Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mfundo Zodalirika Zokhudza Tsogolo Lathu

Mfundo Zodalirika Zokhudza Tsogolo Lathu

Mfundo Zodalirika Zokhudza Tsogolo Lathu

PAKUTI kukhulupirira manambala ndiponso njira zina zowombezera maula n’zosadalirika, kodi tingati palibenso njira iliyonse yodziŵira zam’tsogolo? Ayi sitingatero m’pang’ono pomwe!

Manambala paokha sangathe kuuza anthu za tsogolo lawo. Koma “Mulungu wamoyo” amene ‘alalikira za chimaliziro kuyambira pachiyambi,’ ndiye anatero kudzera m’Mawu ake olembedwa, omwe ndi Baibulo. (1 Timoteo 4:10; Yesaya 46:10) Mawu a Mulungu wamoyo ameneŵa, ndiwo ‘amazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima,’ osati mawu a anthu okhulupirira manambala. Komanso mawu ameneŵa angathe kukuthandizani kuti mudziŵe bwino zinthu zimene zingakulimbikitseni ndiponso kukupindulitsanidi.—Ahebri 4:12.

Mlengi wathu, amene analemba Baibulo, ndi yekhayo amene anganeneretu zoona za tsogolo lathu. Ichi n’chifukwa chakuti Mulungu ndi wamphamvu zosaneneka, ndipo nthaŵi zonse wakhala akukwaniritsa zimene amanena. Yehova anati chimene iye ‘wanena . . . adzachichitanso.’ (Yesaya 46:11) Yoswa atawatsogolera Aisrayeli poloŵa m’Dziko Lolonjezedwa ananena mosapeneka kuti: “Pa mawu okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwa padera mawu amodzi; onse anachitikira inu.”—Yoswa 21:45; 23:14.

M’Baibulo muli maulosi ambirimbiri amene adzakwaniritsidwabe m’tsogolo muno. Ena mwa maulosi amenewo amanena za nthaŵi imene dzikoli lidzakhale lopanda kuipa n’kusanduka paradaiso. (Salmo 37:10, 11; Miyambo 2:21, 22) Kodi inuyo mungakonde kudzakhala choncho m’tsogolo muno? Kodi mukukhulupirira kuti Mlengi ali ndi nzeru ndiponso mphamvu zoti angathe kukonza zinthu kuti zikhale bwino padziko pano? Ngati mukukhulupirira zimenezi, ndiye kuti mungakonde kuona bwinobwino zimene Baibulo limanena zokhudza tsogolo la dzikoli. *

Choncho gwiritsirani ntchito bwino nthaŵi yanu tsopano, osati poyesa kudziŵa za tsogolo lanu mwakutanthauzira manambala koma poyesetsa kulidziŵa bwino Baibulo ndi maulosi ake. Mboni za Yehova n’zokonzeka kukuthandizani kudziŵa bwino zam’tsogolo mwanu malingana ndi mmene amanenera Mawu a Mulungu, omwe ndi Baibulo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Onani mitu 1, 10 ndi 19 ya buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.