Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mdima Ukagwa Masana

Mdima Ukagwa Masana

Mdima Ukagwa Masana

YOLEMBEDWA NDI OLEMBA GALAMUKANI! KU ANGOLA NDI KU ZAMBIA

ENA anganene kuti: ‘Mdima kugwa masana? N’zosatheka zimenezo!’ Zimatheka ndiponso zimachitika kangapo konse m’zaka khumi zilizonse pakangochitika kadamsana woti dzuŵa lonse n’kuphimbika. Kodi n’chiyani chimachititsa kadamsana, ndipo n’chifukwa chiyani kadamsana amakhala wochititsa chidwi? Kuti tidziŵe yankho lake tiyeni tiyambe taona mmene mwezi umayendera.

Kodi mukudziŵa bwino kuti mwezi umasintha bwanji maonekedwe pamene ukuzungulira dziko lapansi? Mwezi ndi dzuŵa zikayang’anizana, dziko n’kukhala pakati pawo, timaona mwezi umene timautcha kuti wathunthu uja ukutuluka kum’maŵa dzuŵa likamaloŵa kumadzulo. Tsiku lililonse mwezi umatuluka mochedwerako, ndipo pang’ono ndi pang’ono umaloŵera kumene kumatulukira dzuŵa. Chigawo cha mwezi chomwe chimaunikidwa ndi dzuŵa chimamka chichepa pang’onopang’ono, ndipo kenako chimaoneka ngati mwezi woti wangokhala kumene. Mwezi ukamayendera pamodzi ndi dzuŵa tsiku lonse, kumakhala kovuta kuuona ndipo ngakhale chigawochi sichioneka, chifukwa chakuti dziko limayang’anizana ndi mbali ya mwezi yomwe kuli mdima. Apa ndi pamene timati mwezi wakhala. Ndiyeno ukamatalikirana ndi dzuŵa, umayambanso kukula kenako ndi kudzakhala wathunthu. Zimenezi zimachitika m’masiku 28 alionse.

Mwezi wokhala kumene ndiwo umachititsa kadamsana. Nthaŵi zambiri mweziwo umadutsana ndi dzuŵa masana koma ife sitidziŵa chifukwa mwezi ukamazungulira dziko sudutsa m’njira yoongoka mwakuti n’kutsitira dziko. Komabe, nthaŵi zina, dzuŵa, mwezi, ndi dziko zimakhala pa mzere woongoka. Zikatero, mthunzi wa mwezi umafika padziko, n’kuchititsa kadamsana.

Kadamsana amachitika chifukwa cha kugwirizana kwapadera kwa dzuŵa, mwezi, ndi dziko. Dzuŵa n’lalikulu koopsa, chifukwa mlitali mwake ndi motalika maulendo 400 kuposa mlitali mwa mwezi. Komabe, chochititsa chidwi kwambiri n’chakuti kuchoka pa mwezi kukafika pa dzuŵa pali mtunda wa maulendo pafupifupi 400 kuposa mtunda umene uli pakati pa ife ndi mwezi. Chotero, malinga ndi mmene ifeyo timaonera, dzuŵa ndi mwezi n’zosasiyana kwenikweni kukula kwake. Chifukwa cha zimenezi, nthaŵi zina mwezi umaoneka ngati ungaphimbe dzuŵa lonse.

Kuti pachitike kadamsana wophimbiratu dzuŵa lonse woteroyo, dzuŵa, mwezi, ndi dziko zimayenera kukhala pa mzere umodzi, komanso mwezi uyenera kukhala moyandikana ndi dziko. * Zikatero, kumapeto kwa mthunzi wa mwezi kumene kuli kosongoka ngati nguli kumachititsa mdima m’madera ena a dzikoli.

Mthunzi wa kadamsana wa pa June 21, 2001, yemwe dzuŵa lonse linaphimbika, unali wa makilomita 200 m’mimba mwake. Kadamsanayu anayambira kugombe la kum’maŵa kwa South America dzuŵa litangotuluka ndi kudutsa kum’mwera kwa nyanja ya Atlantic, komwe anakhala kwa mphindi pafupifupi zisanu. Atadutsa ku Angola, Zambia, Zimbabwe, ndi Mozambique, anakathera kugombe la kum’maŵa kwa Madagascar, dzuŵa likuloŵa. Tiyeni tione mmene anthu a ku Angola ndi Zambia anaonera chozizwitsa chakuthambo chimenechi.

Kukonzekera Kadamsanayu

Pokhala ndi chikhulupiriro chonse choti kudzachitika kadamsana, akatswiri a zofufuzafufuza, anthu ena okonda zakuthambo, ndi ena ambiri anakhamukira ku Africa kudzaona kadamsana woyamba mu Zaka 1000 zatsopano zimene tayambazi, dzuŵa lonse litaphimbikiratu. Mwa mizinda yonse imene munachitika kadamsanayu, Lusaka ndi mzinda wokhawo womwe ndi likulu la dziko, chotero alendo ambiri anapita kukamuonera kumeneko.

N’kutheka kuti kadamsanayu anakopa alendo ochuluka kwambiri kupita ku Zambia kusiyana ndi zochitika zina za m’mbuyomo. Patangotsala masiku ochepa kuti kadamsanayu achitike, mu Lusaka munafika alendo ankhaninkhani. Anthu anakonzekera kadamsanayu padakali miyezi yambiri. M’mahotela, m’nyumba zokhala alendo, m’misasa ya apaulendo, ndi m’nyumba za anthu osiyanasiyana anali atasungiratu malo onse, kuti alendo ankhaninkhaniwo adzafikiremo.

Ena mwa malo omwe anakonzedwa kuti anthu akaonerepo kadamsanayu ndi bwalo la ndege la mu Lusaka, komwe alendo akanatha kufika m’maŵa, n’kuona kadamsanayo, n’kunyamuka madzulo. Ma TV ndiponso mawailesi anakhala akulengeza za kadamsanayu milungu yambirimbiri ndipo anali kuchenjeza anthu za kuopsa koyang’ana dzuŵa popanda kuvala magalasi. Malonda a magalasi apadera a dzuŵa anakwera kwambiri kuposa mmene ankayembekezerera, ndipo m’masitolo ambiri magalasiwo anatheratu.

Komatu, mu Africa, kadamsanayu anayambira ku Angola, mumzinda wa Sumbe, womwe uli kugombe la nyanja. Mu mzindawu munachitika kadamsana, dzuŵa lonse linaphimbidwa kwa mphindi zinayi ndi theka. Chotero linali dera lokhali la kumtunda kwa nyanja lomwe kadamsana anakhalitsa kwambiri.

Miyezi yambiri kadamsanayu asanachitike, mu Luanda, likulu la dziko la Angola, ndi m’matawuni ena akuluakulu munakhomedwa zikalata zolengeza za kadamsanayu ndiponso zochenjeza za kuopsa kwake. Mthunzi wa mwezi unadutsa cham’katikati mwa dzikolo, choncho m’dziko lonse la Angola munachitika kadamsana wamkulu ndithu chifukwa mbali yaikulu ya dzuŵa inaphimbika. Anthu mu Luanda anaona dzuŵa litaphimbika kungotsalako kachigawo kochepa kwambiri. Boma, mogwirizana ndi makampani omwe si a boma, anakonza zoitanitsa kunja kwa dzikolo mamiliyoni ambiri a magalasi apadera a dzuŵa kuti adzapatse anthu. Magalasi ambiri anaperekedwa ulere kwa anthu osauka.

Ntchito zambiri zoona za kadamsanayu ku Angola, zinachitikira ku Sumbe, umene uli mzinda wokongola wam’kadera kopanda mapiri komwe kali pakati pa nyanja ya Atlantic ndi dera la mapiri a pakati pa dziko la Angola. Nkhondo yoopsa kwambiri yomwe yasakaza Angola sinkachitika ku Sumbe, motero alendo amapeza kuti mzindawu uli bwinobwino ndipo uli ndi anthu pafupifupi 25,000, ansangala, aubwenzi, ndi ochezeka. Pofuna kuwapezera malo okwanira anthu onse okacheza kumeneko, anakonza malo ena owonjezera oti alendo azidzagonako ndi kupezako chakudya, ndipo anakonza makina amphamvu za magetsi a m’deralo kuti azigwira ntchito bwino. Akatswiri a sayansi, nduna za boma, ndiponso anthu a ku Angola ndiponso m’mayiko ena ogwira ntchito zothandiza anthu anaphunzitsidwa mozama za kadamsanayu. Anakonza malo aakulu m’mphepete mwa nyanja komwe kunali zochitika za chisangalalo chachikulu chimene sichinachitikepo ku Sumbe.

Tsiku la Chisangalalo Linafika

Ubwino umodzi woonera kadamsanayu muli ku Angola unali wakuti mu June kumakhala kouma. Koma taganizani momwe anthu anakhumudwira pamene kunachita mitambo m’dera la Sumbe, kutatsala tsiku limodzi kuti kadamsanayu achitike! Mtambo wa bii unakuta mzindawu usiku wonse mpaka m’maŵa. Kodi anthu anangolemba m’madzi poyembekezera kuona kadamsanayu? Dzuŵa litakwera mitambo inayamba kuchoka, ndipo lisanafike pamutu, thambo n’kuti lili biriwiri, kulibe mtambo ndi umodzi womwe. Zitatero m’pamene mitima ya anthu inakhala m’malo. N’chimodzimodzinso ku Zambia, anthu anali ndi nkhaŵa chifukwa chakuti kunacha ndi mitambo. Koma nakonso, kunayera panthaŵi yake. Tamverani momwe anthu oona ndi maso akufotokozera mmene zinthu zinachitikira.

Angola: “Tinasankha kuonerera kadamsanayu tili pa malo ena otchuka kwambiri pomwe nyanja imaonekera m’munsi kwambiri. Pamene ola la kadamsanayu limayandikira, khwimbi la anthu linasonkhana m’mphepete mwa nyanja ya m’tauniyi ndiponso m’malo ena omwe anakonzedwa. Dzuŵa lili paliwombo, kadamsana atatsala pang’ono kuyambika, anthu ambiri anavala magalasi awo oteteza maso n’kuyamba kuyang’ana kuti mwezi uyambira pati kuphimba dzuŵa. Dzuŵa litangoyamba kupendeka pang’ono kadamsana anayamba. Kudzera m’zipangizo zoonera zinthu zili patali kapena telesikopu, anthu ankatha kuona madontho angapo a padzuŵa. Anthu ankaona madontho ameneŵa akubisika limodzi ndi limodzi. Pamene dzuŵa linali kubisika pang’onopang’ono, kunayamba kuzizira ndipo kunayamba kuŵala mwachilendo. Kenako, kachigawo komaliza ka dzuŵa kanabisika, ndipo kunagwa mdima.”

Zambia: “Ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Zambia, yomwe ili ku Makeni, mu Lusaka, inali pamalo abwino kwambiri oonerapo kadamsanayu, dzuŵa lonse litabisika. Panthaŵi ya 3:07 masana, mwezi unayamba kutchinga dzuŵa. Kunayamba kuchita mdima ndipo makoma a nyumba anayamba kukhala ndi mthunzi wosonyeza kuti kwayamba kuda. Mphepo inasiya kuwomba, ndipo mbalame zinasiya kuimba. Nyama zakuthengo zinayamba kukonzekera zokagona. Panthaŵi ya 3:09, patatsala masekondi angapo kuti dzuŵa lonse libisike, dzuŵa linkangooneka madontho angapo othwanima, kenako panangotsala dontho limodzi. Madontho ameneŵa amatchedwa kuti mikanda ya Baily ndipo dontho lomalizira limatchedwa kuti mphete ya diamondi. * Kenako mlengalenga mwa dzuŵa munaoneka ngati changululu chofiirira, kenako dzuŵa lonse linabisikiratu ndipo kunachita mdima!”

Angola: “Anthu anali kupuma mwa befu ndiponso ankafuula pochita chidwi ndi zomwe zinachitika zooneka ngati mphete ya diamondi. Kenako, pa 1:48 masana, nthaŵi ya ku Angolako, dzuŵa linabisikiratu. Zimenezi zinawakhudza anthu m’njira zosiyanasiyana. Ena anali kalikiliki kutola zithunzi. Ena anayamba kufuula mothirirana mang’ombe, amvekere, ‘Labisikiratu! Labisikiratu! Labisikiratu!’ Komabe ena anayamba kuliza malikhweru ndi kufuula podabwa ndi kugwa kwa mdima masanasana. Cheza chotentha koopsa cha m’mlengalenga wa dzuŵa chinaoneka ngati chikufutukuka. Tinkatha kuona malaŵi m’mbali monse mwa mwezi, womwe unkaoneka wakuda. Mwadzidzidzi, ngati kuti wina wafulumizitsa nthaŵi, cheza cha dzuŵa chinayamba kuoneka mbali ina ya mthunziwo.

“Dzuŵa litayamba kuoneka, tinaona madontho a padzuŵa, omwe anabisika, akutulukira limodzi limodzi kuchokera mu mdima dzuŵa likubwerera m’chimake pang’ono ndi pang’ono.”

Zambia: “Kuno dzuŵa lonse linabisika kwa mphindi zitatu ndi masekondi 14, chotero panali nthaŵi yokwanira yoona bwinobwino zomwe zinali kuchitika. Kunali mdima, koma anthu akaponya maso kutali kwambiri ankatha kuona cheza. Ngakhale kuti thambo linali lobiriŵira, linkaonetsa mapulaneti omwe nthaŵi zambiri amabisika ndi dzuŵa, mwachitsanzo, mapulaneti a Jupiter ndi Saturn, ankaoneka bwinobwino. Mwina chochititsa chidwi kwambiri panthaŵi ya kadamsanayu chinali kuŵala kwa m’mlengalenga wa dzuŵa. Kunkaoneka ngati cheza chofiirira chitazungulira chimbale chakuda. Pochita kaso, oonerera ankati kuŵala kumeneko ‘n’kodabwitsa koopsa, n’kokongola kwabasi.’ Pang’ono ndi pang’ono mwezi unayamba kupita kumbali, dzuŵa n’kumayamba kuonekera ndipo kuŵala kwake kunayamba kufika pa dziko bwinobwino popanda chotchinga chilichonse. Pamene nthaŵi imakwana 4:28 masana, kadamsana anatha!”

Zimene Kadamsanayu Anaphunzitsa Anthu

Pambuyo pake, ambiri ananenapo za mmene kadamsanayo wawakhudzira mtima. Ku Angola mayi wina anati anatsala pang’ono kulira. Wina anaona kuti imeneyi ndi mphatso yokongola kwambiri yomwe Mulungu anapatsa anthu. Winanso anati Mlengi wachikondi yekha ndi yemwe angaonetse anthu zinthu zodabwitsa zoterozo n’cholinga choti anthu aone kukongola kochititsa kaso kwa dzuŵa.

Zinaonekeratu kuti anthu ambiri a ku Africa amalemekeza kwambiri Mlengi ndiponso Baibulo. Pamene Mboni za Yehova za mu mzinda wa Sumbe zimauza anthu ena za kadamsanayo ndi kuwafotokozera kuti kadamsana ndi ntchito imodzi chabe mwa ntchito zodabwitsa za Yehova, Mlengi wathu, anthu okhala mu mzindawo anasonyeza chidwi chenicheni choti akufuna kukambirana nawo za nkhaniyo. Ambiri analandira mwansangala magazini a Nsanja ya Olonda omwe anali atangofalitsidwa kumene ofotokoza ntchito zodabwitsa zimenezi.

Kadamsanayu anathandiza anthu ambiri kuiwala mavuto kwa kanthaŵi kochepa ndi kuika malingaliro awo pa chinthu chinachake cholimbikitsa ndiponso chochititsa kaso. Ataona zinthu zochititsa chidwi kwambiri zokhudza dzuŵa zomwe nthaŵi zambiri sizionekaoneka, ena anaganiza za zinthu zosaoneka koma makamaka za ulemelero wapamwamba wa Mlengi wake, Yehova.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Chifukwa chakuti mwezi ndi dziko zimadutsa m’njira zozungulira ngati dzira, kukula kwa dzuŵa ndi mwezi kumasinthako pang’ono malinga ndi malo omwe zili m’njira zawozo. Mwezi ukapita kutali kwambiri ndi dziko, chigawo cha mdima kwambiri cha mthunzi wake sichingafike padziko pano. Zikatere, m’madera omwe mwadutsa mthunziwo padziko lapansi pano mumachitika kadamsana yemwe dzuŵa limaphimbika pakati, ndipo limaoneka ngati mphete yonyezimira itazungulira chinthu chakuda.

^ ndime 19 Mkanda wa Baily umachitika chifukwa cha kuŵala kwa dzuŵa kukamadutsa m’zigwa za mwezi dzuŵalo lisanabisike lonse. Mawu akuti “mphete ya diamondi” amafotokoza mmene dzuŵa limaonekera likangotsala pang’ono kuti libisike lonse, pamene kachigawo kakang’ono ka dzuŵa kamakhala kakuwonekabe, zomwe zimaoneka ngati mphete yoyera yonyezimira, monga momwe mphete ya diamondi imaonekera.

[Chithunzi patsamba 28]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

→ →

Dzuŵa → Mwezi ⇨ Chigawo cha mdima ⇨ Dziko lapansi

→ →

[Mawu a Chithunzi]

© 1998 Visual Language

[Zithunzi patsamba 31]

Mkanda wa Baily

Dzuŵa lonse labisikiratu

Mphete ya diamondi

[Mawu a Chithunzi]

Mwachilolezo cha Juan Carlos Casado, www.skylook.net

[Chithunzi patsamba 31]

Oonerera kadamsana ku Lusaka, m’dziko la Zambia