Mapemphero Amene Mulungu Amamva
Lingaliro la Baibulo
Mapemphero Amene Mulungu Amamva
“Pemphani, ndipo adzakupatsani; funani, ndipo mudzapeza; gogodani ndipo adzakutsegulirani. Pakuti yense wakupempha alandira; ndi wofunayo apeza; ndi iye amene agogoda adzam’tsegulira.”—LUKA 11:9, 10.
POSONYEZA kukhulupirira kwambiri mawu a Yesu Kristu amene ali pamwambapa, Akristu ambiri amapemphera kwa Mulungu pankhani zamavuto awo ndiponso pamene zinthu zikuwadetsa nkhaŵa. Ndipo amatero ali ndi chikhulupiriro chonse chakuti Mulunguyo amawakonda ndiponso kuti amawasamalira. Komabe ena amataya mtima akamadikirira kuti mapemphero awo ayankhidwe. Kodi mumaganiza kuti mapemphero anu ndi osamveka? Kodi Mulungu amamvetsera mukamapemphera?
Ngakhale mapemphero athu atamaoneka ngati kuti sakuyankhidwa, si ndiye kuti Mulungu sanamve ayi. Baibulo limatitsimikizira kuti: ‘Maso a Yehova ali pa olungama, ndi makutu ake akumva pembedzero lawo.’ (1 Petro 3:12) Ndiye kuti Yehova Mulungu amamva mapemphero a anthu olungama, kaya ochita kutulutsa mawu kapena amumtima. (Yeremiya 17:10) Yehova amaonanso bwinobwino maganizo a munthu amene akupempherayo ndi mmene munthuyo akumvera mumtima mwake pamene mwina munthuyo sangadziŵe kwenikweni kapena kumvetsa zinthuzi.—Aroma 8:26, 27.
Ngakhale zili choncho, pali zinthu zina zofunika pa mapemphero kuti Mulungu awamve. Choyambirira chenicheni n’chakuti mapemphero ayenera kulunjika kwa Mulungu basi, osati kwa Yesu, munthu winawake woyera mtima, kapena fano lina lililonse. (Eksodo 20:4, 5) Tikamapemphera, tiyeneranso kupemphera kudzera m’dzina la Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu. (Yohane 14:6) Kodi pamenepa ndiye kuti Yesu ndiye amene amayamba kumva mapemphero athu kenaka n’kukafikitsa uthengawo kwa Mulungu? Si choncho ayi. Koma kuti timati tikamapemphera kwa Yehova m’dzina la Yesu, timasonyeza kuti ndife ophunzira a Kristu ndiponso kuti tikuzindikira kuti timatha kumufikira Mulungu chifukwa cha dipo lake basi.—Ahebri 4:14-16.
Tiyenera kupemphera ndi chikhulupiriro. Mtumwi Paulo anati: “Wopanda chikhulupiriro sikutheka kum’kondweretsa [Mulungu]; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphoto iwo akum’funa Iye.” (Ahebri 11:6) Kodi munthu amadziŵa bwanji kuti ali ndi chikhulupiriro choterocho? Yakobo yemwe analemba nawo Baibulo akuyankha kuti: “Ine ndidzakuonetsa iwe chikhulupiriro changa chotuluka m’ntchito zanga.” (Yakobo 2:18) Indedi, chikhulupiriro chimaonekera pa zochita zathu, ndipo zochitazo zimasonyeza kuti timam’konda Mulungu ndi kuti tikuyesetsa kum’kondweretsa.
Anthu olambira Mulungu ayeneranso kulimbikira kupemphera. Yesu ananena mfundo imeneyi momveka bwino pa lemba la Luka 11:9, 10, lomwe mawu ake ndi amene ali poyambirira pankhani ino. Ndipotu munthu atangopempherera za vuto linalake kamodzi kokha, kodi sizingasonyeze kuti zimene akupemphazo alibe nazo ntchito kwenikweni?
Zimene Mulungu Amalonjeza
Zilibe kanthu kuti kaya timapemphera kangati ndiponso kaya timapemphera mochokera pansi pamtima bwanji, mfundo ndi yakuti tikukhala mu “nthaŵi zoŵaŵitsa.” (2 Timoteo 3:1) N’zoona kuti Yesu ananena kuti om’tsatira adzakhala achimwemwe, koma iye sananene kuti iwo sadzavutika n’komwe ayi. (Mateyu 5:3-11) M’malo mwake iye ananena kuti ophunzira ake angadzakhale achimwemwe ngakhale kuti angadzakhale akulira maliro, komanso anjala, aludzu, kapena akuzunzidwa.
Chimwemwe chimene Yesu ankanena si chodalira kuti zinthu zonse zikhale zikuyenda bwino ayi. M’malo mwake chimwemwechi ndicho kukhutira mumtima mwathu chifukwa chotumikira Mulungu. Motero, tikhoza kupeza chimwemwe chinachake ndithu ngakhale tili m’kati mwa mavuto.—2 Akorinto 12:7-10.
Kulimbana ndi Mavuto Ongokhudza Inuyo Basi
Kodi pamenepa ndiye kuti n’kupanda nzeru kuti munthu apemphere kwa Mulungu pankhani zimene zikum’khudza iyeyo basi monga nkhani ya kupeza mwamuna kapena mkazi woyenerera woti n’kukwatirana naye kapena kulimbana ndi mavuto okhudza m’banja, matenda, kapenanso kupeza ntchito? Ayi, sichoncho chifukwa chakuti ngakhale kuti Mulungu salonjeza kuti angathetse mavuto athu modabwitsa, iye angatipatse nzeru zoti tithane nawo bwinobwino. Pankhani yokhudza mayesero, Yakobo analemba kuti: “Wina wa inu ikam’soŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzam’patsa iye.” (Yakobo 1:5) Choncho mwa mzimu wake woyera, Yehova angatisonyeze zochita. Zimenezi zingatithandize kumvetsa ndiponso kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo tikafuna kuchita zinthu.
Inde, si kuti mzimu wa Mulungu umatiganizira zoti tichite. Koma ifeyo tokha tifunika kuchitapo kanthu. Mwachitsanzo ngati tili ndi vuto linalake, kodi tafufuza mbali zonse za vutolo mozama? Imeneyi ndiyo ntchito yosonyeza Mulungu kuti tili ndi chikhulupiriro. (Yakobo 2:18) Kodi takhala tikulimbikira poyesetsa kuthetsa mavuto athu mwa kupempha Mulungu mosalekeza kuti atitsogolere? (Mateyu 7:7, 8) Kodi tasanthula mosamala kwambiri mfundo za m’Baibulo zimene zikugwirizana ndi vutolo? Mawu a Mulungu angatipangitse kukhala ‘oyenera, okonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.’—2 Timoteo 3:16, 17.
N’zoona kuti Mulungu amatha kuloŵerera pazochita za anthu n’kutichotsera mavuto athu onse, koma iye watilola kuchita zinthu mwaufulu wathu. N’zodandaulitsa kuti anthu ambiri amagwiritsa ntchito ufulu wawo poika anzawo m’mavuto. Motero, mavuto ena amene timapempherera kuti achoke angapitirirebe mpaka dziko latsopano la Mulungu litafika. (Machitidwe 17:30, 31) N’kutheka kuti vutoli lingakhale lomwe lili m’dera limene timakhala, monga umbanda kapena nkhondo yomwe yabuka; kapena lingakhalenso lokhudza mavuto omwe anthu otitsutsa abweretsa. (1 Petro 4:4) Tiyenera kudziŵa kuti m’dziko la anthu osaopa Mulungu lino, mavuto ena sangasinthe.
Komabe Mulungu amakonda anthu ake amene amam’lambira ndipo amafuna kuwathandiza. Ufumu wake ukadzayamba kulamulira popanda wopikisana nawo padziko lonse, iye adzathetseratu mavuto oopsa onseŵa amene ali padzikoli. (Chivumbulutso 21:3, 4) Tiyenera kulimbikirabe kum’pempha kuti atithandize polimbana ndi mavuto athu mpaka nthaŵi imeneyo idzafike. Tikatero tikhoza kutsimikiza kuti Yehova adzakwaniritsa lonjezo limene lili m’Baibulo pa Yesaya 41:10, lakuti: “Usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; ine, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.”