Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Amanyalanyaza Zofooka Zathu?

Kodi Mulungu Amanyalanyaza Zofooka Zathu?

Lingaliro la Baibulo

Kodi Mulungu Amanyalanyaza Zofooka Zathu?

‘Ine si munthu woipa ayi! Ndayesetsa kuti ndisiye khalidwe langa loipali, kungoti munthune ndili n’zofooka zikuluzikulu!’

KODI mawu ameneŵa akugwirizana ndi mmene inuyo kapena munthu wina amene mumam’dziŵa amaganizira? Anthu ambiri amaona kuti n’zovuta kwambiri kuti munthu athetse makhalidwe enaake oipa amene anam’loŵerera kwambiri. Anthu ena zinthu monga moŵa, fodya ndiponso mankhwala osokoneza bongo zinaŵaloŵerera kwabasi. Anthu ena ambiri ngaumbombo maka. Ndiye pali enanso osaugwira mtima omwe amanena kuti pankhani ya chimasomaso yokha sangathe kuchitira mwina ayi.

Lemba la Mateyu 26:41 limasonyeza kuti Yesu amamvetsa zofooka za anthufe. * Ndipo Baibulo lonse limatsimikizira ndithu kuti Yehova Mulungu ndi Yesu, amatichitira chifundo kwambiri anthufe. (Salmo 103:8, 9) Koma kodi tiyenera kuganiza kuti Mulungu amanyalanyaza zophophonya zathu zonse?

Mose ndi Davide

Taganizirani nkhani ya Mose. Iye ankadziŵika kuti anali munthu “wofatsa woposa anthu onse a padziko lapansi,” ndipotu anayesetsa kuti mtima umenewu asausiye. (Numeri 12:3) Aisrayeli akuyenda m’chipululu, nthaŵi zambiri ankachita zinthu zoduka mutu komanso zosalemekeza Mulungu ndiponso anthu amene ankamuimira. Mose anadutsa monsemu n’kumangomvera Mulungu modzichepetsa.—Numeri 16:12-14, 28-30.

Komano chakumapeto kwenikweni kwa ulendo wautali wotopetsa umenewu m’pamene Mose analephera kuugwira mtima pamaso pa mtundu wonsewo ndipo anachita zinthu zosamvera malangizo a Mulungu. Inde Mulungu anam’khululukira, koma kodi zimene zinachitikazo anangozinyalanyaza? Ayi ndithu. Mulungu anauza Mose kuti: “Popeza simunandikhulupirira ine . . . , simudzaloŵetsa msonkhano uwu m’dziko ndinawapatsali.” Mose sanaloŵe m’Dziko Lolonjezedwa. Atapupulika kwa zaka 40 kuti apeze chimwayi chimenechi, chofooka chachikulu kwambiri chaumunthu chinam’lepheretsa kutero.—Numeri 20:7-12.

Munthu wina woopa Mulungu amene anali ndi chofooka ndi Mfumu Davide. Panthaŵi ina iye analephera kuugwira mtima n’kugonana ndi mkazi wa mwini. Ndipo kenaka anayesa kubisa mlanduwu popha mwamuna wake. (2 Samueli 11:2-27) Pambuyo pake iye ananong’oneza bondo chifukwa cha milandu imene anachitayi ndipo Mulungu anam’khululukira. Komatu Davide anapasula banja la mwini, motero Yehova sanam’tetezere ku masoka oopsa amene anadzakumana nawo chifukwa cha zimenezi. Kamwana ka Davide kanadwala kwambiri, ndipo Yehova ankangoyang’ana basi, ngakhale kuti Davide anayesetsa kupemphera kuti kamwanako kachire. Kenaka kamwanako kanafa, ndipo zitatero m’banja la Davide munagwa mavuto ambiri. (2 Samueli 12:13-18; 18:33) Chifukwa cholekerera chofooka chake, Davide anachimina.

Zitsanzo zimenezi zikusonyeza kuti Mulungu amaimba anthu mlandu pa zochita zawo. Anthu amene amafuna kumutumikira ayenera kulimbikira kuthetsa zofooka zawo zauzimu n’kukhala Akristu abwino. Izi n’zimene anthu ambiri anachita m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino.

Kulimbana Nawo Machimo

Panopa anthu amaona kuti mtumwi Paulo ndi chitsanzo chabwino cha mmene Akristu ayenera kukhalira, ndipotu amalondola poganiza choncho. Koma kodi mukudziŵa kuti nthaŵi zonse ankakhalira kulimbana nazo zofooka zake? Lemba la Aroma 7:18-25 limafotokoza mwatsatanetsatane vuto kapena kuti ‘kulimbana’ kumeneku malingana ndi mmene vesi 23 limanenera. Paulo analimba nazo, chifukwa chakuti ankadziŵa kuti tchimo ndi chinthu chankhakamira.—1 Akorinto 9:26, 27.

Anthu ena a mumpingo wachikristu ku Korinto wakale poyamba anali n’zizoloŵezi zoipa. Baibulo limati anali ‘adama, achigololo, akudziipsa ndi amuna, ambala, osirira ndiponso oledzera.’ Koma limanenanso kuti ‘anasambitsidwa.’ (1 Akorinto 6:9-11) Kodi anasambitsidwa bwanji? Analimbikitsidwa kuti asiye makhalidwe awo oipa pophunzira choonadi bwinobwino, pochezerana ndi anzawo achikristu, ndiponso pokhala ndi mzimu wa Mulungu. Mpaka anafika poti Mulungu wayamba kuwaona monga anthu olungama kudzera m’dzina la Kristu. Inde, Mulungu anawakhululukira, motero anawapatsa chikumbumtima choyera.—Machitidwe 2:38; 3:19.

Paulo ndi Akristu a ku Korinto sanazione zizoloŵezi zawo zauchimozo ngati zazing’ono. Koma analimbana nazo, ndipo Mulungu anawathandiza kuzigonjetsa. Anthu akale olambira Mulunguŵa anali ndi makhalidwe okoma ngakhale kuti anali pakati pa anthu oipa ndiponso kuti iwowo anali ndi zofooka. Nanga ifeyo bwanji?

Mulungu Amafuna Kuti Tizilimbana Nazo Zofooka Zathu

Sikuti tikamalimbana ndi choofoka chinachake ndiye kuti tingadzachigonjetseretu ayi. Inde sitiyenera kugonja koma sikuti tingathe kuthetseratu kupanda ungwiro. Kupanda ungwiro kumabweretsa zofooka zosatherapo. Komabe sitiyenera kugonjera zofooka zathu. (Salmo 119:11) Kodi n’chifukwa chiyani n’kofunika kwambiri kutero?

Chifukwa chakuti Mulungu samalola kuti kupanda ungwiro kukhale chodzikhululukira pochita zinthu zoipa. (Yuda 4) Yehova amafuna kuti anthu adziyeretse n’kuyamba khalidwe labwino. Baibulo limati: “Dana nacho choipa.” (Aroma 12:9) Kodi n’chifukwa chiyani Mulungu amalimbikira kwambiri pa mfundo imeneyi?

Chifukwa choyamba n’chakuti kugonjera chofooka n’kopweteketsa. Pa Agalatiya 6:7 Baibulo limati, “chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.” Anthu amene amalekerera zizoloŵezi zinazake zoipa, umbombo, ndiponso chimasomaso nthaŵi zambiri moyo wawo amadzaumva kuwawa kwabasi. Koma pali chifukwa china chachikulu.

Tchimo limamuipira Mulungu. ‘Limatilekanitsa’ ndi Yehova. (Yesaya 59:2) Pakuti anthu ochita uchimo sangayanjidwe ndi Mulungu, iye amawalimbikitsa kuti: “Sambani, dziyeretseni; . . . lekani kuchita zoipa.”—Yesaya 1:16

Mlengi wathu ngwachikondi ndiponso ngwachifundo. “Wosafuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.” (2 Petro 3:9) Kugonjera nthaŵi zonse zofooka zathu kumatilepheretsa kuyanjana ndi Mulungu. Pakuti Mulungu samanyalanyaza zofooka zathu, nafenso tichite zomwezo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Palembali Yesu anati: “Mzimutu uli wakufuna, koma thupi lili lolefuka.”