Manambala—Kodi Mumakhudzidwa Nawo?
Manambala—Kodi Mumakhudzidwa Nawo?
KODI manambala amatiuza zinthu zinazake zachinsinsi? “Si nkhani yoti n’kuchita kufunsa imeneyi!” ena amatero n’kumati chitsanzo chochititsa chidwi kwambiri pankhaniyi ndi zija zauchigaŵenga zimene zinachitika pa September 11, 2001.
Munthu wina wokhulupirira kuti manambala angatiuze zinthu zachinsinsi anati: “Nditangomva za nkhaniyi, chimene ndinaona n’chakuti patsikuli deti linali 9-11-2001.” Anthu ambiri okhulupirira manambala amati nambala ya 11 ili m’gulu la manambala apadera amene amawakhulupirira kwambiri. Motero anthuŵa akonza ndandanda ya zinthu zosiyanasiyana zogwirizana ndi nambala yapaderayi zokhudzana ndi zauchigaŵenga zimene zinachitikazo. Zina mwa zinthu zochepa chabe zimene apeza ndi izi:
▪ Zoopsazo zinachitika mwezi wa 9 pa tsiku la 11. Tikaphatikiza 9 + 1 + 1 timapeza 11.
▪ Tsiku la September 11 linali tsiku la nambala 254 la chaka. Tikaphatikiza 2 + 5 + 4 timapeza 11.
▪ Nambala ya ndege imene inagunda nyumba yosanja ya chakumpoto inali 11.
▪ M’ndegeyi munakwera anthu 92. Tikaphatikiza 9 + 2 timapeza 11.
▪ M’ndege imene inagunda nyumba yosanja ya chakummwera munakwera anthu 65. Tikaphatikiza 6 + 5 timapeza 11.
▪ Nyumba zosanja ziŵirizo zinaima ngati 11.
▪ Dzina lachizungu la mzindawu lakuti “New York City” lili ndi zilembo 11.
Chikhulupiriro chakuti manambala paokha kapena akakhala pamodzi ndi ena, kapenanso akaphatikizidwa amatha kukudziŵitsani zinthu zinazake, chakhala chofala kwambiri ku Africa, Asia ndiponso ku America. Kodi anthu akutengeka nacho maganizo chifukwa chiyani? Malingana ndi nkhani ina imene ili m’kompyuta ina yolumikizidwa ku intaneti akuti njira ina yotchuka kwambiri yokhulupirira manambala, yomasulira chilembo chilichonse m’dzina la munthu, “imathandiza kudziŵa bwinobwino za mmene munthuyo alili, mtima wake, khalidwe lake ndi zofooka zake.” Nkhaniyi inanena kuti tikachita masamu enaake pogwiritsa ntchito “tsiku limene tinabadwa tingathe kudziŵa mmene moyo wathu ukhalire, mavuto ndiponso zosangalatsa zimene tikumane nazo.”
Kodi zimenezi n’zoona? Kapena kodi n’kutheka kuti kufufuza manambala m’njira imeneyi kungangotigwetsera m’mavuto enaake?