Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Tinapulumukira Zoopsa Phiri Litaphulika N’kumatuluka Chiphalaphala!

Mmene Tinapulumukira Zoopsa Phiri Litaphulika N’kumatuluka Chiphalaphala!

Mmene Tinapulumukira Zoopsa Phiri Litaphulika N’kumatuluka Chiphalaphala!

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU CONGO (KINSHASA)

LERO ndi Lachiŵiri, pa January 15, 2002 ndipo zikuoneka kuti kunja kwacha bwinobwino m’dzikoli la m’chigawo chino cha pakati pa Africa. Ine ndi mnzanga wina yemwenso ndi wa Mboni za Yehova tikufika mumzinda wa Goma m’chigawo cha Kivu, kuno ku Congo (Kinshasa), kuti tikumane ndi Mboni zochokera m’chigawo chimene chili ndi nyanja zikuluzikulu muno mu Africa.

Kodi Palibedi Chodetsa Nkhaŵa?

Ngakhale kuti phiri limene lili ndi chiphalaphala chotentha la Nyiragongo (lomwe n’lalitali mamita 3,470) lili pamtunda wa makilomita 19 kuchokera mumzinda wa Goma, ife tonse tikudabwa ndi zimene zikuchitika kuphiriko. * Tikumva kugunda kwa chivomezi kuchokera kuphiriko, ndipo tikuonanso utsi ukutuluka paphiri lokhala ndi chiphalaphalalo. M’nyengo inoyi anthu a kunoko anazoloŵera kuti phirili limachita zimenezi, moti sizikuwakhudza n’komwe.

Masana atsikuli, tinapita kumisonkhano ya mipingo iŵiri ya Mboni za Yehova. Zivomezi zikumvekabe ndiponso kuphiriko kukumvekabe kugunda. Koma zikuoneka kuti palibe amene zimenezi zikum’khudza. Akuluakulu oyang’anira mzindawo akuuzabe anthu kuti palibe chodetsa nkhaŵa ayi. Ngakhale kuti katswiri wina wa zivomezi wa ku Congo wakhala akuchenjeza kwa miyezi ingapo kuti phirili liphulika, palibe amene akukhulupirira. Mnzanga wina akunena mongocheza kuti, “Madzulo ano kumwambaku kufiira chifukwa cha moto wochokera m’phirili, likaphulika.”

“Akuluakulu, Watsala Watsala!”

Titabwerera kunyumba kumene tikukhalako akutiuza mosapita m’mbali kuti: “Akuluakulu, watsala watsala!” Zinthu zathina. Mzindawu uona zoopsa. Koma ndiye zinthu zimatha kusintha mwamsanga bwanji! Posachedwa pompa tinali kukambirana zoti mzinda wa Goma ndiwo ukhale malo okumaniranapo pantchito yathu yolalikira. Koma panopa mmene dzuŵa likupendekamu, tikuuzidwa kuti tichoke mumzindawu chifukwa n’kutheka kuti usanduka chipere!

Momwe kwayamba kuda chonchi thambo langoti psuu ndipotu n’zosadabwitsa chifukwa chiphalaphala chophulika m’phirilo chikuyenderera kuchokera ku Nyiragongo kuloŵera cha mumzindawu. Phirili likungooneka ngati chimphika chachikulu chimene muli zinthu zimene zikutokota n’kuyamba kutayikira, chifukwa chiphalaphala chamoto chikutuluka m’phirili n’kumawononga paliponse pamene chafikapo. Sitinalongedzeko katundu wathu mwachangu chonchi! Nthaŵi yangotsala pang’ono kukwana seveni koloko usiku.

Anthu Ambirimbiri Othaŵa Ali Piringupiringu Mumsewu

Tikuthaŵa mwachangu chonchi, tikuona kuti msewu wotuluka mumzinda wa Goma wadzaziratu ndi khwimbi la anthu amene akuthaŵa poopa kufa. Ambiri akuyenda wapansi, atanyamula katundu aliyenseyo amene akwanitsa kutenga mwachangu kunyumba kwawo. Ambiri asenza modendekera katunduyo. Ndipo ena adzaza thothotho m’magalimoto. Onse akuloŵera kumalire a dzikoli ndi la Rwanda. Komabe, si kuti phiri likaphulika limaona zoti apa anthu anaikapo malire a dziko lawo. Palibe gulu la asilikali limene lingachite chilichonse choliimitsa! Tikuona ngakhale asilikali akuthaŵa chiphalaphalachi pofuna kusunga phukusi la moyo. N’zosatheka kuti galimoto ziyende mofulumira mumsewumu. Ndibwino tingopitiriza kuyenda wapansi. Tili pakati pa anthu 300,000 amene akukankhanakankhana, amuna, akazi, ana ndi makanda, omwe akuthaŵa phiri lophulika mochititsa manthalo. Kugunda kwa chivomezicho kukupitirirabe ndipo chikugwedezabe nthaka.

Aliyense akufuna kupulumutsa phukusi lamoyo. Ine ndi mnzanga ndife alendo ochokera mumzinda wina waukulu, ndipo tili m’gulumo pamodzi ndi anthu ena angapo a Mboni, amene akutiyang’anira. Tikulimbikitsidwa kwabasi pokhala ndi anthu ameneŵa ndiponso akutisamalira kwambiri m’nthaŵi yovutayi. Anthu akuthaŵa atanyamula zinthu zosiyanasiyana, monga zovala, mapoto, mapani, ndiponso timaphukusi ta zakudya zitangoti tutuwiri. Pali chinamtindi cha anthu, ndiyetu si kukankhanakankhana kwake. Ena akukankhidwa ndi galimoto ndipo zikumawaphumitsa katundu wawo, basi anthu n’kumupondaponda. Apatu amene wagwa akumaona zakuda. Aliyense mtima uli gu gu gu chifukwa chogwidwa mantha. Tikufuna tikafike ku Gisenyi m’dziko la Rwanda, kumene sikutali kwenikweni ayi. Tikupitiriza ulendo wathu mosapumira.

Usiku Uno Mtima Wakhala M’malo

Tikufika pa nyumba ina yogonapo alendo koma tapeza malo atatha. Palibenso kuchitira mwina koma kungokhalakhala mozungulira katebulo kapanja basi. Komatu apa n’kuti titayenda wapansi kwa maola atatu ndi theka. Komabe chachikulu n’chakuti tili moyo ndipo tawomboka m’zoopsazi komanso kuti tili pamodzi ndi abale athu achikristu amene tayenda nawo limodzi. Mwayi wake palibe wa Mboni za Yehova aliyense amene wafa.

Zikuoneka kuti tigona panja. Kutali, cha kumene kuli mzinda wa Goma tikutha kuona kumwamba kuli psuu. Komatu sikukongola kwake! Kunja nako sikukucha msanga. Chivomezicho chakhala chikugunda ndi kugwedeza nthaka usiku onse. Chisoni chikutigwira tikamaganizira zimene zachitika dzulo pamene mabanja ochuluka zedi athaŵa ndi tiana tawo.

Thandizo Lafika Msangamsanga

Mboni za Yehova za mumzinda wa Kigali, womwe ndi likulu la dziko la Rwanda, zikutipeza Lachisanu masana, pa January 18. Komiti yopereka chithandizo yokhala ndi abale ochokera ku Goma ndi ku Gisenyi ikuyamba ntchito yake. Ntchito yoyamba ndiyo kupezera malo a Mboni othaŵawo m’Nyumba za Ufumu zisanu ndi imodzi zimene zili chapafupi pompo. Ntchito imeneyi ikuchitika tsiku lomweli. Pamsewu aikapo chikwangwani cha m’Chifalansa ndi m’Chiswahili cholozera njira yopita ku Nyumba ya Ufumu ya kumeneku, kumene othaŵa akathandizidwireko kutinso mitima yawo ikhazikike pansi. Tsiku limenelinso, zinthu zofunikira zokwana matani atatu zikufika ku Nyumba za Ufumu zimene kukukhala Mbonizo. Maŵa lake pa Loŵeruka, chigalimoto chachikulu chikufika kuchokera ku Kigali chitadzaza ndi zakudya, mabulangete, mapulasitiki opangira matenti, sopo, ndiponso mankhwala.

Anthu Akuda Nkhaŵa Kwambiri

Iyi ndi nthaŵi yodetsa nkhaŵa kwambiri. Kodi anthu onseŵa asamalidwa bwanji? Nanga phiri laphulika lija bwanji? Kodi chiphalaphalacho chisiya liti kutuluka? Kodi mzinda wa Goma watsala pati tsopano? Nkhani zimene tikumva ndiponso zivomezi zimene zikuchitikabe sizikutilimbikitsa m’pang’ono pomwe. Akatswiri ena akuganiza kuti nthunzi yoopsa imene ikutuluka paphiri lophulikalo iwononga mpweya mlengalenga. Anthu akudanso nkhaŵa kuti madzi a m’nyanja ya Kivu awonongeka ndi zimene zachitikazi.

Patangotha masiku aŵiri okha chiphulikireni phirili, nkhani zosautsa zangofala paliponse. Kenaka Loŵerukali madzulo, tikumva kuti anthu pafupifupi 10,000, kuphatikizapo a Mboni 8 komanso mwana, azunguliridwa ndi chiphalaphala chomwe m’madera ena n’chakuya mamita aŵiri. M’deralo mphepo yadzaza ndi mpweya woipa. Tikungopempherera kuti bola anthuwo asafe. Zinthu sizili bwino m’pang’ono pomwe. Ngakhale tchalitchi cha Katolika cha ku Goma chagumulidwa ndi chiphalaphalacho. Panthaŵiyi palibe amene akuganiza kuti mzinda wa Goma ubwereranso mwakale.

Nkhani Yolimbikitsa

Lamlungu nthaŵi ya 9 koloko m’maŵa, tikulandira uthenga pa telefoni kuchokera kwa mbale wina amene ali m’gulu la anthu ozunguliridwa ndi chiphalaphala aja. Akuti zinthu zayamba kusintha. Panopo ziliko bwino. Kukugwa mvula, chiphalaphalacho chikuzizira, ndipo kumwamba kwayamba kuyera. Ngakhale kuti chiphalaphalacho n’chotenthabe ndithu ndiponso n’choopsa, anthu ayamba kuwoloka n’kumatulukamo. Mzindawo sunatheretu wonse ayi.

Aka n’koyamba kumvapo nkhani yolimbikitsa chiyambireni zoopsazi. Zikuoneka kuti phirilo layamba kuzizira. Akatswiri a m’deralo sakunena chimodzi pankhaniyi. Tsopano tikutha kulankhulitsana ndi anthu a mumzinda wapafupi nafe wa Bukavu, umene uli kumapeto kwa nyanja ya Kivu. Tikumva kuti mabanja asanu pamodzi ndi ana atatu opanda makolo awo afika ku Bukavu pa boti. Mboni za Yehova za mumzindawu ziwasamalira.

Tingathe Kubwerera M’makwathu!

Lolemba, pa January 21 tikulimbikitsa ndi kupepesa anthu ochokera ku Gisenyi amene akumana ndi zovutazi ndipo tikufuna tione kuti akufunikira zinthu zotani. Tikuona kuti abale amene amakhala mongoyembekezera chabe m’Nyumba za Ufumu zisanu ndi imodzi zija ayambapo kulongosola zinthu. Tapeza kuti anthu onse amene anathaŵa kuphatikizapo ana, analipo 1,800.

Nanga bwanji zam’tsogolo? Mwamsangamsanga aboma akukonza makampu a anthu othaŵawo. Komabe ena mwa anthuŵa zimenezi zikuwakumbutsa makampu aanthu othaŵa nkhondo yapachiweniweni mu 1994. Tikubwerera ku Goma, ndipo tikufikako masana. Gawo lalikulu ndithu la mzindawo lawonongeka. Tikuyenda pachiphalaphala cholimba chimene chinali kuyenderera m’misewu. Sichinazizire kwenikweni, ndipo chikutulutsa nthunzi imene ikupita mlengalenga. Anthu ambiri akufunitsitsa kubwerera mumzindawo.

Nthaŵi ya 1 koloko masana, tikukumana ndi akulu 33 m’Nyumba ya Ufumu ya mpingo wa Goma Center. Onse akuvomerezana pa mfundo imodzi yakuti abwerere ku Goma. Iwo akuti, “kwanu n’kwanu basi.” Kuwafunsa kuti, nanga phirilo litaphulikanso mutani? Akungoyankha kuti, “Tinangozoloŵera basi, si zachilendo zimenezo.” Akuopa kuti akapanda kubwerera msanga, katundu wawo yense akapeza atasesedwa ndi akuba. Maŵa lake mabanja onse a Mboni amene anathaŵa abwerera kale ku Goma. Anthu ambiri mwa anthu 300,000 amene anawoloka malire a dzikolo akubwereranso ku mzinda umene unaona zoopsawu.

Patatha Mlungu Umodzi

Anthu ayambanso piringupiringu mumzindawu. Zikuoneka kuti anthu a mumzindawu sasiya kuchita ntchito zawo ayi. Mosakhalitsa akuyamba ntchito yochotsa chiphalaphalacho kuti mbali ziŵiri zogaŵanika za mzindawu zigwirizanenso. Paliponse pamene chiphalaphalacho chinadutsa panawonongekeratu. Chigawo chimene amachitirako zamalonda ndiponso chigawo chimene kuli maofesi a boma chinawonongekeratu. Akuti kubwalo landege, mbali yaikulu ndithu ya msewu umene ndege zimayendapo inawonongeka.

Ataŵerengetsera bwinobwino anapeza kuti mabanja a Mboni za Yehova 180 ali m’gulu la anthu amene zinthu zawo zonse zinawonongeka ndipo alibe ngakhale m’pogona pomwe. Komiti yopereka chithandizo yakonza zakuti ithandize amuna, akazi ndiponso ana 5,000 kuti azilandira zakudya tsiku lililonse. Mboni za Yehova za ku Belgium, France, ndi Switzerland zatumiza mapulasitiki omangira misasa kuti muzikhala anthu amene alibe nyumba komanso kuti amangire malo osonkhaniranamo a mipingo imene Nyumba zawo za Ufumu zinawonongeka kwambiri kapena kugumukiratu. Mabanja ena opanda nyumba azikakhala kwa a Mboni amene nyumba zawo zidakalipo, ndipo ena azikakhala m’misasa.

Lachisanu pa January 25, patatha masiku khumi pambuyo pa zoopsa zimene zinachitika usiku zija, anthu 1,846 akusonkhana panja pa sukulu ina ku Goma kudzamvetsera mawu olimbikitsa a m’Malemba. Abalewo akuthokoza kwambiri chifukwa cholimbikitsidwa ndiponso kuthandizidwa ndi Yehova kudzera m’gulu lake. Alendofe talimbikitsidwa kwambiri poona kulimba mtima ndiponso chikhulupiriro chawo cholimba ngakhale m’kati mwa mavuto. Pa zovuta zonsezi, n’zosangalatsa kwambiri kukhala m’gulu la ubale wogwirizana chonchi chifukwa cholambira Mulungu woona yekha, Yehova, amene ali Mwini chilimbikitso chosatha!—Salmo 133:1; 2 Akorinto 1:3-7.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 M’Chiswahili phiri lachiphalaphalali amalitcha kuti mulima ya moto, kutanthauza kuti “phiri la moto.”

[Mapu pamasamba 12, 13]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Mizere ya mivi kutsogolo ikusonyeza kumene chiphalaphalacho chinaloŵera

CONGO (KINSHASA)

Phiri la Nyiragongo

↓ ↓ ↓

Bwalo la ndege la Goma ↓ ↓

↓ GOMA

↓ ↓

NYANJA YA KIVU

RWANDA

[Zithunzi patsamba 13]

Anthu ankhaninkhani anathaŵa kwawo ku Goma chifukwa cha chiphalaphalachi

[Mawu a Chithunzi]

AP Photo/Sayyid Azim

[Zithunzi pamasamba 14, 15]

Patangotha mlungu umodzi wokha Mboni zinayamba kuchitanso misonkhano yawo yachikristu