la “European Union amasiya kugwiritsa ntchito galimoto pafupifupi nayini miliyoni chaka chilichonse.” Kutaya galimoto zimenezo si ntchito ya maseŵera. Ndipotu funso lovuta kwambiri ndi lakuti, Kodi mungataye motani zipangizo zotha ntchito za nyukiliya kapena za mankhwala oopsa popanda ngozi iliyonse? M’mbuyomu mu 1991, akuti dziko la United States linali ndi “miyulumiyulu ya zinyalala za nyukiliya ndipo linalibe malo enieni ozisungirako.” Migolo wani miliyoni ya zinthu zoopsa kwambiri, akuti anaisunga m’malo ena ongoyembekezera oti nthaŵi ina iliyonse “zikanatha kukhuthuka, kubedwa ndiponso kuwononga malo okhala chifukwa chosasamalidwa bwino.” Mu 1999 mokha, mabizinesi osiyanasiyana ndiponso makampani a boma ku United States okwana 20,000 anali ndi zipangizo zotha ntchito zoopsa kwambiri zokwana matani 40 miliyoni.

China chomwe chikuchititsa vutoli ndi chiŵerengero cha anthu padziko lonse, chomwe chakwera kwambiri m’zaka 100 zapitazi. Kuchuluka kwa anthu kukuchulukitsanso zinyalala! Ndipo ambiri mwa anthu ameneŵa ali pa kalikiliki wofuna kupeza katundu wambiri. Posachedwapa, bungwe la Worldwatch Institute linanena kuti: “Kuyambira mu 1950 tagwiritsa ntchito katundu wambiri ndiponso anthu ena atigwirira ntchito zambiri kusiyana ndi kale lonse.”

Ndi zoona kuti ndi anthu ochepa okhala m’mayiko olemera omwe akufuna kusiya kugwiritsa ntchito ‘katundu ndi anthu owachitira ntchito’ onsewo. Mwachitsanzo, taganizani momwe zinthu zimapepukira kupita kusitolo ndi kugula katundu amene amukutira kale n’kumunyamulira m’pepala kapena m’jumbo kupita naye kunyumba. Ngati kukutira zinthu kwamakonoku kutasiyidwa mwadzidzidzi, sipangapite nthaŵi yaitali kuti anthu azindikire kuti amakudalira kwambiri. Ndipo chifukwa chakuti ndi kwaukhondo kwambiri, kukutira zinthu kumathandiza mwanjira ina yake pa kukhala ndi moyo wabwino.

Komabe, ngakhale kuti pali ubwino woterowo, kodi pali chifukwa chilichonse chokhalira ndi nkhaŵa kuti anthu anyanyira kukonda kutaya zinthu masiku ano? Mwachionekere chifukwa chilipo, popeza kuti njira zosiyanasiyana zoyesa kuthetsera vuto la kuchuluka kwa zinyalala sizinathandize kwenikweni kuchepetsa kuchuluka kwa zinthu zomwe anthu amataya. Ndipo choopsa kwambiri n’chakuti mtima umene ukuchititsa kuti anthu amasiku ano azikonda kutaya zinthu ndi wodetsa nkhaŵa kwambiri.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Maloŵa ndi aakulu mahekitala 341.

[Chithunzi patsamba 4]

N’kovuta zedi kutaya zinyalala zoopsa kwambiri popanda kubweretsa vuto lililonse