Ndinasiya Khalidwe Lokakala Mtima
Ndinasiya Khalidwe Lokakala Mtima
YOSIMBIDWA NDI JOSÉ GOMEZ
NDINABADWA pa September 8, 1964, m’tauni yaing’ono yotchedwa Rognac kum’mwera kwa dziko la France. Makolo anga ndi agogo a mbali zonse ziŵiri anali a mtundu wotchedwa Gypsy wa ku Andalusia, ndipo ena anabadwira ku Algeria, ena ku Morocco, kumpoto kwa Africa. Kumtundu kwathu tinalipo gulu ndithu, ndipo izi sizachilendo kwa a Gypsy.
Bambo anga anali munthu wandewu koopsa, ndipo zinthu zina zimene ndimakumbukira ndili mwana kwambiri ndi zinthu monga bambowo akumenya amayi anga. Kenaka amayi anaganiza zongowasudzula. Zimenezi sizichitikachitika pakati pa a Gypsy. Amayiwo anatenga ineyo, mchimwene wanga ndi mchemwali wanga n’kupita nafe ku Belgium komwe tinakhalako zaka zisanu ndi zitatu mwamtendere.
Komabe zinthu zinadzasintha. Anafe tinkafuna kuonana ndi bambo athu, choncho tinabwereranso ndi amayi ku France n’kukayambiranso kukhala limodzi ndi bambowo. Kukhaliranso limodzi ndi bambo kunandiika pampanipani kwambiri. Pamene tinali ku Belgium ndi amayi, tinkapita nawo kulikonse kumene tikufuna. Koma kwawo kwa bambo, amati amuna amafunika kucheza ndi amuna anzawo basi. Amuna anali ndi kamtima koti iwo ndiwo ali amfulu ndipo akazi ndiwo akapolo. Mwachitsanzo, tsiku linalake pamene ndinkafuna kuthandiza azakhali anga kuchotsa mbale patebulo ndiponso kuzitsuka titamaliza kudya, bambo anga aang’ono anandinyoza, n’kundinena kuti ndine mkazi weniweni. Kumtundu kwawo amati kutsuka mbale ndi ntchito yogwira azimayi basi. M’kupita kwa nthaŵi, maganizo opondereza akaziŵa anandiloŵerera.
Sipanatenge nthaŵi yaitali n’komwe kuti bambo ayambirenso khalidwe lawo lija lowamenya koopsa amayi. Kangapo konse ine ndi mchimwene wanga tikafuna kuleletsa amayiwo, bambowo ankazipulumutsa zibakera, ife n’kuthaŵira pawindo. Ngakhale mchemwali wathunso ankakumana nazo. Ndiye chifukwa chake nthaŵi zambiri sindinkakonda kukhala pakhomo. Ndinakwanitsa zaka 15 ndisakudziŵa kwenikweni kuti tsogolo langa lidzakhala lotani.
Mapeto ake ndinayamba kutchuka chifukwa cha khalidwe lokonda ndewu. Ndinkakonda kupezerera anzanga. Nthaŵi zina ndinkachita kuwaputa dala ena ochepa msinkhu kwa ine, koma ambiri sankayerekeza kundichitira mwano, makamaka chifukwa chakuti nthaŵi zambiri ndinkayenda ndi mpeni kapena tcheni. Posakhalitsa ndinayamba kuba galimoto n’kumagulitsa. Nthaŵi zina ndinkangoziyatsa basi ndipo ndikamaona ozimitsa moto akulimbana ndi motowo ine si kusangalala kwake. Kenaka ndinayamba kuswa ndi kuba m’masitolo ndiponso m’nyumba zosungiramo katundu. Anandimanga kangapo konse. Ndipo ndinkati akandimanga, ndinkapemphera kuti Mulungu andithandize!
Inde sindingakane, Mulungu yekha ndinkam’khulupirira ndithu. Panthaŵi imene tinali ku Belgium, ndinaphunzirapo pasukulu ya Akatolika. Choncho ndinkadziŵa ndithu kuti zimene ndinali kuchitazo zinali zoipa. Komabe ngakhale kuti Mulungu ndinkam’khulupirira choncho, sindinasinthe khalidwe langalo. Ndinkangoti chachikulu apa n’kum’pempha ndipo ndikatero ndiye kuti andikhululukira machimo anga.
M’chaka cha 1984, anandilamula kuti ndikhale m’ndende kwa miyezi 11 chifukwa cha kuba. Ananditumiza kundende ya Baumettes, yomwe ili ku Marseilles. Ndili kundendeku, ndinadzilembalemba m’malo osiyanasiyana
pathupi langa. Penapake ndinadzilemba kuti ndine “chirombo cham’mudzi.” Zoti anthu amasintha akapita kundende, kwa ine zimenezo kunalibiretu koma zinangowonjezera kuti ndikhale wokakala mtima kwambiri kwa akuluakulu oimira boma ndi anthu ena onse. Atandimasula, nditatha miyezi itatu yokha ndili m’ndende, ndinasanduka chimunthu chokakala mtima kwambiri kuposa mmene ndinalili poyamba. Kenaka titakumana ndi tsoka linalake, ndinasanduka chimbalangondo chenicheni.Ndinkangoti Zivute Zitani Ndithana Nawo Basi
Tsiku linalake anthu akwathu anayambana ndi a kubanja lina la mtundu wathu womwewu. Ineyo pamodzi ndi azichimwene a bambo anga tinaganiza zokakumana nawo maso ndi maso kuti nkhaniyo ingotha. Iwowo ngakhalenso ifeyo tinali ndi zida. Ndiye mkangano utabuka pokambiranapo, akulu awo a bambo anga dzina lawo a Pierre ndiponso mbale wawo winawake anaomberedwa n’kuferatu pompo. Zimenezi zinandipengetsa moti ndinaimirira mumsewu mfuti ili kumanja n’kumalalata ndikulilima nawo ukali. Wina wa azichimwene a bambo angawo analimbana nane kwabasi kuti andilande mfutiyo.
Imfa ya bambo anga aakuluwo, omwe ineyo ndinkangowatenga ngati bambo anga enieni inandipweteka kwabasi. Ndinachita nawo mwambo wa maliro monga mmene zimakhalira kumtundu kwathu. Ndinakhala masiku ambirimbiri osameta ndevu kapena kudya nyama iliyonse. Ndinafika mpaka pokana kuonera TV kapena kumvera nyimbo. Ndinalumbira kuti zivute zitani ndibwezera basi imfa ya bambowo, koma achibale sankandilola n’komwe kutenga mfuti.
M’mwezi wa August m’chaka cha 1984, mwalamulo ndinafunika kuti ndipite kunkhondo. Ndinali ndi zaka 20 pamene ndinalembetsa kuti ndikhale nawo m’gulu la asilikali othandiza bungwe la United Nations lokakhazikitsa bata m’dziko la Lebanon. Zakupha munthu kapena kuphedwa ndinalibe nazo ntchito ngakhale pang’ono. Panthaŵi imeneyo n’kuti ndikusuta chamba mogometsa. Chambacho chinkandipangitsa kuti moyo ndizingoumva kukoma nthaŵi iliyonse komanso kuti ndizingoona ngati palibe chilichonse chingandivulaze.
Ku Lebanon kunali kosavuta kupeza zida, choncho ndinaganiza zotumiza zida zina kwathu ku France kuti ndikapitirize zofuna zanga zobwezera imfa ya ang’ono awo a bambo anga aja. Ndinagula mfuti za volovolo ziŵiri ndi zipolopolo zake kwa anthu a ku Lebanon komweko. Ndinamasulamasula mfutizo n’kuzibisa mu wailesi ziŵiri kenaka n’kuzitumiza kumudzi.
Kutangotsala masabata aŵiri kuti timalize ntchito yathu ya nkhondoyo, ine ndi anzanga ena atatu tinangochokapo kaye osatsazika. Titabwerera kuntchitoko anatimanga n’kutitsekera komweko. Tidakali m’ndende choncho, ndinamulusira msilikali yemwe ankatilondera. Sin’kadalola ngakhale pang’ono kuti kamunthu wamba, kosati kamtundu wathu, kazindisoŵetsa mtendere ineyo m’Gypsy. M’maŵa mwake ndinamenyananso ndi msilikali wina, ndipo uyu anali bwana. Zitatero ananditumiza kundende ya ku Lyons yotchedwa Montluc komwe ndinakhalako kwa nthaŵi yonse imene inatsala kuti ndimalize ntchito yanga yankhondoyo.
Ndinayamba Kusintha Ndili Kundende
Tsiku langa loyamba ndili kundende kumeneku, mnyamata winawake anandipatsa moni mwansangala kwabasi. Ndinamva kuti iyeyu anali wa Mboni za Yehova ndiponso kuti ena a m’gulu lomweli anali m’ndendemo chabe chifukwa chakuti sagwiritsira ntchito zida zankhondo. Zimenezo zinandidabwitsa kwambiri. Zinandipangitsa kufuna kuti ndimvetsetse.
Ndinaona kuti anthu a Mboni za Yehova amakondadi Mulungu kwambiri, ndipo makhalidwe awo abwino kwambiri ananditenga mtima. Koma mafunso ndinali nawobe ambirimbiri. Makamaka ndinkafuna kudziŵa ngati zinalidi zoona kuti akufa amalankhula ndi amoyo kudzera m’maloto, chifukwa zimenezi n’zimene anthu amtundu wathu amakhulupirira. Wa Mboni wina dzina lake Jean-Paul anadzipereka kuphunzira nane Baibulo pogwiritsira ntchito buku la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso Padziko Lapansi. *
Buku lonselo ndinaliŵerenga tsiku limodzi lokha usiku, ndipo zonse zimene ndinaŵerengazo zinandikhudza kwambiri. Ndinayambadi kusintha ndili kundendeku! Nthaŵi yanga yondimasula itafika, ndinakwera sitima ya pamtunda ulendo wa kunyumba, kwinaku nditanyamula chikwama changa chili ndi mabuku ofotokoza za m’Baibulo okhaokha.
Kuti ndipezane ndi a Mboni kwathuko, ndinapita ku Nyumba ya Ufumu ya ku Martigues. Ndinapitirizabe kuphunzira Baibulo, ndipo panthaŵiyi mnyamata wina dzina lake Eric yemwe anali mtumiki wanthaŵi zonse ndiye ankaphunzira nane. Patangotha masiku ochepa chabe, ndinasiya kusuta ndipo ndinasiyanso kuonana ndi anzanga akale amenenso anali zigandanga. Ndinatsimikiza ndi mtima wanga wonse kuchita zinthu mogwirizana ndi mawu a pa Miyambo 27:11, amene amati: “Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.” Yehova ndiye Atate wachikondi amene ndinkafuna kuti ndizim’kondweretsa.
Kunali Kovutirapo Kuti Ndisinthiretu
Kuti ndizitsatira mfundo zabwino za Chikristu sinali nkhani yamaseŵera. Mwachitsanzo nthaŵi inayake ndinayambiranso kusuta chamba ndipo panatenga masabata angapo kuti ndisiyenso. Koma nkhani yaikulu yomwe siinkandigonetsa tulo inali yoti ndiiwaliretu zofuna kubwezera zija. Nthaŵi zonse ndinkayenda ndi mfuti ndipo ndinkakonzabe chiwembu chofuna kubwezera anthu amene anapha bambo anga aja, koma zimenezi Eric sankazidziŵa. Nthaŵi zambiri ndinkayenda usiku wonse powasakasaka.
Nditamuuza Eric nkhani imeneyi, iye sanandibisire mawu pondiuza kuti Mulungu sangagwirizane nane n’komwe ndikamayenda ndi zida pofuna kubwezera. Apa, ndinafunika kuti ndisankhe chimodzi. Ndinaganizira mozama mawu a mtumwi Paulo a pa Aroma 12:19, akuti: “Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo.” Mawu ameneŵa komanso kupemphera mochokera pansi pamtima, kunandithandiza kuphwetsa ukali wanga. (Salmo 55:22) Kenaka ndinataya zida zangazo. Pa December 26, 1986, nditaphunzira Baibulo kwa chaka chathunthu, ndinaonetsa kuti ndadzipereka kwa Yehova Mulungu pobatizidwa m’madzi.
Akwathu Ananditsatira
Kusintha khalidwe langa kunapangitsa kuti makolo anga ayambe kuphunzira Baibulo. Anabwererana ukwati, ndipo mayi anga anabatizidwa m’mwezi wa July m’chaka cha 1989. Patapita kanthaŵi, achibale anga ena angapo anamvera uthenga wa m’Baibulo ndipo panopa ndi Mboni za Yehova.
Mu August m’chaka cha 1988, ndinaganiza zoti ndikhale mtumiki wa nthaŵi zonse. Kenaka ndinayamba kukondana ndi kamtsikana kenakake ka mumpingo wathu dzina lake Katia, ndipo tinakwatirana pa June 10, 1989. Chaka chathu choyamba chinali chovuta chifukwa chakuti ineyo ndinali ndisanasinthiretu maganizo anga ndikamaona munthu wamkazi. Zinkandivuta kutsatira mawu a pa 1 Petro 3:7, amene amalimbikitsa amuna kulemekeza akazi awo. Nthaŵi zambiri ndinkapemphera kuti Mulungu andithandize kuthetsa kudzikuza kwangaku ndi kusintha mmene ndimaganizira. Pang’ono ndi pang’ono zinthu zinasinthadi.
Imfa ya bambo anga aang’ono imandipwetekabe, ndipo nthaŵi zina misozi imangotuluka ndikayamba kuwaganizira. Ndikaganiza mmene anafera, zimandisoŵetsa mtendere kwambiri. Kwa zaka zingapo, ngakhale kuchokera panthaŵi imene ndinabatizidwa, ndinakhala ndikuopa kuti kaya zingadzathe bwanji nditangoti gululu, kukumanizana ndi wina aliyense wa kubanja limene linatiphera bambo anga aang’ono lija. Atayamba kulimbana nane ndingatani? Kodi sadzandikumbutsa zamakedzana?
Tsiku lina ndinakakamba nkhani ya onse mumpingo winawake wa kufupi ndi kwathu. Ndiye ndinaona mbale wa anthu amene anapha ang’ono awo abambo anga aja, dzina lake Pepa. Koma ndisaname, nditangomuona thupi langa lonse linayendayenda, ndipo ndinatsala pang’ono kuiwala zoti ndine Mkristu. Koma zonsezo ndinangozikankhira kunkhongo basi. Kenaka tsiku limene iyeyo anabatizidwa, ndinam’kumbatira n’kumuthokoza kwambiri chifukwa chakuti anasankha kutumikira Yehova. Ndinaiwaliratu zonse zija zimene zinachitika n’kumamuona kuti ndi mlongo wanga wauzimu basi.
Ndimathokoza Yehova tsiku lililonse chifukwa chondithandiza kusiyana nalo khalidwe lokakala mtimali. Chipanda Yehova kundichitira chifundo, bwenzi ndili pati kodi? Banja langa likuyenda bwino chifukwa cha iyeyo. Panopa ndimakhulupiriranso kuti m’tsogolomu tidzakhala ndi dziko latsopano lopanda anthu okakala mtima kapena andewu. Kunena zoona, sindikukayikira n’komwe kuti lonjezo la Mulungu lakuti: “Adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwaopsa; pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu padanena,” lidzakwaniritsidwadi.—Mika 4:4.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 18 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Chithunzi patsamba 19]
Apa, ndinali m’gulu la bungwe la United Nations lokhazikitsa bata ku Lebanon, mu 1985
[Chithunzi patsamba 20]
Ineyo ndi mkazi wanga Katia pamodzi ndi ana athu, Timeo ndi Pierre