Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kholo Lopanda Linzake Koma Losasoŵa Wolithandiza

Kholo Lopanda Linzake Koma Losasoŵa Wolithandiza

Kholo Lopanda Linzake Koma Losasoŵa Wolithandiza

“Palibenso chinthu china chondikomera ine monga mayi choposa kuti ana anga akafika panyumba ali osangalala andiuze kuti amandikonda.”—ANATERO MAYI WINA WOPANDA MWAMUNA YEMWE ALI NDI ANA AŴIRI DZINA LAKE DORIS.

MAKOLO olera ana ali okha angalimbikitsidwe ndi mawu a m’Baibulo akuti: “Ana ndi madalitso ndiponso mphatso yochokera kwa AMBUYE.” (Salmo 127:3, Baibulo la Contemporary English Version) Si kuti Mulungu amawaona ana a m’banja lakholo limodzi kuti ndi osafunika kwenikweni. Mlengi wathu amasangalala kuona mabanja akholo limodzi akuyenda bwino. Baibulo limanena Mulungu kuti: “Agwiriziza mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye.” (Salmo 146:9) Makolo olera ana ali okha ayenera kukhulupirira kuti Mulungu amafuna kuwathandiza.

Mwana amafunika kuleredwa mwachikondi, ndiponso motetezeka kuti akule motakasuka, akhwime maganizo, ndiponso kuti akule mwauzimu. Kuphunzitsa mwana ndi ntchito ndiponso mwayi wapadera wa kholo lililonse wochokera kwa Mulungu.

Makolo ambiri olera ana ali okha aona kuti ayenera kupemphera mwakhama, kupitirizabe kugwiritsira ntchito mfundo za m’Baibulo, ndiponso kudalira kwambiri Yehova kuti banja liziyenda bwino. Zimenezi n’zogwirizana ndi malangizo opezeka pa Salmo 55:22 akuti: “Um’senze Yehova nkhaŵa zako, ndipo iye adzakugwiriziza.”

Nthaŵi zina agogo, akulu, ndiponso makolo anzeru mumpingo wachikristu angathe kuthandiza banja lakholo limodzi zinthu zikavuta. Inde, achibale ndiponso opemphera nawo angawathandize kwambiri makolo olera ana ali okha, koma udindo waukulu umene Mulungu anapereka uli m’manja mwa makolo a mwanayo. *

N’zosangalatsa kuti makolo ambiri olera ana ali okha akwanitsa bwinobwino kuthetsa mavuto apadera amene amakumana nawo n’kulera ana anzeru, amakhalidwe abwino, oopa Mulungu. Atolankhani a Galamukani! analankhula ndi makolo angapo otere. Zinthu zina zimene makolo onseŵa amachita ndi izi.

Kuyendetsa bwino zinthu pakhomo. Makolo olera ana ali okha amene amayendetsa bwino banja lawo amayesetsa kuchita zinthu mwadongosolo ndiponso mwandondomeko yake. Kukonzekera ndi kulinganiza bwino zinthu n’kofunika. Baibulo limati: “Zoganizira za wakhama zichulukitsadi katundu.”—Miyambo 21:5.

Kudzipereka. Makolo olera ana ali okha amene amayendetsa bwino banja lawo amaona kuti banja ndi chinthu chofunika kwambiri. Amalimbikira kuthandiza ana awo m’malo mongodzithandiza okha.—1 Timoteo 5:8.

Kuchita zinthu mosapupuluma. Makolo olera ana ali okha amene amayendetsa bwino banja lawo sachepetsa kapena kukokomeza mavuto; iwo amafunafuna njira zothetsera mavutowo. Iwo amavomereza kuti zovuta zawagwera basi, ndipo amayesetsa kulimbana nazo popanda kudzimvera chisoni kwambiri kapena kuipidwa.

Kulankhulana bwinobwino. Makolo olera ana ali okha amene amayendetsa bwino banja lawo amalimbikitsa ana kuti asamaope kulankhula nawo momasuka. Amalimbikitsa kuti m’banjamo azilankhulana momasuka ndiponso kuti aliyense azitulutsa maganizo ake. Ponena za ana ake, bambo wina yemwe akulera anawo ali yekha anati: “Ndimalankhula nawo nthaŵi ina iliyonse. Timachezetsana kwambiri tikamaphika chakudya chamadzulo. Ndipo nthaŵi imeneyi ndi imene amandiuzadi zakukhosi kwawo.”

Kudzisamalira. Ngakhale kuti amakhala n’zochita zambiri, makolo olera ana ali okha amene amayendetsa bwino banja lawo amazindikira kuti n’kofunika kusamalira zofuna zawo zauzimu, zam’maganizo, ndiponso zam’moyo wawo. Mayi wina wa ana aŵiri yemwe ali yekha dzina lake Ethel anafotokoza kuti: “Ndimayesetsa kukhala ndi nthaŵi ya phee ndekhandekha. Mwachitsanzo, mnzanga wina akamaphunzitsa ana angawo kuimba nyimbo, ndimakhala ndekha kwa ola lathunthu, ndipo ndimangokhala pansi osayatsa TV.”

Kusadandaula ndi zina zilizonse. Makolo olera ana ali okha amene amayendetsa bwino banja lawo sadandaula chifukwa chokhala ndi ana kapena kudandaula ndi zina zochitika m’moyo. Akakhala pamavuto amaona kuti mavutowo awaphunzitsapo kanthu kena. Mayi wina wolera ana ali yekha anati: “Tsopano ndazindikira kuti kukhala kholo lolera ana uli wekha kuli ndi ubwino wake.”

Nkhani za Anthu Amene Mabanja Awo Anayenda Bwino

Kodi mfundo zimenezi n’zothandiza? Nkhani zambirimbiri za makolo olera ana ali okha amene zinthu zinawayendera bwino zikusonyeza kuti mfundozi n’zothandizadi. Mayi amene tinam’tchula m’nkhani yoyamba uja wotchedwa Gloria, yemwe ukwati wake unatha ndipo amagwira ntchito ku England, analera yekha ana ake aamuna aŵiri ndi wamkazi mmodzi. Ana atatu onseŵa anakula n’kukhala atumiki a nthaŵi zonse achikristu, odzipereka kupititsa patsogolo ntchito yophunzitsa anthu Baibulo. Mayiyu atafunsidwa kuti anakwanitsa bwanji kulera bwino anawo, iye anafotokoza kuti: “Choyamba ndinkalimbikira kuchititsa phunziro la Baibulo losangalatsa ndi banja langa. Ndinkafuna kuti anawo azisangalala, asamakhale ndi maganizo ambirimbiri, azikhala okhutira, ndiponso kuti akhale otetezeka kuzinthu zoopsa. Ndinapeza ntchito yogwira usiku. Cholinga changa chinali chakuti ndizikhala ndi ana angawo nthaŵi ina iliyonse yomwe ndili ndi mpata wotero. Ndisanapite kuntchito, tinkapemphera kaye kenaka n’kuwasiya kuti akagone. Amayi anga aang’ono ankatsala m’nyumba momwemo ineyo ndikapita kuntchito.”

Kodi mayiyu anathandiza bwanji ana akewo kuti alinganize zinthu moyenera? Iye akupitiriza kunena kuti: “Cholinga changa chachikulu chinali chakuti tizikonda zinthu zauzimu kuposa china chilichonse. Tinalibe ndalama zambiri, ndipo sindinkawabisira zonsezi anaŵa. Zimene ndinkawauza kuti azichita, inenso ndinkachita zomwezo ndipo onse ankandimvera.” Pokumbukira chimene chinachititsa kuti banja lake lizikhala logwirizana kwambiri, mayiyu anati: “Chinsinsi chake chinali kuchitira zinthu pamodzi. Palibe aliyense amene ankangochoka n’kukabindikira m’chipinda chake. Tinkaphika, kuyeretsa, kukongoletsa zina ndi zina tili limodzi. Chilichonse chimene tinkachita tinkachipatsa nthaŵi yake. Ndinkaonetsetsa kuti tilinso ndi nthaŵi yochita zinthu zongosangulutsa moyo.”

Mayi wina wotchedwa Carolyn, yemwe akulera yekha mwana wake wamwamuna dzina lake Joseph, amakondwera ndi mmene mwanayo akukulira. Kodi mayiyu amachita zotani kuti mwanayu azikula bwino chonchi? Iye anati: “Timaŵerengera pamodzi Baibulo tikamakagona, ndipo kenaka ndimam’funsa mafunso okhudza zinthu zimene waphunzira. Komanso timaŵerenga ndime zina zimene tasankha m’mabuku ofotokoza za m’Baibulo n’kuona mmene zikutikhudzira. Zimenezi zimam’thandiza Joseph akakumana ndi mavuto, monga kuzunzidwa ndi ana ovutitsa anzawo kusukulu.” Mayiyu amavomereza kuti moyo amaumva kuŵaŵa ndithu, koma amaona kuti sali yekha ayi. Iye anati: “Ndi vuto lalikulu kwambiri, koma ndimaona kuti Yehova ali nane. Komanso anthu a kumpingo wathu wachikristu amandilimbikitsa kwambiri.”

Nkhani za makolo ambirimbiri monga Gloria ndi Carolyn, amene akulera bwinobwino ana ali okha zikutsimikiziradi kuti masiku ano makolo angadalire malangizo akalekale a m’Baibulo olerera ana kuti akhale abwino, olimba mwauzimu. (Miyambo 22:6) Ndithu, mabanja otere angayende bwinobwino! Makolo olera ana ali okha amakhala ndi mavuto ambirimbiri amene amachititsa kuti anthuwo akhwime maganizo ndiponso kuti azithandizana. Njira yabwino kwambiri yoti munthu athe kulimbana ndi chintchito cholera ana payekha, ndiyo kudalira Mulungu kwambiri ndiponso kusakayikira kuti iye angam’thandize.—Salmo 121:1-3.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Kuti mudziŵe zinanso zokhudza mmene mabanja akholo limodzi angayendere bwino, onani buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja, mutu 9, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Zithunzi patsamba 11]

Phunziro la Baibulo la banja lathandiza ana atatu a Gloria kuti akhale atumiki a nthaŵi zonse. Apa akuŵerenga kalata ndiponso akuyang’ana chithunzi cha mwana wawo wamkulu, yemwe tsopano ndi mmishonale

[Zithunzi patsamba 12]

Carolyn ndi mwana wake wotchedwa Joseph