Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chikondi Chinaokera Pothandiza Anthu Amene Tsoka Lalikulu Linawagwera

Chikondi Chinaokera Pothandiza Anthu Amene Tsoka Lalikulu Linawagwera

Chikondi Chinaokera Pothandiza Anthu Amene Tsoka Lalikulu Linawagwera

MKONZI wa nyuzipepala yotchedwa Houston Chronicle dzina lake Richard Vara, yemwe amaidziŵa bwino ntchito yake, sayamikira ena wambawamba. Koma chaka chatha anakanika kuti asatero. “Ine sindinaonepo zoterezi, ndipo sindikukhulupirira kuti izi zachitikadi!” anagoma motero. Nayenso mkulu woyang’anira mzinda wa Houston, ku Texas m’dziko la America, dzina lake Lee P. Brown anagoma. Iye anati: “Ndikulakalaka aliyense mumzinda uno akanaona zimene mwachita. Ndagoma nazo kwambiri.” Kodi anthuŵa ankakamba za nkhani yanji? Mkonziyu ndi mkuluyu ankakamba za ntchito yothandiza anthu amene anaona tsoka imene Mboni za Yehova zinagwira mumzinda wa Houston. Kodi pantchitoyi panachitika zotani? N’chifukwa chiyani inali yoti igwirike basi? Ndipo n’chiyani chinagometsa kwambiri anthu pantchitoyi? Kuti tiitsate bwinobwino nkhaniyi, tiyeni tiyambire pachiyambi penipeni.

Kusefukira kwa Madzi Komwe Sikunachitikepo N’kale Lonse

Kumayambiriro kwa mwezi wa June chaka cha 2001, chimvula cha mkuntho choopsa chomwe anachipatsa dzina loti Allison, chinakantha dera lopanda zitunda la kum’mwera cha kum’maŵa kwa boma la Texas. Lachisanu, June 8, chimvulachi chinatsakamuka modetsa nkhaŵa usana ndi usiku wonse mumzinda wa Houston, womwe ndi wachinayi kukula pa mizinda yonse ya ku America. * Pakanthaŵi kochepa chabe, madzi analoŵerera m’masitolo, maofesi ndiponso m’nyumba zankhaninkhani. Misewu ikuluikulu ya mumzindawu inasanduka mitsinje yoopsa ya madzi omwe anachititsa kuti magalimoto aang’ono ndi aakulu omwe asathe kuyenda ngakhale pang’ono. Madziŵa analepheretsa ngakhale magalimoto ozimitsa moto pamodzi ndi magalimoto othandiza pangozi kudutsa m’misewu ina. Ndege zamtundu wa helikoputala ndiponso zimagalimoto zamphamvu zankhondo anazigwiritsira ntchito populumutsa anthu.

Kenaka Lolemba, pa June 11, kunja kutayera, anthu anamva kuti chimvulachi chinaphetsa anthu ndi kuwonongetsa katundu wambiri. Anthu 22 anamwalira, ndipo aŵiri anali Mboni za Yehova: Jeffrey Green, yemwe anali mkulu wachikristu ndiponso mlamu wake Frieda Willis. * Komanso nyumba pafupifupi 70,000 zinawonongeka, ndipo kusefukira kwa madzi koopsa chonchi kunali kusanachitikepo n’kale lonse mumzinda uliwonse waukulu. Chimvula choopsachi chinawonongetsa katundu wandalama zotsala pang’ono kukwana madola 5 biliyoni, ndipo ndalamazi zinaposa ndalama zimene ankazigwiritsira ntchito kumbuyoku ku America kukagwa mvula yowononga.

Chigulu cha Anthu Odzipereka Kuthandiza

Mitima ya anthu sinali m’malo. Munthu wina amene anathandiza nawo anati: “Mabedi ndiponso makapeti awo ananyoweratu. Zithunzi zawo adakali aang’ono zinawonongekeratu.” Katundu wa anthu ambiri pagulu la Mboni za Yehova zoposa 16,000 mumzindawu anawonongeka. Nyumba za Ufumu zokwana 8 pamodzi ndi nyumba mazanamazana za Mboni za Yehova zinaphwasuka. M’nyumba zina pagululi madzi anali khatikhati; moti m’nyumba zina madziwo anachita kudzaza mpaka kudenga. Mipingo yonse ya Mboni za Yehova imene inakhudzidwa ndi vutoli inali yoposa 80. Komabe anthu amene vutoli linawagwera sanangosiyidwa kuti adzionere okha vuto lawolo. Patangopita masiku ochepa okha, chigulu cha anthu ongodzipereka chinafika kudzawathandiza. Kodi zimenezo zinachitika bwanji?

Akulu a m’mipingo ya Mboni za Yehova mumzindawu, sanachedwetse kuchitapo kanthu ngakhale kuti madziwo anali asanayambe kuphwa. Mkulu wina anafotokoza kuti: “Tinaimbira foni abale ndi alongo athu ndipo tinawayendera. Kenaka tinaonaona zonse zowonongeka, ndipo pamene tinkafika tsiku Lolemba, pa June 11, n’kuti titalemba zonse zokhudza anthu amene katundu wawo anasakazidwa, nyumba zowonongeka, ndiponso kukula kwa vutolo. Zimenezi tinazitumiza kulikulu la Mboni za Yehova ku Brooklyn, mumzinda wa New York.” Patangotha masiku ochepa chabe, ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku America inakhazikitsa komiti yoona zantchito yothandiza ovutikawo. Komitiyo inali ndi akulu okwana 8 achikristu a mumzinda womwewo wa Houston, ndipo nthambiyo inawapatsa ndalama zoyendetsera ntchitoyo. Kodi ntchito ya komitiyi inali yotani makamaka? Inali yokhazikitsa pansi mitima ya anthu amene anaona tsokawo ndiponso kukonzanso nyumba zoposa 700 za Mboni za Yehova zimene zinawonongeka!

‘Kodi chintchito chimenechi tichiyendetsa bwanji?’ akuluakulu a m’Komiti ya Mboni za Yehova Yopereka Chithandizo ya ku Houston ya 2001 anaima mutu. Iwo ankagwira ntchito ndi usiku womwe polinganiza mmene ntchitoyo ingayambikire ndipo anaitanitsa anthu m’mipingo yoposa 160 ya Mboni za Yehova mumzindawo kuti adzathandizepo. Wapampando wa komitiyo anafotokoza kuti: “Zinali zodabwitsa kuona chigulu cha anthu amene anadzipereka atamva pempholi. Anthu a Mboni za Yehova oposa 11,000 analolera kupereka nthaŵi, mphamvu ndiponso luso lawo popanda kulipidwa chilichonse.”

Othandiza Analimbana ndi Nkhungu

Patatha masiku ochepa chisefukireni madziwo, anthu othandizaŵa anapita kukagwira ntchito kunyumba za anthu okhudzidwawo n’kumakanganula makapeti omwe anali matope okhaokha, kugumulagumula simenti yapansi m’nyumbazo, makoma a ming’ankha, kuchotsa makabati okhuta madzi, zitseko zophwasukaphwasuka, ndi chinthu china chilichonse chomwe chinali bii chifukwa cha madzi onyansa osefukirawo. Winawake wongodzipereka kudzathandiza nawo anafotokoza kuti: “Chachikulu chimene tinkafuna sikukonza nyumba za abale athuzo basi, komanso kuwateteza kuti asadwale.” Popeza kuti nkhungu yoopsa ikanatha kuyamba mwamsanga kumera m’makoma ndiponso m’makabati, chinthu choyenera kuchita moyambirira chinali kupopera mankhwala amphamvu m’nyumbazo.

Pofuna kudziŵa mmene angagwirire ntchitoyi bwinobwino, a Mboni ambiri anapempha kuti aphunzitsidwe ndi bungwe la boma limene mbali yaikulu limaona za masoka lotchedwa Federal Emergency Management Agency (FEMA). Atachita zimenezi, wa Mboni aliyense yemwe anakaphunzitsidwa ndi bungweli ankatenga anthu khumi n’kupita nawo kumene kuli nyumba yowonongeka n’kuwaphunzitsanso mmene angapoperere bwinobwino mankhwala panyumbayo. M’maŵa mwake aliyense wa anthu khumi ongophunzitsidwa kumenewo ankatenganso ake khumi n’kuchita chimodzimodzi. Winanso wongodzipereka anafotokoza kuti: “M’masiku ochepa kwambiri, anthu amene anakhoza kugwira ntchitoyi bwinobwino anachuluka modabwitsa kwambiri.” Nkhunguyo inacheperatu chifukwa chakuti anthu olimbana nayo ankangochulukirabe! Opuma pantchito ndiponso achinyamata omwe anali paholide kusukulu ankagwira ntchitoyi masana. Kukada, othandiza enanso ankafika n’kumapitiriza. Nyumba zonse za a Mboni zimene zinali ndi nkhungu zinabwerera mwakale patangotha masabata 6 okha.

Anakhazikitsa Likulu ndi Malo Aang’onoang’ono Seveni

Panthaŵiyi, komiti yopereka thandizo ija inagula zipangizo zambirimbiri zogwiritsira ntchito pa zomangamanga. Koma kodi zipangizo zimenezi anazisunga kuti? Mneneri wa komitiyo anafotokoza kuti: “Mkulu wa kampani inayake atamva za mavuto athu, anapereka chinyumba chachikulu chosungiramo akatundu cha malo okwana masikweya mita 5,000 kuti tichigwiritsire ntchito kwaulere!” Kuwonjezera pokhala ndi malo osungiramo katundu wa zomangamanga, chinyumbachi chinalinso ndi malo oti n’kukhazikitsamo maofesi. Posakhalitsa, chinyumbachi chinasanduka likulu la ntchito yothandizayi, ndipo anthu 200 mpaka 300 ankagwira ntchito pamenepa usana ndi usiku, ngakhalenso Loŵeruka ndi Lamlungu lomwe.

Popeza kuti malo a nyumba zowonongeka anali aakulu kwambiri, Nyumba za Ufumu zokwana seveni anazisandutsa malo ofikirako katundu wa ntchitoyo. Loŵeruka ndi Lamlungu, kulikonse kumene kunali malo ofikirako katundu kunkakhala yakaliyakali kuchitika zinthu zosiyanasiyana. (Onani m’bokosi lakuti “Pankakhala Yakaliyakali.”) Ambiri mwa anthuŵa anagwirirapo limodzi ntchito yomanga Nyumba za Ufumu. Ndipotu omwe ankadziŵa zomangamanga ochokera m’Makomiti Omanga a Zigawo 11 a ku Arkansas, Louisiana, Oklahoma, ndiponso ku Texas anathandiza nawo. * Kulikonse, akalipentala, openta, okonza mapaipi a madzi, ndiponso ena amene ankadziŵa ntchito zina n’zina ndiwo ankatsogolera anzawo ndiponso kuwaphunzitsa ntchitozo.​—⁠Onani m’bokosi lakuti “Kuphunzitsa Ena Ntchito.”

Dongosolo ndi Kaundula wa Ntchito Yonse

Ntchitoyi inagaŵidwa m’zigawo seveni. Zipangizo zomangira ankazifikitsa ku nyumbazo m’magulu anayi, ndipo nyumba iliyonse yoti ikonzedwe ankailembera mawikendi atatu kuti ithe kuikonza. Potero akanatha kumaliza ntchito yonseyo pafupifupi m’miyezi 6.

Kuti dongosololi liyende bwino, komitiyo inakhazikitsa madipatimenti 22, ndipo pamenepa, ina inali yoona za kayendetsedwe ka zinthu, yoona zogulagula, yoona za malo ogona ndiponso yoona za magalimoto. Chimene chinathandiza kwambiri madipatimenti onseŵa n’chakuti zonse anazilemba pakompyuta. Ntchito yokonza zowonongekayi isanayambike, anthuŵa anatha masiku khumi akulemba zonse zofunika m’makompyuta. Nkhani ina ya panyuzi inati: “Kulemba zonsezi sinali ntchito yamaseŵera ayi.” Komabe pamapeto pa chintchitochi, m’makompyutamo munadzaza ndi zinthu zofunika kwambiri. Munthu ankangoti akatabwanya kabatani kenakake, ankatha kudziŵa pamene anthu 11,000 ameneŵa angafike kudzathandiza, ankatha kuona kuti iwo amadziŵa ntchito zotani, ndiponso kuti angawapeze kuti. Akatabwanyanso kachiŵiri, ankadziŵa kuti zimene akonza zafika pati, kuti ndi nyumba ziti zimene zaikidwa pandandanda yokonzedwa, ndiponso zinthu zina n’zina zokhudzana ndi nyumba zowonongedwazo. Anthu anayamba kunena kuti zimene zinali m’kompyutazi ndizo “chimake chenicheni cha ntchito yonseyo.”

Zinawakhudza Mtima Ndiponso Anayamikira

Odziŵa ntchito zomangamanga anayendera nyumba zimene zinalibenso nkhungu ndipo zouma kuti aone zomwe zingafunike pokonza zowonongekazo. Mneneri wa anthuŵa ananenapo kuti: “Iwo ankalembera zonse zofunika mpakanso misomali yeniyeniyo. Sitinkafuna kuwononga ndalama ina iliyonse kapena katundu yemwe anthu anapereka.” Panthaŵi yomweyo, enanso ongodzipereka ankapeza zilolezo za zomangamanga kwa akuluakulu a mzindawo.

Pambuyo pa zimenezo, anaitana mabanja ogwa m’tsokali kosungirako katundu kuti akasankhe zomwe zinalipo, monga makapeti, makabati, matailosi ndiponso zinthu zina zoti atenge pobwezeretsa zimene zinawonongeka. Anthuŵa anakhudzidwa mtima kwambiri ndipo misozi sinkachoka m’maso mwawo poona katundu yemwe anapatsidwayo. Anthuŵa analangizidwanso ndi ena ongothandiza omwe amadziŵa nkhani za inshuwalansi ndiponso malamulo a boma pankhaniyi. Kenaka anaika ndondomeko ya mmene akonzere nyumbazo, ndipo onyamula katundu womangira nyumbazo ankafikitsa katunduyo kwa omangamangawo pa magalimoto tsiku lenileni limene iwo akum’funa. Mwamuna winawake yemwe nyumba yake inali kukonzedwa anauza mkazi wake wa Mboni kuti: “Anthu a Mboni ndi odabwitsa. Ena akachokapo, nthaŵi yomweyo uona kuti enanso afika. Amagwira ntchito ngati nyerere!”

Kukonza zinthu zikuluzikulu pa nyumba imodzi kunkatenga pafupifupi mawikendi atatu. “Komabe nthaŵi zina tinkatha mawikendi asanu kapena asanu ndi atatu,” anatero wapampando wa komitiyo. Ankati akamagumula makoma ena n’kuona kuti nyumbayo inali kale ndi vuto lina, ankayamba akonza kaye vutolo n’kumalizitsa bwino kwinako. Iwo sankafuna kuimika makoma atsopano asanakonze makoma oyambawo. Munthu wina wodziŵa ntchito yamanja anati: “Nthaŵi zina tinkaona kuti chiswe chawononga zinthu zinazake zamatabwa, ndiye tinkaonetsetsa kuti chiswecho tachipha. Tinakonza mwambiri. Tinasiya nyumbazo zili bwino kwambiri.” Poyamikira, munthu wina yemwe anathandizidwa anauza mlendo wina zomwe zinalinso m’maganizo a eni nyumba ambiri kuti: “Tsopano nyumba yanga ikuoneka bwino poyerekeza ndi mmene ndinaigulira!”

Chakudya Chinkafulumira

Kuti anthu ambiriŵa alandire chakudya, a Mboni ambiri anakonza nyumba yosungiramo katundu yomwe inali kuseri kwa Nyumba ya Ufumu kuti ikhale malo ophikira ndiponso ogaŵira chakudya. A Mboni m’dziko lonselo anapereka mwaufulu mafiriji, makina otsukira mbale, masitovu ndi zipangizo zina za kukhitchini. Loŵeruka ndi Lamlungu lililonse, makhukhi okwanira 11 pamodzi ndi anthu ena 200 ongodzipereka ankaphikira anthu ambirimbiri mmenemo. Woyang’anira ophikawo anati: “Kwa zaka 19 takhala tikuphikira omanga Nyumba za Ufumu, koma ntchito iyi inakula kusiyana ndi mmene tinali kuganizira.”

Chakudyacho ankachiika m’makontena aakulu okwana 120. Ndipo makontenaŵa ankawanyamula m’magalimoto 60 n’kupita nawo kumalo onsewo ndiponso kulikulu la ntchitoyi. Ndiye onse amene ankagwira ntchito panyumba inayake ankatumiza munthu mmodzi kukatenga chakudya cha gulu lawo pamalo amene chifikire. Iwo ankadyera m’nyumba zomwezo ndipo akangomaliza ankapitiriza ntchito yawo.

Zonse Zinayenda Bwino!

Kenaka mwezi wa April m’chaka cha 2002, anthu ongodziperekaŵa okwana 11,700 anafika kumalecheleche kwa ntchito imeneyi. Palibenso ntchito ina yomwe Mboni za Yehova zinagwirapo pothandiza anthu amene agwa m’masoka yomwe inatenga nthaŵi yaitali choncho. Anthuŵa anamaliza maola okwana 1,000,000 pokonza kapena kumanganso Nyumba za Ufumu 8 ndiponso nyumba zina 723. Munthu wina wothandizidwa analankhula m’malo mwa anzake onse misozi ili m’maso kuti: “Ndikuthokoza Yehova ndiponso anthu amene atithandiza chifukwa cha zonse zimene atichitira. N’zolimbikitsa kwambiri kukhala m’gulu lotere la anthu achikondi chenicheni!”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Mizinda ya New York, Los Angeles ndiponso Chicago ili ndi anthu ochulukirapo poyerekeza ndi a mumzindawu. Anthu amene amakhala mumzindawu alipo pafupifupi 3,500,000 ndipo mzindawu ndi wochepa pang’ono poyerekeza ndi dziko la Swaziland.

^ ndime 5 Pa mwambo wa maliro a Jeffrey ndi Frieda panali anzawo okwana 1,300. Anthu onseŵa anam’limbikitsa Abigail, yemwe anali mkazi wa Jeffrey komanso mchemwali wa Frieda.

^ ndime 15 Kaŵirikaŵiri Makomiti Omanga a Zigawo amaona za kumangidwa kwa malo oti Mboni za Yehova zizichitiramo misonkhano yawo.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 15]

PANKAKHALA YAKALIYAKALI

Lero ndi Loŵeruka 7 koloko m’maŵa ndipo tili pano pamalo aang’ono a nambala 4 kuno kumadzulo cha kum’maŵa kwa mzinda wa Houston. Antchito ali yakaliyakali, kulankhulitsana, kuseketsana, kumwa khofi, ndiponso ali kalikiliki kujegweda mandasi mu Nyumba ya Ufumu. Ena kuti afike pano, ayenda mtunda wautali kwambiri. Koma nthaŵi itangokwana 7:30 m’maŵa womwewu, anthu onse aja angokhala chetechete, ndipo woyang’anira malo ano wayamba kutsogolera zonse pokambirana lemba la m’Baibulo. Onse asanabalalike kupita kogwirira ntchito zawo, iye akulengeza kuti maŵa Lamlungu nthaŵi ya 7:30 m’maŵa kudzakhala kuphunzira Nsanja ya Olonda, ndipo akulimbikitsa onse kuti akhoza kudzanenapo ndemanga zawo m’Chizungu kapena m’Chisipaniya. Kenaka akuwauza onsewo uthenga wa mafuno abwino wochokera kulikulu la Mboni za Yehova, ndipo nthaŵi yomweyo onsewo akungoti m’manjamo pupupu! mosalekeza kwa kanthaŵi ndithu.

Kenaka woyang’anirayo akuwauza mmene ntchito ikuyendera ndipo akuwathokoza onsewo chifukwa chokhala ndi mtima wofunitsitsa kuthandiza. Kenakanso akufunsa kuti: “Kodi alipo yemwe sakudziŵa choti achite kapena koti aloŵere lero?” Palibe ngakhale mmodzi yemwe akukweza dzanja. Ndiye akufunsanso kuti: “Kodi ndi angati lero omwe afune kudya?” Mwamsangamsanga iwo akukweza manja awo, ndipo onsewo akufa nacho chikhakhali. Pomalizira penipeni, wina akupemphera ndipo anthu onsewo okwana 250, amuna, akazi, achinyamata ndi okalamba omwe, akuyambapo ulendo wokagwiranso ntchito kwa tsiku lonse.

Zoterezi n’zomwe zikuchitikanso kumalo ena aang’ono okwana 6 komanso kosungirako katundu yense kuja. Apatu nthaŵi yonseyi, ena ongodzipereka a kukhitchini yaikulu ayamba kale kalikiliki kugwiragwira mapoto. Chifukwatu dzuŵa likangofika paliwombo, anthu oposa 2,000 ongodzipereka a mumzinda wonsewu, omwe akhale kumimba kuli gwa ndi njala, mitima ikhala dyokodyoko kuti adye chakudya chamoto!

[Bokosi/Chithunzi patsamba 16]

KUPHUNZITSA ENA NTCHITO

Panthaŵi yogwira ntchito yongodziperekayi, ena odziŵa ntchito zamanja ankaphunzitsa anzawo osadziŵa ntchitozi kuti azidziŵa zochita zenizeni. Ena anaphunzitsidwa kupopera mankhwala m’nyumba. Ena anaphunzitsidwa kumanga zipupa ndiponso kukonza makabati. Komanso ena anaphunzitsidwa kupaka pulasitala ndiponso kupenta. Misonkhano yophunzitsa anthuyi ankaijambula pa mavidiyo ndipo mavidiyowo ankawatumiza kumalo ena kuti akaphunzitsire anthu enanso. Mmodzi mwa anthu amene anali m’komitiyo anati: “Misonkhano imeneyi, inathandiza kuti tigwire ntchito yabwino kwambiri yokonzanso zinthu.”

[Chithunzi]

Odziŵa ntchito zamanja akuphunzitsa anzawo

[Bokosi patsamba 18]

ZOCHITADI ZA MULUNGU”

“Makampani a inshuwalansi amati masoka achilengedwe ndi zochita za Mulungu,” anatero wa m’komiti yothandiza. Iye anapitiriza kuti: “Komabe zochitadi za Mulungu ndizo zimene anachita anthu amene anangodzipereka kudzathandiza kuno kwa miyezi yonseyo. Ubale wathu ndi wodabwitsa!” Panthaŵi yogwira ntchitoyi, anthu 2,500 kapena kuposapo ankafika kudzagwira nawo Loŵeruka ndi Lamlungu. Wapampando wa komitiyo anati: “Anthu amene anadzipereka pantchito yopanda malipiroyi sanapitenso ku maholide amene ankafuna kupita, komanso anasiya kaye zomwe ankafuna kuchita ndi mabanja awo ndiponso paokha, n’cholinga choti athandize nawo pa chintchitochi. Iyi inali ntchito yaikulu kwambiri yothandiza amene tsoka linawagwera yomwe Mboni za Yehova zinagwirapo.”

Chintchito chimenechi chinali chofunika anthu odzipereka kwathunthu. Munthu wina yemwe anadzipereka pantchitoyi kuchokera pachiyambi mpaka kumapeto ankagwiranso ntchito yolembedwa yopanikiza kwa maola 50 pamlungu. Ngakhale zinali choncho, ankathandiza nawobe mlungu uliwonse kwa maola 40. Iye anati: “Yehova ankandipatsa mphamvu. Anthu odziŵana nawo ankandifunsa kuti, ‘Kodi amakulipira pantchitoyi?’ Ndipo ndinkawauza kuti, ‘Ntchito imeneyi ikanakhala yolipidwa palibe malipiro amene akanandikwanira.’ ” Banja lina linkati likagwiragwira ntchito yawo yolembedwa kwa mlungu wonse, Loŵeruka ndi Lamlungu linkayenda pagalimoto ulendo wamakilomita pafupifupi 400 pochokera ku Louisiana kukafika kuntchito yongothandizayi. Ambiri ankalaŵirira kuntchitoku m’mamaŵa n’kumaŵeruka kuli kachisisira pobwerera kwawo pagalimoto. Gulu lina lomwe linali ndi anthu aluso pantchito yawo okwana 30, omwe ankayenda pagalimoto kwa maola 7 mpaka 10 popita pokha linati: “Mpakedi kuti tichite zonsezi.” Mkazi wina ankaŵeruka kuntchito kwake nthaŵi ili 3:30 masana n’kupita kukathandiza kulikulu la ntchitoyi mpaka 10 koloko usiku. Iyeyu ankathandizanso Loŵeruka ndi Lamlungu lililonse. “Zinali zosangalatsa kwambiri,” iye anatero.

Kunenadi zoona, anthuŵa ndiponso ena onse amene anangodzipereka pantchitoyi anali ofunitsitsa kutero chifukwa cha chikondi cha pa abale, chomwe ndi chizindikiro cha Akristu enieni. (Yohane 13:35) Mkulu wa boma woyang’anira mzinda wa Houston atayendera likulu la ntchitoyi ananena pamaso pagulu la a Mboni kuti: “Koma inu mumakondadi kuchita zimene Mulungu amatiuza kuti tichite. Zimene mukuchita n’zogwirizana ndi zimene mumakhulupirira.”

[Chithunzi pamasamba 14, 15]

Madzi osefukira mumzinda wa Houston pa June 9, 2001

[Mawu a Chithunzi]

© Houston Chronicle

[Chithunzi patsamba 15]

Misewu ikuluikulu inasanduka mitsinje

[Chithunzi patsamba 15]

Madzi analoŵerera m’nyumba zambiri

[Zithunzi patsamba 17]

Ena mwa a Mboni ambirimbiri omwe anangodzipereka kuthandiza

[Chithunzi patsamba 18]

Ogwira ntchito kukhitchini anaphika chakudya choti chikanakwanira anthu oposa 250,000!

[Mawu a Chithunzi patsamba 13]

NOAA