Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamatengeke N’zochita za Anzanga?

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamatengeke N’zochita za Anzanga?

Achinyamata Akufunsa Kuti . . .

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamatengeke N’zochita za Anzanga?

Munthu ungatengere zochita za anzako kwina kuli konseko.”—Anatero mnyamata wina wa zaka 16, dzina lake Jesse.

“Vuto limodzi lalikulu kwambiri limene ndinkakumana nalo ndidakali wamng’ono linali loyesetsa kuti ndisatengere zochita za anzanga a kusukulu.”—Anatero mnyamata wina wa zaka 21, dzina lake Johnathan.

KUNENADI zoona, kuti musatengeke n’zochita za anzanu m’pofunika kusamala kwambiri. Komabe tikukutsimikizirani kuti mungathe ndithu kusatengeka nazo. Ndipotu mutazitenga bwino mungathe kupindula nazo. Koma kodi zingatheke bwanji?

M’nkhani yoyamba yangati yomweyi, tinakambapo za mfundo yoyamba yofunika kwambiri yakuti: N’kofunika kudziŵa kuti khalidwe la anzanu lingathedi kukusokonezani ndiponso kudziŵa mbali zomwe inuyo mumalephera. * Kodi ndi mfundo zina ziti zofunika zimene mungachite? Zinthu zothandiza zoti n’kuzitsatira zili m’Mawu a Mulungu. Miyambo 24:5 amati: “Munthu wodziŵa ankabe nalimba.” Kodi n’kudziŵa kuti kumene kungam’pangitse munthu kukhala wolimba anzake akafuna kum’sokoneza? Tisanayankhe funso limenelo, choyamba tikambe kaye za vuto limene lingapangitse kuti inuyo mutengeke n’zochita za anzanu.

Kudzikayikira N’koopsa

Nthaŵi zina achinyamata omwe ndi Mboni za Yehova amaona kuti amavutika kwambiri chifukwa cha anzawo popeza kuti amafunika kuuzako ena zimene iwowo amakhulupirira. (Mateyu 28:19, 20) Kodi nthaŵi zina mumaona kuti zikukuvutani kufotokoza zimene mumakhulupirira kwa achinyamata anzanu amene mwakumana nawo? Zimenezi zimachitika. Mtsikana wina wa zaka 18 dzina lake Melanie anati: “Kuti ndiuze anzanga kuti ndine wa Mboni, zinkandivuta kwambiri.” Mtsikanayu anapitiriza kuti: “Ndinkangoti ndikalimba mtima kuti pano pokha ndiwauza basi, ndinkangoona kuti china chandibwerera mumtimamu, basi n’kuchitanso mantha.” Apa zikuoneka kuti kuchita mantha ndi anzakewo kunkamulepheretsa kuti awauze zimene amakhulupirira.

Baibulo limatitsimikizira kuti ngakhale amuna ndi akazi okhala ndi chikhulupiriro champhamvu kwambiri anachitako mantha kuuza anthu za Mulungu. Mwachitsanzo, Yeremiya adakali wamng’ono ankadziŵa kuti akamvera lamulo la Mulungu lakuti alankhule molimba mtima adzanyozedwa ndi kuzunzidwa. Komanso Yeremiya ankadzikayikira. N’chifukwa chiyani anatero? Iye anauza Mulungu kuti: “Taonani, sindithayi kunena pakuti ndili mwana.” Kodi Mulungu anavomereza kuti popeza Yeremiya ndi wamng’ono sangathe kulankhula? Ayi ndithu. Yehova anauza mneneriyo kuti: “Usati, ‘ndine mwana.’” Yehova sanalekere pompo koma anapitiriza kum’patsa mnyamata wodzikayikirayu ntchito yofunika kwambiri.—Yeremiya 1:6, 7.

Tikayamba kudzikayikira tokha, zingativute kuti tisatengere za ena. Zimene ofufuza angapo akhala akupeza zikutsimikizira zimenezi. Mwachitsanzo, kumbuyoku m’chaka cha 1937 katswiri wina wa sayansi dzina lake Muzafer Sherif anachita kafukufuku amene anatchuka kwambiri. Iye anaika anthu m’chipinda cha mdima bii, n’kuwayatsira kagetsi kakang’ono zedi kenaka n’kuwafunsa kuti anene kuti kagetsiko kanasuntha mwautali wotani.

Komatu kagetsiko sikanasunthe n’komwe, kungoti maso awo sanaone bwinobwino. Anthuwo atawafunsa payekhapayekha, aliyense ananena zinthu zosiyana ndi za anzake. Komano anawafunsa ali pagulu kuti anene mokweza zomwe aona. Ndiyeno atatero, zinachitika n’zotani? Posadzidalira, ena anayamba kutengera zonena za anzawo. Atafunsidwa kambirimbiri, mayankho awo anayamba kufanana mpaka panapezeka kuti onse akuyankha za “m’chigulugulu.” Ngakhale pamene anadzafunsidwanso aliyense payekhapayekha, iwo anayankhabe za m’chigulugulu zomwezo.

Zimenezi zikuonetsa mfundo yofunika kwambiri yakuti kulephera kukhala munthu wotsimikiza kapena wodzidalira kumapangitsa anthu kuti atengeke n’zochita za anzawo. N’zochititsa chidwi, si eti? Ndipotu anthu angatengeke n’zochita za anzawo ngakhale pankhani zikuluzikulu, monga zokhudza mmene amaonera nkhani ya kugonana asanakwatirane, kugwiritsira ntchito mankhwala ozunguza bongo ngakhalenso zimene amalakalaka m’moyo wawo. Ngati titatayirira n’kumangotsatira za “m’chigulugulu” pankhani zoterezi, tikhoza kudzisokonezera tokha tsogolo lathu. (Eksodo 23:2) Kodi n’chiyani chimene tingachite?

Kodi pamenepa, inuyo mukanafunsidwa za kagetsi kaja koma mukuchita kudziŵiratu kuti sikanasunthe n’komwe mukuganiza kuti mukanayankha bwanji? N’kutheka kuti simukanalola kuti mutengere za m’chigulugulu. Eetu, timafunika kuti tizidzidalira. Koma kodi n’kudzidalira kotani kumene tikunena pano, ndipo kodi mphamvu yake yokhala odzidalira tingaipeze kuti?

Dalirani Yehova

N’kutheka kuti mumamva nkhani zambirimbiri zoti mudzikhala odzidalira. Koma anthu sagwirizana chimodzi pankhani ya mmene tingakhalire odzidalira ndiponso zomwe timafunika kuchita pankhaniyi. Baibulo lili ndi malangizo omveka bwino akuti: “Ndiuza munthu aliyense wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa; koma aganize modziletsa yekha.” (Aroma 12:3) M’Baibulo la Charles B. Williams, vesi limeneli analimasulira kuti: “Ndikuuza aliyense wa inu kuti asadzione ngati wolemekezeka kuposa mmene alilidi, koma azidziona moyenera.”

‘Kusadziona ngati wolemekezeka kuposa mmene ulilidi’ kumam’pangitsa munthu kukhala wosadzikuza, wosadzithemba kapena wosatumbwa. Koma kukhala munthu wotere, kungafunikebe kudzidalira poganiza ndiponso kuchita zinthu mwanzeru. Mlengi wanu anakupatsani mphatso yotha kuganiza, ndipo imeneyi si mphatso wamba ayi. (Aroma 12:1) Kudziŵa zimenezi kungakuthandizeni kupeŵa kuti anthu amene mumakhala nawo azikupangirani zochita. Komabe pali kudzidalira kwina kumene kungakhale kothandiza kwambiri kuti zinthu zikuyendereni bwino.

Mfumu Davide inauziridwa kulemba kuti: “Inu ndinu chiyembekezo changa, Ambuye Yehova; mwandikhalira wokhulupirika kuyambira ubwana wanga.” (Salmo 71:5) Eetu, Davide anadalira kwambiri Atate wake wakumwamba, ndipo anayamba kuchita zimenezi adakali wamng’ono. Iye anali “mwana,” mwinatu wazaka zosakwana 20 pamene Mfilisti wamphamvu dzina lake Goliati anaderera asilikali onse a ku Israyeli kuti palibe yemwe akanam’gonjetsa pomenyana naye. Asilikaliwo anaopadi. (1 Samueli 17:11, 33) Mwinatu ankangoopa chifukwa chongomvera zonena za anzawo. Sitikukayikira kuti iwo ankaopsezana pokambirana za msinkhu ndiponso mphamvu zimene Goliati anali nazo n’kumangoti aliyense amene angalolere kukamenyana naye ndiye kuti mutu wake sukuyenda bwino. Zimenezo sizinam’khudze n’komwe Davide. Sizinam’khudze chifukwa chiyani?

Taonani mawu aŵa amene Davide anauza Goliati: ‘Iwe ukudza kwa ine ndi lupanga, ndi mkondo, ndi nthungo; koma ine ndafika kwa iwe m’dzina la Yehova wa makamu, Mulungu wa ankhondo a Israyeli amene iwe unam’nyoza.’ (1 Samueli 17:45) Sikuti Davide sankadziŵa za msinkhu wa Goliati, mphamvu zake kapenanso zida zankhondo zimene anali nazo ayi. Koma kuti ankadziŵa zakuti kumwambaku kuli winawake wamphamvu kuposa wina aliyense pansi pano. Ankadziŵa kuti Goliati angakhalenso yani pomuyerekeza ndi Yehova Mulungu. Ndiye ngati Yehovayo anali kumbali yake, kodi Davideyo akanaopanso Goliati ngati? Kudalira Mulungu kotereku kunam’pangitsa Davide kuona kuti anali wotetezereka. Sanatengeke n’zonena za wina aliyense.

Kodi inunso mumadalira Yehova chimodzimodzi? Iye sanasinthebe chichokereni nthaŵi ya Davideyo. (Malaki 3:6; Yakobo 1:17) Mukaphunzira kwambiri za iye mudzakhulupirira kwambiri zimene amakuuzani m’Mawu ake. (Yohane 17:17) M’menemo mudzapezamo malangizo odalirika okutsogolerani zochita m’moyo mwanu ndiponso okuthandizani kusatengeka n’zochita za anzanu. Palinso chinthu china chomwe mungachite kuwonjezera pa kudalira kwanu Yehova.

Sankhani Anthu Abwino Okulangizani

Mawu a Mulungu amalimbikitsa za kufunika kofunafuna anthu abwino okulangizani. Miyambo 1:5 amati: “Wozindikira afikire kuuphungu.” Makolo anu, omwe amafunitsitsa kwambiri kuti zinthu zikuyendereni bwino ndiwo angakulangizeni. Mtsikana winawake dzina lake Indira akuzidziŵa bwino zimenezi. Iye anafotokoza kuti: “Ineyo panopo ndikutsatira choonadi chifukwa chakuti nthaŵi zonse makolo anga ankandithandiza maganizo pogwiritsira ntchito Malemba ndiponso ankandithandiza kuona kuti Yehova alikodi.” Achinyamata ambiri amaonanso choncho.

Ngati muli mumpingo wachikristu, okuthandizani abwino kwambiri ali komweko, oyang’anira oikidwa kapena kuti akulu ndiponso Akristu anzathu achikulire. Mtsikana winawake dzina lake Nadia anati: “Ndinkachita chidwi kwambiri ndi akulu a kumpingo kwathu. Ndikukumbukira nkhani ina imene woyang’anira wotsogolera anakamba imene makamaka inali yokhudza achinyamata. Msonkhanowo utangotha, ineyo ndi mnzanga winawake tinakondwera kwambiri chifukwa chakuti zimene anali atanena n’zomwe ifeyo tinkaona kuti zimatichitikira.”

Njira ina yothandiza kwambiri yoti musatengeke n’zochita za anzanu ochita zoipa ndiyo kutsatira zochita za anzanu abwino. Mukasankha bwino anzanu ocheza nawo, iwo angakuthandizeni kuti muzikhala ndi zolinga zabwino ndiponso makhalidwe abwino. Kodi tingawasankhe motani? Musaiwale uphungu uwu: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: Koma mnzawo wa opusa adzaphwetekedwa.” (Miyambo 13:20) Nadia anali wosamala kwambiri posankha anzake kusukulu, omwe anali okhulupirira anzake, amakhalidwe ofanana ndi ake. Iye anati: “Tinkati anyamata akabwera ‘kudzatiyamba,’ tinkaikirana kumbuyo.” Anzathu abwino angathandize kuti tikhale abwino kwambiri. M’pofunikadi khama kuti tiwapeze.

Choncho tikukutsimikizirani kuti ngati mutadalira kwambiri Yehova, mutafunitsitsa kuti Akristu achikulire akulangizeni ndiponso mutasankha bwino anzanu, simungatengeke n’zochita za anzanu onse. Makamaka tinene kuti mukhoza kukhala chitsanzo chabwino kwa anzanu ndipo mungawathandize kuti akhale nanu limodzi panjira ya kumoyo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Onani nkhani yakuti “Kodi N’zothekadi Kuti Khalidwe la Anzanga Lingandisokoneze?” mu Galamukani! ya pa December 8, 2002.

[Mawu Otsindika patsamba 16]

Funafunani anzanu abwino omwe amakonda Mulungu ndiponso makhalidwe ake abwino ngati mmene mumachitira inunso.

[Zithunzi patsamba 16]

“Mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.”—1 Akorinto 15:33

“Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru.”—Miyambo 13:20