Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Maso a Chiwombankhanga

Maso a Chiwombankhanga

Maso a Chiwombankhanga

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU SPAIN

MUNTHU ukakhala wakuthwa maso, anthu a ku Spain amati uli ndi maso a chiwombankhanga. Ajeremani nawonso ali ndi mawu ofanana ndi ameneŵa. Kwa zaka zambiri anthu akhala akugwiritsira ntchito kuthwa kwa maso a chiwombankhanga m’miyambi, ndipo m’pomveka ndithu kutero. Buku la Yobu lomwe linalembedwa zaka zoposa 3000 zapitazo, limanena za chiwombankhanga kuti: “Maso ake achipenyetsetsa chili kutali.”—Yobu 39:27, 29.

Kodi chiwombankhanga chingaone patali motani makamaka? Buku lofotokoza za zinyama lakuti The Guinness Book of Animal Records limanena kuti: “Zinthu zikakhala kuti zili bwino, ziwombankhanga zina zingathe kuona kalulu akusuntha pang’onopang’ono ali pa mtunda wa makilomita oposa aŵiri.” Ena akuti izo zingathe kuona patali kuposa pamenepo!

N’chifukwa chiyani maso a chiwombankhanga ali akuthwa choncho? Choyamba, maso a ziwombankhanga zimene zimaona patali kwambiri kuposa zina zonse n’ngakuluakulu kwambiri. Buku lakuti Book of British Birds limati maso a ziwombankhanga za mtunduwu “ngakuluakulu kwambiri moti angamazilepheretse kuuluka bwino ngati atangoposa pamenepo.”

Komanso, diso la chiwombankhanga lili ndi mitsempha yambiri kuŵirikiza kasanu kuposa mitsempha yomwe ili m’maso mwathu. Motero, chili ndi mitsempha yambiri yotenga mauthenga kuchoka m’maso kupita nawo ku ubongo ndipo ndi yochuluka moŵirikiza kaŵiri kuposa yathu. M’posadabwitsa kuti mbalame zimenezi sizivutika m’pang’ono pomwe kuti zisiyanitse mitundu ya zinthu. Ndipo chotsirizira n’chakuti mbalame zodya nyama zina, mofanana ndi mbalame zina zonse, zili ndi maso omwe savutikira kuona chinthu chomwe chili pafupi komanso nthaŵi yomweyo n’kuona chomwe chili patali. Apanso, maso athu sangafanane ndi maso a mbalamezi ngakhale pang’ono.

Ziwombankhanga zimaona bwino kwambiri masana, koma usiku sizingapose akadzidzi. Mbalame zosaka usiku zimenezi zili ndi maso amphamvu ndiponso akuluakulu omwe amatha kuona bwino usiku. Moti usiku kadzidzi amaona bwino kwambiri kuŵirikiza maulendo 100 kuposa mmene anthufe timaonera usikuwo. Komabe, mwakamodzikamodzi kukakhala mdima wandiweyani, kadzidzi amasaka pomvetsera mwatcheru mtswatswa kapena kuweresa kwa tinyama.

Kodi ndani anachititsa mbalamezi kuti zizitha kuchita zinthu zotere? Mulungu anafunsa Yobu kuti: “Kodi chiwombankhanga chikwera m’mwamba pochilamulira iwe?” N’zodziŵikiratu kuti palibe munthu aliyense amene anganene kuti ndiye anachita zodabwitsazi. Ngakhale Yobuyo anavomera modzichepetsa kuti: “Ndidziŵa kuti [inu Yehova] mukhoza kuchita zonse.” (Yobu 39:27; 42:1, 2) Maso a chiwombankhanga ndi umboni winanso wa nzeru za Mlengi wathu.

[Chithunzi patsamba 21]

Chiwombankhanga

[Chithunzi patsamba 21]

Kadzidzi