Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kukhala Osamala Poganizira Zachitetezo

Kukhala Osamala Poganizira Zachitetezo

Kukhala Osamala Poganizira Zachitetezo

ANTHU ena amachita mantha akakhala m’ndege imene ikuuluka m’mwamba makilomita 11 kuchokera panthaka. Amaona kuti kutereko n’chinthu chachilendo. Popeza tsopano akhwimitsa kwambiri chitetezo pa ulendo wa pandege n’zokayikitsa kuti chinachake choopsa chingachitike muli m’ndege imene ikuuluka m’mwamba. Komabe pali zinthu zina zimene zimachitika mwakamodzikamodzi zimene zimatikumbutsa kuti zoterezi zingathe kuchitika ndithu.

Kuthetsa Mantha

Izo zili apo, anthu anayamba kalekale kufuna kupeza njira youlukira. Zaka 1,000 Kristu asanabwere, Mfumu Davide inalemba kuti: “Ha, wina akadandipatsa mapiko onga a njiwa! Bwenzi nditauluka.” (Salmo 55:6) Paja tanena kale kuti umisiri wamakono wachititsa kuti kuyenda pandege kukhale ina mwanjira zabwino kwambiri zoyendera paulendo. Koma sikuti ilibiretu vuto lililonse. Palibe chilichonse padziko pano chopandiratu vuto lililonse kapena chosakayikitsa ngakhale pang’ono.

Ndi bwino osaiwala mfundo imeneyi ngati timalephera kukhazikitsa mtima pansi moyo wathu ukakhala m’manja mwa anthu ena. Anthu ena akakhala amaganiza kuti, ‘Ineyo mtima umakhala m’malo ndikamadziŵa kuti chinachake chitachitika kumene ndiliko, ndingathe kuchitapo kanthu pandekha.’ Anthu otere zimawavuta panthaŵi imene alibe mwayi woti angachitepo kanthu pa chinthu chinachake. Nthaŵi ina yotere ndiyo pamene akwera ndege.

Ngakhale kuti anthu ayesetsa kuti ulendowu uzikhala wosaopsa, sipofunika kuchita mphwayi ayi. Anthu onse amene amayenda pandege angathandize kupeŵa ngozi. Anthu oyang’anira za maulendo a pandege akuchenjezabe anthu kuti zoopsa zidakalipo. Mwambi wina wothandiza wa m’Baibulo umati: “Wochenjera amaoneratu zoopsa, n’kuzipeŵa.” (Miyambo 22:3, New Living Translation) N’chinthu chanzeru kudziŵa kuti palibe chinthu chimene chili chosaopsa ngakhale pang’ono. Chachikulu n’chakuti mukamayenda ulendo wa pandege musamaiwale kuchita zinthu mosamala monga mmene mungachitire kwina kulikonse.

Anthu amene amakwera ndege kaŵirikaŵiri angathe kudzisamalira mosavuta. Ichi n’chifukwa chakuti anthu amene amayendayenda amazoloŵera kwambiri zochitika za pabwalo la ndege ndiponso zochitika m’ndege kuposa anthu ena apaulendo. Inunso mungathe kuzoloŵera ndiponso kukhazikika mtima pansi potsatira malangizo osavuta amene tawalongosola m’mabokosi amene ali m’nkhani inoŵa.

Kuyenda Momasuka

Zosecha anthu zija n’zofunika kwambiri koma anthu ena apaulendo, makamaka amene akufuna kuyenda mwachangu, amaona ngati n’zongochedwetsana. Podziŵa kuti m’mabwalo ambiri a ndege ayamba kukhwimitsa chitetezo, mungathe kugwiritsira ntchito malangizo otsatiraŵa kuti muyende mosavutikira:

▪ Fikani msanga. Konzani zokafika pabwalo la ndege mwamsanga nthaŵi idakalipo ndithu kuti muzikachita zinthu mwa phee, mtima uli m’malo, ndipo mukatero simungasoŵe pogwira ngati patachitika chinachake chamwadzidzidzi kapena chosokoneza.

▪ Sankhani ndege zimene makamaka zimatenga anthu apaulendo wa zantchito. Anthu otere amaudziŵa bwino ulendo wa pandege komanso satenga zinthu tutuwiri, ndipo amafuna kuchita zinthu mwachangu.

▪ Musanafike pachitseko pamene pali makina ounikira zida zachitsulo, musiyiretu zinthu zimene mukuona kuti zingathe kuchititsa kuti alamu ilire. Izi ndi zinthu monga makiyi, makobidi, tizibangiri, ndiponso telefoni zam’manja. Zisungitseni kaye kwa munthu wina amene akuyang’anira pamenepo mukamadutsa pachitsekopo.

▪ Ikani zikwama ndi katundu wina wam’manja momugonetsa bwinobwino pa makina onyamulira katundu; munthu amene amayang’ana zimene zikuoneka pakompyuta yoonetsera zam’kati mwa katunduyo akaona chinachake chosadziŵika bwinobwino, angathe kukutsegulitsani chikwama chanucho kapena kukuuzani kuti muchiikenso pa makinawo.

▪ Muuzirenitu amene akuyang’anira pamenepo ngati mwatenga chinachake chimene mukuona kuti chingathe kudabwitsa anthu ounikawo, mwachitsanzo mphatso inayake yachitsulo imene mwatenga. Munthu woyang’anirayo mukamuuza momveka bwinobwino mwina sangalimbane n’zakuti akutsegulitseni chikwamacho kuti aone chinthu chooneka mokayikitsacho. Ngati mukufuna kuchita zinthu mwachangu, muchitulutsiretu chinthucho n’kupempha kuti angochiona yekha.

▪ Ngati makina ounikira zida atalira, musachedwe kuwafotokozera mwaulemu chimene chingakhale chitapangitsa zimenezi. Woyang’anira pamenepo akadziŵa kuti makinawo analira chifukwa cha chinthu chinachake chachitsulo ndipo ngati ali ndi mnzake wokhala ndi chindodo chounikira zinthu zachitsulo, angathe kukuuzani kuti mupititse katundu wanu kwa mnzakeyo.

▪ Ngati mutafunitsitsa kuti musiyidwe pa ulendo wanu wa pandege, ingoyerekezani kunena moseka kuti mulanda ndegeyo kapena kuti mwatenga bomba. Mukatero anthu oona zachitetezo pabwalo la ndegepo angathe kukusechani kwadzaoneni, mwinanso kukuimbani mlandu kumene.

Yendani Bwino!

Kodi n’zotheka kuchita kusankha kuti muyende bwino? Inde n’zotheka ndithu. Mungayende bwinobwino ndithu ngakhale mutakwera ndege ina iliyonseyo. Ngati mukukayika, fufuzani kuti mudziŵe ngati ndege za kampani imeneyo sizichitachita ngozi. Musaiwale kuti ngakhale kuti ndege zimachita ngozi, anthu amaona kuti ulendo wa pandege udakali ulendo wabwino koposa.

Pakalipano, tonse tingathe kungoyembekezera nthaŵi imene dzikoli lidzalamulidwe ndi Mulungu pamene sikudzakhala choopsa chilichonse kapena chokayikitsa. Pakati pa anthu oopa Mulungu sipadzakhala wina aliyense woika moyo wa anthu anzake pachiswe. Anthu “adzakhala osatekeseka” ndipo “osaopa zoipa.”—Miyambo 1:33. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 19 Palinso nkhani ina yotere yakuti “Kodi Ndege N’zodalirika Motani?” imene mungathe kuipeza mu Galamukani! ya pa September 8 1999.

[Bokosi/Chithunzi pamasamba 10, 11]

MALANGIZO ENA OTHANDIZA KUTI MUYENDE BWINO

Kwerani ndege zosaima m’njira. Ngozi zambiri zimachitika ndege ikayamba kuthamanga pansi, ikamasiya nthaka kapenanso ikamatera. Mukakwera ndege yosaima paliponse mumachepetsa tsoka lokumanizana ndi ngozi zimenezi.

Kwerani ndege zazikulu. Ndege zokwera anthu oposa 30 nthaŵi zambiri pozipanga ndiponso pozipatsa chilolezo choti ziziyenda, amatsatira malamulo okhwima kwambiri poyerekezera ndi ndege zazing’onopo. Komanso ngati patachitika ngozi yaikulu, ngakhale kuti sizichitikachitika, m’ndege zazikulu m’posavuta kuti anthu apaulendo apulumuke.

Mvetserani bwino malangizo operekedwa ndege isananyamuke. Ngakhale kuti malangizo ameneŵa amakhala ngati obwerezabwereza, makomo apafupi kwambiri otulukira pangozi amakhala osiyanasiyana malingana ndi ndege yake ndiponso mpando umene mwakhala.

Musaike katundu wolemera pamwamba. Ndege ikakumana ndi chimphepo katundu amalephera kukhazikika m’malo oikapo katundumo, choncho ngati muli ndi katundu winawake amene angakuvuteni kum’loŵetsa mmenemu, mum’perekeretu pasadakhale kuti akamuike kosungira katundu wotere.

Mukakhala pansi lamba wanu azikhala chimangire. Kumanga lamba mukakhala pansi kumakutetezani ndege ikakumana ndi chimphepo.

Mvetserani zimene okuyang’anirani m’ndegemo akunena. Chifukwa chachikulu chimene amaikira anthu oyang’anira apaulendo m’ndege n’chakuti akuthandizeni paulendo wanuwo. Motero ngati munthu wina wotere atakuuzani kuti muchite chinachake, chitani kaye chinthucho n’kumafunsa bwino mafunso pambuyo pake.

Musatenge zinthu zilizonse zangozi. Pali zinthu zambiri zimene zingathe kuchititsa ngozi zimene siziloledwa m’ndege koma zina n’zosachita kulira kufunsa. Mungathe kudziŵa panokha kuti musatenge zinthu monga petulo, zinthu zokhala ndi asidi, gasi wakupha, ndi zinthu zina zotere pokhapokha ngati kampani ya ndegeyo itavomereza ndipo ngati atazinyamulira m’chinthu choyenera.

Osamwa kwambiri. Mukamwa moŵa, umakula mphamvu mukapita m’mwamba kuposa mukakhala pansi. Nthaŵi zonse ndi bwino kusamwetsa moŵa pena paliponse, kaya ndi m’mwambamo ngakhalenso pansi pompano.

Khalani tcheru. Ngati zosaonekaoneka zija zitachitika mwadzidzidzi, monga zakuti nonse mutulukemo m’ndegemo mwamsanga poopa chinachake, muyenera kutsatira malangizo a anthu oyang’anira apaulendo aja komanso anthu ena ogwira ntchito m’ndegemo ndipo tulukanimo mwamsanga.

[Mawu a Chithunzi]

Zachokera ku Airsafe.com

[Bokosi/Chithunzi patsamba 12]

KUWAKHAZIKA MTIMA PANSI ACHIBALE ANU

Ngati muli paulendo, umu ndi mmene mungawakhazikitsire mtima pansi achibale anu.

Mukambirane nawo achibale anuwo. Musananyamuke, pezani nthaŵi yokambirana nawo achibale anu zinthu zimene muchite kuti inuyo ndiponso iwowo azikhala mtima uli m’malo. Alongosolereni kuti sayenera kuda nkhaŵa paulendowo chifukwa chakuti masiku ano akhwimitsa kwambiri chitetezo.

Asiyeni anenepo zimene zikuwadetsa nkhaŵa. Alekeni achibale anuwo kuti anenepo nkhaŵa zawo. Iwo amakukondani ndipo akungofuna kuti muyende bwino. Mvetserani bwinobwino ndipo osafulumira kutsutsa. Musanyozere chilichonse chimene chikuwaopsa ndiponso kuwadetsa nkhaŵa.

Alimbitseni mtima zenizeni. Auzeni zakuti pali mabungwe osiyanasiyana amene akuyesetsa kuti zigaŵenga zisathenso kuchita ziwembu. Akutero pochita zinthu monga kukhwimitsa chitetezo pabwalo la ndege ndiponso m’ndege mmene. Si kaŵirikaŵiri chinthu choopsa kuchitika m’ndege yoti mwakwera anthu.

Musawaiwale achibalewo. Lonjezani kuti mukakafika kumene mukupitako mukaimba foni. Muziimbaimba foni kwanu mukatalikira choncho. Ndi bwinonso kuti achibale anu azidziŵa mmene angakupezereni ngati patachitika chinachake cha mwadzidzidzi.

[Mawu a Chithunzi]

Mfundo zimenezi zachokera pa kompyuta yolumikizidwa ku Intaneti ya bungwe lotchedwa United Behavioral Health

[Zithunzi patsamba 10]

Osavutavuta mukafika posechera anthu