Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndikufunika Telefoni ya M’manja?

Kodi Ndikufunika Telefoni ya M’manja?

Achinyamata Akufunsa Kuti . . .

Kodi Ndikufunika Telefoni ya M’manja?

“Ndikayenda opanda telefoni ya m’manja ndimaona ngati ndikusoŵa kanthu kenakake ndipo sindimva bwino.”—Anatero Akiko. *

M’MAYIKO ambiri matelefoni a m’manja ayamba kufala kwabasi. Amathandiza m’njira zambiri. Anzanu ndiponso makolo anu angalankhule nanu nthaŵi ina iliyonse, kulikonse, komanso inu mungalankhule nawo. Pali mitundu ina ya matelefoni ameneŵa imene mungalemberanepo mauthenga achidule ndi anthu ena, ndipo imeneyi ndi “njira yatsopano yomwe achinyamata akugwiritsira ntchito akafuna kulankhulana,” inatero nyuzipepala ya The Times ya ku London. Ndipo palinso matelefoni ena a m’manja amene mungathe kuonerapo zinthu zimene zili m’makompyuta ena akutali komanso kulemberapo makalata odzera m’makompyuta.

Mwina muli nayo kale telefoni ya m’manja kapena mukufuna kugula yanu. Mulimonse mmene zilili, lingalirani mwambi wakuti: “Walira mvula walira matope.” Telefoni ya m’manja ili ndi ubwino wake. Komabe, ndi bwino kulingalira kaye kuipa kokhala ndi telefoniyi, popeza kuti ngakhale mutaganiza zogula yanu, kudziŵa bwinobwino kuipa kwake kungakuthandizeni kuigwiritsira ntchito mwanzeru.

‘Ŵerengerani Mtengo’

Yesu ananena mfundo yabwino yakuti munthu asanayambe ntchito yofunika ‘aziŵerengera mtengo wake.’ (Luka 14:28) Kodi mfundo imeneyi ingagwire ntchito pankhani ya matelefoni a m’manja? Inde, ingagwire ntchito. Ndi zoona kuti mungagule telefoniyo motchipa kwambiri, kapena angakupatseni yaulere. Komabe, monga momwe mtsikana wina wa zaka 17, dzina lake Henna anaonera, “bilu ya matelefoni imatha kukula modabwitsa.” Nthaŵi zambiri mungakakamizikenso kuwonjezera zinthu zina zoti muzigwiritsa ntchito pa telefoni yanu ya m’manja ndiponso kugula mitundu ina ya matelefoni okwera mtengo kwambiri. N’chifukwa chake Hiroshi akuti: “Ndimagwira ganyu kuti ndizipeza ndalama ndipo ndimasunga ndalama zogulira telefoni ya m’manja yatsopano chaka n’chaka.” Achinyamata ambiri amachitanso zomwezi. *

Ngakhale makolo anu atanena kuti azikulipirirani biluyo, n’kofunikabe kulingalira mofatsa. Mtumiki wachikristu wina woyendayenda ku Japan anati: “Azimayi ena amapezanso ntchito ina n’cholinga choti azipeza ndalama zolipirira mabilu a matelefoni a ana awo, oti samafunika n’komwe kukhala ndi telefoni.” N’zoona inuyo mungafune kuwapatsa makolo anu chimtolo chotere?

‘Imawawonongera Nthaŵi’

Anthu ambiri amene poyamba ankagwiritsira ntchito telefoni mosamala amaona kuti yayamba kuwathera nthaŵi yambiri kuposa momwe amayembekezera ndiponso kuti ikuwononga nthaŵi yochitira zinthu zofunika kwambiri. Mika ankakonda kucheza kwambiri ndi makolo ake komanso azibale ake panthaŵi yachakudya cha madzulo. Iye anati: “Pano tikadya chakudya timakaloŵa m’zipinda mwathu ndi [matelefoni athu a m’manja].”

“Wachinyamata m’modzi pa achinyamata atatu aliwonse a zaka 16 mpaka 20, amakonda kwambiri kulemberana mauthenga pa telefoni kuposa kulemberana uthenga m’njira zina zonse,” inatero nyuzipepala ya The Guardian ya ku London. Kulemberana uthenga pa telefoni n’kotchipa poyerekezera ndi kulankhulana kwenikweni, koma kulemba uthenga kumatenga nthaŵi yambiri. Mieko anavomereza kuti: “Ngati wina wanditumizira uthenga wakuti ‘gona bwino,’ ndimayankha kuti ‘iwenso ugone bwino.’ Zikatero, ndiye kuti tayambapo ndipo mpaka timapezeka kuti tatha ola limodzi tikutumiziranabe mauthenga. Nkhani zake zambwerera zokhazokha.”

Anthu ambiri amene ali ndi matelefoni a m’manja atati aphatikize nthaŵi yonse imene akhala akugwiritsira ntchito telefoni yawo pa mwezi, angadabwe zedi. Mtsikana wina wa zaka 19, dzina lake Teija anati: “Anthu ambiri telefoni ya m’manja imawawonongera nthaŵi m’malo mowasungira nthaŵi.” Ngakhale mutakhala ndi zifukwa zomveka zokhalira ndi telefoniyi, n’kofunika kusamala kuti isakuwonongereni nthaŵi yambiri.

Mtsikana wina wachikristu dzina lake Marja anati: “Achinyamata ambiri pamisonkhano yachikristu amalembera anzawo mauthenga opanda pake. Ndipo izi n’zofala.” Zimenezi n’zimenenso aona kuti achinyamata ena amachita mu utumiki wachikristu. Baibulo limalangiza Akristu kuwombola nthaŵi yochita zinthu zauzimu. (Aefeso 5:16) Zimakhala zokhumudwitsa kwambiri ngati nthaŵi imeneyi ikuthera polankhulana patelefoni.

Kulankhulana Mobisa

Marie ananenanso kuipa kwa telefoni zimenezi, iye anati: “Popeza kuti telefoniyo imafikira kwa iweyo osati kwa wina aliyense pabanjapo, kuipa kwake n’kwakuti makolo sangadziŵe ngati ana awo akulankhula pa telefoni ndiponso kuti akulankhula ndi ndani.” Choncho, achinyamata ena amagwiritsira ntchito matelefoni a m’manja kuyambitsa chibwenzi chobisa ndi anthu amene si amuna kapena akazi anzawo. Ena atayirira, anyalanyaza mfundo zimene nthaŵi zonse amatsatira polankhula ndi anthu ena. Motani?

“Mwa kulemberana uthenga pa telefoni palibe angadziŵe kuti [achinyamata] akuchita zotani,” inatero nyuzipepala ya The Daily Telegraph ya ku London. Kusamuona munthu amene akulankhula naye kapena kumumva mawu ake kungakhudze zochita zanu. Timo akuti: “Ena amaona kuti kulemberana uthenga patelefoni ndi njira yolankhulirana imene sikhudza zochita za munthu. Ena angalembe zinthu zimene angaone kuti n’zosayenera kunena ngati akulankhulana pamaso m’pamaso.”

Mtsikana wina wachikristu wazaka 17, dzina lake Keiko, atayamba kugwiritsira ntchito telefoni ya m’manja, anapatsa anzake ambiri nambala ya telefoni yake. Mosakhalitsa anayamba kulemberana mauthenga tsiku ndi tsiku ndi mnyamata wina wa mu mpingo wake. Keiko anati: “Poyamba tinkangokambirana nkhani wamba, kenako tinayamba kuuzana mavuto athu. Tinayamba kuchita zodziŵa tokha pogwiritsira ntchito matelefoni athu.”

Mwayi wake makolo ake ndiponso akulu achikristu anamuthandiza zinthu zisanafike poipa kwambiri. Pano akuti: “Ngakhale kuti makolo anga asanandipatse telefoni ya m’manja, anandilangiza kwambiri pankhani yolemberana uthenga pa telefoni ndi anyamata, ndinkamulembera mauthenga tsiku lililonse. Sinali njira yabwino yogwiritsira ntchito telefoni.” *

Baibulo limatilimbikitsa “kukhala nacho chikumbumtima chabwino.” (1 Petro 3:16) Zimenezi zikutanthauza kuti polankhula patelefoni ya m’manja muzionetsetsa kuti ngati wina ataona mauthenga anuwo kapena kumva zimene mukulankhula, “simungachite nazo manyazi,” monga momwe Koichi ananenera. Nthaŵi zonse kumbukirani kuti simungam’bisire chilichonse Atate wathu wakumwamba. Baibulo limafotokoza kuti: “Palibe cholengedwa chosaonekera pamaso [pa Mulungu], koma zonse zikhala za pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake pa Iye amene tichita naye.” (Ahebri 4:13) Choncho, n’kuvutikiranji kukhala ndi chibwenzi chobisa?

Khalani ndi Malire

Ngati mukuganiza zogula telefoni ya m’manja, bwanji osalingalira kaye bwinobwino ngati mukufunikadi kukhala nayo? Kambiranani nkhaniyi ndi makolo anu. Ena ali ndi maganizo angati a mtsikana wina dzina lake Jenna amene anati: “Kukhala ndi telefoni ya m’manja ndi udindo waukulu umene achinyamata ambiri sangaukwanitse.”

Ngakhale mutatsimikiza kuti mugula yanu, ndi bwino kuti muziigwiritsa ntchito bwino. Motani? Ikani malire oyenera. Mwachitsanzo, musamagwiritsire ntchito zinthu zina pa telefoni yanuyo kapena muzichepetsa nthaŵi ndi ndalama zimene mumathera pa telefoniyo. Popeza makampani ambiri a matelefoni amatumiza bilu ya mmene mwagwiritsira ntchito telefoni yanu, nthaŵi zina mungaonere limodzi biluyo ndi makolo anu. Ena amaona kuti ndi bwino kugwiritsira ntchito telefoni ya m’manja yolipiriratu kuti achepetse kuigwiritsira ntchito.

Komanso, lingalirani mofatsa kuti muziyankha nthaŵi yanji mauthenga a patelefoni yanu ndipo muziwayankha motani. Khalani ndi malamulo anu oyenera. Shinji akuti: “Ndimayang’ana mauthenga kamodzi kokha patsiku, ndipo nthaŵi zambiri ndimayankha mauthenga pokhapokha ndikaona kuti ndi ofunika. Chifukwa cha zimenezi, anzanga anasiya kundilembera mauthenga opanda pake. Ngati ndi nkhani yofunika kwambiri, ndimadziŵa kuti angathe kungondiimbira telefoni basi.” Chofunika kwambiri n’chakuti muzisankha anthu olankhulana nawo. Samalani ndi zomangopatsa aliyense nambala ya telefoni yanu. Tsatirani mfundo zimene mumagwiritsira ntchito nthaŵi zonse pankhani ya mayanjano abwino.—1 Akorinto 15:33.

Baibulo limati: “Kanthu kali konse kali ndi nthaŵi yake . . . mphindi yakutonthola ndi mphindi yakulankhula.” (Mlaliki 3:1, 7) Mwachionekere, palinso nthaŵi yakuti matelefoni a m’manja ‘atonthole.’ Misonkhano yathu yachikristu ndiponso utumiki ndi “nthaŵi yake” yolambira Mulungu, osati kuimbirana telefoni. Nthaŵi zambiri oyang’anira malesitanti ndiponso malo a zisudzo amapempha makasitomala awo kuti asagwiritsire ntchito matelefoni a m’manja. Ndipo timamvera mwaulemu zimenezi. Ndithudi Mfumu ya chilengedwe chonse imafunanso kuimvera kuposa pamenepa.

Anthu ambiri akamachita zinthu zofunika panthaŵi yomwe sakuyembekezera telefoni yofunika kwambiri, amatseka telefoni yawo kapena amaitchera kuti isamveke mawu poitana. Ena amaika matelefoni awo a m’manja patali. Ndiponsotu mauthenga ambiri tingathe kuwaŵerenga nthaŵi ina.

Ngati mwasankha kukhala ndi telefoni ya m’manja, onetsetsani kuti inuyo ndi amene muziilamulira osati kuti iyoyo izikulamulirani. Ndithudi, muyenera kukhala maso ndiponso kuonetsetsa kuti sikukulepheretsani kuchita zinthu zofunika kwambiri. Baibulo limatilimbikitsa kuti: ‘Penyani bwino kuti umo muyendera ndi monga anthu anzeru.’ (Aefeso 5:15) Ngati mwaganiza zokhala ndi telefoni ya m’manja, chonde tsimikizani mtima kusonyeza nzeru poigwiritsira ntchito.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Tasintha mayina ena.

^ ndime 7 Onani nkhani yakuti “Achinyamata Akufunsa Kuti—Kodi N’kulakwa Kupeza Ndalama?” mu Galamukani! ya October 8, 1997, kuti mumve zambiri pankhani yogwira ntchito mukaŵeruka kusukulu.

^ ndime 18 Kulankhulana kapena kulemberana mauthenga kaŵirikaŵiri patelefoni ndi munthu amene si mwamuna kapena mkazi mnzanu ndi njira ina yochitira chibwenzi. Onani nkhani yakuti “Achinyamata Akufunsa Kuti—Kodi Cholakwika N’chiyani ndi Kulankhulana?” mu Galamukani! ya September 8, 1992.

[Zithunzi patsamba 18]

Achinyamata ena amakhala ndi zibwenzi zobisa kudzera patelefoni ya m’manja