Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Maseŵera a Ana Ayamba Kukhala Achiwawa

Maseŵera a Ana Ayamba Kukhala Achiwawa

Maseŵera a Ana Ayamba Kukhala Achiwawa

▪ Ana akusekondale akumana pamaseŵera a mpira wa miyendo. Mpirawo ukutha ndi ndeu timu inayo italuza panthaŵi yowonjezera. Makolo opitirira 100, makochi, ndiponso oseŵerawo akutukwanizana kenaka n’kuyamba kumenyana.

▪ Tiatsikana ndi tianyamata tikuseŵera mpira pamodzi. Ndipo kam’nyamata kena ka zaka teni kalanditsa mpira kwa mdani. Ndiye akochi ake akukagwira n’kukagwetsera pansi mpaka manja ake onse n’kuthyoka.

▪ Kochi wina wa timu ya ana akutulutsa mnyamata wina m’bwalo. Kenaka bambo a m’nyamatayo akuopseza kochiyo kuti amupha ndipo mapeto ake anawatsekera m’ndende kwa mwezi umodzi ndi milungu iŵiri.

▪ Papulakatesi ya maseŵera enaake a ana, abambo aŵiri akukangana pankhani ya malamulo a maseŵerawo. Ndiye bambo winayo akumenya mnzakeyo mpaka kumupha pamaso pa ana ake atatu.

NKHANI zochititsa nthumanzi ngati izi zayamba kuchuluka kwambiri. Zikuoneka kuti m’mabwalo a maseŵera osiyanasiyana a mpira, mwayambika kamzimu kenakake kachiwawa. Chiwawachi chikuyambitsidwa ndi makolo ndiponso makochi amene amalolera kuchita ndeu akamaona kuti akuluza. Mtsogoleri wa bungwe la zamaseŵera la Jupiter-Equesta (ku Florida) Athletic Association, dzina lake Jeffrey Leslie anati: “Ndaonapo makolo akukalipira ana awo mwamtima bii, n’kumawakakamiza kuti awine basi. Ndaonapo ana akumenyana pamaseŵera mochita kupsepsezeredwa ndi makolo awo. Ndaonapo ana akulira m’bwalo la mpira chifukwa choyalutsidwa . . . ndi makolo awo.” Iye anapitiriza kunena kuti: “Maseŵera a ana amapengetsa makolo kwambiri.” Pofuna kuteteza ana ku chiwawa chimenechi, anthu a m’madera ena afika pongoletseratu makolo enaake kuti asamapezeke pamaseŵera a ana awo.

Kodi ndi mavuto otani amene abwera chifukwa cha kamzimu kosaugwira mtimaka? Fred Engh, yemwe ndi mtsogoleri komanso amene anayambitsa bungwe la ku Florida la National Alliance for Youth Sports, anati: “Anthu ambiri achikulire, ayamba kuchita khalidwe lochititsa manyazi limeneli lomwe likuwononga maseŵera a ana moti sakusangalatsanso, ndipo zimenezi zikuwapatsa ana ambiri chitsanzo choipa.

Kamtima Kakuti Wafawafa

Vuto limeneli likuoneka kuti limabwera chifukwa chakuti makolo ena amafunitsitsa kwambiri kuti ana awo aziposa ana ena ndipo kuti aziseŵera ndi kamtima kakuti tipambane basi, wafawafa. Nthumwi ina ya bungwe lina la ku Canada loona za ufulu wa ana la Institute for the Prevention of Child Abuse inati: “Pakakhala kamtima kakuti tiwine basi kapena kuti tikule mphamvu basi zivute zitani, amene ali ocheperapo mphamvu amavulala. Pamaseŵera otere, ana ndiwo amakhala ocheperapo mphamvu.” Mkulu wina wa m’bungwe la ku Ontario (ku Canada) lotchedwa Physical and Health Education Association anati ana amene amaseŵera maseŵera otere “amayamba kuvuta adakali aang’ono. Ndiye akakula amadzakhala anthu oti akalephera pa chinthu chinachake, sikuvuta kwake.”

N’zosadabwitsa kuti anaŵa amatengera mtima wapachala wa makolo awo ndiponso wa makochi ankhakamiraŵa. Pamaseŵera ena a mpira wa atsikana, atsikanawo anaukira oimbira mpirawo kasanu n’kaŵiri. Pamaseŵera amtundu winanso, mtsikana wina atatulutsidwa m’bwalo anakalipa n’kukawononga galimoto ya mmodzi wa akuluakulu oyang’anira maseŵerawo. Mnyamata wina wa kusekondale, wochita maseŵera enaake omenyana anagwira woimbira maseŵerawo n’kumugunda ndi mutu mpaka kumukomoleratu chifukwa anaimbira kuti mnyamatayo sanachite bwino penapake. Darrell Burnett, amene ndi dokotala wa matenda a maganizo a ana wamba komanso ana ochita maseŵera osiyanasiyana anati: “Kale maseŵera a ana anali chitsanzo chabwino kwambiri cha kaseŵeredwe koyenera. Koma zonsezo zinatha. Masiku ano maseŵeraŵa asanduka zinazina.”

Zimene Makolo Angachitepo

Makolo asamaiwale kuti ana amaseŵera pofuna kusangalala ndiponso kulimbitsa thupi. Ndiye makolowo akamachititsa kuti maseŵerawo asanduke chimpikisano chadzaoneni komanso akamanyoza anawo, ndiye kuti sakudziŵa cholinga cha maseŵeraŵa ndiponso alibe chikondi. Baibulo limati: “[Makolo] musakwiyitse ana anu.”—Aefeso 6:4.

Kodi n’chiyani chingathandize makolo kuti azikhala osamala pankhani imeneyi? Choyamba ndi bwino osaiwala mmene inuyo munalili muli mwana. Kodi n’zoona kuti munkaseŵera ngati katswiri? Nangano n’zokuonerani inuyo kumafuna kuti mwana wanu wamwamuna kapena wamkazi akwanitse kutero? Musaiwalenso kuti paja “ana ali ambowa,” kapena kuti ngosalimba. (Genesis 33:13) Chinanso n’chakuti ndi bwino kumaiona bwino nkhani ya kuwina ndiponso kuluza. Baibulo limanena kuti kuchitira ena nsanje ‘n’kwachabe ndipo n’kongosautsa mtima.’—Mlaliki 4:4.

N’zochititsa chidwi kuti munthu wina yemwe kale anali katswiri wa mpira wamanja akulimbikitsa makolo kuti ayenera kuona moyenera nkhani ya kuwina ndi kuluza, osamakwiya mwana akalephera kuseŵera bwino kapena kukomedwa kwambiri mwanayo akawina. M’malo momangoganiza zowina basi, makolo ayenera kumaganiza kwambiri zakuti kodi ana awo akusangalala ndipo kodi akulimbitsadi thupi?

Motero makolo ena aona kuti maseŵera omachita kukhala ndi timu, amalimbikitsa ana awo kukhala ndi kamzimu koipa kampikisano. Komabe sikuti makolo otereŵa salola ana awo kuseŵera ndi anzawo. Mwachitsanzo, makolo ambiri achikristu amaona kuti ana awo amasangalala akamaseŵera ndi Akristu anzawo mwina kuseri kwa nyumba yawo kapena kumalo enaake okongola amene anthu amapitako powongola miyendo. Motero, makoloŵa amatha kuwayang’anira ana awowo bwinobwino akamaseŵera. Chinanso, kupita kwinakwake ndi banja lonse kumakupatsani mpata wochita maseŵera amtendere. N’zoona kuti maseŵera ochitira panyumba mwina sangakhale otenga mtima ngati maseŵera oseŵera n’cholinga choti muwine basi. Komabe musaiwale kuti “chizoloŵezi cha thupi” ngakhale chitakupindulitsani bwanji “chipindula pang’ono [basi], koma chipembedzo chipindula zonse.” (1 Timoteo 4:8) Nkhani ya maseŵera mukamaiona motere mungam’pulumutse mwana wanu ku zoopsa zimene zabwera chifukwa cha kamzimu kachiwawa kamene kayamba pamaseŵera otere.

[Chithunzi patsamba 21]

Maseŵera azisangalatsa, osati kuyambanitsa anthu