Kodi Ndani Adzabweretse Mtendere Wosatha?
Kodi Ndani Adzabweretse Mtendere Wosatha?
KODI n’chifukwa chiyani Mulungu sanayankhe mapemphero a akuluakulu a zipembedzo zosiyanasiyana opempherera mtendere? Baibulo limayankha funsoli mochititsa chidwi. Si kuti Mulungu safuna kuti kukhale mtendere. Amafunitsitsa zitatero kuposa mmene amachitira akuluakulu a zipembedzo omwe amapempherera za nkhaniyi. Ndipotu, Mulungu anakonza kale zobweretsa mtendere padziko lonse. Iye anayamba kale kuchita zinthu zoti zimenezo zitheke basi. Mosabisa mawu, iye anawauza anthu onse zimene akufuna kuchita. Koma n’zomvetsa chisoni kuti akuluakulu a zipembedzo amanyozera kwambiri zimene Mulungu ananena.
Mulungu analonjeza kalekale kuti adzabweretsa “mbewu,” kapena kuti wolamulira. Baibulo limayamba kumufotokoza mwapang’onopang’ono mpaka limafika polongosola zinan’zina zothandiza kuti anthu adzam’dziŵe. (Genesis 3:15; 22:18; 49:10) Mneneri Yesaya, yemwe amadziŵika ndi maulosi ake odabwitsa okhudza Mesiya, analemba kuti Mtsogoleri wonenedweratu ameneyu adzakhala “Kalonga wa mtendere” padziko lonse ndiponso kuti iyeyu akamadzalamulira, “za mtendere sizidzatha.” (Yesaya 9:6, 7) Monga Wolamulira wakumwamba, iye adzathandiza nawo kuthetsa kuipa konse ndiponso kusandutsa dziko lapansili kuti likhale paradaiso, ndipo sikudzakhalanso kupanda chilungamo, matenda, umphaŵi, kapena imfa. Padzakhala mtendere ndiponso moyo wamuyaya. (Salmo 72:3, 7, 16; Yesaya 33:24; 35:5, 6; Danieli 2:44; Chivumbulutso 21:4) Kodi zimenezi zidzachitika liti?
Posachedwapa Padziko Lonse Pakhala Mtendere
Yesu anauza ophunzira ake kuti mapeto dziko loipali ndiponso chiyambi cha dziko latsopano chisanafike, choyamba padzachitika zinthu zingapo zogwedeza dzikoli zomwe zidzachitikire m’nyengo imodzi. (Mateyu 24:3, 7-13) Zambiri mwa zinthuzi, monga nkhondo, njala, zivomezi, kungotchulapo zochepa chabe, zakhala zikuchitika kambirimbiri m’nyengo zonse. Komabe sizinasautsepo anthu onse panthaŵi imodzimodzi ndiponso padziko lonse monga zachitira m’nyengo yathu ino. Ndipo mavuto amene amakhalapo chifukwa cha masoka otereŵa ngoopsa kwambiri kuposa kale chifukwa chakuti anthu achuluka kwambiri padzikoli.
Chinanso chimene Baibulo linalosera ndicho Chivumbulutso 11:18) Komanso china n’chakuti mapeto amene ananenedweratu asanafike, ntchito ya padziko lonse yochenjeza iyenera ithe, ndipo ntchitoyi ndi yolalikira ‘uthenga wabwino wa Ufumu.’ Panopa Mboni za Yehova zikuchita ntchito imeneyo padziko lonse.—Mateyu 24:14.
kuwononga malo komwe anthu akungokuchitabe. (Kukwaniritsidwa kwa maulosi amenewo ndi uthenga wabwino kwa anthu okhulupirika. Dziko lamtendere weniweni limene analonjeza lili pafupi kwambiri! M’dziko limenelo simudzakhalanso chidani ndiponso zauchigaŵenga. Baibulo limafotokoza kuti: “Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.”—Yesaya 11:9.
Mapemphero Amene Mulungu Amawamva
Si kuti kupemphera kwa Mulungu n’kungotaya nthaŵi pachabe kapena kungodzivutitsa. M’Baibulo, Yehova amatchedwa kuti “Wakumva pemphero.” (Salmo 65:2) Choncho, nthaŵi ina iliyonse iye amakhala akumvera mapemphero osaŵerengeka amene anthu okhulupirika padziko lonse amapemphera. Komabe kodi pali zinthu zinazake zofunika zimene ziyenera kuchitidwa kuti mapemphero amvedwe? Baibulo limasonyeza kuti anthu oona mtima amene amaphunzira zinthu zoonadi za m’Baibulo zokhudza Mulungu ayenera kutsatira zimene aphunzirazo, n’kukhala “olambira oona,” omulambira “mumzimu ndi m’choonadi.” (Yohane 4:23) Mapemphero a anthu amene samvera zofuna zake sawayankha: “Wopewetsa khutu lake kuti asamve chilamulo [cha Mulungu], ngakhale pemphero lake linyansa.”—Miyambo 28:9.
N’zomvetsa chisoni kuti masiku ano akuluakulu ambiri a zipembedzo saphunzitsa kapena kupempherera zimene Mulungu amafuna zakuti abweretse mtendere. Koma iwo amapempherera maboma a anthu kuti athetse mavuto otereŵa pamene Mawu a Mulungu amanena mosapsatira mawu kuti “sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.”—Yeremiya 10:23.
Ulosi unanena kalekale kuti ‘m’masiku otsiriza,’ imene ili nthaŵi yathu ino, anthu okonda mtendere adzakhamukira ku “phiri [lophiphiritsira] la nyumba ya Yehova” ndipo izi zikutanthauza kulambira koona. Anthu ameneŵa amasintha zochita zawo zambiri: “Iwo adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.”—Yesaya 2:2-4.
Kodi lilipo gulu la anthu opembedza masiku ano lomwe likuyesetsa kutsatira mawu amenewo? Kapena kodi zipembedzo zonse zikungolankhula nkhani ya mtendere ndi pakamwa pokha pamene zikulimbikitsa nkhondo? Mukakumana ndi Mboni za Yehova, tikukulimbikitsani kuti mukambe nawo za nkhani ya mtendere kuti mudziŵe chipembedzo chimene chimaphunzitsa anthu kukhala pamtendere ndi wina aliyense.