Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Zinthu Zakale Zofukulidwa Pansi N’zofunikadi Kuti Tikhale ndi Chikhulupiriro?

Kodi Zinthu Zakale Zofukulidwa Pansi N’zofunikadi Kuti Tikhale ndi Chikhulupiriro?

Lingaliro la Baibulo

Kodi Zinthu Zakale Zofukulidwa Pansi N’zofunikadi Kuti Tikhale ndi Chikhulupiriro?

M’chaka cha 1873, ponena za mzinda wa Yerusalemu mbusa wa ku England dzina lake Samuel Manning analemba kuti: “Apaulendo wa zachipembedzo ochokera padziko lonse atachita chidwi kwambiri ndi mzindawo anangoti ndondondo kuloŵera komweko. Anthu ambirimbiri anatengeka mtima kwabasi ndi zipupa zogumukagumuka, misewu ya zinyalala zongoti mbwee komanso mabwinja opasukiratu, ngati kuti palibenso malo ena aliwonse ochititsa chidwi padzikoli.”

ANTHU akhala akutengeka mtima ndi Mzinda Woyera chiyambireni pafupifupi nthaŵi imene Mfumu Constantine inkalamulira Roma. * Zaka 1,500 zinatha, apaulendo wa zachipembedzo akumafikako n’kubwererako pofuna kukapembedza, komanso kuti akadzionere okha Mzinda Woyerawo. Koma kudabwitsa kwake n’kwakuti nthaŵi yonseyi akatswiri amaphunziro sankapita nawo anthu apaulendo wa zachipembedzoŵa mpaka cha kumayambiriro kwa m’ma 1800. Ndipo atatero anayambitsa kufufuza zinthu zofukulidwa za m’nthaŵi ya Baibulo.

Zimene akatswiri ofufuza zinthu zofukulidwa pansi anapeza zachititsa kuti anthu ayambe kumvetsa zinthu zambiri za m’nthaŵi ya Baibulo. Komanso nthaŵi zambiri zinthu zimenezi zakhala zikugwirizana ndi mbiri ya m’Baibulo. Koma kodi kudziŵa zimenezi n’kofunika kuti Mkristu akhale ndi chikhulupiriro? Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tikambirane mwatsatanetsatane za mzinda wa Yerusalemu ndiponso kachisi wake, komwe kunafukulidwa zinthu zambiri zakale.

‘Sudzasiyidwa Mwala Umodzi Pamwamba pa Unzake’

Tsiku la Nisani 11 pa kalendala ya Chiyuda, m’ngululu ya 33 C.E., Yesu Kristu pamodzi ndi ophunzira ake ena anachoka pakachisipo m’Yerusalemu kwa nthaŵi yake yomaliza. Pamene ankapita ku phiri la Azitona, wophunzira wake wina anati: ‘Mphunzitsi, onani, miyala yotere ndi nyumba zotere.’—Marko 13:1.

Ayuda okhulupirika ameneŵa ankakonda kwambiri Mulungu pamodzi ndi kachisi wake. Ankazinyadira kwambiri nyumba zochititsa kaso zimenezi zimene mtundu wawo unakhala nazo kwa zaka 1,500. Zimene Yesu anam’yankha wophunzira wakeyu zinali zodabwitsa kwambiri. Iye anati: “Kodi waona nyumba izi zazikulu? Sudzasiyidwa pano mwala umodzi pamwamba pa unzake, umene sudzagwetsedwa.”—Marko 13:2.

Popeza kuti Mesiya yemwe Mulungu analonjeza kuti adzafika anali atafika, nanga Mulunguyo akanalola bwanji kuti kachisi wakeyo awonongedwe? Mzimu woyera utawathandiza, m’pamene ophunzira a Yesu anadzayamba pang’ono ndi pang’ono kuzindikira bwinobwino zimene iye ankanena. Nanga kodi mawu a Yesuwo akugwirizana pati ndi zinthu zofukulidwa pansi za m’nthaŵi ya Baibulo?

Mzinda “Watsopano”

Pa tsiku la Pentekosite m’chaka cha 33 C.E., Mulungu anasiya kuuyanja mwapadera mtundu wa Ayuda. (Mateyu 21:43) Izi zinapangitsa kuti atsegulire njira boma limene lidzabweretsere anthu onse madalitso, losati n’kuliyerekezera ndi mtunduwu. (Mateyu 10:7) Mongadi mmene Yesu analoserera, Yerusalemu ndi kachisi wake anawonongedwa m’chaka cha 70 C.E. Akatswiri ofufuza zinthu zofukulidwa pansi amaikira umboni zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi. Komabe si kuti Akristu amakhulupirira zimenezi chifukwa chakuti zidutswa zogumuka za kachisi wakaleyo zinapezekadi. Chikhulupiriro chawo chili pa Yerusalemu wina amene sali ngati Yerusalemu woyambayu.

M’chaka cha 96 C.E., mtumwi Yohane yemwe anali atamva ulosi wa Yesu wokhudza za kuwonongedwa kwa Yerusalemu ndi kachisi wake ndipo analipobe pamene ulosiwu unkakwaniritsidwa, anaonetsedwa masomphenya aŵa: “Ndinaona mzinda woyerawo, Yerusalemu watsopano, uli kutsika kumwamba kwa Mulungu.” Mawu ochokera kumpando wachifumu anati: “Adzakhalitsa nawo [anthu onse] ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa.”—Chivumbulutso 21:2-4.

“Mzinda” umenewu ndiwo Akristu okhulupirika amene adzakhala mafumu kumwamba pamodzi ndi Kristu. Iwo onse pamodzi adzapanga boma lakumwamba, kapena kuti Ufumu wa Mulungu umene udzalamulira padziko lonse, n’kuwasandutsa anthu a mitundu yonse kukhalanso angwiro panyengo ya zaka 1,000. (Mateyu 6:10; 2 Petro 3:13) Akristu achiyuda a m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino omwe anali m’gulu limenelo anazindikira kuti panalibe chinthu chomwe anali nacho m’dziko la Ayuda limenelo chomwe chikanafanana ndi mwayi wolamulira pamodzi ndi Kristu kumwamba.

Pankhani ya zinthu zonse zomwe zinam’tchukitsa m’Chiyuda mtumwi Paulo analemba kuti: “Zonse zimene zinandipindulira, zomwezo ndinaziyesa chitayiko chifukwa cha Kristu. Komatu zenizeninso ndiyesa zonse zikhale chitayiko chifukwa cha mapambanidwe a chizindikiritso cha Kristu Yesu Ambuye wanga.”—Afilipi 3:7, 8.

Popeza kuti mtumwi Paulo ankaopa kwambiri Malamulo a Mulungu ndi zonse zochitika pa kachisi, ndiye kuti apa mawu ake sakunena kuti makonzedwe a Mulungu ameneŵa anali onyozeka ayi. * (Machitidwe 21:20-24) Paulo ankangosonyeza kuti Chikristu chinali choposa Chiyuda.

Si zokayikitsa kuti Paulo pamodzi ndi Akristu ena Achiyuda a m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino ankadziŵa kwambiri zinthu zambiri zochititsa chidwi zokhudza dziko lachiyuda. Ndipo popeza kuti kufufuza zinthu zofukulidwa pansi kumathandiza kudziŵa zakale, Akristu tsopano akhoza kumvetsa zina mwa zinthu zimenezo. Komabe taonani zimene Paulo anauza Timoteo adakali mnyamata kuti azizisamalira kwambiri pamene anati: ‘Izi [zokhudzana ndi mpingo wachikristu] uzisamalitse; mu izi ukhale; kuti kukula kwako kuonekere kwa onse.’—1 Timoteo 4:15.

Kunenadi zoona, zinthu zofukulidwa pansi za m’nthawi ya Baibulo zatithandiza kwambiri kumvetsa zina n’zina zokhudza Baibulo. Komabe Akristu amazindikira kuti chikhulupiriro chawo si chodalira umboni wa zinthu zimene anthu afukula pansi ayi, koma n’chodalira Mawu a Mulungu, omwe ali Baibulo.—1 Atesalonika 2:13; 2 Timoteo 3:16, 17.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Constantine pamodzi ndi mayi ake a Helena ankafunitsitsa kudziŵa malo opatulika a ku Yerusalemu ndipo mayi akewo anapitako. Kungoyambira pamenepo anthu enanso ambiri anali kuchitabe chimodzimodzi kwa zaka zambirimbiri.

^ ndime 15 Kwa nthaŵi yaitali ndithu, Akristu a Chiyuda a m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino omwe anali ku Yerusalemu ankasunga mbali zosiyanasiyana za Chilamulo cha Mose, mwina chifukwa chakuti: Chilamulocho chinali chochokera kwa Yehova. (Aroma 7:12, 14) Chinali chitawaloŵerera kwambiri anthu a Chiyuda n’kungosanduka mwambo wawo. (Machitidwe 21:20) Chinali lamulo lokhazikitsidwa ndi boma, ndipo aliyense wotsutsa chilamulocho akanangochititsa kuti uthenga wachikristu utsutsidwe.

[Zithunzi patsamba 16]

Pamwambapa: Yerusalemu m’chaka cha 1920; Ndalama imene Ayuda ankagwiritsira ntchito m’chaka cha 43 C.E.; chiboliboli chamnyanga cha chipatso cha khangaza, n’kutheka kuti chinali pa kachisi wa Solomo, mu 700 B.C.E.

[Mawu a Chithunzi]

Pa masamba 2 ndi 18: Ndalama: Photograph © Israel Museum, Jerusalem; mwachilolezo cha Israel Antiquities Authority; khangaza: Mwachilolezo cha Israel Museum, Jerusalem