Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kulimbana Ndi Mavuto a M’dziko Lokonda Kutaya Zinthu

Kulimbana Ndi Mavuto a M’dziko Lokonda Kutaya Zinthu

Kulimbana Ndi Mavuto a M’dziko Lokonda Kutaya Zinthu

“M’CHILENGEDWE . . . mulibe zinthu zomwe tingati zimafika pena potha ntchito.” Malinga n’kunena kwa magazini ya Time, ameneŵa ndi maganizo a katswiri wina wotchuka pa ntchito yokonzanso zinthu zotha ntchito. Anali kunena za mmene nthaŵi zonse zinthu zina zachilengedwe zimagwiritsira bwino ntchito zinthu zimene zinthu zina zam’chilengedwe zatha nazo ntchito. Akuti katswiri yemweyu amakhulupirira kuti “anthu angatengere chilengedwe posataya zinthu, koma kuti atero m’pofunika kukhala ndi umisiri wotsogola ndiponso kusinthiratu mitima.”

N’kutheka kuti ambirife sitingayambitse umisiri wotsogola. Koma ndithu mtima wathu ndi woti tingaulamulire! Ndipo kuona moyenera mfundo zina zikuluzikulu za makhalidwe abwino kungatithandize kulimbana bwinobwino ndi mavuto okhala m’dziko lokonda kutaya zinthuli.

Peŵani Kuwononga Zinthu

Munthu mmodzi pa anthu asanu alionse padziko pano amagona ndi njala. Kudziŵa zimenezi kuyenera kutithandiza kuona kuti n’kofunika kusamala chakudya ndi kupeŵa kuchiwononga. Mwamuna wina ndi mkazi wake omwe anabwerera ku Ulaya atatha zaka 28 akugwira ntchito yaumishonale ku Africa ananena kuti vuto lina lalikulu lomwe anakumana nalo pamene amakhazikikanso m’dziko lakwawo linali loti azoloŵere “khalidwe la anthu lotaya chakudya mwachisawawa.”

Makolo ena anzeru amaphunzitsa ana awo kuti m’mbale mwawo aziikamo chakudya chomwe angachikwanitse kudya. Kuchita zimenezi kumachepetsa zakudya zotayidwa komanso kuwononga zinthu. Ndi bwino kutenga chakudya chochepa poyamba, ndiyeno n’kutenganso china. Makolo ayenera kupereka chitsanzo. Yesu anatipatsa tonsefe chitsanzo poyamikira mochokera pansi pa mtima zinthu zomwe Mulungu anapereka, zakuthupi ndi zauzimu zomwe. Baibulo limasonyeza kuti Yesu anapeŵeratu kuwononga chakudya, ngakhale kuti chinachulukitsidwa mozizwitsa!—Yohane 6:11-13.

Mfundo ya kukhala wosamala ingagwiritsidwenso ntchito pa zovala, mipando, ndi makina. Tikamaonetsetsa kuti zinthu zili bwino nthaŵi zonse ndiponso tikamazigwiritsabe ntchito ngati n’kotheka timasonyeza kuti timayamikira zinthu zomwe tili nazo. Tisanyengedwe ndi otsatsa malonda amene amafuna kutipangitsa kuti tisamakhutire ndi zimene tili nazo potitsatsa zinthu zina zazikulupo, zabwinopo, zochita zinthu mofulumirirapo kapenanso zamphamvu. Ndi zoona kuti tili ndi ufulu wonse wochotsa katundu yemwe akugwirabe ntchito n’kupezerapo wina. Koma tisanatero, tiyenera kuganizira mtima womwe ukutichititsa zimenezo komanso zolinga zathu.

Peŵani Dyera

Pamene ankadutsa m’chipululu kupita ku Dziko Lolonjezedwa, Aisrayeli anapatsidwa mana kuti chikhale chakudya chawo. Baibulo limanena kuti iwo ankapatsidwa mana ambiri. Komabe, Aisrayeli anachenjezedwa kuti asachite dyera; ankafunika kutola mana ongokwanira kudya akakhala ndi njala basi. Amene sanamvere anazindikira kuti dyera lilibe phindu, chifukwa chakuti mana otsala ankagwa mphutsi n’kuyamba kununkha. (Eksodo 16:16-20) N’zoonekeratu kuti Baibulo limadzudzula mtima wa dyera mwamphamvu ndi mobwerezabwereza.—Aefeso 5:3.

Si Baibulo lokha limene limanena zimenezi. Mwachitsanzo, katswiri wina wachiroma wokonda kuganiza kwambiri yemwenso ankalemba zisudzo, wam’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino dzina lake Seneca, anaona kuti munthu wadyera sakhutitsidwa. Iye anati: “Chilengedwe chonse sichikhutiritsa dyera.” Erich Fromm, katswiri winanso wokonda kuganiza kwambiri wa m’zaka za m’ma 1900, ananena mfundo yofanana ndi imeneyi. Iye anati: “Dyera lili ngati dzenje lakuya kwambiri lomwe limam’thetsa mankhalu munthu wofuna kudzikhutiritsa koma wosakhutira n’komwe.” Kuwonjezera pa kupeŵa dyera ndi kuwononga zinthu, pali njira zina zabwino zomwe anthu ambiri akutsatira.

Phunzirani Kupatsa

Musanataye zinthu zomwe zidakali zabwino, ganizirani kuti ndani omwe angazifune. Mwachitsanzo, zovala zikayamba kuwathina ana, kodi angapatse ana ena kuti azivala? Kodi mungachitenso chimodzimodzi ndi zinthu zina zomwe zidakali bwino koma simukonda kuzigwiritsa ntchito ngati kale? Apatseniko ena chinthu chinachake chimene inuyo munasangalala nacho kuti nawonso asangalale nacho. Mark Twain wa ku America, yemwe anali wolemba mabuku ndiponso katswiri wanthabwala, nthaŵi inayake analemba kuti: “Kuti munthu asangalaledi ndi chinthu chinachake payenera kukhala wina woti asangalale naye pamodzi.” Mwina munaonapo kuti chisangalalo chanu chimakula kwambiri pakakhalanso wina amene akusangalala nanu. Komanso, mukakhala ndi mtima woganizira ena motere, mumathandiza polimbana ndi mavuto obwera chifukwa cha mtima wokonda kutaya zinthu.

Kupatsako ena zinthu ndi khalidwe lomwe Baibulo limalimbikitsa kwambiri. (Luka 3:11; Aroma 12:13; 2 Akorinto 8:14, 15; 1 Timoteo 6:18) Ndithudi, anthu onse akanakhala okonda kupatsa, bwenzi dziko likukoma!

Khutirani ndi Zofunika Zikuluzikulu M’moyo

Munthu amene amakhala wokhutira amasangalala. Mfundo imeneyi imagwira ntchito kulikonse ndiponso nthaŵi zonse. Pa Chigiriki pali mwambi wakuti: “Munthu wosakhutira ndi zochepa sangakhutire ndi chilichonse.” Ndipo pa Chijapani pali mawu akuti: “Munthu wosakhutira ndi mphaŵi.” Baibulo nalonso limayamikira kwambiri mtima wokhutira. Timaŵerenga kuti: “Koma chipembedzo pamodzi ndi kudekha chipindulitsa kwakukulu; pakuti sitinatenga kanthu poloŵa m’dziko lapansi, ndiponso sitikhoza kupita nako kanthu pochoka pano; koma pokhala nazo zakudya ndi zofunda, zimenezi zitikwanire.”—1 Timoteo 6:6-8; Afilipi 4:11.

Ndi zoona kuti kukhala wokhutira ndi zimene tili nazo kungafune “kusinthiratu mitima.” Mayi wina wachitsikana dzina lake Susanne anazindikira posachedwapa kuti anafunikira kusintha mtima koteroko. Iye anati: “Ndinatsimikiza mtima kuti ndibwino kuti ndiyambe kukonda zomwe ndili nazo kale popeza sindikanatha kupeza zonse zomwe ndinkafuna. Ndine wokondwa tsopano ndiponso wokhutira.”

Kukhutira kumabweretsadi chimwemwe. Pulofesa Argir Hadjihristev, yemwe ndi katswiri wa maphunziro a zaukalamba ku Bulgaria, anati: “Chinthu choyamba choipitsitsa ndicho kusakhutira ndi zochepa zomwe munthu ali nazo.” Potchulapo mmene kukhala wokhutira kumathandizira pa thanzi, iye anapitiriza kuti: “Munthu amene sayesa kukhala wolemera kuposa anzake, yemwe sayesa nthaŵi ndi nthaŵi kuti akhale n’zinthu zambiri, salimbana n’kupikisana ndi ena ndipo savutika m’maganizo. Ndipo zimenezi zimam’thandiza kukhala munthu wokhazikika maganizo.”

Inde, anthu okonda kutaya zinthu sangabweretse chimwemwe chenicheni. Ndipo nawo mtima wokonda kutaya zinthu sungabweretse chimwemwe ngakhale pang’ono! Zikuoneka kuti ambiri ayamba kumvetsa zimenezi. Nanga inuyo bwanji?

[Chithunzi patsamba 9]

Ana amafunika kuphunzira kupeŵa kuwononga chakudya

[Chithunzi patsamba 9]

Yesu anasonyeza chitsanzo chabwino popeŵa kuwononga zinthu

[Chithunzi patsamba 10]

Bwanji osapatsa ena chinthu chimene simukuchigwiritsanso ntchito mmalo mochitaya?