Kukumananso Modabwitsa Patatha Zaka 30
Kukumananso Modabwitsa Patatha Zaka 30
MU 1967 anyamata aŵiri anakumana mwadzidzidzi. Anyamataŵa anawaika kuti azikhala m’chipinda chimodzi pa yunivesite ya zaumisiri ya Michigan ku United States. Panthaŵiyo, Dennis Sheets wochokera mu mzinda wa Lima ku Ohio, anali ndi zaka 18 ndipo anali m’chaka chake choyamba cha maphunziro a zankhalango. Mark Ruge anali ndi zaka 20, ndipo kwawo ndi ku Buffalo ku New York. Iye anali m’chaka chake chachitatu cha umisiri wa zomangamanga.
Panthaŵiyo, ubale wawo sunakhalitse, unali wachidule. Onse aŵiri sanapitirize maphunziro awo a kuyunivesite ndipo anasiyana. Panapita zaka zoposa 30. Kenaka, tsiku lina anakumanizana m’dziko la Dominican Republic. Unali mwayi kuti akumanenso mwadzidzidzi chonchi. Komabe panali chinthu chinanso chomwe chinachititsa. Kodi chinali chiyani? Kuti tichidziŵe, tiyeni tione zimene aliyense anachita atasiyana.
Dennis Aloŵa Usilikali
Dennis anabwerera kwawo ataphunzira pakoleji chaka chimodzi. Kenaka, mu December 1967, anam’tenga kuti akhale m’gulu la asilikali a dziko la United States, ndipo mu June 1968 anam’tumiza ku Vietnam. Ali kumeneko anakumana ndi zoopsa zosiyanasiyana za ku nkhondo. Mu 1969, nthaŵi yake yokhala msilikali itatha, iye anabwerera ku United States, kenaka n’kupeza ntchito pakampani ina yaikulu ku Ohio. Komabe, sankakhutira nayo.
“Ndili mnyamata ndinkalakalaka nditasamukira ku Alaska n’kumakachita uchikumbe,” anatero Dennis. Choncho, m’chaka cha 1971 iye ndi mnzake wina amene anaphunzira naye ku sekondale anayamba kukwaniritsa cholinga chakecho. Komabe, m’malo mochita uchikumbe, iye anakaloŵa ntchito wamba zosiyanasiyana. Pakanthaŵi kena ankakhala m’tenti ndi kumagwira ntchito yolondolera moto m’nkhalango. Anaŵeta ndevu ndi tsitsi ndipo anayamba kusuta chamba.
Mu 1972, Dennis anachoka ku Anchorage kuti akachite nawo mwambo wachikatolika wotchedwa Mardi Gras mumzinda wa New Orleans ku Louisiana. Kenaka anamanga kanyumba kamitengo m’nkhalango ya ku Arkansas. Kumeneko, iye anayamba kugwira ntchito ya zomangamanga. Mu June 1973, pofuna kupeza njira yakuti moyo wake ukhale waphindu, Dennis anayamba kuyendayenda m’madera osiyanasiyana m’dzikolo pokwera matola.
Mark Alimbana ndi Zankhondo
Mark anaphunzirabe pa yunivesite paja kwa miyezi ingapo chichokereni Dennis, koma kenako maganizo anam’fikira oti asakhale nawo ku mbali yothandiza zankhondo. Motero anabwerera ku Buffalo komwe anakagwira ntchito kwa nthaŵi pang’ono monga kapitawo pa kampani ina yopanga zitsulo. Chifukwa chosakhutitsidwabe ndi nkhani zankhondo, iye anasiya ntchito, n’kugula njinga yamoto, ndipo anauyatsa ulendo wa ku San Francisco, ku California. Dennis ndi Mark anakhalapo ku San Francisco panthaŵi yofanana, ngakhale kuti iwo sanadziŵe zimenezi panthaŵiyo.
Mofanana ndi Dennis, Mark anaŵeta ndevu ndi tsitsi ndipo anayamba kusuta chamba. Koma Mark analimbikira kwambiri kulimbana ndi zankhondo, ndipo ankachita nawo zionetsero zosonyeza kusakondwa ndi zankhondo. Apolisi ofufuza milandu ku United States anali kum’funafuna chifukwa chozemba kupita kunkhondo, motero poopa kugwidwa
iye ankagwiritsa ntchito mayina achinyengo ndipo anachita izi kwa zaka zingapo. Anapita ku San Francisco n’kuyamba kukhala moyo wodzisambula kwambiri. Kumeneko, m’chaka cha 1970, anthu aŵiri a Mboni za Yehova anafika panyumba pake.Mark anafotokoza kuti: “Ayenera kuti ankaganiza kuti ndikusangalala nazo, motero anabweranso. Sanandipeze, koma anasiya Baibulo lamtundu wobiriwira ndi mabuku atatu.” Komabe, Mark sanaŵerenge Baibulolo ndi mabukuwo chifukwa chakuti anali wotanganidwa kwambiri ndi zandale. Komanso apolisi aja anali kum’sakasaka kwambiri. Motero, iye anasamukira ku Washington, D.C., pogwiritsa ntchito dzina linanso lachinyengo. Chibwenzi chake, Kathi Yaniskivis, chimene anakumana nacho pamene anali ku yunivesite, chinamulondola kumeneko.
Kenako, mu 1971, Mark anagwidwa ndi apolisi aja. Apolisi aŵiri anam’perekeza pandege kuchoka ku Washington, D.C., kupita ku New York ndipo anaonetsetsa kuti wakafika ku Toronto ku Canada. N’zoonekeratu kuti apolisiwo sankaona Mark ngati munthu woti angasokoneze bata; iwo ankangofuna kuti atuluke m’dzikomo. Chaka chotsatira iye anakwatirana ndi Kathi ndipo anasamukira ku chilumba cha Gabriola, British Columbia, ku Canada komweko. Sankafuna kukhala pamodzi ndi anthu ena, komabe sankaumva kukoma moyo.
Onse Anakhala Mboni za Yehova
Paja tati kuti Dennis anali kuyendayenda pofuna kupeza njira yakuti moyo wake ukhale waphindu. Ulendo wake unakam’fikitsa ku Montana, kumene anakaloŵa ntchito yothandiza mlimi wina panthaŵi yokolola kufupi ndi tauni ya Chinook. Mkazi wa mlimiyo ndiponso mwana wake wamkazi anali a Mboni za Yehova. Anapatsa Dennis magazini ya Galamukani! kuti aŵerenge. Sipanapite nthaŵi yaitali, iye anakhulupirira kuti Mboni zimapembedza moona.
Atanyamula Baibulo, Dennis anachoka pafamupo n’kupita mumzinda wa Kalispell ku Montana. Kumeneko anakakhala nawo koyamba pa msonkhano wa Mboni za Yehova. Pamsonkhanowo iye anapempha kuti aziphunzira Baibulo. Patapita nthaŵi pang’ono iye anameta tsitsi ndi ndevu zija. Mu January 1974 anapita kukalalikira kwa nthaŵi yoyamba, ndipo anabatizidwira m’chibeseni chomwetsera ziŵeto pa March 3, 1974, ndipo uku kunali kutauni ya Polson, ku Montana komweko.
Panthaŵiyi, Mark ndi Kathi, omwe ankakhala ku chilumba cha Gabriola, anaganiza zoliphunzira bwino Baibulo popeza kuti anali ndi nthaŵi. Anayamba kuŵerenga Baibulo la King James Version, koma Chingelezi chake chachikale chinkawavuta kumva. Kenako Mark anakumbukira kuti anali akusungabe Baibulo ndiponso mabuku omwe Mboni zinam’patsa zaka zingapo zapitazo. Pauŵiri wawo anaŵerenga Baibulolo ndiponso mabuku akuti Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya ndi Is the Bible Really the Word of God? Mark ndi Kathi anakhudzidwa mtima kwambiri ndi zimene anaphunziramo.
Mark anafotokoza kuti: “Mfundo ya m’buku lakuti Coonadi yonena za gulu la Akristu omwe sapita kunkhondo zivute zitani ndiyo imene inandilasa. Ndinaona kuti amenewo ndiwo akuchita Chikristu chenicheni.” Patapita masiku pang’ono, Mark ndi Kathi anabwerera ku Houghton, Michigan, kukaona anthu kwawo kwa Kathi, ngakhale kuti akanatha kumangidwa. Kumeneko, ngakhale kuti ankaonekabe osambuka, anakhala nawo pa msonkhano wa Mboni za Yehova. Anavomera kuphunzira Baibulo ndipo anaphunzira kwa mwezi wonse umene anali ku Michigan.
Atabwerera ku chilumba cha Gabriola, iwo anakumana ndi munthu wina wa Mboni mumsewu wa m’tauni ya Nanaimo, ku British Columbia, ndipo anamufotokozera kuti akufuna phunziro la Baibulo. Tsiku lomwelo Mboni zinafika pachikepe choolotsa anthu kuti zikumane nawo, ndipo phunziro la Baibulo linayamba. Patatha miyezi itatu, Mark ndi Kathi anayamba ntchito yolalikira. Ndipo atalalikira kwa miyezi itatu, pa March 10, 1974, onse aŵiri anabatizidwa. Panali patangotha mlungu umodzi Dennis atabatizidwa!
Dennis Achita Utumiki wa Nthaŵi Zonse
Dennis anakhala mpainiya, kapena kuti mtumiki wa nthaŵi zonse, mu September 1974. Iye anati: “Ndinkasangalala nawo upainiya, koma ndinkafuna kuchita zambiri mu utumiki; motero mu July 1975, ndinalemba kalata yofunsira utumiki kulikulu la dziko lonse la Mboni za Yehova ku Brooklyn, New York. Anandiitana m’December chaka chomwecho.”
Ntchito yoyamba yomwe Dennis anapatsidwa inali yothandiza kukonza nyumba yomwe poyamba inali hotela yotchedwa Towers kuti ikhale nyumba yogona anthu ogwira ntchito palikulupo. Anagwira
ntchito pamenepo kwa zaka zingapo, ndipo ankayang’anira gulu loika matailosi. Kenako, pamene ankafuna kukwatira, anapita ku California. Mu 1984, akutumikira monga mkulu mu mpingo wa Cathedral City, anakwatira Kathy Enz, yemwe anali mpainiya.Dennis ndi Kathy ankayesetsa kusafuna zambiri pa moyo wawo chifukwa chakuti anali n’cholinga choti achite ntchito za Ufumu wa Mulungu. Motero nthaŵi zambiri Dennis ankakana ntchito zambirimbiri za zomangamanga kum’mwera kwa California zomwe zikanam’pezetsa ndalama zambiri. Mu 1988 iye ndi Kathy anafunsira kukathandiza ku mayiko ena pa ntchito ya zomangamanga ya Mboni za Yehova. M’mwezi wa December chaka chomwecho, anatumizidwa kukagwira ntchito yomanga nthambi ku Buenos Aires, m’dziko la Argentina.
M’chaka cha 1989, Dennis ndi Kathy anaitanidwa kuti azikagwira ntchito ya nthaŵi zonse ya zomangamanga ya Mboni za Yehova. Mu utumiki wapadera wa nthaŵi zonse umenewu, anakatumikira kaŵiri m’mayiko a Suriname ndi Colombia. Anamanga nawonso nthambi m’mayiko a Ecuador ndi Mexico, komanso Dominican Republic.
Mark Achita Utumiki wa Nthaŵi Zonse
Mu 1976, Mark, pamodzi ndi achinyamata ena masauzande ambirimbiri a ku America omwe anathaŵira ku Canada chifukwa choopa kutengedwa kuti akhale asilikali, anapatsidwa ufulu ndi boma la United States. Iye ndi mkazi wake, Kathi, nawonso sankafuna zambiri pa moyo wawo n’cholinga choti azikhala nthaŵi yambiri mu utumiki. Motero Mark ankagwira ganyu yoyeza malo, ndipo pang’onom’pang’ono iye ndi Kathi anamaliza kubweza ngongole zonse zomwe anatenga asanabatizidwe.
Mu 1978, pamene Mboni za Yehova m’dziko la Canada zinkalingalira zomanga nthambi yatsopano kufupi ndi ku Toronto ku Ontario, Mark ndi Kathi anakatumikira nawo. Popeza Mark ankadziŵa ntchito yoyeza malo, iwo anawaitana kukagwira nawo ntchito yomanga. Anagwira nawo ntchito yomangayo ku Georgetown mpaka anamaliza nawo m’mwezi wa June mu 1981. Kenako, anabwerera ku British Columbia ndipo kwa zaka zinayi iwo anathandiza nawo kumanga Nyumba ya Msonkhano ya Mboni za Yehova kumeneko. Ntchitoyi itatha, anawaitananso kukagwira ntchito yowonjezera nthambi ya Canada.
Mu 1986, Mark ndi Kathi, atakhala miyezi yochepa ku Georgetown, anaitanidwa kuti azikagwira ntchito nthaŵi zonse panthambi ya ku Canada. Kuyambira nthaŵi imeneyo iwo akhala akutumikira panthambipo ndipo akhalanso ndi mwayi wina wothandiza pantchito zomanga m’mayiko ena ambiri. Chifukwa chakuti Mark amadziŵa ntchito yoyeza malo, iye anayamba kugwiritsidwa ntchito monga woyeza malo a nyumba za nthambi ndiponso Nyumba za Msonkhano za Mboni za Yehova m’mayiko a kum’mwera ndi pakati pa America ndiponso m’zisumbu za Caribbean.
Kwa zaka zonsezi, iye ndi Kathi atumikira m’mayiko a Venezuela, Nicaragua, Haiti, Guyana, Barbados, Bahamas, Dominica, United States (ku Florida), ndi Dominican Republic. Utumiki wa nthaŵi zonse wapadera umenewu unachititsa kuti Mark ndi Dennis akumanenso.
Anakumananso ku Dominican Republic
Mark ndi Dennis ankagwira ntchito zofananana zomangamanga ku Dominican Republic, koma onse sankadziŵa. Tsiku lina pa nthambi ya Mboni za Yehova ku Santo Domingo, iwo anangoti gululu, kukumana. Ndiye tangoganizira chisangalalo chakecho atakumananso. Ndipotu, panali patatha zaka 33 atasiyana motero anali ndi nkhani zambiri zoti afotokozerane. Anafotokozerana zinthu zambiri mwa zimene mwaŵerengazi, ndipo zinawadabwitsa kwambiri.
Koma chinthu chomwe chinawachititsa chidwi kwambiri, chomwenso chinachititsa chidwi anthu onse omwe anawafotokozera nkhani zawozi, chinali chakuti pali zinthu zambiri zofanana pa moyo wawo.Onse anakhalapo moyo wodzisambula ndipo anasamukira kumadera akumidzi kuti atalikirane ndi moyo wamakono wolira zambiri ndiponso kuti apeŵe zovuta zake. Dennis anakwatira mtsikana wotchedwa Kathy; Mark anakwatiranso mtsikana wotchedwa Kathi. Amuna onseŵa anavomera kuphunzira Baibulo panthaŵi yoyamba kusonkhana ndi Mboni za Yehova. Onseŵa anabatizidwa m’March 1974. Onse anakhalapo pa nthambi ya Mboni za Yehova, Dennis anatumikira ku United States ndipo Mark anatumikira ku Canada. Onse aŵiri anayesetsa kuti akhale moyo wosalira zambiri n’cholinga choti akwaniritse zolinga zauzimu. (Mateyu 6:22) Onseŵa anagwirapo ntchito zomangamanga kumayiko ena ndipo agwirapo ntchito kumayiko ambirimbiri. Asanakumanenso mwamwayi ku Dominican Republic, onse aŵiriŵa anali asanakumanepo ndi mnzawo wina aliyense wakale amene anaphunzira choonadi cha Baibulo.
Kodi Mark ndi Dennis amaganiza kuti anakumana modabwitsa chonchi chifukwa ndi mmene anakonzera Mulungu? Satero m’pang’ono pomwe. Iwo amadziŵa kuti, malinga ndi zomwe Baibulo limanena, ‘tonse timangoona zotigwera m’nthaŵi yake,’ ndipo nthaŵi zina zimenezi zimachitika mochititsa chidwi kwambiri. (Mlaliki 9:11) Komabe, amadziŵanso kuti pali chinachake chomwe chinathandiza kwambiri kuti akumanenso: cholinga chawo choti apeze njira yakuti moyo wawo ukhale waphindu ndiponso kukonda kwawo Yehova Mulungu.
Nkhani za Dennis ndi Mark zikusonyezanso zinthu zina zomwe zimachitikira anthu onse a mitima yoongoka omwe amaphunzira choonadi cha Baibulo. Dennis anati: “Zomwe zachitikira ineyo ndi Mark zikusonyeza kuti Yehova amadziŵa zomwe zimachitika pa moyo wa anthu, ndipo pamene mitima yawo ikufunadi, iye amawakokera kwa iye.”—2 Mbiri 16:9; Yohane 6:44; Machitidwe 13:48.
Mark akuwonjezera kuti: “Zomwe zatichitikirazi zatithandizanso kudziŵa kuti munthu akasintha n’kumatsatira miyezo ya Yehova, akapatulira moyo wake kwa iye, ndiponso akadzipereka, Yehova angagwiritsire ntchito luso lake kuthandiza pa kulambira koona n’cholinga choti anthu ake apindule.”—Aefeso 4:8.
Zomwe zinawachitikirazi zikusonyezanso kuti Yehova Mulungu amadalitsa anthu ake akam’tumikira mokhulupirika. Dennis ndi Mark akuona kuti adalitsidwa. Dennis akuti: “Ndi mwayi waukulu kutumikira pa zinthu za Ufumu mu utumiki wapadera wa nthaŵi zonse. Utumikiwu watithandiza kuti tizilimbikitsana pamene tikugwira ntchito ndi abale komanso alongo achikristu ochokera padziko lonse.”
Mark akuwonjezera kuti: “Yehova amadalitsadi anthu omwe amatsogoza Ufumu. Ndimaona kuti ndi madalitso apadera kutumikira banja la nthambi ya ku Canada ndiponso kukagwira nawo ntchito zachimango m’mayiko ena.”
Kodi tingati kukumananso kumeneku n’kwapadera? Inde, chifukwa monga momwe Mark akunenera: “Chifukwa chachikulu chomwe chinachititsa kuti kukumana kwathu kwa mwadzidzidziku kukhale kosangalatsa kwambiri n’chakuti tonse tadziŵa, kukonda, ndi kutumikira Mulungu wapadera kwambiri, Yehova.”
[Chithunzi patsamba 28]
Dennis mu 1966
[Chithunzi patsamba 28]
Mark mu 1964
[Chithunzi patsamba 30]
Dennis ku South Dakota mu 1974
[Chithunzi patsamba 30]
Mark ku Ontario mu 1971
[Chithunzi patsamba 31]
Dennis ndi Mark pamodzi ndi azikazi awo, patangotha nthaŵi pang’ono kuchokera pamene anakumananso m’chaka cha 2001