Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi AKristu Amafunika Kuti Azikhala Osauka?

Kodi AKristu Amafunika Kuti Azikhala Osauka?

Lingaliro la Baibulo

Kodi AKristu Amafunika Kuti Azikhala Osauka?

NTHAŴI inayake Yesu anauza wolamulira wina wachinyamata kuti ayenera kukagulitsa katundu wake yense n’kuthandiza anthu osauka. Nkhaniyi imati mawu a Yesuŵa sanam’sangalatse munthuyu ndipo anachokapo akudandaula, “pakuti anali mwini chuma chambiri.” Kenaka Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Okhala nacho chuma adzaloŵa mu Ufumu wa Mulungu ndi kuvuta nanga!” Ndipo ananenanso kuti: “N’kwapafupi kuti ngamila ipyole diso la singano, koposa mwini chuma kuloŵa Ufumu wa Kumwamba.”—Marko 10:21-23; Mateyu 19:24.

Kodi Yesuyo ankatanthauza chiyani? Kodi chuma ndi kulambira koona siziyenderana? Kodi Akristu azidzimvera chisoni akakhala andalama? Kodi Mulungu amafuna kuti Akristu azichita kukhala amphaŵi enieni?

Mulungu Amalandira “Anthu Onse”

Kalekalelo Mulungu sanafune kuti Aisrayeli akhale amphaŵi. Taganizirani izi: Iwo atayamba kukhala m’dziko limene anapatsidwa, anayamba kuchita ulimi ndi ntchito zina zowathandiza ndi mabanja awo. Zinthu monga mavuto a zachuma, nyengo yoipa, matenda kapena kusadziŵa ntchito zinkawabwezera m’mbuyo ngakhale atayesetsa ndithu. Chilamulo cha Mose chinalamula Aisrayeli kuti aziganizirana ngati wina wagwa m’vuto la zachuma n’kusauka. (Levitiko 25:35-40) Komabe ena analemera. Akuti Boazi, munthu yemwe anali wokhulupirika kwambiri amene anadzakhala mu fuko limene Yesu anabadwira anali “munthu mwini chuma chambiri.”—Rute 2:1.

Zinthu zinakhalabe choncho mpaka panthaŵi ya Yesu. Poyankhula kwa munthu wachuma amene tam’tchula kuchiyambi kwa nkhaniyi, sikuti Yesu anali ndi maganizo olimbikitsa zakuti Akristu azikhala amphaŵi otheratu. Koma kuti ankaphunzitsa anthu phunziro lofunika kwambiri. Anthu angamaonedi ngati kuti n’zosatheka kuti anthu achuma akhale odzichepetsa n’kumatsatira zimene Mulungu amanena kuti tipulumutsidwe. Komatu Yesu anati: “Ichi sichitheka ndi anthu, koma zinthu zonse zitheka ndi Mulungu.”—Mateyu 19:26.

Akristu amene analipo zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino ankalandira “anthu onse.” (1 Timoteo 2:4) Pakati pa anthu ameneŵa, ena anali achuma kwambiri, ena analibe chuma chambiri ndiponso ena anali amphaŵi. Anthu ena angakhale oti anapeza chuma chawo asanakhale Akristu. N’kuthekanso kuti nthaŵi zina ena zinthu zikawayenderako bwino ndiponso akamayendetsa bwino ndalama zawo, ankalemera.

N’chimodzimodzinso masiku ano, ubale wa Akristu onse uli ndi anthu opata mosiyanasiyana. Iwo onse amayesetsa kutsatira malangizo a m’Baibulo pankhani ya ndalama, chifukwatu munthu aliyense angayambe kukondetsa chuma. Phunziro limene Yesu anaphunzitsa lokhudza wolamulira wachinyamata wachuma uja n’lochenjeza Mkristu aliyense kudziŵa kuti ndalama ndiponso katundu amene ali naye angathedi kum’lamulira munthu molakwika.—Marko 4:19.

Chenjezo kwa Anthu Olemera

Kukhala ndi chuma sikoletsedwa m’Baibulo, koma choletsedwa n’kukonda ndalama. Paulo, amene analemba nawo Baibulo anati: “Muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pandalama.” Iye ananena kuti ponyalanyaza zinthu zauzimu chifukwa chofunitsitsa kulemera, ‘ena anataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zowawa zambiri.’—1 Timoteo 6:10.

N’zochititsa chidwi kuti Paulo anapereka malangizo osapita m’mbali kwa anthu achuma okha. Iye anati: “Lamulira iwo achuma m’nthaŵi ino ya pansi pano, kuti asadzikuze, kapena asayembekezere chuma chosadziŵika kukhala kwake, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kochulukira, kuti tikondwere nazo.” (1 Timoteo 6:17) Zikuonekeratu apa kuti ngozi imene ilipo ndi yakuti anthu achuma angathe kuyamba kunyada n’kumadziona kuti iwowo ndi apamwamba kuposa ena. Komanso akhoza kumadzipusitsa poganiza kuti chuma n’chimene chingawapatse moyo wabwino, pamene Mulungu yekha ndiye angatero.

Akristu achuma angapeŵe zoopsazi pochita ‘ntchito zabwino zochuluka,’ monga kukonda “kugaŵira ena,” kuwapatsako thandizo anthu ovutika. (1 Timoteo 6:18) Akristu onse, kaya achuma kapena osauka, akhozanso kugwiritsira ntchito zina mwa zinthu zimene ali nazo pantchito yofalitsa uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu yomwe ili ntchito yofunika kwambiri kwa Akristu oona masiku ano. Mtima wooloŵa manja woterewu umasonyeza kuti munthuyo amadziŵadi kugwiritsira ntchito bwino chuma chake ndipo Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu, omwe amakonda munthu wopereka mokondwera, amasangalala naye.—Mateyu 24:14; Luka 16:9; 2 Akorinto 9:7.

“Zinthu Zofunika Kwambiri”

Ndithudi, si kuti Akristu ayenera kukhala osauka. Komanso si kuti azichita kufunitsitsa “kukhala achuma.” (1 Timoteo 6:9) Kwawo n’kuchita khama basi pogwira ntchito zawo kuti akhale ndi moyo wosachita kuzunzika nawo. Iwo angakhale opata mosiyanasiyana malingana ndi khama lawo ndiponso kusiyanasiyana kwa zinthu ndiponso kayendedwe kachuma kumene akukhalako.—Mlaliki 11:6.

Kaya ngachuma kapena ayi, Akristu ayenera kuonetsetsa kuti ‘akulimbikira pa zinthu zofunika kwambiri.’ (Afilipi 1:10, NW) Zinthu zauzimu zikamakhala zofunika kwambiri kwa iwowo, ndiye kuti ‘akudzikundikira okha maziko okoma ku nyengo ikudzayi, kuti akagwire moyo weniweniwo.’—1 Timoteo 6:19.