Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khoti Lalikulu Ligamula Kuti Pakhale Ufulu Woyankhula

Khoti Lalikulu Ligamula Kuti Pakhale Ufulu Woyankhula

Khoti Lalikulu Ligamula Kuti Pakhale Ufulu Woyankhula

TSIKU LA CHIGAMULO cha mlanduwu linali June 17, 2002, pamene Khoti Lalikulu linatulutsa chikalata chake. Kodi linagamula zotani? Zonse zinali m’mitu yankhani m’manyuzipepala. Nyuzipepala ya The New York Times inati: “Khoti Likana Zoletsa a Mboni za Yehova Kuyendera Ena.” The Columbus Dispatch ya ku Ohio inati: “Khoti Lalikulu Liletsa Lamulo Lotenga Kaye Chilolezo.” The Plain Dealer ya ku Cleveland, Ohio, inangonena momasula kuti: “Oyendera Anthu M’makomo Safunikira Chilolezo cha Boma.” Nkhani ina ya mu USA Today inati: “Ofuna Ufulu Woyankhula Zawayendera.”

Oweruza 8 pa oweruza 9 anakana zimene khoti la apilo lija linagamula! Chikalata cha chigamulo cha khotilo, chomwe chinali ndi masamba 18, chinalembedwa ndi Jasitisi John Paul Stevens. Chigamulocho chinasonyezeratu kuti Lamulo Loyamba Lowonjezera likugwiritsidwabe ntchito kwambiri polola ntchito ya Mboni za Yehova. M’chigamulocho khotilo linafotokoza kuti a Mboniwo sanapemphe chilolezo chifukwa chakuti amaona kuti “Malemba ndi amene amawalamula kuti azilalikira.” Kenaka khotilo linatchulapo mawu a m’chikalata chodandaulira khotilo chimene Mbonizo zinalemba akuti: “Ifeyo timaona kuti kupempha chilolezo kuboma chakuti tizilalikira n’kunyoza Mulungu kumene.”

Ndiyeno chikalata cha khotilo chinati: “Kwa zaka zoposa 50, khoti lino lakhala likukana zoletsa kuyenda khomo ndi khomo poyankhula ndi ena ndiponso pogaŵira timabuku. Sikuti zinkangochitika mwangozi kuti milandu yambiri yotere inali ya a Mboni za Yehova yokhudza za Lamulo Loyamba Lowonjezera, koma n’chifukwa chakuti kuyendera anthu khomo ndi khomo ndi lamulo la chipembedzo chawo. Tinaonanso m’landu wina wa Murdock ndi boma la Pennsylvania, . . . (wa mu 1943) ndipo tapeza kuti a Mboni za Yehova ‘amati amatsanzira Paulo, akamaphunzitsa “pabwalo ndi m’nyumba ndi m’nyumba.” Machitidwe 20:20. Amangotsatira ndendende lamulo la m’Malemba lakuti, “Mukani, kudziko lonse lapansi, lalikirani Uthenga Wabwino kwa olengedwa onse.” Marko 16:15. Akamatero amakhulupirira kuti akutsatira lamulo la Mulungu.’”

Kenaka chikalatacho chinatchulanso mfundo ya mlandu wa mu 1943 womwewu yakuti: “Mu Lamulo Loyamba Lowonjezera ntchito imeneyi n’chimodzimodzi ndi kupemphera m’matchalitchi ndi kulalikira kugome. Njofunikanso kuiteteza mofanana ndi mmene timatetezera zochitika zina zilizonse zodziŵika bwino za zipembedzo.” Potchulapo mfundo ya mlandu wina wa mu 1939, chikalatacho chinati: “Kuika lamulo lotenga kaye chilolezo komwe kumachititsa kuti anthu asathe kugaŵira timabuku mwaufulu ndiponso mosadodometsedwa n’kotsutsana kwambiri ndi ufulu umene malamulo a boma amapatsa anthu.”

Kenaka khotilo linatchula mfundo yofunika kwambiri yakuti: “Milandu yonseyi ikusonyeza kuti zimene Mboni za Yehova zakhala zikuyesa kuchita kuti anthu asamaletsedwe kuyankhula mwaufulu si zopindulitsa iwo okha.” Chikalatacho chinalongosola kuti a Mboni “si anthu wamba okhawo amene angaletsedwe kuyankhula mwaufulu chifukwa cha malamulo ngati a tauniyi.”

Chikalatacho chinapitiriza kunena kuti, ponena kuti anthu akafuna kuyankhulana ndi anzawo mmene amachitira tsiku n’tsiku ayenera kuuza kaye boma kenaka n’kutenga chilolezo, lamuloli . . . “likunyoza mfundo zabwino zimene zili mu Lamulo Loyamba Lowonjezera komanso likunyoza ufulu umene anthu ayenera kukhala nawo. Lamulo lofuna kuti anthu azikatenga kaye chilolezo pofuna kuyankhulana motere n’losemphana kwambiri ndi chikhalidwe ndiponso malamulo amene dziko lathu lakhala likutsatira kuyambira kalekale.” Kenaka chikalatacho chinakamba za mmene “lamulo lotere lingaipitsire zinthu.”

Kuopa Kuchitidwa Chipongwe

Nanga bwanji zoti lamuloli n’loteteza anthu ku mbava ndi anthu achipongwe? Khotilo linati: “Inde, zimenezi n’zodetsadi nkhaŵa koma m’mbuyo monsemu khoti lino lakhala likuonetsetsa kuti lisachite zinthu monyanyira mwakuti n’kulanda nazo anthu ufulu wawo wolembedwa mu Lamulo Loyamba Lowonjezera.”

Chikalatacho chinapitiriza kunena kuti: “N’zokayikitsa kuti lamuloli lingachititse anthu achipongwe kusiya kugogoda m’makomo kapena kuyankhula ndi anthu m’njira zina zimene sizinatchulidwe m’lamuloli. Mwachitsanzo iwo angathe kufunsira njira kapena kupempha kuti aimbe nawo telefoni, . . . kapenanso angathe kukalembetsa dzina labodza kuboma popanda wodziŵa.”

Pobwerera ku chigamulo cha m’mbuyomo m’ma 1940, khotilo linati: “Nthaŵi ndi nthaŵi anthu odandaula [a Watch Tower Society] zinthu zinkawayendera bwino pa timilandu tosadziŵika bwino m’nthaŵi ya nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse ndipo zinkatero chifukwa cha mmene khoti lino linkaonera mfundo za mu Lamulo Loyamba Lowonjezera. Panonso mfundozi tikuziona chimodzimodzi.”

Kodi khotilo linagamula kuti chiyani? “Takana chiweruzo cha khoti la apilo chija, ndipo mlanduwu tikuubweza ku khotili kuti akauonenso malingana ndi mfundo tanenazi. Ifeyo talamula zimenezi.”

Motero, mapeto a nkhaniyi anali akuti “Khoti Linaikira Kumbuyo Mboni za Yehova,” monga mmene inanenera nyuzipepala ya Chicago Sun-Times. Ndipo oweruza 8 pa oweruza 9 anaikira kumboyo a Mboni.

Nanga Bwanji Zam’tsogolo?

Kodi a Mboni za Yehova a mpingo wakufupi ndi tauniyo wa Wellsville anaiona bwanji nkhani imeneyi ya kupambana mu Khoti Lalikulu? Palibe chifukwa chodzitamandira pofuna kuchititsa manyazi nzika za tauniyi. Mboni za Yehova zilibe nawo mlandu anthu abwino a m’tauniyi. Gregory Kuhar, yemwe ndi wa Mboni wa kumeneku anati: “Ifeyo sitikanapita n’komwe kukhoti kuja ayi. Kungoti lamulo lija linali lolakwika basi. Zimene tinachitazi sikuti n’zongopindulitsa ife tokha ayi, koma aliyense.”

Ndithu, a Mboni anayesetsa kwambiri kuti asasokoneze anthu a m’tauniyi. Gene Koontz, yemwenso ndi wa Mboni, anafotokoza kuti: “Nthaŵi yotsiriza kulalikira ku Stratton inali pa March 7, 1998, moti patha zaka zinayi zathunthu.” Ndiye anapitiriza kunena kuti: “Ineyo anachita kundiuza kuti andimanga. M’mbuyo monsemu takhala tikumva nkhani zosiyanasiyana zoti apolisi anali kutiopseza kuti atimanga. Ndiye tikapempha kuti ationetse chikalata chosonyeza lamulolo, palibe chimene ankachitapo.”

Koontz anatinso: “Ifeyo timakonda kukhala bwino ndi anthu anzathu. Ngati ena sakufuna kuti tiwachezere sitilimbana nawo. Koma pali ena amene zimawasangalatsa ndipo amafuna kukambirana za m’Baibulo.”

Gregory Kuhar analongosola kuti: “Sikuti ifeyo tinasuma mlandu umenewu n’cholinga choyambana ndi anthu a ku Stratton. Tinkangofuna kukhala ndi ufulu woyankhula movomerezedwa ndi lamulo.”

Iye anatinso: “Tikuona kuti tipitakonso ku Stratton. Ndingakonde kuti ineyo ndikakhale munthu woyamba kugogoda pakhomo la munthu tikapitako. Tiyenera kupitakonso basi chifukwa ndi lamulo limene Yesu anapereka.”

Panopo chigamulo cha mlandu umenewu chinakhudza madera ambiri. Akuluakulu a maboma osiyanasiyana ku America atamva zimene Khoti Lalikulu linagamula anazindikira kuti malamulo awo alibenso mphamvu yoletsa ntchito ya Mboni za Yehova yofalitsa uthenga wabwino. Tikunena pano, mavuto a kulalikira khomo ndi khomo athetsedwa m’madera pafupifupi 90 ku United States.

[Bokosi patsamba 9]

“A MBONI ZA YEHOVA ZINTHU ZAWAYENDERANSO”

Charles C. Haynes, yemwe ndi wophunzira kwambiri ndipo amayang’anira ntchito zamaphunziro ku bungwe loteteza Lamulo Loyamba Lowonjezera, analemba mawu ali pamwambaŵa m’nkhani inayake yonena za ufulu yomwe ili m’kompyuta yawo yolumikizidwa pa Intaneti. Mutu wa nkhani yake unali wakuti “Ufulu wa Chipembedzo.” Haynes anapitiriza nkhani yake motere: “Mlungu watha [a Mboni] anapambana mlandu wa nambala 48 wogamulidwa ndi Khoti Lalikulu ndipo milandu yawoyi yathandiza kwambiri kuti ufulu wa nzika zonse za ku America umene uli m’Lamulo Loyamba Lowonjezera utetezedwe kwambiri.” Ndiye anachenjeza kuti: “Musaiwale kuti boma litaletsa chipembedzo chinachake kuchita zinthu mwaufulu, lingathenso kuletsa chipembedzo china chilichonse, mwinanso zonse zimene. . . . N’zoona kuti amene sakufuna ali ndi ufulu wokana kumvetsera ndiponso wotseka chitseko chawo. Koma si kuti boma ndilo likhale ndi mphamvu zomasankha anthu oyenera kugogoda m’makomo mwa ena. Moti apa Khoti Lalikulu tikulithokoza kwambiri.”

Haynes anamaliza n’kunena kuti: “Tonse tiyenera kuwathokoza kwambiri a Mboni za Yehova. Kaya anyozedwe motani, kupitikitsidwa, ngakhale kumenyedwa kumene, saleka kumenyera nkhondo ufulu wawo wachipembedzo (umene ifenso timapindula nawo.) Ndipo akapambana, tonsefe timapindula nawo.”

[Bokosi/Zithunzi pamasamba 10, 11]

ZIMENE MANYUZIPEPALA ANANENAPO ZA CHIGAMULO CHA KHOTI LALIKULU

“Khoti Liikira Kumbuyo Mboni za Yehova; Ntchito Yoyenda Khomo ndi Khomo Siyofunika Chilolezo

Nthaŵi zonse a Mboni za Yehova amakhulupirira kuti Mulungu ndiye amawathandiza akamayenda khomo ndi khomo. Koma tsopano akuthandizidwanso ndi Khoti Lalikulu m’dziko muno.”Inatero Chicago Sun-Times, pa June 18, 2002.

“Ofuna Ufulu Woyankhula Zawayendera

Nthaŵi ina a Mboni za Yehova akadzakusokonezani muli m’kati mwakudya, mwina mudzawathokoze. N’kutheka kuti palibenso gulu lina limene latetezapo ufulu wa kuyankhula wa nzika za dziko lino kuposa kagulu kosagonja pa mfundo zake zachipembedzo kameneka, komwe kali ndi anthu pafupifupi 1 miliyoni [ku United States kuno]. . . .

“Kwa a Mboni, kupita ku Khoti Lalikulu n’chizoloŵezi chawo. Agonjetsa anthu ambiri owapondereza pa milandu yoposa 24 m’zaka 65.”Inatero USA TODAY, ya pa June 18, 2002

“Kuyenda Khomo ndi Khomo Akuvomereza Mwalamulo. Apa Zinthu Zawakomera a Mboni za Yehova.

Lolemba, Khoti Lalikulu linagamula kuti andale, magulu achipembedzo, mabungwe a achinyamata, ndiponso anthu ena ngovomerezedwa mwalamulo kuyenda khomo ndi khomo n’kumachita ntchito yawo popanda kukatenga kaye chilolezo kuboma.”—Inatero San Francisco Chronicle, pa June 18, 2002.

Khoti Lalikulu Lati: Palibe Zoletsa Mboni za Yehova Ndiponso Magulu a Achinyamata Kugogoda M’makomo

WASHINGTON—Khoti Lalikulu lero lagamula kuti Malamulo a dziko lino amateteza ufulu wa amishonale, andale ndiponso anthu ena wogogoda m’makomo a anthu popanda kukatenga kaye chilolezo kuboma. . . .

“Movomerezedwa ndi oweruza 8 pa oweruza 9, khotili lanena momveka bwino kuti kuuza munthu uthenga winawake pakhomo pake kuli m’gulu la ufulu woyankhula woperekedwa ndi Lamulo Loyamba Lowonjezera.”Inatero Star Tribune, ya ku Minneapolis, pa June 18, 2002.

[Chithunzi patsamba 9]

Jasitisi Stevens

[Mawu a Chithunzi]

Stevens: Collection, The Supreme Court Historical Society/Joseph Bailey