Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zipembedzo Zinakakumana ku Assisi Pofuna Mtendere

Zipembedzo Zinakakumana ku Assisi Pofuna Mtendere

Zipembedzo Zinakakumana ku Assisi Pofuna Mtendere

“Sitikufunanso zachiwawa! Sitikufunanso nkhondo! Sitikufunanso zauchigaŵenga! Tikupempha m’dzina la Mulungu kuti chipembedzo chilichonse chithandize kuti padzikoli pakhale chilungamo ndi mtendere, kukhululukirana ndi kulemekeza moyo, ndiponso chikondi!”—Anatero Papa Yohane Paulo Wachiŵiri.

PA JANUARY 24, 2002, nthumwi zoimira zipembedzo zosiyanasiyana padziko lonse zinasonkhana m’tauni ya Assisi, ku Italy kuti zipempherere mtendere womwe ukusoŵa chifukwa cha uchigaŵenga, kusalolerana ndiponso kupanda chilungamo. Papa ndiye anaitanitsa msonkhanowo patangotha miyezi iŵiri Nyumba Ziŵiri Zosanja zitagwa mumzinda wa New York City. Akuluakulu a zipembedzo ambiri sananyinyirike n’komwe atamva pempho la ku Vatican limenelo.

Kumbuyoku, papayu anaitanitsa anthu kaŵiri konse kuti akhale ndi tsiku lamapemphero m’tauni yomweyi ya ku Italy. Koyamba kanali m’chaka cha 1986 ndipo kachiŵiri m’chaka cha 1993. * Atolankhani oposa 1,000 ochokera m’mayiko osiyanasiyana anapitako kukakhala nawo pamsonkhano wa m’chaka cha 2002. Zipembedzo zambiri za m’Matchalitchi Achikristu (Akatolika, a Lutheran, Anglican, Orthodox, Methodist, Baptist, Pentecostal, Mennonite, Quakers ndi zina zotero), komanso zipembedzo za Chisilamu, Chihindu, Chikofyusiyasi, Chisiki, Chijaini, Chitenirikiyo, Chibuda, Chiyuda, zipembedzo za makolo a anthu akuda, Chishinto ndiponso Chizorowasita, zinali ndi nthumwi zawo pamapemphero a mtenderewo. Kunalinso nthumwi zochokera m’zipembedzo zina komanso nthumwi ya Bungwe Loona za Matchalitchi Padziko Lonse.

Zimene Ananena Polimbikitsa Mtendere

Zochitika za tsikuli zinayamba m’maŵa nthaŵi ya 8:40, pamene sitima ya pamtunda imene inanyamula anthu opita kumsonkhanowo inanyamuka pa siteshoni ina yaing’ono ku Vatican. Sitimayo inali ndi mabogi seveni okonzedwa bwino kwambiri, ndipo ndege ziŵiri zamtundu wa helikoputala zinatsagana ndi sitimayo poonetsetsa kuti chitetezo chilipo. Ulendo umenewu wa papa pamodzi ndi akuluakulu ena a zipembedzo zina unawatengera maola aŵiri kuti akafike ku Assisi. Anakhwimitsa chitetezo kwabasi ndipo panali apolisi pafupifupi 1,000 omwe anali tcheru.

Akuluakuluŵa anasonkhana pa chikhonde chachikale chofoleredwa ndi chilona chachikulu zedi. M’kati mwake munali chibwalo chofiira, chosongoka changati chilembo cha V, ndipo akuluakulu oimira zipembedzo zawo anakhala m’menemo, ndipo mpando wa papa ndiwo unali pakati penipeni. Cha kumbali kwa chibwalocho kunali mtengo wa azitona, umene unali kuimira mtendere. Kumaso kwa bwalolo kunali alendo oposa 2,000 omwe anachita kuwasankha. Ndipo akuluakulu ena a ku Italy anakhala mzera wakutsogolo. Makwaya oimba modolola mtima ankaimba nyimbo zawo zotchula zamtendere munthu wina akamaliza kulankhula. Kumadera ena a tauniyo, anthu osaŵerengeka, makamaka achinyamata ankasonyeza zikwangwani zokhala ndi mawu odana ndi nkhondo m’zinenero zambirimbiri n’kumaimba nyimbo zokhudza mtendere. Anthu ambiri ananyamula nthambi za mtengo wa azitona.

Atakhala pampando wake, papayo anauza nthumwi za zipembedzo zosiyanasiyanazo kuti zalandiridwa ndi manja aŵiri pamsonkhanowo. Kenaka atatha kuimba m’Chilatini nyimbo imene inkatchula mawu a pa Yesaya 2:4, omwe amalosera nthaŵi imene “mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina,” anthu ambiri mwa nthumwizo, aliyense atavala mogwirizana ndi chipembedzo chake, analankhula zakukhosi kwake polimbikitsa kuti kukhale mtendere. Mwachitsanzo ena analankhula zotsatirazi.

“Panopa mmene zinthu zililimu anthu akufunika kuona zinthu zosonyeza mtendere ndiponso kumva mawu owalimbikitsa.”—Anatero Kadinala François Xavier Nguyên Van Thuân.

Mulungu “si wankhondo kapena wamikangano ayi koma ndi Mulungu wamtendere.”—Anatero Bartholomeus Woyamba, yemwe ndi mkulu wa mabishopu a matchalitchi a Orthodox.

“Kusiyana kwa zipembedzo kusapangitse [anthu] kuti azinyalanyaza kapena kudana ndi ena amene sali m’chipembedzo chawo.”—Anatero Dr. Setri Nyomi, wa m’bungwe la World Alliance of Reformed Churches.

“Zinthu ziŵiri zomwe zingakhazikitsedi mtendere weniweni pakati pa anthu ndizo chilungamo ndi chikondi chenicheni.”—Anatero Chief Amadou Gasseto yemwe ankaimira zipembedzo za makolo a anthu akuda.

“Mtendere wokha ndiwo wopatulika, koma nkhondo ayi!”—Anatero Andrea Riccardi, wa Tchalitchi cha Katolika.

Nthumwi zina zinavomereza kuti zipembedzo ndizo zili ndi mlandu waukulu wolimbikitsa kusalolerana ndiponso nkhondo. Nthumwi yoimira gulu la matchalitchi a Lutheran padziko lonse inanena kuti anthu padzikoli akhala “asakugwirizana chifukwa cha chidani chachikulu choyambitsidwa ndi anthu aliuma pankhani zachipembedzo.” Nthumwi yoimira Chiyuda inati: “Zipembedzo zalimbikitsa nawo kuti pakhale nkhondo zambiri zoopsa kwabasi ndiponso zopulula anthu.” Nthumwi yoimira Chihindu inalengeza kuti: “M’mbuyo monsemu zakhala zikuoneka kuti anthu amene amadzitama kuti akumanga chipembedzo akhala akupangitsa chipembedzocho kulamulira anthu pazochita zawo ndiponso kuwasemphanitsa maganizo.”

Nthumwizo zitanena zinthu zambiri zodzudzula uchigaŵenga ndiponso nkhondo, zinabalalika, aliyense n’kupita komwe anauzidwa n’kumakapempherera mtendere kwa mulungu amene amam’pembedza.

Kupempherera Mtendere

Nthumwi zoimira zipembedzo za Matchalitchi Achikristu zinapempherera pamodzi m’tchalitchi cha St. Francis, pafupi ndi manda amene amatchedwanso ndi dzina lomweli. Mwambowu unayamba ndi pemphero lonena za Utatu lakuti, “Dzina la atate ndi la mwana ndi la mzimu woyera,” limene papa ndi nthumwi zina zitatu anatsogolera. Ankati akapempherapemphera ankadukiza ndi nyimbo ndipo m’mapempherowo ankatamanda mtendere komanso ankaŵerenga malemba a m’Baibulo otchula za nkhani yomweyo. Wina popemphera anapempha kuti anthu akhale ndi “chikhulupiriro chonse.” Pomalizira pa mwambowu, onse amene analipo anaimba nyimbo ya m’Chilatini yotchula pemphero la Atate Wathu, lochokera pa lemba la Mateyu chaputala 6, mavesi 9 mpaka 13.

Pa nthaŵi yomweyo, nthumwi za magulu a zipembedzo zina n’kuti zikupempheranso m’timagulu tawotawo. Asilamu anali mu holo yomwe inayang’ana ku Mecca atagwada pansi, akupemphera kwa Allah. Azolowasita omwe ankapemphera moyandikana ndi Ajaini ndiponso Akonfyusiyasi, anakoleza moto wopatulika. Nthumwi zoimira zipembedzo za makolo a anthu akuda zinkapemphera kwa mizimu ya makolo awo. Ahindu ankapempha mtendere kwa milungu yawo. Onse ankachita mogwirizana ndi mmene amapembedzera.

Anagwirizana Chimodzi Kuti Kukhale Mtendere

Nthumwizo zinabwereranso pachikhonde chija kuti zimalize msonkhanowo. Kenaka amonke akuoneka kuti atenga zinthu zopatulika anapereka nyali zoyaka kwa nthumwi zonse. Nyalizo zinali kuimira chiyembekezo choti kukhala mtendere. Zimene ankachitazo zinali zochititsa chidwi kwabasi. Kenaka nthumwi za magulu osiyanasiyana zinaŵerenga mfundo zosiyasiyana zokhala ndi cholinga chimodzi choti kukhale mtendere.

“Kuti tikhale pamtendere m’pofunika kuti tizikondana ndi anansi athu.”—Anatero Bartholomeus Woyamba, yemwe ndi mkulu wa mabishopu a matchalitchi a Orthodox.

“Tikamati chipembedzo ndiye kuti n’zosemphana kwambiri ndi zachiwawa ndiponso zauchigaŵenga.”—Anatero Dr. Konrad Raiser, nthumwi ya Bungwe Loona za Matchalitchi Padziko Lonse.

“Tikudzipereka ndi mtima wonse kuti tiphunzitse anthu kulemekezana ndiponso kuonana kuti aliyense ndi wofunika.”—Anatero Bhai Sahibji Mohinder Singh, nthumwi ya chipembedzo cha Chisiki.

“Mtendere wopanda chilungamo si mtendere weniweni.”—Anatero Vasilios, Bishopu wa chipembedzo cha Orthodox.

Potsirizira, m’pamene papa anaŵerenga mawu amene ali kuchiyambi kwa nkhaniyi. Msonkhano wa anthu osiyana zikhulupirirowu utafika pamapeto nthumwi zonsezo zinayamba kukumbatirana posonyeza mtendere. Nthumwizo zinalankhula mawu akupsa ndipo pambuyo pake panali mwambo wadzaoneni. Komabe, kodi msonkhano wochititsa kasowu utatha anthu anachita zotani?

‘Akanamachita Zimene Amanena’

Manyuzipepala ndiponso ma TV anatama papa poganiza zoitanitsa msonkhanowo. Ena anafika mpaka ponena kuti papa ndiye “wolankhulira Matchalitchi onse Achikristu.” Nyuzipepala ya ku Vatican yotchedwa L’Osservatore Romano inasimba za tsiku la msonkhano wa ku Assisi kuti linali “chiyambi chobweretsa mtendere.” Tsamba loyamba la nyuzipepala yotchedwa Corriere dell’Umbria linali ndi mutu waukulu wakuti “Mfundo za ku Assisi Zikuonetsa Kuti Mtendere Ungatheke.”

Si kuti onse omwe analipo zinawagwira mtima kwenikweni. Ena anakayikira chifukwa chakuti kumbuyoku, m’chaka cha 1986 ndiponso 1993 kunali masiku ena opempherera mtendere, koma anthu akuvutitsidwabe ndi nkhondo zomenyedwa m’dzina la chipembedzo. Kudana chifukwa cha zipembedzo kwaphetsa anthu ambiri m’dziko la Uganda, dziko lomwe kale ankalitcha Yugoslavia, Indonesia, Pakistan, Middle East ndiponso ku Northern Ireland.

Nyuzipepala ya ku Italy yotchedwa La Repubblica inanena kuti ena osagwirizana ndi msonkhanowo anafotokoza kuti unali “wachiphamaso chabe.” Phungu wina wa Nyumba ya Malamulo ku Ulaya ananena kuti ngati anthu opembedza akufuna kulimbikitsa mtendere ayenera “kuchita zimene Uthenga Wabwino umanena,” kuti “kondani adani anu, muwatembenuzire tsaya linalonso.” Iye akuona kuti zimenezi “palibe aliyense amene akuzichita.”

Pulezidenti wa bungwe la Ayuda a ku Italy ananena kuti “talekani tione kuti achitapo chiyani pa zimene anenazi, tione ngati achitedi zinthu zogwirizana ndi zimenezi.” Nthumwi yoimira Abuda a ku Italy inanena maganizo ake ofanana ndi omweŵa ponena kuti ndi bwino “kuonetsetsa kuti mawu opempha kuti kukhale mtendere asamakhale ongowatchula m’pakamwa pokha ayi.” Mtolankhani wina polemba m’magazini a ku Italy otchedwa L’Espresso ananena kuti kwa nthumwi za Matchalitchi Achikristu, msonkhano wa ku Assisi unali n’cholinga china. Iye anati msonkhanowo unalinso n’cholinga “choletsa anthu kusiya kukonda zachipembedzo, kusamvera zipembedzo, ndiponso kusakhulupirira zipembedzo,” komanso unali n’cholinga choletsa “anthu ambiri kusiya kupembedza” limene lili vuto lalikulu kwambiri ku Ulaya ngakhale kuti “kumeneko Chikristu chinayamba kale kwambiri.”

Ena mwa anthu omwe anadana kwambiri ndi msonkhanowo anali anthu ofuna kuti Chikatolika chisasinthe, omwe ankaopa kuti miyambo ya tchalitchi chawo iwonongedwa. Polankhula pa wailesi yakanema, Vittorio Messori, yemwe ndi Mkatolika wotchuka kwambiri pa zolembalemba anati zimene zinachitika ku msonkhano wa ku Assisi zingachititse anthu kulephera kusiyanitsa bwinobwino zipembedzo. N’zoonadi kuti akuluakulu amatchalitchiwo anayesetsa kuti asachititse anthu kuona ngati kuti akuphatikiza zipembedzo. Papa weniweniyo ananenapo mawu otsutsa maganizo oterowo. Komabe, anthu ambiri anaona kuti malinga ndi mmene msonkhanowo unalili, zinasonyeza kuti zipembedzo zosiyanasiyanazo zangokhala njira zosiyanasiyana zolankhulirana ndi Mulungu m’modzi yemweyo.

Nkhani ya Chipembedzo ndi Mtendere

Kodi magulu azipembedzo zotchuka ayenera kutani kuti abweretse mtendere? Anthu ena amaona kuti sitifunika kufunsa choncho, chifukwa chakuti zipembedzo zikuoneka kuti ndizo zikuchita zinthu zambiri zoyambitsa nkhondo kuposa kuletsa nkhondozo. Akatswiri a mbiri yakale analembapo mmene olamulira mayiko agwiritsira ntchito zipembedzo polimbikitsa nkhondo. Komabe funso n’lakuti: N’chifukwa chiyani zipembedzozo zalola kuti azigwiritsire ntchito choncho?

Komatu zipembedzo za Matchalitchi Achikristu zili ndi lamulo lopatulika limene likanawathandiza kupeŵa mlandu wokhudzana ndi nkhondo. Yesu ananena kuti om’tsatira sangakhale “a dziko lapansi.” (Yohane 15:19; 17:16 ) Kukanakhala kuti zipembedzo za Matchalitchi Achikristu zikutsatira mawu amenewo, si bwenzi zitagwirizana ndi olamulira andale, n’kuvomereza ndiponso kudalitsa asilikali komanso nkhondo.

Kunenadi zoona, kuti zipembedzo zichite zinthu mogwirizana ndi mawu amene ananenedwa ku Assisi, akuluakulu a zipembedzozo ayenera kusiyana nawo akuluakulu andale. Chinanso n’chakuti ayenera kuphunzitsa anthu awo zinthu zamtendere. Komabe akatswiri a mbiri yakale amati padziko lonse anthu ambiri amene amachita zachiwawa amakhala anthu okhulupirira Mulungu, kapena amene amanena ndithu kuti amam’khulupirira. Nkhani ina yolembedwa ndi mkonzi mu nyuzipepala inayake inati: “Patangotha masiku ochepa chabe kuchokera pa September 11, munthu wina analemba pakhoma lina ku Washington D.C. mawu opatsa maganizo akuti: ‘Wokondedwa Mulungu, mutipulumutse m’manja mwa anthu amene amakukhulupirirani.’”

Msonkhano wadzaoneni wa ku Assisiwo sunayankhe mafunso ena ovuta kuyankha. Komabe mwina palibenso funso lofunika kwambiri, kapena kuti losautsa kwambiri kwa anthu opembedza kuposa ili lakuti: Kodi n’chifukwa chiyani mpaka panopa zikuoneka kuti Mulungu sakufuna kuyankha mapemphero a zipembedzo za padziko lonse oti kukhale mtendere?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Kuti mumve zambiri za nkhani ya tsiku la mapemphero a mtendere la mu 1986, chonde onani magazini ya Galamukani! ya December 8, 1987.

[Chithunzi patsamba 23]

Nthumwi zitanyamula nyali zoyaka zoimira chiyembekezo choti kukhala mtendere

[Mawu a Chithunzi]

AP Photo/Pier Paolo Cito

[Mawu a Chithunzi patsamba 21]

AP Photo/Pier Paolo Cito