“Sipanakhaleko Mliri Wosakaza Kwambiri Chonchi N’kale Lonse”
“Sipanakhaleko Mliri Wosakaza Kwambiri Chonchi N’kale Lonse”
YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU SOUTH AFRICA
“Padziko pano palibe nkhondo imene yasakaza anthu koposa mliri wa Edzi.”—ANATERO A COLIN POWELL OMWE NDI NDUNA YA ZAM’DZIKO YA KU UNITED STATES.
NTHAŴI yoyamba kuti pamveke zakuti kwabwera matenda owononga chitetezo cha thupi otchedwa Edzi inali mu June 1981. A Peter Piot, omwe ndi mkulu wa nthambi ya bungwe la United Nations yoona za matendaŵa yotchedwa UNAIDS anati: “Pa anthu tonse amene tinkalimbana ndi matenda a Edzi atangobwera kumene panalibe aliyense amene ankaganizako zakuti matendaŵa angadzasanduke mliri waukulu motere.” Chibwerereni, mliriwu watha zaka 20 tsopano ndipo wasanduka mliri waukulu koposa miliri ina yonse imene inakhalapo ndiponso zikuoneka kuti upitirirabe kufala.
Akuti anthu oposa 36 miliyoni ali ndi kachilombo kowononga chitetezo cha thupi ka HIV kamene kamayambitsa matenda a Edzi, ndipo anthu enanso 22 miliyoni afa nawo kale matendaŵa. * M’chaka cha 2000, anthu 3 miliyoni anafa ndi Edzi padziko lonse, ndipo aka kanali koyamba kuti anthu ambiri chonchi afe ndi matendaŵa m’chaka chimodzi chokha ngakhale kuti ena, makamaka a m’mayiko olemera ankagwiritsira ntchito mankhwala ochepetsa mphamvu ya kachilombo koyambitsa matendaŵa.
Mliri wa Edzi Ukufala mu Africa
M’mayiko a m’dera lino la kum’mwera kwa chipululu cha Sahara kuli anthu odwala matendaŵa mwina opitirira 25 miliyoni ndipo n’kumene mliriwu ukusakaza kwambiri. M’dera limeneli lokha, anthu pafupifupi 2 miliyoni ndi theka anafa ndi matendaŵa m’chaka cha 2000, kutanthauza kuti pa anthu 10 aliwonse amene anafa ndi Edzi padziko lonse 8 anali a m’derali. Matenda a Edzi ndi amene akupha anthu ambiri m’dera limeneli. *
M’dziko la South Africa ndi mmene muli anthu ambiri odwala
matendaŵa kuposa m’dziko lina lililonse, ndipo akuti angotsala pang’ono kukwana 5 miliyoni. M’dzikolo, mwezi uliwonse mumabadwa ana 5,000 okhala ndi kachilombo ka HIV. M’mawu ake pa msonkhano wa nambala 13 wa padziko lonse wokambirana za matendaŵa womwe unachitikira ku Durban mu July 2000, mtsogoleri wakale wa dziko la South Africa a Nelson Mandela anati: “Tinagwidwa nthumanzi kwambiri kumva kuti ku South Africa kuno pa achinyamata aŵiri aliwonse m’modzi adzafa ndi matenda a Edzi. Ndipo chokhumudwitsa kwambiri n’chakuti matendaŵa ndiponso mavuto onse amene matendaŵa amatibweretsera anthufe . . . akanatha kupeŵedwa ndiponso angathe ndithu kupeŵedwa.”Edzi Ikufalanso Kwambiri M’mayiko Ena
Anthu amene akutenga matendaŵa akuchulukanso kwambiri m’mayiko a kum’maŵa kwa Ulaya, ku Asia ndi ku Caribbean. Kumapeto kwa chaka cha 1999, mayiko a kum’maŵa kwa Ulaya anali ndi anthu 420,000 odwala matendaŵa. Kumapeto kwa chaka cha 2000, akuti anthuwo anawonjezeka n’kufika pa 700,000 mwinanso kuposa pamenepa.
Atafufuza m’mizinda ikuluikulu isanu ndi umodzi ya ku America, anapeza kuti anyamata opitirira 12 pa anyamata 100 aliwonse ogonana ndi amuna anzawo anali ndi kachilombo ka HIV. Ndiponso pagululo ndi anyamata 29 okha pa anyamata 100 amene ankadziŵa kuti ali ndi kachilomboka. Katswiri wofufuza za kufala kwa matendaŵa yemwe anatsogolera kufufuzaku anati: “Zinatikhumudwitsa kwambiri kuona kuti ndi amuna ochepa chabe amene ali ndi kachilomboka amene akudziŵa kuti ali nako. Kutanthauza kuti anthu amene angotenga kumene matendaŵa akumawafalitsa mosadziŵa.”
Pamsonkhano wina wa akatswiri odziŵa bwino za matenda a Edzi ku Switzerland womwe unachitika mu May 2001, anati, “sipanakhaleko mliri wosakaza chonchi n’kale lonse.” Paja tanena kale kuti Edzi yafala kwambiri m’mayiko a kuno kum’mwera kwa chipululu cha Sahara. Nkhani yathu yotsatira ilongosola chifukwa chake.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 5 Chiŵerengero chimenechi n’chimene bungwe la UNAIDS linafalitsa litaŵerengetsera mongoyerekezera.
^ ndime 7 Onani magazini ya Galamukani! ya March 8, 2001, masamba 14 mpaka 15.
[Mawu Otsindika patsamba 3]
“Ndipo chokhumudwitsa kwambiri n’chakuti matendaŵa . . . ndiponso mavuto onse amene matendaŵa amatibweretsera . . . akanatha kupeŵedwa ndiponso angathe ndithu kupeŵedwa.”—ANATERO A NELSON MANDELA
[Chithunzi pamasamba 2, 3]
Anthu ambiri amene ali ndi kachilombo ka HIV sadziŵa kuti ali nako
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
UN/DPI Photo 198594C/Greg Kinch