Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ngati Mliri wa Edzi Udzagonjetsedwe, Kodi Ungadzagonjetsedwe Bwanji?

Ngati Mliri wa Edzi Udzagonjetsedwe, Kodi Ungadzagonjetsedwe Bwanji?

Ngati Mliri wa Edzi Udzagonjetsedwe, Kodi Ungadzagonjetsedwe Bwanji?

KWA nthaŵi yaitali m’mayiko ambiri mu Africa anthu ambiri nkhani ya Edzi amangoikankhira kunkhongo. Ndi nkhani imene anthu ena safuna n’komwe kuitchula. Komabe chaposachedwapa, anthu ayesetsa kuphunzitsa makamaka achinyamata ndi kuwathandiza kuti azikhala omasuka kukambirana nkhaniyi. Komabe sizinaphule kanthu kwenikweni. Khalidwe la anthu ndiponso miyambo yawo inawaloŵerera kwabasi, ndipo kuisintha n’kovuta kwambiri.

Kutsogola kwa Zachipatala

Asayansi odziŵa nkhani zachipatala adziŵa zinthu zambiri zokhudza kachilombo ka HIV ndipo apanga mankhwala amene awonjezera moyo wa anthu ambiri odwala matendaŵa. Mankhwala osanganiza mitundu itatu ya mankhwala olimbana ndi kachilomboka, akhala akuwagwiritsira ntchito kuthandizira odwala matendaŵa.

Ngakhale kuti mankhwalaŵa sachiritsa, athandiza kuti anthu okhala ndi kachilombo ka HIV asamafe ambiri makamaka m’mayiko olemera. Anthu ambiri amanena kuti n’kofunika kwambiri kupereka mankhwalaŵa ku mayiko osauka. Komano mankhwalaŵa ngokwera mtengo ndipo anthu ambiri m’mayiko otere sangawakwanitse n’komwe.

Zimenezi zikupangitsa anthu kudzifunsa kuti: Kodi ndalama n’zofunika kuposa moyo wa anthu? Mkulu wa bungwe la ku Brazil loona za kachilombo ka HIV ndiponso matenda a Edzi, dzina lake Dr. Paulo Teixeira anavomereza kuti zinthu sizilidi bwino ponena kuti: “Sitingalole kuti anthu ambirimbiri azidzivutikira okha pofuna kupeza mankhwala owathandiza chifukwa chongoti ena akufuna kupezerapo phindu mwa kudyera anthu masuku pamutu.” Iye anapitiriza kunena kuti: “Zimandifoola nkhongono kwambiri n’kamaona anthu akuganizira kwambiri za ndalama kuposa za anthu.”

Pali mayiko ochepa chabe amene anyalanyaza malamulo ena amakampani aakuluakulu popanga okha kapena kuitanitsa mankhwala opangidwa ndi makampaniwo motsika mtengo kwambiri. * Ofufuza ena anapeza kuti, “mitengo yotsika kwambiri ya mankhwalaŵa inali yotsika ndi madola 82 pa madola 100 aliwonse poyerekezera ndi mitengo ya mankhwalaŵa ku United States,” inatero magazini ya South African Medical Journal.

Mavuto Okhudza Kupereka Chithandizo

Kenaka, makampani akuluakulu opanga mankhwala anayamba kuwatsitsira mitengo ya mankhwala a Edzi mayiko osauka ofuna kwambiri mankhwalaŵa. Ankaganiza kuti potero ndiye kuti anthu ambiri apindula nawo mankhwalaŵa. Komabe pali mavuto ena aakulu ofunika kuwathetsa kuti mankhwalaŵa azipezeka mosavuta m’mayiko osauka. Kukwera mtengo ndi lina mwa mavuto ameneŵa. Ngakhale atawatsitsa mtengo kwambiri, anthu ambiri amene amafunikira mankhwalaŵa sangakwanitsebe kugula.

Vuto linanso n’lakuti mankhwalaŵa ngovuta kupereka kwa odwala popanda kuwayang’anira bwino. Tsiku lililonse odwala ayenera kumwa mapilisi ambirimbiri, panthaŵi yake. Ngati odwalawo sakumwa mankhwalawo molondola kapena ngati walekeza panjira osawamaliza, angathe kudzakhala ndi tizilombo ta HIV tosamva mankhwala otere. Mmene zinthu zilili ku Africa kuno m’povuta kutsimikizira kuti odwala akumwabe mankhwalaŵa moyenerera chifukwa tilibe chakudya chokwanira, madzi akumwa ngovuta, ndiponso zipatala n’zochepa.

Chinanso n’chakuti anthu amene akumwa mankhwalaŵa ayenera kuyang’aniridwa. Ngati matendaŵa afika posamva mankhwala, odwalawo ayenera kusintha ena mwa mankhwalawo. M’pofunikanso anthu oidziŵa bwino ntchito ya zachipatala, ndipo kuyeza anthu odwalaku kumafunika ndalama zambiri. Chinanso n’chakuti mankhwalaŵa amabweretsa mavuto ena, ndipo pali tizilombo tina ta matendaŵa timene tayamba kuwazoloŵera mankhwalaŵa.

Mwezi wa June chaka cha 2001 pa msonkhano wapadera wokambirana za Edzi umene Gulu Loyang’anira Ntchito za Bungwe la United Nations unakonza, anakambirana zokhazikitsa thumba lothandiza pa zaumoyo padziko lonse kuti lizithandiza mayiko osauka. Anati, thumbali limafunika ndalama zokwana madola mabiliyoni 7 kapena mpaka mabiliyoni 10. Koma pakali pano ndalama zimene mayiko alonjeza kuti apereka ku thumba limeneli n’zopereŵera kwambiri.

Asayansi sakukayikira n’komwe kuti adzapeza katemera wa Edzi, ndipo akatemera ena otere ayamba kale kuwayesa m’mayiko osiyanasiyana. Ngakhale ntchito imeneyi itayenda bwino, patenga zaka zingapo ndithu asanatulukire katemera wotere, n’kumuyesa, n’kutsimikiziradi kuti anthu angathe kum’gwiritsa ntchito bwinobwino.

Mayiko ena, monga Brazil, Thailand ndi Uganda, zinthu zawayendera bwino kwambiri pa ntchito yopereka chithandizo kwa anthu odwala. Dziko la Brazil limagwiritsira ntchito mankhwala opangidwa komweko, ndipo latha kuchepetsa ndi theka anthu ofa ndi matenda obwera chifukwa cha Edzi. Dziko la anthu ochepa kwambiri la Botswana, limene lili ndi ndalama zokwanira zothandizira kulimbana ndi matendaŵa, likuyesetsa kupereka mankhwalaŵa kwa anthu onse amene akuwafuna m’dzikomo ndipo likuyesetsa kupereka chithandizo chofunikira.

Kugonjetsa Edzi

Kusiyana kumodzi kwakukulu pakati pa mliri wa Edzi ndi miliri ina yonse n’kwakuti mliriwu ungathe kupeŵedwa. Ngati anthu atafuna kutsatira mfundo zikuluzikulu za makhalidwe abwino za m’Baibulo angathe kupeŵa matendaŵa m’njira zambiri.

Mfundo za m’Baibulo zimenezi n’zosachita kupita m’mbali. Anthu osakwatirana ayenera kudzisunga. (1 Akorinto 6:18) Anthu okwatirana ayenera kukhulupirika ndipo sayenera kuchita chigololo. (Ahebri 13:4) Kumvera malangizo a m’Baibulo akuti tisale magazi kumatetezeranso.—Machitidwe 15:29, 30.

Anthu amene anatenga kale matendaŵa angathe kupeza chimwemwe chachikulu ndi chilimbikitso pophunzira za dziko lopanda matenda limene Mulungu walonjeza kuti libwera posachedwa ndipo akatero azichita zinthu zogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna.

Baibulo limatitsimikizira kuti nthaŵi yake ikadzakwana mavuto onse a anthu kuphatikizapo matenda, adzatha. Lonjezo limeneli lili m’buku la Chivumbulutso ndipo limati: “Ndinamva mawu akulu ochokera ku mpando wachifumu, ndi kunena Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4.

Mawu amenewo sakunena za anthu okhawo amene angakwanitse kugula mankhwala okwera mtengo. Ulosi wa lonjezo wa pa Chivumbulutso 21 umenewu umatsimikiziridwa pa Yesaya 33:24 pamene pamati: “Ndipo wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” Zikadzatero anthu onse okhala padziko lapansi azidzatsatira malamulo a Mulungu ndipo adzakhala ndi thanzi langwiro. Motero mliri wopulula anthu wa Edzi pamodzi ndi matenda ena onse, adzathetsedweratu mpaka kalekale.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Mankhwala otere amawapanga motsanzira mankhwala amene makampani ena opanga mankhwala amapanga. Mayiko amene ali m’Bungwe Loona Zamalonda la Padziko Lonse amaloledwa mwalamulo kupanga mankhwala a makampani enaake pakachitika zinthu zamwadzidzidzi.

[Bokosi/Zithunzi pamasamba 9, 10]

AŴA NDIWO MANKHWALADI AMENE NDAKHALA NDIKUFUNA

Ndimakhala m’dziko lina la kum’mwera kwa Africa, ndipo ndili ndi zaka 23. Tsiku limene ndinadziŵa kuti ndili ndi kachilombo ka HIV ndimalikumbukira mpaka pano.

Ndinali ndi amayi anga m’chipinda choonerana ndi dokotala ndipo dokotalayo anandiuzira nkhani imeneyi m’chipindamu. M’moyo wanga wonse, palibe nkhani imene inandipwetekapo moyo koposa imeneyi. Ndinasokonezeka maganizo. Sindinakhulupirire kuti n’zoona. Ndinkangoti mwina alakwitsa poyeza matendawo. Malovu anauma mkamwa ndipo ndinangoti kakasi. Ndinkafuna kulira koma m’maso munali gwaa. Dokotalayo anayamba kuwauza amayi anga zina n’zina kuphatikizapo zokhudza mankhwala ochepetsa mphamvu ya kachilomboka koma ine maganizo anali pwirikiti moti zinkangoloŵera m’khutu limodzi n’kutulukira linalo.

Ndinadziŵa kuti anandipatsa matendaŵa ndi mnyamata winawake ku yunivesite kumene ndinkaphunzira. Ndinkafunitsitsa nditalankhula ndi winawake amene akanatha kundimvetsa maganizo anga, koma n’taganizaganiza sindinathe kupeza wina aliyense. Ndinayamba kudziona ngati wopanda ntchito ndiponso wolephera. Achibale ankayesetsa kundilimbikitsa koma ndinkangoona kuti kwaine kwatha basi ndipo ndinali ndi mantha. Pali zinthu zambirimbiri zimene ndinkalakalaka kudzachita m’tsogolo monga amachitira wachinyamata aliyense. Kunangotsala zaka ziŵiri zokha kuti ndimalize maphunziro a digiri yanga yoyamba ya za sayansi, koma zitangochitika izi basi ndinaiŵalako zonsezo.

Ndinayamba kumwa mankhwala ochepetsa mphamvu ya kachilomboka ndipo ndinapitanso kwa alangizi osiyanasiyana a matendaŵa, komabe ndinali wolefuka mtima kwambiri. Ndinapemphera kuti Mulungu andionetse Chikristu chenicheni ndisanafe. Ndinali m’tchalitchi chinachake cha Pentekositi koma palibe aliyense wam’tchalitchichi amene anabwera kudzandizonda. Ndinkafuna kudziŵa kuti kodi kwenikweni ndikadzamwalira ndidzapita kuti?

Tsiku lina m’maŵa cha kumayambiriro kwa mwezi wa August m’chaka cha 1999, anthu aŵiri a Mboni za Yehova anagogoda pakhomo pathu. Tsiku limeneli ndinali nditadwalika kwambiri komabe ndinatha kukhazikika pa balaza. Ndinalonjerana nawo azimayi aŵiriwo ndipo anandiuza kuti akuthandiza anthu kuphunzira Baibulo. Apa ine mtima unakhala pansi poona kuti mapemphero anga aja ayankhidwa. Koma n’kuti ndili wofooka kwambiri mwakuti sindinathe kuŵerenga kapena kumvetsera kwa nthaŵi yaitali.

Komabe, ndinawauza kuti ndikufuna kuphunzira Baibulo, ndipo tinapangana nthaŵi yoti adzabwerenso. Tsoka ilo tsikuli lisanafike, ndinagonekedwa m’chipatala chifukwa cha vuto la maganizo. Ananditulutsa nditakhalamo milungu itatu ndipo nditaona kuti Amboniwo sanandiiwale mtima wanga unakhala m’malo. Ndikukumbukira kuti mayi m’modziyo ankakonda kudzandifunsa za moyo wanga. Apa n’kuti ndikupezako bwino ndithu, ndipo ndinayamba kuphunzira Baibulo cha kumapeto kwa chakacho. Komabe vuto langa linachititsa kuti ndizivutika kwambiri pophunzira. Koma mayi amene ankaphunzira naneyo anali womvetsa zinthu ndiponso woleza mtima.

Ndinachita chidwi kwambiri nditaphunzira za Yehova ndi makhalidwe ake kuchokera m’Baibulo, komanso nditaphunzira za tanthauzo lenileni la kum’dziŵa Yehovayo ndiponso kuyembekezera moyo wosatha. Kwa nthaŵi yoyamba ndinamvetsetsanso chifukwa chimene anthu amavutikira. Ndinasangalala kwambiri kudziŵa za Ufumu wa Mulungu umene posachedwapa udzaloŵe m’malo mwa maboma onse aanthu. Zinandichititsa kuti ndisinthiretu moyo wanga.

Aŵa ndiwo mankhwaladi amene ndakhala ndikufuna. Kudziŵa kuti Yehova amandikondabe ndiponso kuti amandiganizirabe kunandilimbikitsa kwambiri! Poyamba, ndinkaganiza kuti Mulungu sandikonda ndipo n’chifukwa chake ndinatenga matenda ameneŵa. Koma ndinaphunzira kuti Yehova mwachikondi anakonza kuti anthu azikhululukidwa machimo kudzera m’nsembe ya dipo ya Yesu Kristu. Tsopano ndinazindikira kuti Mulungu amandiganizira, monga mmene lemba la 1 Petro 5:7 limanenera kuti, ‘tayani pa iye nkhaŵa zanu zonse pakuti iye asamalira inu.’

Ndikuyesetsa kwambiri kukhala mnzake wapamtima wa Yehova pophunzira Baibulo tsiku lililonse ndiponso popita kumisonkhano ku Nyumba ya Ufumu. Inde nthaŵi zina ndimavutika ndithu koma nkhaŵa zanga zonse ndimazitaya m’manja mwa Yehova popemphera kuti andipatse mphamvu komanso kuti andilimbikitse. Anthu akumpingo nawonso amandithandiza, motero ndine wosangalala.

Nthaŵi zambiri ndimachita nawo ntchito yolengeza uthenga wabwino pamodzi ndi mpingo wanga. Ndikufuna kuthandiza anthu ena pankhani yauzimu, makamaka amene ali ndi vuto langati limene ndili nalo ineli. Ndinabatizidwa m’December 2001.

[Chithunzi]

Nditadziŵa za Ufumu wa Mulungu ndinasangalala kwambiri

[Chithunzi patsamba 8]

Gulu lolangiza anthu za matenda a Edzi ku Botswana

[Chithunzi patsamba 10]

Padziko lapansi la Paradaiso, anthu onse adzakhala ndi thanzi langwiro