Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuvutikira Chikhulupiriro ku Slovakia

Kuvutikira Chikhulupiriro ku Slovakia

Kuvutikira Chikhulupiriro ku Slovakia

YOSIMBIDWA NDI JÁN BALI

INE NDINABADWA pa December 24, 1910, m’mudzi wa Záhor, umene tsopano uli kum’maŵa kwa dziko la Slovakia. Panthaŵi imeneyo mudzi wathu unali m’manja mwa dziko la Austria-Hungary. Mu 1913, mayi anga ananditenga kupita nane ku United States potsatira bambo anga. Titatha zaka ziŵiri ku Gary, m’boma la Indiana komwe tinafikira, mlongo wanga Anna anabadwa. Kenaka bambo anga anadwala n’kumwalira mu 1917.

Ndinayamba kukonda kuŵerenga, ndipo ndinkakonda kwambiri mabuku a zachipembedzo. Ndinkachita maphunziro a ana, otchedwa Sande Sukulu, ku tchalitchi cha Calvinist Church ndipo aphunzitsi anga anaona kuti ndine munthu wokonda kwambiri za Mawu a Mulungu. Motero, pofuna kundithandiza, anandipatsa Baibulo la Holman, limene linali ndi mafunso okwana 4,000 okhala ndi mayankho ake. Kwa mwana wa zaka 11 zokha ngati ine, mafunso amenewo anali okwanira kuti ndiganizepo mozama.

‘Choonadi N’chimenechi’

M’nthaŵi imeneyi, anthu ena amene anasamukira m’derali kuchokera ku Slovakia analoŵa m’gulu lotchedwa Ophunzira Baibulo, lomwe linali dzina la Mboni za Yehova masiku amenewo. Bambo anga aang’ono a Michal Bali anali m’gulu limeneli ndipo ankatiuzako choonadi cha m’Baibulo. Koma m’chaka cha 1922, mayi anga anabwerera nafe ku Záhor pamodzi ndi mlongo wanga. Panthaŵi imeneyi mudzi wa Záhor unakhala mbali ya kum’maŵa kwa dziko la Czechoslovakia.

Posakhalitsa, bambo anga aang’ono aja ananditumizira mabuku onse otchedwa Studies in the Scriptures, olembedwa ndi Charles Taze Russell, komanso magazini onse a Nsanja ya Olonda a m’mbuyomo kuyambira yoyambirira yeniyeni ya July 1, 1879. Ndinawaŵerenga onse, ena n’kumachita kuwabwereza kangapo, mpaka ndinafika potsimikiza kuti choonadi cha Baibulo chimene ndakhala ndikufunafuna chija n’chimenechi basi.

Panthaŵi imeneyi Ophunzira Baibulo ena ochokera ku Slovakia anabwerera kumudzi kuchokera ku United States. Aŵa ndiwo anayambitsa gulu loyamba la Ophunzira Baibulo olankhula Chisilovaki ku Czechoslovakia. Ine ndi mayi tinkapita ku misonkhano imeneyi kwathu ku Záhor ngakhalenso kumadera ena akufupi.

Misonkhano yake inkafanana ndi ya Akristu a m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino. Nthaŵi zambiri tinkakumana kunyumba ya munthu wina wa m’gulu la Ophunzira Baibulowo, ndipo tinkakhala mozungulira tebulo titaika nyali pakati pa tebulopo. Pagulu ponsepo mwana kwambiri ndinali ineyo motero ndinkakhala kumbuyo pang’ono, n’kumamvetsera ndili kukamdima. Koma nthaŵi zina ankandiuza kuti ndiyankhulepo. Penapake pakavuta kumvetsa m’Chisilovaki, ankangoti: “Ján, tatiuza, kodi Chingelezi ichi chikutanthauza kuti chiyani?” Ndinkayandikira panali nyalipo mwachangu n’kumasulira m’Chisilovaki zimene zanenedwa m’buku la Chingelezilo.

Munthu wina amenenso analoŵa gulu la Ophunzira Baibulo ku United States n’kubwerera m’dziko limene panthaŵiyi anali atalitcha kuti Czechoslovakia anali Michal Šalata. Iye anabwerera m’mudzi wakufupi ndi kwathu wa Sečovce komwe ankakhala poyamba, ndipo anathandiza pokhazikitsa ntchito yolalikira ku Czechoslovakia. Mbale Šalata ankapita nane kolalikira. Kenaka m’chaka cha 1924, ndili ndi zaka 13, ndinam’pempha kuti andibatize. Mayi anga ankaona kuti ndachepa nazo, koma ndinawatsimikizira kuti mtima wanga wonse unali pamenepa. Motero, m’mwezi wa July, posonyeza kuti ndadzipereka kwa Yehova, ndinabatizidwa mumtsinje wa Ondava pamsonkhano wina watsiku limodzi womwe unachitikira pafupi ndi mtsinjewo.

Mwayi Waukulu Kwambiri Wotumikira

Ndili ndi zaka 17, ndinamva kuti m’mudzi wapatali pang’ono ndi kumene ndinali kulalikira muchitika mwambo wamaliro. Aka kanali koyamba kwa Ophunzira Baibulo m’deralo kuchita mwambo wamaliro. Nditafika, ndinadutsa pagulu la anthu a m’mudziwo amene ankangondiyang’ana mwachidwi uku ndikuyenda molunjika munthu wokamba nkhani yamalirowo. Nditafika pamene iye anali, anandiyang’ana n’kunena kuti: “Ndiyambe kuyankhula ndi ineyo, kenaka iweyo upitiriza.”

Mutu wa nkhani yanga unagona pa lemba la 1 Petro 4:7 limene limati: “Chitsiriziro cha zinthu zonse chili pafupi.” Ndinafotokoza mwa Malemba kuti ngakhale kuvutika ndiponso kufa kwatsala pang’ono kutha, ndipo ndinalongosolanso za chiyembekezo cha chiukiriro. (Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15) Ndinkaoneka ngati kamwana kwambiri koma anthu onse anali tcheru kumvetsera, mwinanso anatero pochita chidwi ndi msinkhu wangawo.

Mu Nsanja ya Olonda ya pa September 15, 1931, munali nkhani yosangalatsa kwambiri yakuti sitikufunanso kumatchedwa Ophunzira Baibulo kapena kutchedwa mayina ena otere koma tikufuna kumatchedwa kuti Mboni za Yehova. Ophunzira Baibulo a m’dera lathu ataŵerenga zimenezi anakonza zoti akumane mwapadera. Motero Ophunzira Baibulo pafupifupi 100 anakumana m’mudzi wa Pozdišovce. Pamsonkhanowu ndinapatsidwa mwayi wokamba nkhani yakuti: “Dzina Latsopano,” yotengedwa mu Nsanja ya Olonda ndaitchula ija.

Anthu onse pamsonkhanopo anakweza manja ali osangalala atawafunsa ngati akugwirizana nayo mfundo yomwe Akristu anzawo anamanga m’madera ena apadziko lonse. Kenaka tinatumiza telegalamu ku likulu la padziko lonse la Mboni za Yehova ku Brooklyn, mumzinda wa New York. Tinalemba kuti: “Ife, Mboni za Yehova amene tasonkhana lero kuno ku Pozdišovce, tagwirizana ndi zimene Nsanja ya Olonda yalongosola zokhudza dzina latsopano, ndipo tikulivomera dzina latsopano limeneli lakuti Mboni za Yehova.”

Dera lalikulu la Slovakia ndi Transcarpathia, lomwe linali m’dziko la Czechoslovakia nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse isanachitike, linasanduka gawo labwino kulalikiramo. Tinalalikira m’gawo lalikulu kwambirili poyenda wapansi komanso pokwera sitima, mabasi ndiponso njinga. Panthaŵiyi “Seŵero la Pakanema la Chilengedwe,” lomwe linkakhala ndi zithunzithunzi komanso mawu ofotokozera zithunzizo, anali atalionetsa m’mizinda yambiri. Nthaŵi iliyonse akaonetsa seŵeroli, ankalemba maadiresi a anthu onse amene anachita nalo chidwi. Ineyo ndinapatsidwa maadiresi ambiri otereŵa ndipo anandipempha kuti ndipeze a Mboni oti akacheze ndi anthuwo. M’mizinda ina, tinkalipira holo kuti ndikambiremo nkhani yotsendera mfundo zimene zinalongosoledwa m’kanemayo.

Cha m’ma 1930, ndinali ndi mwayi wokhala nthumwi m’misonkhano ikuluikulu imene inachitikira mumzinda wa Prague, likulu la dzikoli. M’chaka cha 1932 analinganiza kuti ku Czechoslovakia kudzakhale msonkhano woyamba wa mayiko. Tinakakumana m’bwalo lotchedwa Varieté Theatre. Mutu wa msonkhanowo unali wakuti, “Ulaya Asanawonongedwe,” ndipo unachititsa chidwi anthu ambiri mwakuti panafika anthu pafupifupi 1,500. Msonkhano wina wotere unachitikira ku Prague komweko, mu 1937, ndipo ndinakambaponso nkhani imodzi pamsonkhanowu. Panali nthumwi zochokera m’mayiko ambirimbiri a ku Ulaya, ndipo tonse tinalimbikitsidwa mwakuti tinatha kupirira mavuto amene tinakumana nawo pasanathe nthaŵi yaitali, pa nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse.

Ndinakwatira, Kenaka N’kukumana ndi Mavuto Osasimbika

Titabwerera ku Czechoslovakia, ineyo pamodzi ndi mayi anga tinkakonda kuchitira limodzi ntchito yolalikira ndi Ophunzira Baibulo anzathu m’dera la kufupi ndi ku Pozdišovce. Kumeneku ndinakumanako ndi kamtsikana kenakake kodolola mtima dzina lake Anna Rohálová. Titasinkhukirapo, kukondana kwathu kunafika pena osangoti kwa mbale ndi mlongo wachikristu. Motero m’chaka cha 1937 tinakwatirana. Kuyambira pamenepo, Anna ankandilimbitsa mtima, ngakhale pamavuto amene tinadzakumana nawo mosakhalitsa.—2 Timoteo 4:2.

Titangokwatirana, tinadziŵa kuti ku Ulaya kuyambika nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse. Pofika mwezi wa November 1938, madera a kum’mwera kwa Transcarpathia ndi Slovakia anali atalandidwa ndi dziko la Hungary, lomwe linkagwirizana ndi dziko la Germany lolamulidwa ndi chipani cha Nazi. Apolisi a ku Hungary analetsa misonkhano yathu, ndipo nthaŵi zambiri tinkaitanidwa kuti tikaonekere kupolisi.

Nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse itayamba mu September 1939, ambiri mwa ife amene tinachokera ku Záhor, amuna ndi akazi omwe, tinagwidwa n’kukaikidwa m’chinyumba china chakale kufupi ndi ku Mukacheve, kumene tsopano amati ku Ukraine. Kumeneko tinapezako anzathu a Mboni ambirimbiri ochokera m’mipingo ya ku Transcarpathia. Titakhala kwa miyezi itatu kapena inayi akutifunsa n’kumatimenya kaŵirikaŵiri, anatizenga mlandu m’khoti linalake la asilikali. Tonse anatifunsa funso limodzi lokha lakuti: “Kodi mukuvomera kukhala asilikali a dziko la Hungary pomenya nkhondo ndi dziko la U.S.S.R.?” Titakana anatipatsa chilango kenaka n’kutitumiza kundende ya ku Budapest, ku Hungary komweko yomwe ili pamalo otchedwa 85 Margit Boulevard.

Akaidi tonse kumeneku sankatipatsa chakudya chokwanira. Posachedwa matenda anafalikira ndipo akaidi anayamba kufa. Mtima wanga unakhalako pansi mkazi wanga atafika kudzandiona kuchokera ku Záhor komwe n’kutali kwambiri! Ngakhale kuti tinayankhulana kwa mphindi zisanu zokha basi komanso motchingiridwa ndi zitsulo, ndinam’yamika kwambiri Yehova pondipatsa mkazi wokhulupirika chonchi. *

Kuchoka Kundende Kupita ku Kampu Yozunzira Anthu

Nditangochoka kundende anapita nane m’tauni yotchedwa Jászberény ku Hungary, ndipo Mboni zinanso 160 anali atazipititsa kale komweku. Tili kumeneku, msilikali wina wa ku Hungary anatipatsa mwayi komaliza pofuna kuti timvere boma la Hungary. Iye anati: “Ngati mwavomera kuloŵa usilikali imani apa.” Koma palibe amene anatero. Ndiye msilikaliyo anati: “Zimene mukuchitazi ineyo sindikugwirizana nazo, koma chinan’china anthu inu muli ndi chikhulupiriro cholimba.”

Patapita masiku angapo, tinakwera sitima ya pamtsinje wa Danube kupita ku kampu yozunzirako anthu ya kufupi ndi mzinda wina wa ku Yugoslavia wotchedwa Bor. M’sitimamo, asilikali aja pamodzi ndi bwana wawo anatiyesa kambirimbiri kuti tigonje pa chikhulupiriro chathu. Bwana wawoyo anawauza kuti azitimenya ndi mfuti zawo, kutimenya mateche ndi jombo zawo, ndi kutizunza m’njira zina.

Atatipereka m’manja mwa Lefutenanti Kolonelo András Balogh, msilikali yemwe ankayang’anira kampu ya ku Bor imeneyi, iyeyu anatiuza kuti: “Ngati zimene ndakumverani zili zoona, zamoyo muiwaliretu.” Koma ataŵerenga kalata yochokera kwa akuluakulu aboma yomwe inali mu enivulupu yomata, mkuluyu anayamba kuchita zinthu motilemekeza. Iye anatilola kumayendayendako ndipo mpaka anatilola kumanga kamphala kathukathu. Ngakhale kuti chakudya chinali chosoŵa, ifeyo tinali ndi khitchini yathuyathu motero tinkagaŵana chakudya mosakondera.

Mu March, m’chaka cha 1944, dziko la Germany linayamba kulanda dziko la Hungary. Panthaŵi imeneyi Balogh anam’chotsa n’kubweretsapo msilikali wina wamkulu wa chipani cha Nazi dzina lake Ede Marányi. Mkulu ameneyu anakhwimitsa malamulo kwambiri n’kungokhala ngati ku makampu a chipani cha Nazi. Komabe pasanapite nthaŵi yaitali, gulu la asilikali a ku Russia linafika, ndipo kampu ya ku Bor anaisamutsa. Kenaka tili paulendo wosamukawu, tinaona Ayuda ambirimbiri akupululidwa ku Cservenka. Sitinamvetse kuti tinapulumuka bwanji.

Titafika pamalire a dziko la Hungary ndi Austria, anatilamula kuti tizikumba maenje ozikamo mfuti za mtundu wa chiwaya. Ndiye tinalandula kuti ifeyo tinagwidwa ukaidi chifukwa chokana kuchita nawo zinthu zokhudza nkhondo zomwezi. Popeza ndinakhala patsogolo, msilikali wina wamkulu wa ku Hungary anandigwira n’kuyamba kundimenya zolimba. Anakalipa kwambiri, amvekere: “Ndikupha ukumva! Iweyo ukakana ntchitoyi anzakoŵa atengera zopusa zakozo!” Apa n’kadafa chipanda wa Mboni wina wachikulire ndithu, András Bartha amene ankatsogolera ntchito yathu yolalikira. Iyeyu analimba mtima kundilanditsa. *

Patapita milungu yochepa chabe, nkhondoyo inatha ndipo tinayamba ulendo wobwerera kwathu. Akaidi anzathu ku Bor amene anayambirira kumasulidwa, anakanena kuti tonse amene anatipititsa ku Cservenka tinaphedwa. Motero kwa miyezi isanu ndi umodzi mkazi wanga ankadziona ngati wamasiye. Koma anadabwa kwambiri tsiku lina ine nditangoti mbwee, kutulukira! Misozi yachisangalalo inali chuchuchu uku tikukumbatirana pokumananso patatha zaka zambirimbiri.

Kuyambitsanso Ntchitoyo

Nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse itatha, dziko la Slovakia analiphatikizanso ndi dziko la Czechia n’kupanga dziko la Czechoslovakia. Komano chigawo cha Transcarpathia, chomwe mbali yake yaikulu inali m’dziko la Czechoslovakia nkhondoyo isanayambe, chinakhala mbali ya Ukraine, dziko lomwe linali mu Soviet Union. M’chaka cha 1945, ine ndi Michal Moskal tinapita mumzinda wa Bratislava, umene tsopano uli likulu la Slovakia, ndipo kumeneku tinakakumana ndi abale ena amaudindo kuti tiyambitsenso ntchito yolalikira. Inde tinali otopa komanso othedwa nzeru, komabe tinali ofunitsitsa kupitiriza kukwaniritsa ntchito imene tinatumidwa, yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.—Mateyu 24:14; 28:18-20.

Nkhondoyo itatha, misonkhano ikuluikulu inalimbikitsa kwambiri ntchito yathu. M’mwezi wa September 1946, tinachita msonkhano woyamba wadziko lathu lonselo m’mzinda wa Brno. Ndinapatsidwa mwayi wokamba nkhani ya mutu wakuti: “Kututa, Kutha Kwa Dzikoli.”

M’chaka cha 1947 tinachitanso msonkhano wina wadziko lonse ku Brno. Pamsonkhanowu, Nathan H. Knorr, Milton G. Henschel, ndi Hayden C. Covington, amene amadzatichezera kuchokera ku likulu la padziko lonse la Mboni za Yehova ku Brooklyn, New York, anakamba nkhani zolimbikitsa kwambiri. Ndinapatsidwa mwayi womasulira nkhanizo. Ngakhale kuti panthaŵiyi ku Czechoslovakia kunali ofalitsa a Ufumu okwana pafupifupi 1,400 basi, pa nkhani ya onse panali anthu 2,300.

Kuzunzidwa Muulamuliro Wachikomyunizimu

M’chaka cha 1948 achipani cha Chikomyunizimu analanda boma, ndipo panatha zaka 40 akuletsabe ntchito yathu yolalikira. M’chaka cha 1952 ambirife omwe aboma ankationa ngati atsogoleri anatitsekera m’ndende. Ambiri ankawaimba mlandu wofuna kusokoneza boma, koma enafe omwe tinali ochepa chabe anatiimba mlandu waukulu woukira boma. Ndiye ananditsekera m’ndende ndipo kwa chaka chimodzi ndi theka anali kufufuza nkhani yanga pondifunsa mafunso. Nthaŵi ina nditafunsa kuti kodi munthune ndagalukira boma m’njira yotani, woweruzayo anati: “Wagalukira boma chifukwa ukunena za Ufumu wa Mulungu. Ndipo ukunena kuti Ufumu umenewowo udzalanda dziko lonse. Kutanthauza kuti udzalandanso ngakhale dziko lathu la Czechoslovakia.”

Ndiye ndinam’yankha kuti: “Ngati ndi choncho ndiye kuti anthu onse amene amapempha kuti ‘Ufumu wanu udze,’ m’Pemphero la Ambuye muwaimbenso mlandu wogalukira boma.” Komabe iye analamula kuti ndikhale m’ndende kwa zaka zisanu ndi theka ndipo ananditumiza kundende yotchuka ya m’dera la Jáchymov, ku Czechoslovakia.

Zaka zimene analamula kuti ndikhale m’ndendemo zitatsala pang’ono kutha, ananditulutsa. Mkazi wanga Anna, sanatope kundilimbikitsa m’makalata, kudzandizonda ndiponso kusamalira mwana wathu, Mária. Mapeto ake tonse a m’banja langa tinayamba kukhalira limodzi ndipo tinayambanso kuchita ntchito yathu yachikristu, yomwe tinali kuchita mobisa.

Ndachita Zambiri Zosangalatsa Potumikira Yehova

Kwa zaka zoposa 70, Mboni za Yehova m’dera lathu zakhala zikuchita ntchito yawo movutikira, ndipo kwa nthaŵi yaitali, zatero zili muulamuliro wa Chikomyunizimu. N’zoona kuti panopo ndakalamba ndipo mphamvu zatha m’thupi, koma ndikuthabe kutumikira monga mkulu wa mpingo wachikristu ku Záhor pamodzinso ndi anthu ena okhulupirika monga Ján Korpa-Ondo, yemwe adakali ndi moyo ndipo ali ndi zaka 98. * Mkazi wanga wapamtima, yemwe anali mphatso yochokeradi kwa Yehova, anamwalira mu 1996.

Ndimakumbukira bwinobwino zimene zinalongosoledwa pa masamba 228 mpaka 231 m’buku lakuti The Way to Paradise (Njira ya ku Paradaiso), lomwe linafalitsidwa mu 1924. Bukulo linauza amene akuŵerengayo kuti angoganizira kuti akumvetsera anthu aŵiri amene auka kwa akufa. Anthuwo sakudziŵa kuti ali kuti makamaka. Ndiyeno pakufika munthu wina amene anapulumuka Armagedo ndipo akuwalongosolera anthu aŵiriwo kuti aukitsidwa m’paradaiso. (Luka 23:43) Ineyo ngati ndidzadutse pa Armagedo, ndingadzakonde kwambiri kuwalongosolera zinthu zotere anthu apamtima panga onse monga, mkazi wanga, mayi anga ndi ena akadzaukitsidwa. Koma ngati nditafa Armagedo isanafike, n’dzasangalalanso kwambiri kuti munthu wina m’dziko latsopano adzandilongosolere zimene zimachitika ine nditafa.

Pakali pano kwanga n’kuthokoza kwambiri pokhala ndi chimwayi chankhaninkhani chotha kuyankhula ndi Wolamulira Wamkulu m’chilengedwe chonse ndiponso kupalana naye ubwenzi wapamtima. Ndikufunitsitsa kwambiri kuti m’moyo mwanga ndizitsatirabe mawu a mtumwi Paulo pa Aroma 14:8 omwe amati: “Tingakhale tili ndi moyo, tikhalira Ambuye moyo; kapena tikafa, tikhala ake a Ambuye.”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 22 M’nkhani ya Andrej Hanák yomwe ili mu Galamukani! ya Chingelezi ya pa April 22, 2002, pa masamba 19 mpaka 24 analongosolamo mmene zinthu zinalili kundendeko komanso zimene zinachitika ku Cservenka, zomwe tizifotokoze kutsogoloku.

^ ndime 28 Onani Nsanja ya Olonda ya July 15 1993, tsamba 11, kuti mumve zina zokhudza András Bartha.

^ ndime 39 Onani nkhani yake mu Nsanja ya Olonda ya pa September 1, 1998, pa masamba 24 mpaka 28.

[Chithunzi patsamba 30]

Ineyo ndi Anna, patatha chaka chimodzi titakwatirana

[Zithunzi patsamba 31]

Ineyo ndi Mbale Nathan H. Knorr pamsonkhano wa mu 1947 ku Brno