Kodi Zamtendere Zikukayikitsa Tsopano?
Kodi Zamtendere Zikukayikitsa Tsopano?
“Masiku ano tikuona kuti tikukhala . . . m’nthaŵi imene zinthu zangoti pwirikiti, nthaŵi ya masoka osaneneka.”—Inatero nyuzipepala yotchedwa “La Repubblica” ya mumzinda wa Rome ku Italy.
PAMBUYO pa chiwembu chimene zigaŵenga zinachita chaka chatha ku New York City ndi Washington, D.C., anthu ochuluka kuposa kale lonse aima mitu posadziŵa kuti kaya tsogolo la anthu onse n’lotani. Zithunzi za pa TV zosonyeza Nyumba Zosanja Ziŵiri zili m’malaŵi amoto okhaokha, komanso zosonyeza anthu opulumuka omwe ankasoŵa pogwira, akhala akuzionetsa kambirimbiri. Zithunzi zimenezi zasokoneza mitu ya anthu padziko lonse. Pokhala osokonezeka mitu chonchi, anthuŵa akuganizanso kuti zinthu padzikoli zasinthiratu. Koma kodi zilidi choncho?
Zimenezi zitachitika pa September 11, 2001, nkhondo inabuka. Mayiko omwe kumbuyoku sankaonana ndi diso labwino sanachedwe kugwirizana poyesetsa kulimbana ndi uchigaŵenga. Zonsezi zinaphetsa anthu ambiri zedi ndi kuwonongetsanso katundu wambiri. Komabe mwina chachikulu chimene anthu ambiri padziko lonse aonapo kuti chasintha n’kusoŵeka kwa chitetezo, kuganizira kwambiri kuti palibe munthu aliyense, kulikonseko, yemwe alidi wotetezeka.
Atsogoleri a mayiko akukumana ndi mavuto aakulu. Atolankhani ndiponso olemba ndemanga aima mitu posadziŵa kuti kaya zauchigaŵenga angaziletse bwanji kuti zisafalikire mmene zikuchitikira ngati moto wolusa, popeza kuti zikuoneka ngati zikuchitika chifukwa cha umphaŵi ndiponso mtima waliuma ndipotu izi ndi zinthu zosautsa zomwe zikuoneka kuti palibe yemwe akudziŵa njira yozithetsera. Kupanda chilungamo kwafala kwambiri padzikoli moti n’kokwanira kubutsa chisokonezo choopsa mwa njira ina iliyonse. Anthu amitundu yonse akukayikira ngati zinthu zosautsazi zingathe kudzathetsedwa. Kodi nkhondo komanso zosautsa zonse zomwe imabweretsa monga imfa ndiponso kuwonongeka kwa zinthu, zidzathadi?
Anthu mamiliyoni ambiri amaganiza kuti zipembedzo zotchuka n’zimene zingayankhe mafunso ameneŵa. Komanso anthu ena sadziŵa n’komwe koloŵera. Nanga inuyo bwanji? Kodi mukuganiza kuti akuluakulu azipembedzo angayankhe mafunso otereŵa? Ndipo kodi iwo angathandizedi kuti mtendere ubwere chifukwa cha mapemphero awo?