Kufunafuna Njira Zothetsera Vutoli
Kufunafuna Njira Zothetsera Vutoli
KUYAMBIRA mu 1972 mayiko opitirira 100 anasaina mgwirizano woletsa, kukonza, ndi kusunga zida zofalitsa tizilombo topereka matenda. Mgwirizano umenewu umene anautcha kuti Biological and Toxin Weapons Convention (BTWC), unali woyamba kuletseratu zida zonse za m’gulu linalake. Koma vuto lake linali lakuti sunatchule njira zodziŵira ngati mayiko analidi kutsatira zimene anagwirizanazo.
M’povuta kutsimikizira kuti mayiko sakupangadi zida zotere, chifukwa njira zopangira zinthu zabwinobwino angathenso kuzigwiritsira ntchito popangira zida zofalitsa matenda. Pakuti sayansi yogwiritsira ntchito tizilombo ingathe kugwiritsidwa ntchito m’njira ziŵiri zimenezi, n’zosavuta kubisa ntchito yokonza zida zimenezi kumafakitale ndi kumalo opangirako mankhwala komwe amakhala ngati akuchitako zinthu zosakhudzana ndi zankhondo.
Pofuna kupeza njira yabwino yotsimikizira kuti mayikoŵa sakupanga zida zotere, mu 1995 nthumwi zochokera m’mayiko osiyanasiyana zinayamba kukambirana zogwirizana chimodzi pankhaniyi. Kwa zaka zoposa zisanu n’chimodzi, akhala akukambirana za njira zenizeni zimene angatsatire kuti atsimikize kuti mayiko onse akutsatiradi mfundo za mumgwirizano wa BTWC. Pa December 7, 2001, msonkhano wa milungu itatu wa mayiko 144 a mumgwirizano wa 1972 uja, unatha popanda kugwirizana chimodzi. Vuto linali lakuti dziko la United States silinagwirizane nazo mfundo zikuluzikulu zimene zinaperekedwa kuti zithandize potsimikizira kuti mayiko onse akutsatira mfundo za mumgwirizano wa BTWC. Dzikoli linati silingalole kuti anthu akunja azidzayendera malikulu awo a zankhondo ndiponso zamafakitale, chifukwa ndiye kuti akazitape angathe kupezerapo mwayi wodziŵira zinsinsi za dzikoli.
Nanga M’tsogolo Muno Muli Zotani?
Sayansi yogwiritsira ntchito tizilombo njothandiza kwambiri komanso njoopsa. Mitundu ina ya sayansi monga sayansi yopanga zitsulo, mabomba, mainjini oyendera mafuta, ndege, zamagetsi, amaigwiritsa ntchito pa zamtendere komanso pa zankhondo. Kodi ndi mmenenso zinthu zikhalire ndi sayansi yogwiritsa ntchito tizilombo? Anthu ambiri amaona kuti ndi mmene zikhalire.
Lipoti la m’chaka cha 1999 la bungwe la ku United States la Commission on National Security linati: “Anthu paokha komanso magulu osiyanasiyana . . . adzakhala ndi mphamvu m’tsogolo muno, ndipo ambiri adzapeza njira zoopsa zotha kuwonongera nazo ena. . . . Padzabuka timabungwe ndiponso anthu ambirimbiri olimbana ndi nkhani zinazake zazing’ono mosaganizira zam’tsogolo, makamaka chifukwa cha khama lawo pa zachipembedzo, zikhulupiriro zawo zina zokaikitsa, kapena chifukwa cha kuikirana mpeni kumphasa. Masiku ano zigaŵenga zingathe kugwiritsira ntchito umisiri umene poyamba unkangodziŵidwa ndi mayiko akuluakulu okha basi ndipo motero zigaŵengazi zingaukire anthu ambiri okhala m’madera enaake.”
Ngakhale kuti sitikudziŵa zimene zichitike m’tsogolo muno, tikudziŵa zimene Mulungu akufuna kudzachitira anthu. Baibulo limalonjeza kuti idzafika nthaŵi imene anthu padziko lapansi “adzakhala osatekeseka, opanda wina wakuwawopsa.” (Ezekieli 34:28) Kuti mudziŵe bwino tsatanetsatane wa lonjezo lolimbikitsa limeneli, pezani Mboni za Yehova kwanuko kapena lembani kalata n’kuitumiza ku adiresi yogwirizana n’kumene mukukhala pa maadiresi amene ali patsamba 5 la magazini ino.
[Chithunzi patsamba 30]
Ofufuza akukonza njira zogonjetsera anthrax
[Mawu a Chithunzi]
Mwachilolezo cha Sandia National Laboratories
[Chithunzi patsamba 30]
Msonkhano wokambirana za zida za tizilombo topereka matenda, pa November 19, 2001, ku Switzerland
[Mawu a Chithunzi]
Ap Photo/Donald Stampfli
[Zithunzi patsamba 31]
Baibulo limalonjeza kuti kudzakhala nthaŵi imene aliyense “adzakhala osatekeseka”